Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Beginning

Read the Bible from start to finish, from Genesis to Revelation.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Machitidwe a Atumwi 9-10

Kutembenuka Mtima kwa Saulo

Pa nthawi imeneyi, Saulo ankaopsezabe okhulupirira Ambuye nafuna kuwapha. Iye anapita kwa mkulu wa ansembe, ndi kukapempha makalata a chilolezo kuti apite nawo ku masunagoge a ku Damasiko, kuti ngati atakapezeka ena kumeneko otsata Njirayo, kaya ndi amuna kapena amayi, akawamange ndi kuwatenga kubwera nawo ku Yerusalemu. Akuyandikira ku Damasikoku paulendo wake, mwadzidzidzi kuwala kochokera kumwamba kunamuzungulira iye. Iye anagwa pansi ndipo anamva mawu akuti, “Saulo, Saulo ukundizunziranji Ine?”

Saulo anafunsa kuti, “Ndinu yani Ambuye?”

Ambuye anayankha kuti, “Ndine Yesu amene iwe ukumuzunza.” “Tsopano dzuka, lowa mu mzindamo, ndipo udzawuzidwa zoyenera kuchita.”

Anthu amene anali naye paulendo, anasowa chonena; iwo anamva mawu koma sanaone wina aliyense. Saulo anayimirira, ndipo pamene anatsekula maso ake sanathe kuona. Kotero anamugwira dzanja ndi kulowa naye mu Damasiko. Anakhala wosaona kwa masiku atatu ndiponso sanadye kapena kumwa kanthu kalikonse.

10 Ku Damasiko kunali wophunzira wina dzina lake Hananiya. Ambuye anamuyitana mʼmasomphenya kuti, “Hananiya!”

Iye anayankha kuti, “Ine Ambuye.”

11 Ambuye anamuwuza iye kuti, “Nyamuka, pita ku nyumba ya Yudasi imene ili pa Njira Yolunjika ndipo ukafunse za munthu wochokera ku Tarisisi dzina lake Saulo, pakuti akupemphera. 12 Ndipo waona mʼmasomphenya munthu, dzina lake Hananiya atabwera ndi kumusanjika manja kuti aonenso.”

13 Hananiya anayankha kuti, “Ambuye, ndinamva zambiri za munthu uyu ndi zonse zoyipa anachitira oyera mtima a ku Yerusalemu. 14 Ndipo wabwera kuno ndi ulamuliro wa akulu ansembe kuti adzamange onse amene amayitana pa dzina lanu.”

15 Koma Ambuye anati kwa Hananiya, “Pita! Munthu uyu ndi chida changa chosankhika chonyamulira dzina langa pamaso pa anthu a mitundu ina ndi mafumu awo ndiponso kwa anthu a Israeli. 16 Ine ndidzamuonetsa zowawa zonse zimene ayenera kumva chifukwa cha dzina langa.”

17 Pamenepo Hananiya ananyamuka ndi kukalowa mʼnyumbayo. Anamusanjika manja Sauloyo ndipo anati, “Mʼbale Saulo, Ambuye Yesu, amene anakuonekera pa msewu pamene umabwera kuno wandituma kuti uwonenso ndi kudzazidwa ndi Mzimu Woyera.” 18 Nthawi yomweyo mʼmaso mwa Saulo munachoka zinthu zokhala ngati mamba ansomba, ndipo anayambanso kuona. Iye anayimirira nabatizidwa, 19 ndipo atadya chakudya, anapezanso mphamvu.

Saulo Alalikira ku Damasiko

Saulo anakhala masiku angapo ndi ophunzira a ku Damasiko. 20 Posakhalitsa anayamba kulalikira mʼsunagoge kuti Yesu ndiye Mwana wa Mulungu. 21 Onse amene anamva iye akulalikira anadabwa ndipo anafunsa kuti, “Kodi uyu si munthu amene anayambitsa kuzunza okhulupirira ku mpingo wa ku Yerusalemu? Kodi siwabwera kuno kuti awamange ndi kuwapereka kwa akulu a ansembe?” 22 Koma mphamvu za Saulo zinali kukulirakulira ndipo anathetsa nzeru Ayuda okhala ku Damasiko powatsimikizira kuti Yesu ndi Mpulumutsi.

23 Patapita masiku ambiri, Ayuda anapangana zoti aphe Saulo, 24 koma iye anadziwa za chiwembucho. Anthu ankadikirira usana ndi usiku pa zipata za mzindawo kuti amuphe. 25 Koma ophunzira ake anamutenga usiku, namutsitsira kunja kwa mpandawo mʼdengu.

Saulo ku Yerusalemu

26 Saulo atafika ku Yerusalemu, anayesetsa kulowa mʼgulu la ophunzira koma onse anamuopa chifukwa sanakhulupirire kuti anali wophunziradi. 27 Koma Barnaba anamutenga napita naye kwa atumwi. Iye anawafotokozera iwo za mmene Saulo anaonera Ambuye pa njira paja, ndi kuti Ambuye anamuyankhula, ndi momwe analalikira ku Damasiko mʼdzina la Yesu mosaopa. 28 Kotero Saulo anakhala nawo nayendayenda mwaufulu mu Yerusalemu akulalikira molimba mtima mʼdzina la Ambuye. 29 Anayankhula ndi kutsutsana ndi Ayuda a Chihelene, koma iwo ankafuna kumupha. 30 Abale atadziwa zimenezi, anamutenga Saulo ndi kupita naye ku Kaisareya, ndipo anamutumiza ku Tarisisi.

31 Pamenepo mpingo wa ku Yudeya konse, ku Galileya ndi ku Samariya unakhala pamtendere, unalimbikitsidwa; ndi kupatsidwa mphamvu ndi Mzimu Woyera, unakula mʼchiwerengero, ndi kukhala moopa Ambuye.

Eneya ndi Tabita

32 Pamene Petro amayendera mpingo, anapita kukachezera oyera mtima a ku Luda. 33 Kumeneko anakapeza munthu dzina lake Eneya, wofa ziwalo amene anagona pa mphasa kwa zaka zisanu ndi zitatu. 34 Petro anati kwa iye, “Eneya, Yesu Khristu akukuchiritsa iwe, dzuka ndipo yalula mphasa yako.” Nthawi yomweyo Eneya anayimirira. 35 Anthu onse amene anakhala ku Luda ndi ku Sharoni anamuona ndipo anatembenukira kwa Ambuye.

36 Ku Yopa kunali wophunzira wina dzina lake Tabita (mʼChigriki amati Dorika) amene nthawi zonse ankachita zachifundo ndiponso kuthandiza osauka. 37 Nthawi imeneyi anadwala ndipo anamwalira, anasambitsa thupi lake, namugoneka mʼchipinda chammwamba. 38 Popeza ku Yopa kunali pafupi ndi Luda; pamene ophunzira anamva kuti Petro anali ku Luda, anatuma anthu awiri kuti akamudandaulire kuti, “Chonde bwerani kuno msanga!”

39 Petro ananyamuka, napita nawo, ndipo atafika anamutengera ku chipinda chammwamba. Amasiye onse anayima momuzungulira akulira ndi kumuonetsa mwinjiro ndi zovala zina zimene Dorika ankapanga akanali moyo.

40 Petro anatulutsa anthu onse mʼchipindamo; ndipo anagwada pansi ndi kupemphera. Anatembenukira mtembo uja nati, “Tabita, dzuka,” Tabita anatsekula maso ake, ndipo ataona Petro anakhala pansi. 41 Petro anamugwira dzanja, namuyimiritsa. Ndipo anayitana okhulupirira ndi amasiye namupereka wamoyo. 42 Zimenezi zinadziwika ku Yopa konse, ndipo anthu ambiri anakhulupirira Ambuye. 43 Petro anakhala ku Yopa kwa masiku ambiri kwa munthu wina, dzina lake Simoni, mmisiri wa zikopa.

Kenturiyo Korneliyo Ayitana Petro

10 Ku Kaisareya kunali munthu wina dzina lake Korneliyo, mkulu wa asilikali 100 wa gulu la Italiya. Iye ndi banja lake lonse amapembedza ndi kuopa Mulungu. Iye amathandiza osowa mowolowamanja ndipo amapemphera kwa Mulungu nthawi zonse. Tsiku lina, nthawi ili ngati 3 koloko masana, anaona masomphenya. Anaona bwino ndithu mngelo wa Mulungu, amene anabwera kwa iye ndi kuti, “Korneliyo.”

Korneliyo anamuyangʼanitsitsa mngeloyo mwa mantha. Iye anafunsa kuti, “Nʼchiyani kodi Ambuye?”

Mngelo anayankha kuti, “Mapemphero ako ndi zachifundo zako zafika pamaso pa Mulungu ngati chikumbutso. Tsopano tuma anthu apite ku Yopa kuti akayitane munthu dzina lake Simoni Petro. Iye akukhala ndi Simoni mmisiri wa zikopa, amene nyumba yake ili mʼmbali mwa nyanja.”

Mngeloyo anayankhula naye anachoka, Korneliyo anayitana antchito ake awiri ndiponso msilikali mmodzi wa iwo amene ankamutumikira yemwe ankapembedza Mulungu. Iye anawafotokozera zonse zimene zinachitika ndipo anawatuma kuti apite ku Yopa.

Masomphenya a Petro

Mmawa mwake, nthawi ili ngati 12 koloko anthuwo atayandikira mzindawo, Petro anakwera pa denga kukapemphera. 10 Iye anamva njala ndipo anafuna chakudya, ndipo akukonza chakudyacho, iye anachita ngati wakomoka. 11 Iye anaona kuthambo kutatsekuka, ndi chinthu china chikutsitsidwa pansi chooneka ngati chinsalu chachikulu chomangidwa pa msonga zake zinayi. 12 Mʼmenemo munali nyama zonse zamiyendo inayi pamodzinso ndi zokwawa za dziko lapansi ndiponso mbalame zamlengalenga. 13 Petro anamva mawu akuti, “Petro, dzuka, ipha nudye.”

14 Petro anayankha kuti, “Ayi, Ambuye! Ine sindinadyepo kanthu kosayeretsedwa kapena konyansa.”

15 Petro anamvanso kachiwiri mawu akuti, “Usachiyese chonyansa chimene Mulungu wachiyeretsa.”

16 Zimenezi zinachitika katatu ndipo nthawi yomweyo chinsalu chija chinatengedwanso kupita kumwamba.

17 Petro akuganizira za tanthauzo la masomphenyawo, anthu amene Korneliyo anawatuma anapeza kumene kunali nyumba ya Simoni ndipo anayima pa chipata. 18 Iwo anayitana nafunsa ngati Simoni amene amadziwika ndi dzina loti Petro amakhala kumeneko.

19 Petro akuganizirabe za masomphenyawo, Mzimu Woyera anati kwa iye, “Simoni, anthu atatu akukufunafuna. 20 Dzuka, tsika. Usakayike upite nawo pakuti ndawatuma ndine.”

21 Petro anatsika ndipo anati kwa anthuwo, “Amene mukufunayo ndine. Mwabwera kuno chifukwa chiyani?”

22 Anthuwo anayankha kuti, “Ife tachokera kwa Korneliyo, mkulu woyangʼanira asilikali 100. Iye ndi munthu wolungama ndiponso woopa Mulungu, amene amalemekezedwa ndi Ayuda onse. Mngelo woyera anamuwuza kuti mupite ku nyumba yake kuti akamve mawu amene inu mukanene.” 23 Pamenepo Petro anawalowetsa mʼnyumba ndipo anawasamala ngati alendo ake. Mmawa mwake Petro ananyamuka napita nawo ndipo abale ena a ku Yopa anapita naye pamodzi.

Petro ku Nyumba ya Korneliyo

24 Tsiku linalo Petro anafika ku Kaisareya. Korneliyo anawadikirira ndipo anali atawasonkhanitsa pamodzi abale ake ndi abwenzi ake a pamtima. 25 Petro akulowa mʼnyumba, Korneliyo anakumana naye ndipo anadzigwetsa pa mapazi ake namulambira. 26 Koma Petro anamuyimiritsa nati, “Imirira, inenso ndine munthu ngati iwe.”

27 Akuyankhula naye, Petro analowa mʼnyumba ndipo anapeza gulu lalikulu la anthu litasonkhana. 28 Iye anawawuza kuti, “Inu mukudziwa bwino kuti ndi kutsutsana ndi lamulo ngati Myuda ayanjana ndi Mkunja kapena kuyendera wina aliyense wa mtundu wina. Koma Mulungu wandionetsa ine kuti ndisatchule munthu aliyense kuti ndi wosayenera kapena wonyansa. 29 Nʼchifukwa chake ndabwera mosawiringula pamene munandiyitana. Tsopano ndikufunseni,” Mwandiyitanira chiyani?

30 Komeliyo anayankha kuti, “Masiku anayi apitawo, nthawi yonga yomwe ino, 3 koloko masana ndimapemphera mʼnyumba mwanga. Mwadzidzidzi patsogolo panga panayimirira munthu wovala zovala zonyezimira. 31 Ndipo anati, ‘Korneliyo, Mulungu wamva mapemphero ako ndipo wakumbukira mphatso zako kwa osauka. 32 Tuma anthu ku Yopa akayitane Simoni wotchedwa Petro. Iye akukhala mʼnyumba ya Simoni mmisiri wazikopa amene amakhala mʼmbali mwa nyanja.’ 33 Nʼchifukwa chake ndinatumiza anthu nthawi yomweyo ndipo mwachita bwino kuti mwabwera. Tsopano ife tonse tili pano pamaso pa Mulungu kuti timve zonse zimene Ambuye akukulamulani kuti mutiwuze ife.”

34 Ndipo Petro anayamba kuyankhula nati, “Zoonadi, tsopano ndazindikira kuti Mulungu sakondera. 35 Koma amalandira anthu a mtundu uli wonse amene amaopa Iye ndiponso kuchita chilungamo. 36 Uwu ndi uthenga umene Mulungu anatumiza kwa Aisraeli, kulalikira Uthenga Wabwino wamtendere mwa Yesu Khristu amene ndi Ambuye wa onse. 37 Inu mukudziwa zimene zinachitika ku Yudeya konse, kuyambira ku Galileya pambuyo pa ubatizo umene Yohane analalikira, 38 kuti Mulungu, anamudzoza Yesu, wa ku Nazareti ndi Mzimu Woyera ndi mphamvu ndiponso mmene Iye anapita nachita zabwino ndi kuchiritsa onse amene anali pansi pa mphamvu ya mdierekezi, popeza kuti Mulungu anali naye.

39 “Ife ndife mboni za zonse zimene anachita mʼdziko la Ayuda ndiponso ku Yerusalemu. Anamupha Iye pakumupachika pa mtengo, 40 koma Mulungu anamuukitsa kwa akufa pa tsiku lachitatu, ndipo analola kuti aonekere poyera. 41 Iye sanaonekere kwa anthu onse koma kwa mboni zimene Mulungu anazisankhiratu, kwa ife amene timadya ndi kumwa naye atauka kwa akufa. 42 Iye anatilamulira ife kuti tilalikire kwa anthu ndi kuchitira umboni kuti Iye ndiye amene Mulungu anamusankha kukhala woweruza wa amoyo ndi akufa. 43 Aneneri onse achitira Iye umboni kuti aliyense amene akhulupirira Iye amakhululukidwa machimo chifukwa cha dzina lake.”

44 Petro akuyankhulabe mawu amenewa, Mzimu Woyera unatsikira pa onse amene amamva uthengawo. 45 Abale a mdulidwe omwe anabwera ndi Petro anadabwa kuona kuti mphatso ya Mzimu Woyera yapatsidwanso kwa anthu a mitundu ina. 46 Pakuti anamva iwo akuyankhula mʼmalilime ndi kuyamika Mulungu. Ndipo Petro anati, 47 “Kodi alipo amene angawaletse anthu awa kubatizidwa mʼmadzi? Iwotu alandira Mzimu Woyera monga ifenso.” 48 Tsono iye analamula kuti abatizidwe mʼdzina la Yesu Khristu. Ndipo anthu aja anamupempha Petro kuti akhale nawo masiku angapo.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.