Beginning
Lonjezo la Mzimu Woyera
1 Mʼbuku langa loyamba, ndinakulembera iwe Teofilo zonse zimene Yesu anayamba kuchita ndi kuphunzitsa, 2 mpaka tsiku limene anatengedwa kupita kumwamba, mwamphamvu ya Mzimu Woyera, atawalangiza atumwi amene anawasankha. 3 Zitatha zowawa zake Yesu anadzionetsa kwa ophunzira ake, ndi kuonetsanso maumboni ambiri kuti anali wamoyo. Iye anadzionetsera kwa iwo ndi kuwaphunzitsa za ufumu wa Mulungu pa masiku makumi anayi. 4 Nthawi ina atasonkhana nawo pamodzi, Yesu analamulira ophunzira ake kuti, “Musachoke mu Yerusalemu, koma mudikire mphatso imene Atate anga analonjeza yomwe ndinakuwuzani. 5 Pakuti Yohane anakubatizani ndi madzi, koma posachedwapa inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera.”
Yesu Akwera Kumwamba
6 Atumwi atasonkhana pamodzi, iwo anamufunsa Iye kuti, “Ambuye, kodi nthawi ino mubwezeretsa ufumu kwa Israeli?”
7 Yesu anawawuza kuti, “Sikofunika kuti mudziwe za nthawi kapena masiku amene Atate ayika mwa ulamuliro wawo. 8 Koma mudzalandira mphamvu Mzimu Woyera akadzafika pa inu; ndipo mudzakhala mboni zanga mu Yerusalemu, ku Yudeya konse ndi ku Samariya, mpaka ku malekezero a dziko lapansi.”
9 Atatha kuyankhula zimenezi, Yesu anatengedwa kupita kumwamba ophunzira ake akuona, ndipo anabisika mʼmitambo.
10 Yesu akukwera kumwamba, ophunzira ake anayangʼanitsitsa ndi chidwi mʼmitambo. Mwadzidzidzi anaona anthu awiri ovala zoyera atayimirira pambali pawo. 11 Iwo anati, “Inu, anthu a ku Galileya, chifukwa chiyani mukuyima ndi kumayangʼana mʼmitambo? Yesu amene wachotsedwa pakati panu ndi kupita kumwamba, adzabweranso mʼnjira yomweyi mwamuona akupita kumwamba.”
Matiyasi Alowa Mʼmalo mwa Yudasi Isikarioti
12 Pamenepo atumwi anabwerera ku Yerusalemu kuchokera ku phiri la Olivi, mtunda wosakwana kilomita kuchokera mu mzindamo. 13 Atafika mu mzindamo, analowa mʼchipinda chammwamba kumene amakhala. Amene analipo anali awa: Petro, Yohane, Yakobo ndi Andreya; Filipo ndi Tomasi, Bartumeyu ndi Mateyu; Yakobo mwana wa Alifeyo ndi Simoni Zelote ndi Yuda mwana wa Yakobo. 14 Onsewa ndi mtima umodzi anapitiriza kupemphera pamodzi ndi amayi, ndi Mariya amayi ake a Yesu, ndiponso abale ake a Yesu.
15 Pa nthawi imeneyo Petro anayimirira pakati pa okhulupirira (gulu la anthu pafupifupi 120). 16 Iye anati, “Abale anga, Malemba anayenera kukwaniritsidwa omwe Mzimu Woyera anayankhula kalekale kudzera mwa Davide za Yudasi, amene anatsogolera amene anamugwira Yesu. 17 Iye anali mmodzi wa gulu lathu ndipo anatumikira pamodzi ndi ife.”
18 (Yudasi anagula munda ndi ndalama zimene anazipeza pochita zoyipa zija; kumeneko, iye anagwa chamutu, naphulika pakati ndipo matumbo ake wonse anakhuthuka. 19 Aliyense mu Yerusalemu anamva zimenezi, kotero anatcha mundawo mʼchiyankhulo chawo kuti Akeledama, kutanthauza, Munda wa Magazi).
20 Petro anati, “Pakuti kwalembedwa mʼbuku la Masalimo kuti,
“Nyumba yake isanduke bwinja,
ndipo pasakhale wogonamo.
Ndiponso,
“Wina atenge ntchito yake yautsogoleri.
21 Chifukwa chake ndi kofunika kusankha mmodzi wa anthu amene akhala nafe nthawi yonse imene Ambuye Yesu ankayenda nafe, 22 kuyambira pa nthawi ya ubatizo wa Yohane mpaka nthawi imene Yesu anatengedwa pakati pathu. Pakuti mmodzi wa anthu awa ayenera kukhala mboni pamodzi ndi ife zakuuka kwake.”
23 Pamenepo anasankha anthu awiri, Yosefe wotchedwa Barsaba (wodziwikanso kuti Yusto) ndi Matiyasi. 24 Kenaka iwo anapemphera nati, “Ambuye mukudziwa mtima wa aliyense. Tionetseni amene mwamusankha mwa awiri awa 25 kuti atenge ntchito iyi ya utumwi, imene Yudasi anasiya napita kumalo womuyenera.” 26 Tsono anachita maere, ndipo maerewo anagwera Matiyasi. Tsono iye anawonjezedwa pa gulu la atumwi khumi ndi mmodziwo.
Kubwera kwa Mzimu Woyera
2 Litafika tsiku la chikondwerero cha Pentekosite, onse anali pamodzi. 2 Mwadzidzidzi kunamveka mkokomo kuchokera kumwamba ngati wa mphepo yamphamvu, ndipo inadzaza nyumba yonse imene amakhala. 3 Iwo anaona zinthu zokhala ngati malilime amoto ogawikana ndipo anakhala pa aliyense wa iwo. 4 Ndipo onse anadzazidwa ndi Mzimu Woyera, nayamba kuyankhula mu ziyankhulo zina, monga Mzimu Woyerayo anawayankhulitsa.
5 Ayuda woopa Mulungu ochokera ku mayiko onse a dziko lapansi ankakhala mu Yerusalemu nthawi imeneyi. 6 Utamveka mkokomo uja, gulu la anthu linasonkhana. Anthuwo anadabwa chifukwa aliyense anawamva atumwiwo akuyankhula ziyankhulo zosiyanasiyana. 7 Mothedwa nzeru anafunsana kuti, “Kodi anthu onse amene akuyankhulawa si Agalileya? 8 Nanga bwanji aliyense wa ife akuwamva iwo mu chinenero cha kwawo? 9 Apanti, Amedi ndi Aelami; okhala ku Mesopotamiya, ku Yudeya ndi ku Kapadokiya, ku Ponto ndi ku Asiya, 10 ku Frugiya ndi Pamfiliya, ku Igupto ndi ku madera a ku Libiya kufupi ndi ku Kurene; alendo ochokera ku Roma, 11 Ayuda ndi otsatira chipembedzo cha Chiyuda onse pamodzi; Akrete ndi Aarabu, ife tonse tikuwamva akuyankhula za ntchito zodabwitsa za Mulungu mu ziyankhulo zathu.” 12 Modabwa ndi mothedwa nzeru anafunsana wina ndi mnzake kuti, “Zimenezi zikutanthauzanji?”
13 Koma ena anawaseka nati, “Aledzera vinyo watsopano.”
Uthenga wa Petro
14 Koma Petro anayimirira pamodzi ndi atumwi khumi ndi mmodziwo ndipo anakweza mawu ake nayankhula kwa gulu la anthu nati: “Ayuda anzanga, ndi nonse amene muli mu Yerusalemu, mvetsetsani izi ndipo tcherani khutu ku zimene ndikunena. 15 Kunena zoona, anthu awa sanaledzere ayi, monga momwe mukuganizira, pakuti ino ndi 9 koloko mmawa! 16 Koma izi ndi zimene ananena Mneneri Yoweli kuti:
17 “ ‘Mulungu akuti, mʼmasiku otsiriza
ndidzakhuthulira Mzimu wanga pa anthu onse.
Ana anu aamuna ndi aakazi adzanenera,
anyamata anu adzaona masomphenya,
nkhalamba zanu zidzalota maloto.
18 Ngakhalenso pa antchito anga aamuna ndi aakazi,
ndidzakhuthulira Mzimu wanga masiku amenewo,
ndipo iwo adzanenera.
19 Ndipo ndidzaonetsa zodabwitsa mlengalenga
ndi zizindikiro pa dziko lapansi pano,
ndizo magazi, moto ndi utsi watolotolo.
20 Dzuwa lidzadetsedwa
ndipo mwezi udzaoneka ngati magazi
lisanafike tsiku lalikulu ndi laulemerero la Ambuye.
21 Ndipo aliyense amene adzayitana
pa dzina la Ambuye adzapulumuka.’
22 “Inu Aisraeli mverani mawu awa; Yesu wa ku Nazareti anali munthu amene anaperekedwa kwa inu ndi Mulungu. Ndipo Mulungu anakutsimikizirani zimenezi ndi zamphamvu, zodabwitsa ndi zizindikiro zimene anachita mwa Iye pakati panu, monga inu mukudziwa. 23 Yesu ameneyu anaperekedwa kwa inu mwa kufuna ndi kudziwiratu kwa Mulungu; ndipo inu mothandizidwa ndi anthu oyipa, munamupha Iye pomupachika pa mtanda. 24 Koma Mulungu anamuukitsa kwa akufa, kumumasula Iye ku zowawa za imfa, chifukwa kunali kosatheka kuti agwiridwe ndi imfa. 25 Pakuti Davide ananena za Iye kuti,
“ ‘Ndinaona Ambuye pamaso panga nthawi zonse.
Chifukwa Iye ali kudzanja langa lamanja,
Ine sindidzagwedezeka.
26 Chifukwa chake mtima wanga ndi wokondwa ndipo lilime langa likukondwera;
thupi langanso lidzakhala ndi chiyembekezo.
27 Chifukwa simudzasiya moyo wanga kumalo a anthu akufa, ku manda,
kapena kulekerera Woyerayo kuti awole.
28 Inu munandidziwitsa ine njira zamoyo;
Inu mudzandidzaza ndi chimwemwe pamaso panu.’
29 “Abale, ine ndikuwuzani motsimikiza kuti kholo lathu Davide anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda, ndipo manda ake alipo lero lino. 30 Koma iye anali mneneri ndipo anadziwa kuti Mulungu analonjeza ndi lumbiro kuti adzayika mmodzi wa zidzukulu zake pa mpando waufumu. 31 Davide ataoneratu zimene zinali mʼtsogolo anayankhula za kuuka kwa Khristu, kuti Iye sanasiyidwe mʼmanda, ndipo thupi lake silinawole. 32 Mulungu wamuukitsa Yesu ameneyu, ndipo ife ndife mboni za zimenezi. 33 Khristu anakwezedwa kukhala kudzanja lamanja la Mulungu, nalandira Mzimu Woyera amene Atate anamulonjeza, ndipo watipatsa ife zimene mukuona ndi kumvazi. 34 Pakuti si Davide anakwera kumwamba koma iye akuti,
“ ‘Ambuye anawuza Ambuye anga kuti:
Khala kudzanja langa lamanja
35 mpaka nditasandutsa adani ako
kukhala chopondapo mapazi ako.’
36 “Nʼchifukwa chake, Aisraeli onse adziwe ndithu kuti, Yesu amene inu munamupachika, Mulungu wamuyika kukhala Ambuye ndiponso Mpulumutsi.”
37 Anthu atamva zimenezi, anatsutsika kwambiri mu mtima ndipo anati kwa Petro ndi atumwi enawo, “Abale, kodi ife tichite chiyani?”
38 Petro anawayankha kuti, “Lapani ndipo mubatizidwe aliyense wa inu, mʼdzina la Yesu Khristu kuti machimo anu akhululukidwe. Ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera. 39 Pakuti lonjezoli ndi lanu ndi ana anu ndiponso la onse amene ali kutali, ndi iwo onse amene Ambuye Mulungu wathu adzawayitane.”
40 Petro anawachenjeza ndi mawu ena ambiri, ndipo anawadandaulira iwo kuti, “Mudzipulumutse ku mʼbado owonongeka uno.” 41 Iwo amene anawulandira uthenga wake anabatizidwa ndipo tsiku lomwelo miyoyo pafupifupi 3,000 inawonjezedwa ku gulu lawo.
Kuyanjana kwa Okhulupirira
42 Iwo ankasonkhana pamodzi kuphunzitsidwa ndi atumwi, pachiyanjano, pachakudya ndi popemphera. 43 Aliyense ankachita mantha chifukwa cha zodabwitsa ndi zizindikiro zambiri zimene atumwi ankachita. 44 Okhulupirira onse anali pamodzi ndipo aliyense ankapereka zinthu zake kuti zikhale za onse. 45 Ankagulitsa minda yawo ndi katundu wawo, ndi kugawira kwa aliyense molingana ndi zosowa zake. 46 Tsiku ndi tsiku ankasonkhana pamodzi pa bwalo la pa Nyumba ya Mulungu. Ankadya pamodzi mʼnyumba zawo mwasangala ndi mtima woona. 47 Ankayamika Mulungu ndipo anthu onse ankawakomera mtima. Ndipo tsiku ndi tsiku Ambuye ankawonjezera ena pa chiwerengero cha olandira chipulumutso.
Petro Achiritsa Wolumala Miyendo
3 Tsiku lina Petro ndi Yohane ankapita ku Nyumba ya Mulungu kukapemphera nthawi ya 3 koloko masana. 2 Ndipo munthu wolumala chibadwire ankanyamulidwa tsiku ndi tsiku kukayikidwa pa khomo la Nyumbayo lotchedwa Khomo Lokongola kuti azikapempha amene amalowa ku bwalo la Nyumbayo. 3 Ataona Petro ndi Yohane ali pafupi kulowa anawapempha ndalama. 4 Iwo anamuyangʼanitsitsa iye. Kenaka Petro anati, “Tiyangʼane!” 5 Munthuyo anawayangʼanitsitsa kuyembekezera kuti alandira kanthu kuchokera kwa iwo.
6 Petro anati kwa iye, “Ine ndilibe siliva kapena golide, koma chimene ndili nacho ndikupatsa. Mʼdzina la Yesu Khristu wa ku Nazareti, yenda.” 7 Ndipo anamugwira dzanja lamanja, namuthandiza kuti ayimirire ndipo nthawi yomweyo mapazi ake ndi akakolo ake analimba. 8 Iye analumpha ndi kuyamba kuyenda. Kenaka analowa nawo pamodzi mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu, akuyenda ndi kulumpha ndiponso kuyamika Mulungu. 9 Anthu onse atamuona akuyenda ndiponso kuyamika Mulungu, 10 anamuzindikira kuti ndi yemwe uja ankakhala pa khomo la Nyumbayo lotchedwa Khomo Lokongola, ndipo anazizwa ndi kudabwa ndi zimene zinamuchitikira.
Petro Ayankhula kwa Anthu
11 Wopempha uja akuyenda pamodzi ndi Petro ndi Yohane, anthu onse anadabwa ndipo anawathamangira iwo kumalo wotchedwa Khonde la Solomoni. 12 Petro ataona zimenezi anawawuza kuti, “Inu Aisraeli, chifukwa chiyani mukudabwa ndi zimene zachitikazi? Bwanji mukuyangʼana ife ngati kuti tamuyendetsa munthuyu ndi mphamvu yathu kapena chifukwa cha kupembedza kwathu? 13 Mulungu wa Abrahamu, Isake ndi Yakobo, Mulungu wa makolo athu, wamulemekeza mtumiki wake Yesu. Amene inu munamukana pamaso pa Pilato ndi kumupereka Iye kuti aphedwe, ngakhale kuti Pilato anafuna kuti amumasule. 14 Koma inu munamukana Woyera ndi Wolungamayo ndipo munapempha kuti akumasulireni munthu wakupha anthu. 15 Inu munapha mwini moyo, koma Mulungu anamuukitsa kwa akufa. Ife ndife mboni za zimenezi. 16 Mwachikhulupiriro mʼdzina la Yesu, munthu uyu amene mukumuona ndi kumudziwa analimbikitsidwa. Mʼdzina la Yesu ndi chikhulupiriro chimene chili mwa iye chamuchiritsa kwathunthu, monga nonse mukuona.
17 “Tsopano abale ine ndikudziwa kuti inu munachita zimenezi mosadziwa, monga momwenso anachitira atsogoleri anu. 18 Koma umu ndi mmene Mulungu anakwaniritsira zimene zinanenedwa kale ndi aneneri onse, kuti Khristu adzamva zowawa. 19 Chifukwa chake, lapani, bwererani kwa Mulungu, kuti machimo anu afafanizidwe, kuti nthawi ya kutsitsimuka ibwere kuchokera kwa Ambuye, 20 ndi kuti Iye atumize Yesu Khristu amene anasankhidwa chifukwa cha inu. 21 Iye ayenera kukhalabe kumwamba mpaka nthawi ya kukonzanso zinthu zonse monga Mulungu analonjeza kale kudzera mwa aneneri ake oyera mtima. 22 Pakuti Mose anati, ‘Ambuye Mulungu wanu adzakuukitsirani mneneri monga ine kuchokera pakati pa anthu anu; mumvere zonse zimene iye akuwuzeni. 23 Aliyense amene sadzamvera mawu a mneneriyo, adzayenera kuchotsedwa pakati pa abale ake.’
24 “Ndipo aneneri onse ambiri amene anayankhula kuyambira Samueli, ananeneratu za masiku ano. 25 Inu ndinu ana a aneneri ndiponso ana apangano limene Mulungu anachita ndi makolo anu. Iye anati kwa Abrahamu, ‘Anthu onse a pa dziko lapansi adzadalitsika kudzera mwa zidzukulu zako.’ 26 Pamene Mulungu anaukitsa mtumiki wake, anamutuma Iye poyamba kwa inu kuti akudalitseni pobweza aliyense wa inu ku zoyipa zake.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.