Beginning
Yesu Achiritsa Munthu Wosaona Chibadwire
9 Iye akuyendabe, anaona munthu wosaona chibadwire. 2 Ophunzira ake anamufunsa Iye kuti, “Rabi anachimwa ndani, munthuyu kapena makolo ake, kuti iye abadwe wosaona?”
3 Yesu anayankha kuti, “Sikuti iyeyu anachimwa kapena makolo ake, koma izi zinachitika kuti Mulungu aonetse ntchito zake mwa iyeyu. 4 Ife tiyenera kugwira ntchito za Iye amene anandituma kukanali masana. Usiku ukubwera, pamene wina aliyense sadzagwira ntchito. 5 Pamene Ine ndili mʼdziko lapansi, Ine ndine kuwunika kwa dziko lapansi.”
6 Atanena izi, Iye anathira malovu pansi ndi kukanda dothi, napaka matopewo mʼmaso a munthuyo. 7 Yesu anamuwuza iye kuti, “Pita kasambe mʼdziwe la Siloamu” (mawu awa akutanthauza Wotumidwa). Choncho munthuyo anapita ndi kukasamba ndipo anabwerako akupenya.
8 Anzake ndi iwo amene anamuona iye poyamba akupempha anafunsa kuti, “Kodi uyu si munthu amene amapemphapempha uja?” 9 Ena ananena kuti anali yemweyo.
Ena anati, “Ayi, sakuoneka ngati yemweyo.”
Koma iye mwini ananenetsa kuti, “Munthuyo ndine.”
10 Iwo anafunsitsa kuti, “Kodi nanga maso ako anatsekuka bwanji?”
11 Iye anayankha kuti, “Munthu wina wotchedwa Yesu anakanda dothi ndi kupaka mʼmaso anga. Iye anandiwuza kuti ndipite ku Siloamu ndi kukasamba. Choncho ndinapita kukasamba, ndipo ndikuona.”
12 Iwo anamufunsa iye kuti, “Ali kuti munthu ameneyu?”
Iye anati, “Ine sindikudziwa.”
Afarisi Afufuza za Kuchiritsidwa Kwake
13 Iwo anabwera naye munthu amene poyamba anali wosaona kwa Afarisi. 14 Tsono linali la Sabata tsiku limene Yesu anakanda dothi ndi kutsekula maso a munthuyu. 15 Choncho Afarisi anamufunsanso iye momwe analandirira kuona kwake. Munthuyo anayankha kuti, “Iye anapaka matope mʼmaso anga, ndipo ine ndinakasamba, ndipo ndikuona.”
16 Ena a Afarisi anati, “Munthu uyu siwochokera kwa Mulungu, pakuti sasunga Sabata.”
Koma enanso anafunsa kuti, “Kodi munthu wochimwa angachite bwanji zizindikiro zodabwitsa ngati izi?” Choncho iwo anagawanika.
17 Pomaliza iwo anatembenukiranso kwa munthu amene anali wosaona uja nati, “Kodi iwe unena chiyani za Iye poti ndi maso ako amene watsekula?”
Munthuyo anayankha kuti, “Iye ndi mneneri.”
18 Ayuda sanakhulupirirebe kuti iye anali wosaona ndi kuti anayamba kuona kufikira atayitana makolo ake. 19 Iwo anafunsa kuti, “Kodi uyu ndi mwana wanu? Kodi iyeyu ndi amene mukunena kuti anabadwa wosaona? Nanga zikutheka bwanji kuti akuona?”
20 Makolo anayankha kuti, “Ife tikudziwa kuti ndi mwana wathu, ndipo tikudziwa kuti anabadwa wosaona. 21 Koma sitidziwa zimene zachitika kuti tsopano azipenya. Amenenso wamupenyetsa sitikumudziwa. Mufunseni ndi wamkulu; iye adziyankhira yekha.” 22 Makolo ake ananena izi chifukwa amaopa Ayuda, popeza Ayuda anatsimikiza kale kuti aliyense amene adzamuvomereza Yesu kuti anali Khristu adzatulutsidwa mʼsunagoge. 23 Ichi ndi chifukwa chake makolo ake anati, “Mufunseni iye ndi wamkulu.”
24 Iwo anamuyitanitsa kachiwiri munthu amene anali wosaonayo. Iwo anati, “Lemekeza Mulungu. Ife tikudziwa kuti munthu uyu ndi wochimwa.”
25 Iye anayankha kuti, “Zakuti Iye ndi wochimwa kapena ayi, ine sindikudziwa. Ine ndikudziwa chinthu chimodzi. Ndinali wosaona koma tsopano ndikuona!”
26 Kenaka anamufunsa kuti, “Kodi Iye anachita chiyani kwa iwe? Iye anatsekula motani maso ako?”
27 Iye anayankha kuti, “Ine ndakuwuzani kale ndipo inu simunamvetsetse. Chifukwa chiyani mukufuna mumvenso? Mukufuna kuti inu mukhale ophunzira akenso?”
28 Pamenepo anamunyoza ndipo anati, “Iwe ndiye ophunzira wa munthuyu! Ife ndife ophunzira a Mose! 29 Ife tikudziwa kuti Mulungu anayankhula kwa Mose, koma za munthu uyu, ife sitikudziwa ngakhale kumene akuchokera.”
30 Munthuyo anayankha kuti, “Tsopano izi ndi zodabwitsa! Inu simukudziwa kumene akuchokera, komabe iye watsekula maso anga. 31 Ife tikudziwa kuti Mulungu samvera wochimwa. Iye amamvera munthu woopa Mulungu amene amachita chifuniro chake. 32 Palibe amene anamvapo za kutsekula maso a munthu wobadwa wosaona. 33 Ngati munthu uyu akanakhala wosachokera kwa Mulungu, palibe chimene Iye akanachita.”
34 Pamenepo anayankha kuti, “Iwe unabadwa mu uchimo kotheratu; bwanji ukuyesa kutiphunzitsa ife!” Ndipo anamutulutsa kunja.
Kusaona kwa Uzimu
35 Yesu anamva kuti anamutulutsa kunja ndipo pamene anamupeza anati, “Kodi ukukhulupirira Mwana wa Munthu?”
36 Munthuyo anafunsa kuti, “Kodi, Ambuye, ameneyo ndi ndani? Ndiwuzeni kuti ndimukhulupirire Iye?”
37 Yesu anati, “Iwe wamuona tsopano. Zoonadi ndiye amene akuyankhula nawe.”
38 Pamenepo munthuyo anati, “Ambuye, ndikukhulupirira,” ndipo anamulambira Iye.
39 Yesu anati, “Ndinabwera pansi pano kudzaweruza kuti osaona aone ndi openya asaone.”
40 Afarisi ena amene anali pafupi naye anamva akunena izi ndipo anafunsa kuti, “Chiyani? Kodi ndife osaonanso?”
41 Yesu anati, “Mukanakhala osaona, simukanachimwa; koma tsopano popeza mukuti mumaona, ndinu ochimwabe.”
Mʼbusa Wabwino ndi Nkhosa Zake
10 “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani inu Afarisi, kuti munthu amene salowera pa khomo mʼkhola la nkhosa, koma amalowera pena pake ndi wakuba ndi wachifwamba. 2 Munthu amene amalowera pa khomo ndi mʼbusa wankhosazo. 3 Mlonda amamutsekulira khomo, ndipo nkhosa zimamvera mawu ake. Iye amaziyitana mayina nkhosa zakezo, nazitulutsa. 4 Akazitulutsa nkhosa zake zonse, iye amazitsogolera, ndipo nkhosa zakezo zimamutsata chifukwa zimadziwa mawu ake. 5 Koma nkhosazo sizidzatsatira mlendo. Izo zidzamuthawa chifukwa sizizindikira mawu a mlendo.” 6 Yesu ananena mawu ophiphiritsawa, koma Afarisi sanazindikire zimene ankawawuza.
7 Choncho Yesu anatinso, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti Ine ndine khomo la nkhosa. 8 Onse amene anadza ndisanabwere Ine ndi akuba ndi achifwamba, ndipo nkhosa sizinawamvere. 9 Ine ndine khomo, aliyense amene alowa kudzera mwa Ine adzapulumuka. Iye adzalowa ndi kutuluka ndi kupeza msipu. 10 Mbala sibwera chabe koma kuti idzabe, kupha ndi kuwononga. Ine ndabwera kuti iwo akhale ndi moyo, ndi kukhala nawo wochuluka.
11 “Ine ndine Mʼbusa wabwino. Mʼbusa wabwino amataya moyo wake chifukwa cha nkhosa zake. 12 Wantchito ndi mʼbusa amene nkhosazo si zake. Choncho, pamene aona mmbulu ukubwera, iye amazisiya nkhosazo ndi kuthawa. Ndipo mmbulu umagwira nkhosazo ndikuzibalalitsa. 13 Munthuyo amathawa chifukwa ndi wantchito ndipo sasamalira chilichonse cha nkhosazo.
14 “Ine ndine mʼbusa wabwino. Ine ndimazidziwa nkhosa zanga ndipo nkhosa zangazo zimandidziwa, 15 monga momwe Atate amandidziwa Ine, ndiponso Ine kudziwira Atatewo. Ndimapereka moyo wanga chifukwa cha nkhosa. 16 Ine ndili ndi nkhosa zina zimene sizili za gulu ili. Ine ndiyenera kuzibweretsanso. Izonso zidzamvera mawu anga, ndipo zidzakhala gulu limodzi ndi mʼbusa mmodzi. 17 Nʼchifukwa chake Atate anga amandikonda, popeza Ine ndikupereka moyo wanga kuti ndiwutengenso. 18 Palibe amene angawuchotse mwa Ine, koma ndikuwupereka mwakufuna kwanga. Ine ndili ndi ulamuliro wa kuwupereka ndi ulamuliro wakuwutenganso. Lamulo ili ndinalandira kwa Atate anga.”
19 Pa mawu awa Ayuda anagawikananso. 20 Ambiri a iwo anati, “Iye ndi wogwidwa ndi ziwanda ndi wamisala. Chifukwa chiyani mukumvera Iye?”
21 Koma ena anati, “Awa si mawu a munthu wogwidwa ndi ziwanda. Kodi ziwanda zingathe bwanji kutsekula maso a wosaona?”
Kusakhulupirira kwa Ayuda
22 Ku Yerusalemu kunali chikondwerero chokumbukira kupatulidwa kwa Nyumba ya Mulungu. Inali nthawi yozizira, 23 ndipo Yesu ankayenda mʼbwalo la Nyumbayo ku malo a Solomoni. 24 Ayuda anamuzungulira Iye akunena kuti, “Kodi iwe udzazunguza malingaliro athu mpaka liti? Ngati iwe ndi Khristu, tiwuze momveka.”
25 Yesu anayankha kuti, “Ine ndimakuwuzani, koma inu simukhulupirira. Ntchito zimene ndikuchita mʼdzina la Atate anga zikundichitira umboni, 26 koma inu simukhulupirira chifukwa simuli a gulu lankhosa zanga. 27 Nkhosa zanga zimamva mawu anga, Ine ndimazidziwa, ndipo zimanditsata Ine. 28 Ine ndimazipatsa moyo wosatha ndipo sizidzawonongeka. Palibe amene adzazikwatula mʼdzanja langa. 29 Atate anga, amene anandipatsa Ine, ndi akulu kuposa onse. Palibe amene angazikwatule mʼdzanja la Atate anga. 30 Ine ndi Atate ndife amodzi.”
31 Ayuda anatolanso miyala kuti amugende Iye, 32 koma Yesu anawawuza kuti, “Ine ndakuonetsani zinthu zambiri zabwino zodabwitsa kuchokera kwa Atate. Nʼchifukwa chiti mwa izi chimene mukundigendera?”
33 Ayuda anayankha kuti, “Ife sitikukugenda chifukwa cha izi, koma popeza ukunyoza Mulungu, chifukwa iwe, munthu wamba, ukuti ndiwe Mulungu.”
34 Yesu anawayankha kuti, “Kodi sizinalembedwa mʼmalamulo anu kuti, ‘Ine ndanena kuti ndinu milungu?’ 35 Ngati anawatcha milungu anthu amene analandira mawu a Mulungu, pajatu Malemba sangasweke, 36 nanga bwanji uyu amene Atate anamuyika padera monga wake weniweni ndi kumutuma ku dziko lapansi? Nanga ndi chifukwa chiyani mukundinena Ine kuti ndikuchita chipongwe? Kodi nʼchifukwa choti ndanena kuti, ‘Ine ndine Mwana wa Mulungu?’ 37 Musandikhulupirire Ine ngati sindichita ntchito za Atate anga. 38 Koma ngati Ine ndikuchita zimenezi, ngakhale kuti simundikhulupirira, khulupirirani ntchito zodabwitsazo, ndipo mudziwe ndi kuzindikira kuti Atate ali mwa Ine, ndiponso Ine ndili mwa Atate.” 39 Iwo anafuna kumugwiranso koma anawapulumuka mʼmanja mwawo.
40 Kenaka Yesu anabwereranso kutsidya la mtsinje wa Yorodani kumalo kumene Yohane ankabatiza mʼmasiku akale. Iye anakhala kumeneko 41 ndipo anthu ambiri anabwera kwa Iye. Iwo anati, “Ngakhale kuti Yohane sanachite chizindikiro chodabwitsa, zonse zimene Yohane ananena za munthu uyu zinali zoona.” 42 Ndipo pamalo amenewo ambiri anakhulupirira Yesu.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.