Beginning
Yesu Mbuye wa Sabata
6 Tsiku lina la Sabata Yesu ankadutsa mʼminda yatirigu, ndipo ophunzira ake anayamba kubudula ngala zatirigu, namazifikisa mʼmanja mwawo ndi kumadya. 2 Ena mwa Afarisi anafunsa kuti, “Kodi nʼchifukwa chiyani mukuchita zosaloledwa pa tsiku la Sabata?”
3 Yesu anawayankha iwo kuti, “Kodi simunawerenge zimene Davide anachita pamene iye ndi anzake anali ndi njala? 4 Iye analowa mʼnyumba ya Mulungu ndipo atatenga buledi wopatulika anadya amene ndi ololedwa kudya ansembe okha. Ndipo anaperekanso wina kwa anzake.” 5 Kenaka Yesu anawawuza kuti, “Mwana wa Munthu ndi Ambuye wa Sabata.”
6 La Sabata lina Iye analowa mʼsunagoge kukaphunzitsa ndipo mʼmenemo anapeza munthu wadzanja lolumala. 7 Afarisi ndi aphunzitsi amalamulo ankamuyangʼana kuti apeze chifukwa Yesu, choncho anamuyangʼanitsitsa kuti aone ngati Iye akanamuchiritsa pa Sabata. 8 Koma Yesu anadziwa zimene ankaganiza ndipo anati kwa munthu wadzanja lolumalayo, “Tanyamuka ndipo uyime patsogolo pa onsewa.” Choncho iye ananyamuka nayima pamenepo.
9 Kenaka Yesu anawawuza kuti, “Ndikufunseni, kodi chololedwa pa Sabata ndi chiti: kuchita chabwino kapena kuchita choyipa, kupulumutsa moyo kapena kuwononga?”
10 Iye atawayangʼana onsewo, anati kwa munthuyo, “Wongola dzanja lako.” Iye anaterodi, ndipo dzanja lake linachiritsidwa. 11 Koma iwo anapsa mtima nayamba kukambirana wina ndi mnzake chomwe akanamuchitira Yesu.
Atumwi Khumi ndi Awiri
12 Tsiku lina, masiku amenewo, Yesu anapita ku phiri kukapemphera ndipo anakhala usiku wonse akupemphera kwa Mulungu. 13 Kutacha, anayitana ophunzira ake ndipo anasankha khumi ndi awiri a iwo amene anawayika kukhala atumwi: 14 Simoni (amene anamutcha Petro), mʼbale wake wa Andreya, Yakobo, Yohane, Filipo, Bartumeyu, 15 Mateyu, Tomasi, Yakobo mwana wa Alufeyo, Simoni amene amatchedwa Zaleti, 16 Yudasi mwana wa Yakobo ndi Yudasi Isikarioti amene anamupereka.
Madalitso ndi Tsoka
17 Iye anatsika pamodzi ndi atumwiwo ndipo anayima pamalo athyathyathya. Gulu lalikulu la ophunzira ake, gulu lalikulu la anthu ochokera ku Yudeya konse, ku Yerusalemu ndi ochokera mʼmphepete mwa nyanja ya Turo ndi Sidoni anali pomwepo. 18 Iwo anabwera kudzamvetsera ndi kuchiritsidwa ku matenda awo. Osautsidwa ndi mizimu yoyipa anachiritsidwa, 19 ndipo anthu ankayesetsa kuti amukhudze chifukwa mphamvu imatuluka mwa Iye ndi kuchiritsa onse.
20 Akuyangʼana ophunzira ake, Iye anati,
“Odala ndinu amene ndi osauka,
chifukwa ufumu wa Mulungu ndi wanu.
21 Inu amene mukumva njala tsopano, ndinu odala
chifukwa mudzakhutitsidwa.
Inu amene mukulira tsopano, ndinu odala
chifukwa mudzasekerera.
22 Ndinu odala, anthu akamakudani,
kukusalani ndi kukunyozani
ndi kumayipitsa dzina lanu chifukwa cha Mwana wa Munthu.
23 “Nthawi imeneyo sangalalani ndipo lumphani ndi chimwemwe chifukwa mphotho yanu ndi yayikulu kumwamba. Pakuti ndi zomwezonso zimene makolo awo anachitira aneneri.
24 “Ndinu atsoka, anthu olemera,
popeza mwalandiriratu zokusangalatsani.
25 Tsoka inu amene mukudya bwino tsopano,
chifukwa mudzakhala ndi njala.
Ndinu atsoka, amene mukusekerera tsopano,
chifukwa mudzabuma ndi kulira.
26 Ndinu atsoka, anthu akamakuyamikirani,
popeza makolo anu anawachitira aneneri onama zomwezi.”
Kukonda Adani
27 “Koma Ine ndikuwuza inu amene mukundimva: Kondani adani anu, chitirani zabwino amene amakudani. 28 Dalitsani amene amakutembererani, apempherereni amene amakusautsani. 29 Ngati wina akumenyani patsaya limodzi mupatseninso tsaya linalo. Ngati wina akulanda mwinjiro wako, umulole atenge ndi mkanjo omwe. 30 Mupatseni aliyense amene akupemphani kanthu ndipo ngati wina atenga chinthu chanu, musamulamule kuti akubwezereni. 31 Inu muwachitire anthu ena, zomwe mukanafuna kuti iwo akuchitireni.
32 “Ngati mukonda okhawo amene amakukondani, mwapindula chiyani? Ngakhale ‘ochimwa’ amakonda amene amawakondanso. 33 Ndipo ngati muchita zabwino kwa amene ndi abwino kwa inu, mwapindula chiyani? Ngakhale ‘ochimwa’ amachita izi. 34 Ndipo ngati mukongoza amene mukuyembekeza kuti abweza, mwapindula chiyani? Ngakhale ‘ochimwa’ amabwereketsa kwa ochimwa anzawo, ndipo amayembekezera kubwezeredwa zonse. 35 Koma kondani adani anu, achitireni zabwino, akongozeni koma osayembekezera kulandira kanthu. Pamenepo mphotho yanu idzakhala yayikulu ndipo inu mudzakhala ana a Wammwambamwamba, chifukwa ndi wokoma mtima kwa anthu osayamika ndi oyipa. 36 Khalani achifundo, monga momwe Atate anu ali achifundo.”
Za Kuweruza Ena
37 “Musaweruze, ndipo inu simudzaweruzidwa. Musatsutse ndipo inu simudzatsutsidwa. Khululukirani ena ndipo mudzakhululukidwa. 38 Perekani ndipo mudzapatsidwa. Adzakupatsani mʼthumba mwanu muyeso wabwino, wotsenderezeka, wokhutchumuka ndi wosefukira. Pakuti muyeso umene mumagwiritsa ntchito, ndi omwewo adzakuyeserani.”
39 Iye anawawuzanso fanizo ili, “Kodi munthu wakhungu angatsogolere munthu wakhungu mnzake? Kodi onse sadzagwera mʼdzenje? 40 Wophunzira sangapose mphunzitsi wake, koma yense amene waphunzitsidwa bwinobwino adzakhala ngati mphunzitsi wake.
41 “Kodi ndi chifukwa chiyani mumaona kachitsotso mʼdiso la mʼbale wanu ndi kusasamala mtengo uli mʼdiso mwanu? 42 Kodi munganene bwanji kwa mʼbale wanu kuti, ‘Mʼbale nʼtakuchotsa kachitsotso mʼdiso mwako,’ pamene inu eni ake mukulephera kuona mtengo uli mʼdiso mwanu? Inu achiphamaso, yambani mwachotsa mtengo uli mʼdiso mwanu, ndipo kenaka mudzaona bwinobwino ndi kuchotsa kachitsotso mʼdiso la mʼbale wanu.”
Mtengo ndi Zipatso Zake
43 Palibe mtengo wabwino umene umabala chipatso choyipa, kapena mtengo oyipa umene umabala chipatso chabwino. 44 Mtengo uliwonse umadziwika ndi chipatso chake. Anthu sathyola nkhuyu pa mtengo waminga, kapena mphesa pa nthungwi. 45 Munthu wabwino amatulutsa zinthu zabwino zosungidwa mu mtima mwake, koma munthu oyipa amatulutsa zinthu zoyipa zosungidwa mu mtima mwake. Pakamwa pake pamayankhula zimene zadzaza mu mtima mwake.
Womanga Nyumba Wanzeru ndi Wopusa
46 “Kodi nʼchifukwa chiyani munditchula kuti, ‘Ambuye, Ambuye’ koma simuchita zimene Ine ndinena? 47 Ine ndidzakuonetsani mmene alili munthu amene amabwera kwa Ine ndi kumva mawu anga ndi kuwachita. 48 Iye ali ngati munthu womanga nyumba, amene anakumba mozama nayika maziko ake pa mwala. Madzi osefukira atabwera ndi mphamvu, nawomba nyumbayo koma sinagwedezeka, chifukwa anayimanga bwino. 49 Koma amene amamva mawu anga koma osawachita, akufanana ndi munthu amene anamanga nyumba yake koma yopanda maziko. Nthawi yomwe madziwo anawomba nyumbayo, inagwa ndipo inawonongekeratu.”
Chikhulupiriro cha Kenturiyo
7 Yesu atamaliza kunena zonsezi pamaso pa anthu amene ankamvetsera, analowa mu Kaperenawo. 2 Kumeneko wantchito wa Kenturiyo, amene amamukhulupirira kwambiri, anadwala ndipo anali pafupi kufa. 3 Kenturiyo anamva za Yesu ndipo anatumiza ena a akulu Ayuda kwa Iye kuti abwere adzachiritse wantchito wakeyo. 4 Iwo atafika kwa Yesu, anamudandaulira kwambiri, nati, “Munthuyu ayenera kuthandizidwa 5 chifukwa amakonda mtundu wathu ndipo anatimangira sunagoge wathu.” 6 Pamenepo Yesu anapita nawo.
Iye sanali patali ndi nyumba pamene Kenturiyo anatumiza anzake kuti akamuwuze kuti, “Ambuye, musadzivutitse, pakuti ndine wosayenera kuti mulowe mʼnyumba mwanga. 7 Nʼchifukwa chake sindinadziyenereze ndi pangʼono pomwe kuti ndibwere kwa inu. Koma nenani mawu, ndipo wantchito wanga adzachira. 8 Pakuti ndili pansi paulamuliro, ndiponso ndili ndi asilikali pansi panga. Ndikamuwuza uyu kuti, ‘Pita,’ iye amapita; ndi uyo kuti, ‘Bwera,’ amabwera. Ndikamuwuza wantchito wanga kuti, ‘Chita ichi,’ amachita.”
9 Yesu atamva izi, anadabwa naye, ndipo anatembenukira gulu la anthu limene limamutsatira nati, “Ndikukuwuzani kuti, sindinapeze chikhulupiriro chachikulu ngati ichi mu Israeli.” 10 Kenaka anthu amene anatumidwawo anabwerera ku nyumba ndipo anakamupeza wantchitoyo atachira.
Yesu Aukitsa Mwana wa Mayi Wamasiye
11 Zitangotha izi, Yesu anapita ku mudzi wa Naini ndipo ophunzira ake ndi gulu lalikulu la anthu linapita naye pamodzi. 12 Akufika pa chipata cha mudziwo, anakumana ndi anthu amene ankatuluka ndi munthu wakufa amene anali mwana yekhayo wa mkazi wamasiye. Gulu lalikulu la anthu a mʼmudziwo linali naye. 13 Ambuye atamuona mayiyo, mtima wawo unagwidwa naye chifundo ndipo anati, “Usalire.”
14 Kenaka anapita nakakhudza chithatha cha maliro ndipo amene anachinyamulawo anayima. Iye anati, “Mnyamata, ndikukuwuza kuti, dzuka!” 15 Wakufayo anakhala tsonga ndi kuyamba kuyankhula, ndipo Yesu anamupereka mnyamatayo kwa amayi ake.
16 Onse anachita mantha kwambiri nalemekeza Mulungu. Iwo anati, “Mneneri wamkulu waonekera pakati pathu. Mulungu wabwera kudzathandiza anthu ake.” 17 Mbiriyi inafalikira ku Yudeya konse ndi ku madera ozungulira.
Yesu ndi Yohane Mʼbatizi
18 Ndipo ophunzira a Yohane anamuwuza Yohaneyo zinthu zonsezi. Atayitana awiri a ophunzirawo, 19 anawatumiza kwa Ambuye kukafunsa kuti, “Kodi ndinu anayenera kubwerayo, kapena tiyembekezere wina?”
20 Anthuwo atafika kwa Yesu anati, “Yohane Mʼbatizi watituma kwa Inu kuti tidzafunse kuti, ‘Kodi ndinu anayenera kubwerayo, kapena tiyembekezere wina?’ ”
21 Pa nthawi yomweyo, Yesu anachiritsa ambiri amene ankavutika, odwala ndi amene anali mizimu yoyipa, ndiponso anapenyetsa anthu osaona. 22 Ndipo Iye anawayankha otumidwawo kuti, “Bwererani ndi kukamuwuza Yohane zimene mwaona ndi kumva: Osaona akuona, olumala akuyenda, akhate akuchiritsidwa, osamva akumva, akufa akuukitsidwa, ndipo Uthenga Wabwino ukulalikidwa kwa osauka. 23 Odala munthu amene sakhumudwa chifukwa cha Ine.”
24 Anthu otumidwa ndi Yohane aja atachoka, Yesu anayamba kuyankhula ndi gulu la anthu za Yohaneyo kuti, “Kodi munkapita ku chipululu kukaona chiyani? Bango logwedezeka ndi mphepo? 25 Ngati si choncho, munkapita kukaona chiyani? Munthu wovala zovala zabwino? Ayi, ovala zovala zodula ndi okhala moyo wapamwamba ali mʼnyumba zaufumu. 26 Koma inu munkapita kukaona chiyani? Mneneri? Inde, Ine ndikukuwuzani, woposa mneneri. 27 Uyu ndi amene malemba akunena za Iye kuti,
“ ‘Ine ndidzatuma mthenga wanga patsogolo panu,
amene adzakonza njira yanu.’
28 Ine ndikukuwuzani kuti pakati pa obadwa kuchokera mwa mkazi palibe wina wamkulu kuposa Yohane; komabe amene ali wamngʼono mu ufumu wa Mulungu ndi wamkulu kuposa iye.”
29 Anthu onse, ngakhale amisonkho, atamva mawu a Yesu, anavomereza kuti njira ya Mulungu ndi yolondola, chifukwa anabatizidwa ndi Yohane. 30 Koma Afarisi ndi akatswiri amalamulo anakana cholinga cha Mulungu kwa iwo okha, chifukwa sanabatizidwe ndi Yohane.
31 “Kodi ndingawafanizire chiyani anthu a mʼbado uno? Ali ngati chiyani? 32 Ali ngati ana amene akukangana pa msika, ena akufunsa anzawo kuti,
“ ‘Ife tinakuyimbirani chitoliro,
koma inu simunavine.
Tinakuyimbirani nyimbo zamaliro,
koma inu simunalire.’
33 Pakuti Yohane Mʼbatizi sanabwere kudzadya buledi kapena kumwa vinyo, koma inu mumati, ‘Ali ndi chiwanda.’ 34 Mwana wa Munthu anabwera nadya ndi kumwa, ndipo inu mukuti, ‘Ali ndi dyera komanso ndi woledzera, bwenzi la amisonkho ndi ochimwa.’ 35 Ndipo nzeru zimaoneka zolondola mwa ana ake onse.”
Yesu Adzozedwa ndi Mayi Wochimwa
36 Tsopano mmodzi mwa Afarisi anayitana Yesu kuti akadye naye ku nyumba kwake ndipo anapita nakakhala pa tebulo. 37 Mayi amene amakhala moyo wauchimo mu mzindawo atadziwa kuti Yesu akudya ku nyumba ya Mfarisiyo, anabweretsa botolo la mafuta onunkhira a alabasta. 38 Iye anayimirira kumbuyo kwa Yesu pa mapazi ake akulira, nayamba kumadontheza misozi pa mapazi ake. Ndipo iye anapukuta mapaziwo ndi tsitsi lake, nawapsompsona ndi kuwathira mafuta onunkhirawo.
39 Mfarisiyo anamuyitanayo ataona izi, anati mu mtima mwake, “Ngati munthuyu akanakhala mneneri, akanadziwa kuti akumukhudzayo ndi mayi otani, kuti ndi wochimwa.”
40 Yesu anamuyankha iye kuti, “Simoni, ndili ndi kanthu koti ndikuwuze.”
Iye anati, “Ndiwuzeni Aphunzitsi.”
41 “Anthu awiri anakongola ndalama kwa munthu wina wokongoletsa ndalama: mmodzi ndalama zokwana 500 ndi winayo ndalama makumi asanu. 42 Panalibe mmodzi mwa iwo anali ndi ndalama zobwezera, ndipo iye anawakhululukira ngongole zawo. Tsopano ndi ndani mwa awiriwa adzamukonde koposa?”
43 Simoni anayankha kuti, “Ndikuganiza kuti ndi amene anamukhululukira ngongole yayikulu.”
Yesu anati, “Wayankha molondola.”
44 Kenaka anatembenukira kwa mayiyo nati kwa Simoni, “Ukumuona mayiyu? Ine ndabwera mʼnyumba yako. Iwe sunandipatse madzi otsukira mapazi anga, koma iyeyu wanyowetsa mapazi anga ndi misozi yake ndi kuwapukuta ndi tsitsi lake. 45 Iwe sunandipsompsone, koma mayiyu, kuyambira pamene Ine ndalowa, sanaleke kupsompsona mapazi anga. 46 Iwe sunadzoze mutu wanga mafuta, koma iye wadzoza mapazi anga mafuta onunkhira. 47 Tsono, ndikukuwuza iwe, machimo ake amene ndi ambiri akhululukidwa, monga chaonetsera chikondi chake chachikulu. Koma iye amene wakhululukidwa zochepa amakonda pangʼono.”
48 Kenaka anati kwa mayiyo, “Machimo ako akhululukidwa.”
49 Alendo enawo anayamba kumanena mʼmitima mwawo kuti, “Uyu ndi ndani amene akhululukiranso machimo?”
50 Yesu anati kwa mayiyo, “Chikhulupiriro chako chakupulumutsa. Pita mu mtendere.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.