Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Beginning

Read the Bible from start to finish, from Genesis to Revelation.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Luka 2-3

Kubadwa kwa Yesu

Mʼmasiku amenewo Kaisara Augusto anapereka lamulo kuti kalembera achitike mʼdziko lonse la Aroma. (Uyu ndi kalembera woyamba amene anachitika pamene Kureniyo anali bwanamkubwa wa Siriya). Ndipo aliyense anapita ku mzinda wa kwawo kukalembetsa.

Choncho Yosefe anachoka ku Nazareti ku Galileya kupita ku Yudeya, ku Betelehemu ku mudzi wa Davide, chifukwa anali wa banja ndi fuko la Davide. Iye anapita kumeneko kukalembetsa pamodzi ndi Mariya, amene anapalana naye ubwenzi kuti akwatirane ndipo anali woyembekezera. Ali kumeneko, nthawi inakwana yakuti mwana abadwe, ndipo anabereka mwana wake woyamba, wamwamuna. Iye anamukulunga mʼnsalu ndi kumuyika modyera ngʼombe, chifukwa kunalibe malo mʼnyumba ya alendo.

Abusa ndi Angelo

Ndipo kunali abusa amene amakhala ku dera lomwelo, kuyangʼanira ziweto zawo usiku. Mngelo wa Ambuye anaonekera kwa iwo ndipo ulemerero wa Ambuye unawala mowazungulira. Iwo anachita mantha. 10 Koma mngeloyo anawawuza kuti, “Musachite mantha. Ine ndakubweretserani Uthenga Wabwino wachimwemwe chachikulu umene udzakhala wa anthu onse. 11 Lero mʼmudzi wa Davide wakubwadwirani Mpulumutsi; Iye ndi Khristu Ambuye. 12 Ichi chidzakhala chizindikiro kwa inu: mukapeza mwana wakhanda wokutidwa ndi nsalu atagona modyera ngʼombe.”

13 Mwadzidzidzi gulu lalikulu la angelo linaonekera pamodzi ndi mngeloyo, kuyamika Mulungu ndi kumati,

14 “Ulemerero kwa Mulungu mmwambamwamba,
    ndi mtendere kwa anthu pa dziko lapansi amene Iye akondwera nawo.”

15 Angelowo atabwerera kumwamba, abusawo anati kwa wina ndi mnzake, “Tiyeni ku Betelehemu tikaone zinthu zomwe zachitika, zimene Ambuye atiwuza ife.”

16 Ndipo iwo anafulumira nyamuka nakapeza Mariya ndi Yosefe ndi mwana wakhanda, amene anagona modyera ngʼombe. 17 Pamene anamuona Iye, iwo anafotokoza zomwe anawuzidwa za mwanayo, 18 ndipo onse amene anamva zimene abusawa ananena anadabwa. 19 Koma Mariya anasunga zonsezi mu mtima mwake ndi kumazilingalira. 20 Abusa anabwerera, akulemekeza ndi kuyamika Mulungu chifukwa cha zonse anazimva ndi kuziona, zomwe zinali monga anawuzidwira ndi angelo aja.

Yesu Aperekedwa mʼNyumba ya Mulungu

21 Pa tsiku lachisanu ndi chitatu, tsiku loti amuchite mdulidwe anamutcha Yesu, dzina limene mngelo anamupatsa asanabadwe.

22 Nthawi yoyeretsedwa kwawo itatha, monga mwa lamulo la Mose, Yosefe ndi Mariya anapita naye ku Yerusalemu kukamupereka kwa Ambuye. 23 (Monga mmene zinalembedwera mu lamulo la Ambuye kuti, “Muzikapereka kwa Ambuye mwana aliyense wamwamuna woyamba kubadwa”), 24 ndi kupereka nsembe posunga zimene zinanenedwa mulamulo la Ambuye: “Njiwa ziwiri kapena mawunda ankhunda awiri.”

25 Ndipo taonani, mu Yerusalemu munali munthu wotchedwa Simeoni, amene anali wolungama ndi wodzipereka. Iye ankadikira chitonthozo cha Israeli, ndipo Mzimu Woyera anali pa iye. 26 Mzimu Woyera anamuwululira kuti sadzafa asanaone Khristu wa Ambuye. 27 Motsogozedwa ndi Mzimu Woyera, iye anapita ku bwalo la Nyumba ya Mulungu. Makolo ake a Yesu atabwera naye kuti achite naye mwambo malingana ndi malamulo, 28 Simeoni anamunyamula mʼmanja mwake nayamika Mulungu, nati:

29 “Ambuye waulamuliro, monga munalonjeza,
    tsopano lolani kuti mtumiki wanu apite mu mtendere.
30 Pakuti maso anga aona chipulumutso chanu,
31     chimene Inu munakonza pamaso pa anthu onse,
32 kuwala kowunikira anthu a mitundu ina
    ndi kwa ulemerero kwa anthu anu Aisraeli.”

33 Abambo ndi amayi a Mwanayo anadabwa chifukwa cha zimene zinanenedwa za Iye. 34 Kenaka Simeoni anawadalitsa ndipo anati kwa Mariya amayi ake: “Mwana uyu wakonzedwa kukhala kugwa ndi kudzuka kwa ambiri mu Israeli, ndi kukhala chizindikiro chimene adzayankhula motsutsana nacho, 35 kotero kuti malingaliro a mitima ya ambiri adzawululidwa. Ndipo lupanga lidzabaya moyo wakonso.”

36 Panalinso mneneri wamkazi, dzina lake Ana, mwana wa Fanuelo, wa fuko la Aseri. Anali wokalamba kwambiri; anakhala ndi mwamuna wake zaka zisanu ndi ziwiri atakwatiwa, 37 ndipo kenaka anakhala wamasiye mpaka pamene anali ndi zaka 84. Iye sanachoke mʼNyumba ya Mulungu koma ankapembedza usiku ndi usana, kusala kudya ndi kupemphera. 38 Pa nthawiyo pamene ankapita kwa iwo, iye anayamika Mulungu ndi kuyankhula za Mwanayo kwa onse amene ankayembekezera chipulumutso cha Yerusalemu.

39 Yosefe ndi Mariya atachita zonse zimene zinkafunikira ndi lamulo la Ambuye, anabwerera ku Galileya ku mudzi wa Nazareti. 40 Ndipo Mwanayo anakula nakhala wamphamvu; Iye anadzazidwa ndi nzeru, ndipo chisomo cha Mulungu chinali pa Iye.

Yesu mʼNyumba ya Mulungu

41 Chaka chilichonse makolo ake ankapita ku Yerusalemu ku phwando la Paska. 42 Iye ali ndi zaka khumi ndi ziwiri, anapita ku phwando, monga mwa mwambo. 43 Phwando litatha, pamene makolo ake ankabwerera kwawo, mnyamata Yesu anatsalira ku Yerusalemu, koma iwo sanadziwe zimenezi. 44 Poganiza kuti anali nawo mʼgulu lawo, anayenda tsiku limodzi. Kenaka anayamba kumufunafuna pakati pa abale awo ndi anzawo. 45 Atalephera kumupeza, anabwerera ku Yerusalemu kukamufuna. 46 Patatha masiku atatu anamupeza ali mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu, atakhala pakati pa aphunzitsi, akumvetsera ndi kuwafunsa mafunso. 47 Aliyense amene anamumva Iye anadabwa ndi chidziwitso chake ndi mayankho ake. 48 Makolo ake atamuona, anadabwa. Amayi ake anati kwa Iye, “Mwanawe, watichitira zimenezi chifukwa chiyani? Abambo ako ndi ine takhala tili ndi nkhawa kukufunafuna Iwe.”

49 Iye anawafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani mumandifunafuna? Kodi simukudziwa kuti ndikuyenera kukhala mʼnyumba ya Atate anga?” 50 Koma iwo sanazindikire chomwe Iye amatanthauza.

51 Kenaka anapita nawo ku Nazareti ndipo anawamvera iwo. Koma amayi ake anasunga zinthu zonsezi mu mtima mwawo.

52 Ndipo Yesu anakula mu nzeru, msinkhu ndi chisomo cha Mulungu ndi anthu.

Yohane Mʼbatizi Akonza Njira

Mʼchaka cha 15 mu ulamuliro wa Tiberiyo Kaisara, Pontiyo Pilato ali bwanamkubwa wa Yudeya, Herode ankalamulira ku Galileya, mʼbale wake Filipo ankalamulira ku Iturea ndi ku dera la Trakoniti, ndipo Lusaniyo ankalamulira ku Abilene. Inalinso nthawi ya mkulu wa ansembe wa Anasi ndi Kayafa, pamene mawu a Mulungu anabwera kwa Yohane mwana wa Zakariya mʼchipululu. Iye anapita ku dziko lonse lozungulira mtsinje wa Yorodani, nalalikira ubatizo wa kulapa ndi kukhululukidwa kwa machimo. Monga analembera mʼbuku la Yesaya mneneri kuti:

“Mawu a wofuwula mʼchipululu,
konzani njira ya Ambuye,
    wongolani njira zake.
Chigwa chilichonse chidzadzazidwa
    ndipo phiri lililonse ndi mtunda uliwonse zidzasalazidwa,
misewu yokhotakhota idzawongoledwa,
    ndi njira zosasalala zidzasalazidwa.
Ndipo anthu onse adzaona chipulumutso cha Mulungu.”

Yohane anati kwa magulu a anthu amene amabwera kudzabatizidwa ndi iye, “Ana anjoka inu! Anakuchenjezani ndani kuti muthawe mkwiyo umene ukubwera? Onetsani zipatso zakutembenuka mtima, ndipo musamanene mwa inu nokha kuti, ‘Tili nalo kholo lathu Abrahamu,’ pakuti ndikuwuzani kuti kuchokera ku miyala iyi, Mulungu akhoza kumuwutsira Abrahamuyo ana. Nkhwangwa ili kale pa muzu wamitengo, ndipo mtengo uliwonse umene subala chipatso chabwino udzadulidwa ndi kuponyedwa pa moto.”

10 Gulu la anthuwo linafunsa kuti, “Nanga tsono tichite chiyani?”

11 Yohane anayankha kuti, “Munthu amene ali ndi malaya awiri apatseko amene alibe, ndi amene ali ndi chakudya achitenso chimodzimodzi.”

12 Amisonkho nawonso anabwera kudzabatizidwa. Iwo anafunsa kuti, “Aphunzitsi, ife tichite chiyani?”

13 Iye anawawuza kuti, “Musalandire moposa zimene muyenera.” 14 Kenaka asilikali ena anamufunsa kuti, “Nanga ife tichite chiyani?”

Iye anayankha kuti, “Musamalande ndalama moopseza ndipo musamanamizire anthu, khutitsidwani ndi malipiro anu.”

15 Anthu ankadikira ndi chiyembekezo ndipo ankasinkhasinkha mʼmitima mwawo kuti mwina Yohane nʼkukhala Khristu. 16 Yohane anayankha onse kuti, “Ine ndikubatizani ndi madzi. Koma wina wondiposa ine mphamvu adzabwera amene sindili woyenera kumasula lamba wa nsapato zake. Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto. 17 Mʼdzanja lake muli chopetera kuti ayeretse powomberapo tirigu ndi kusonkhanitsa tirigu ndipo adzatentha zotsalira zonse ndi moto wosazimitsika.” 18 Ndipo ndi mawu ena ambiri, Yohane anawachenjeza anthu ndi kuwalalikira Uthenga Wabwino.

19 Koma pamene Yohane anadzudzula Herode wolamulirayo chifukwa chokwatira Herodia, mkazi wa mʼbale wake, ndi zoyipa zina zonse anazichita, 20 Herode anawonjezanso choyipa ichi pa zonsezo: Anatsekera Yohane mʼndende.

Ubatizo wa Yesu

21 Pamene anthu onse ankabatizidwa, Yesu anabatizidwanso. Ndipo akupemphera, kumwamba kunatsekuka. 22 Mzimu Woyera anatsika pa Iye mumaonekedwe a nkhunda ndipo mawu anamveka kuchokera kumwamba: “Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa; ndimakondwera nawe.”

Makolo a Yesu

23 Ndipo Yesu anali ndi zaka makumi atatu pamene anayamba ntchito yake. Monga mmene anthu ankaganizira, Iyeyo anali mwana wa Yosefe,

mwana wa Heli, 24 mwana wa Matate,

mwana wa Levi, mwana wa Meliki,

mwana wa Yaneyi, mwana wa Yosefe

25 mwana wa Matati, mwana wa Amosi,

mwana wa Naomi, mwana wa Esli,

mwana wa Nagai, 26 mwana wa Maati,

mwana wa Matatiyo, mwana wa Simeoni,

mwana wa Yosefe, mwana wa Yoda

27 mwana wa Yohanani, mwana wa Resa,

mwana wa Zerubabeli, mwana wa Salatieli,

mwana wa Neri, 28 mwana wa Meliki,

mwana wa Adi, mwana wa Kosamu,

mwana wa Elmadama, mwana wa Ere,

29 mwana wa Jose, mwana wa Eliezara,

mwana wa Yorimu, mwana wa Matati,

mwana wa Levi, 30 mwana wa Simeoni,

mwana wa Yuda, mwana wa Yosefe,

mwana wa Yonamu, mwana wa Eliakimu,

31 mwana wa Meleya, mwana wa Mena,

mwana wa Matata, mwana wa Natani,

mwana wa Davide, 32 mwana wa Yese,

mwana wa Obedi, mwana wa Bowazi,

mwana wa Salimoni, mwana wa Naasoni,

33 mwana wa Aminadabu, mwana wa Arni,

mwana wa Hezronu, mwana wa Perezi,

mwana wa Yuda, 34 mwana wa Yakobo,

mwana wa Isake, mwana wa Abrahamu,

mwana wa Tera, mwana wa Nakoro,

35 mwana wa Serugi, mwana wa Reu,

mwana wa Pelegi, mwana wa Eberi,

mwana wa Sela, 36 mwana wa Kainane,

mwana wa Arfaksadi, mwana wa Semu,

mwana wa Nowa, mwana wa Lameki,

37 mwana wa Metusela, mwana wa Enoki,

mwana wa Yaredi mwana wa Malaleeli,

mwana wa Kainane, 38 mwana wa Enosi,

mwana wa Seti,

mwana wa Adamu, mwana wa Mulungu.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.