Beginning
Fanizo la Aganyu Mʼmunda wa Mphesa
20 “Ufumu wakumwamba uli ngati mwini munda amene anapita mmawa kukalemba anthu aganyu kuti akagwire ntchito mʼmunda wake wa mpesa. 2 Anagwirizana kuwalipira dinari monga malipiro a tsiku limodzi ndipo anawatumiza mʼmunda wake wamphesa.
3 “Nthawi 9 koloko mmawa, anatulukanso naona ena atayimirira pa msika akungokhala. 4 Anawawuza kuti, ‘Inunso pitani mukagwire ntchito mʼmunda wanga wa mpesa, ndipo ndidzakulipirani malipiro oyenera.’ 5 Ndipo anapita.
“Anatulukanso nthawi ya 12 koloko masana, ndi nthawi ya 3 koloko masananso nachita chimodzimodzi. 6 Nthawi ya 5 koloko madzulo anatulukanso ndipo anapeza enanso atangoyimirira. Anawafunsa kuti, ‘Chifukwa chiyani mukungoyimirira pano tsiku lonse osagwira ntchito?’
7 “Iwo anayankha kuti, ‘Chifukwa palibe munthu amene watilemba ganyu.’
“Iye anawawuza kuti, ‘Inunso pitani mukagwire ntchito mʼmunda wanga wa mpesa.’
8 “Ndipo pofika madzulo, mwini munda wamphesa anayitana kapitawo wake nati, ‘Itana antchito ndipo uwapatse malipiro awo, kuyambira omalizira aja mpaka oyamba.’
9 “Antchito amene anawalemba ganyu pa 5 koloko masana anafika ndipo aliyense analandira dinari. 10 Ndipo atabwera kwa amene analembedwa poyamba anayembekezera kuti alandira zambiri. Koma aliyense wa iwo analandira dinari. 11 Atalandira, anayamba kuderera kwa mwini mundayo. 12 Iwo anati, ‘Anthu amene munawalemba pomalizira agwira ntchito ora limodzi, ndipo mwawafananitsa ndi ife amene tathyoka nayo ntchito ndi kutentha kwa dzuwa tsiku lonse.’
13 “Koma iye anamuyankha mmodzi wa iwo nati, ‘Bwenzi, ine sikuti sindinachite chilungamo. Kodi sunavomereze kuti ugwira ntchito ndi kulandira dinari? 14 Tenga malipiro ako pita. Ndikufuna kumupatsa munthu amene ndinamulemba pomaliza mofanana ndi mmene ndakupatsira iwe. 15 Kodi ndilibe ufulu wochita zimene ndikufuna ndi ndalama zanga? Kapena ukuyipidwa chifukwa ndine wopereka mowolowamanja?’
16 “Momwemo omalizira adzakhala oyamba ndipo oyamba adzakhala omalizira.”
Yesu Anenanso za Imfa Yake
17 Tsopano pamene Yesu ankapita ku Yerusalemu, anatengera pambali ophunzira ake khumi ndi awiriwo nati kwa iwo, 18 “Tikupita ku Yerusalemu, ndipo Mwana wa Munthu adzaperekedwa kwa akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo. Iwo adzamuweruza kuti aphedwe, 19 ndipo adzamupereka kwa anthu a mitundu ina kuti amunyoze ndi kumukwapula ndi kumupachika. Pa tsiku lachitatu adzaukitsidwa!”
Pempho la Mkazi wa Zebedayo
20 Amayi a ana a Zebedayo anabwera ndi ana ake kwa Yesu, nagwada pansi namupempha Iye.
21 Yesu anawafunsa kuti, “Mukufuna chiyani?”
Amayiwo anati, “Lolani kuti ana anga awiriwa adzakhale mmodzi ku dzanja lanu lamanja ndi wina ku dzanja lanu lamazere mu ufumu wanu.”
22 Yesu anawawuza kuti, “Simukudziwa chimene mukupempha. Kodi mungathe kumwera chikho chimene ndidzamwera Ine?”
Iwo anayankha nati, “Inde tingathe.”
23 Yesu anawawuza kuti, “Zoonadi mudzamwera chikho changa, koma kuti mudzakhale ku dzanja langa lamanja kapena lamazere si kwa Ine kupereka. Malo awa ndi a iwo amene anakonzeredweratu ndi Atate anga.”
24 Ophunzira khumi aja, anawapsera mtima abale awiriwo. 25 Yesu anawayitana onse pamodzi nati, “Mukudziwa kuti olamulira a mitundu ina ali ndi mphamvu pa iwo, ndipo akuluakulu awo amawalamulira. 26 Siziyenera kutero ndi inu. Mʼmalo mwake, aliyense amene akufuna kukhala wamkulu pakati panu akhale wotumikira wanu. 27 Ndipo aliyense amene akufuna kukhala woyamba akhale kapolo wanu. 28 Momwenso Mwana wa Munthu sanabwere kudzatumikiridwa, koma kudzatumikira, ndi kupereka moyo wake kukhala dipo la anthu ambiri.”
Yesu Achiritsa Anthu Awiri Osaona
29 Pamene Yesu ndi ophunzira ake ankachoka ku Yeriko, gulu lalikulu la anthu linawatsata. 30 Amuna awiri osaona anakhala mʼmbali mwa msewu, ndipo pamene anamva kuti Yesu akudutsa anafuwula kuti, “Ambuye, Mwana wa Davide, tichitireni chifundo!”
31 Gulu la anthulo linawadzudzula iwo ndi kuwawuza kuti akhale chete, koma anafuwulitsabe kuti, “Ambuye, Mwana wa Davide, tichitireni chifundo!”
32 Yesu anayima ndi kuwayitana ndipo anawafunsa kuti, “Mukufuna ndikuchitireni chiyani?”
33 Anamuyankha nati, “Ambuye, tikufuna tione!”
34 Yesu anamva nawo chifundo ndipo anakhudza maso awo. Nthawi yomweyo anaona namutsata Iye.
Yesu Alowa mu Yerusalemu
21 Akuyandikira ku Yerusalemu anafika ku Betifage pa phiri la Olivi, Yesu anatumiza ophunzira awiri, 2 nawawuza kuti, “Pitani ku mudzi uli patsogolo panu, ndipo mukakangolowa mʼmenemo mukapeza bulu womangidwa ali ndi mwana pa mbali pake. Mukawamasule ndipo mubwere nawo kwa Ine. 3 Wina akakayankhula, mukamuwuze kuti Ambuye akuwafuna, ndipo adzawatumiza nthawi yomweyo.”
4 Izi zinachitika kukwaniritsa zimene zinayankhulidwa ndi mneneri:
5 “Uza mwana wamkazi wa Ziyoni,
taona, mfumu yako ikubwera kwa iwe,
yofatsa ndi yokwera pa bulu,
pa kamwana ka bulu, mwana wa nyama yonyamula katundu.”
6 Ophunzirawo anapita nachita monga Yesu anawalamulira. 7 Anabweretsa bulu ndi mwana wake, nayala zovala zawo pa abuluwo, ndipo Yesu anakwerapo. 8 Gulu lalikulu la anthu linayala zovala zawo mu msewu pamene ena anadula nthambi zamitengo ndi kuziyala mu msewumo. 9 Magulu amene anali patsogolo pake ndi amene amamutsatira anafuwula kuti,
“Hosana Mwana wa Davide!”
“Wodala Iye amene abwera mʼdzina la Ambuye!”
“Hosana mmwambamwamba!”
10 Yesu atalowa mu Yerusalemu, mzinda wonse unatekeseka ndipo anthu anafunsa kuti, “Ndani ameneyu?”
11 Magulu a anthu anayankha kuti, “Uyu ndi Yesu, mneneri wochokera ku Nazareti.”
Yesu mʼNyumba ya Mulungu
12 Yesu analowa mʼdera lina la Nyumba ya Mulungu ndipo anatulutsa kunja anthu onse amene ankachita malonda. Anagubuduza matebulo a osinthira ndalama ndi mipando ya ogulitsa nkhunda. 13 Iye anawawuza kuti, “Zinalembedwa kuti Nyumba yanga idzatchedwa Nyumba ya mapemphero koma inu mwayisandutsa phanga la anthu achifwamba.”
14 Anthu osaona ndi olumala anabwera kwa Iye mʼNyumba ya Mulungu ndipo anawachiritsa. 15 Koma akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo ataona zodabwitsa zimene anachita, komanso ana akufuwula mʼNyumbayo kuti, “Hosana kwa Mwana wa Davide,” anapsa mtima.
16 Anamufunsa kuti, “Kodi mukumva zimene anawa akunena?”
Yesu anayankha nati, “Inde. Kodi simunawerenge kuti,
“Kuchokera mʼkamwa mwa ana ndi makanda
mwatuluka mayamiko?”
17 Ndipo anawasiya natuluka mu mzindawo ndi kupita ku Betaniya, kumene anakagona.
Yesu Atemberera Mtengo wa Mkuyu
18 Mmamawa, pamene amabwera ku mzinda, anamva njala. 19 Ataona mtengo wamkuyu mʼmbali mwa msewu, anapitapo koma sanapeze kanthu koma masamba okhaokha. Pamenepo anati kwa mtengowo, “Usadzabalenso chipatso!” Nthawi yomweyo mtengowo unafota.
20 Ophunzira ataona zimenezi, anadabwa nafunsa kuti, “Kodi mtengo wamkuyuwu wauma msanga bwanji?”
21 Yesu anayankha kuti, “Zoonadi, ndikuwuzani kuti ngati muli ndi chikhulupiriro ndipo simukayika, simudzangochita zokha zachitika kwa mkuyuzi, koma mudzatha kuwuza phiri ili kuti, ‘Pita, kadziponye wekha mʼnyanja,’ ndipo zidzachitikadi. 22 Ngati mukhulupirira, mudzalandira chilichonse chimene muchipempha mʼpemphero.”
Amufunsa Yesu za Ulamuliro Wake
23 Yesu analowa mʼNyumba ya Mulungu, ndipo pamene ankaphunzitsa, akulu a ansembe ndi akuluakulu anabwera kwa Iye namufunsa kuti, “Muchita izi ndi ulamuliro wanji ndipo anakupatsani ndani ulamuliro umenewu?”
24 Yesu anayankha kuti, “Inenso ndikufunsani funso limodzi, mukandiyankha, Inenso ndikukuwuzani ndi ulamuliro wa yani umene ndikuchitira izi. 25 Ubatizo wa Yohane unachokera kuti? Kumwamba kapena kwa anthu?”
Anakambirana pakati pawo ndipo anati, “Tikati, ‘Kuchokera kumwamba,’ Iye adzafunsa kuti, ‘Bwanji simunakhulupirire?’ 26 Koma tikati, ‘Kuchokera kwa anthu,’ ife tikuopa anthuwa, pakuti onse amakhulupirira kuti Yohane anali mneneri.”
27 Choncho anamuwuza Yesu kuti, “Sitikudziwa.”
Pamenepo Iye anati, “Inenso sindikuwuzani kuti ndi ulamuliro wa yani umene ndichitira izi.”
Fanizo la Ana Amuna Awiri
28 “Kodi muganiza bwanji? Panali munthu wina anali ndi ana aamuna awiri. Anapita kwa woyamba nati, ‘Mwanawe pita kagwire ntchito lero mʼmunda wamphesa.’
29 “Iye anayankha kuti, ‘Sindipita,’ koma pambuyo pake anasintha maganizo napita.
30 “Kenaka abambowo anapita kwa mwana winayo nanena chimodzimodzi. Iye anayankha kuti, ‘Ndipita abambo,’ koma sanapite.
31 “Ndani wa awiriwa anachita chimene abambo ake amafuna?”
Anamuyankha nati, “Woyambayo.”
Yesu anawawuza kuti, “Ndikuwuzani zoonadi, kuti amisonkho ndi adama akulowa mu ufumu wa Mulungu inu musanalowemo.” 32 Pakuti Yohane anabwera kwa inu kuti akuonetseni njira yachilungamo, koma inu simunakhulupirire iye, koma amisonkho ndi adama anamukhulupirira. Koma ngakhale munaona izi, simunatembenuke mtima ndi kumukhulupirira iye.
Fanizo la Alimi
33 “Tamverani fanizo lina: Panali mwini munda amene anadzala mphesa. Anamanga mpanda kuzungulira mundawo, nakumba moponderamo mphesa ndipo anamanga nsanja. Kenaka anabwereketsa munda wamphesawo kwa alimi ena napita pa ulendo. 34 Pamene nthawi yokolola inakwana, anatumiza antchito ake kwa matenanti aja kuti akatenge zipatso zake.
35 “Alimi aja anagwira antchito ake; namenya mmodzi, napha wina, ndi kumuponya miyala wachitatuyo. 36 Kenaka anatumiza antchito ena oposa oyambawo ndipo matenantiwo anawachitira chimodzimodzi. 37 Pomalizira anatumiza mwana wake. Anati adzamuchitira ulemu mwana wanga.
38 “Koma alimiwo ataona mwanayo anati kwa wina ndi mnzake, ‘Uyu ndiye olowa mʼmalo mwa abambo ake. Tiyeni timuphe ndipo titenge cholowa chake.’ 39 Pamenepo anamutenga namuponyera kunja kwa munda wamphesa namupha.
40 “Tsono akabwera mwini munda wamphesa adzachita nawo chiyani matenantiwo?”
41 Iwo anayankha kuti, “Adzawapha moyipa alimi oyipawo ndipo adzabwereketsa mundawo kwa alimi ena amene adzamupatsa gawo lake la mbewu pa nthawi yokolola.”
42 Yesu anawawuza kuti, “Kodi simunawerenge mʼmalemba kuti:
“ ‘Mwala umene omanga nyumba anawukana,
womwewo wasanduka mwala wofunika kwambiri wa pa ngodya.
Ambuye wachita izi,
ndipo ndi zodabwitsa mʼmaso mwathu.’
43 “Nʼchifukwa chake ndi kukuwuzani kuti ufumu wa Mulungu udzalandidwa kwa inu ndipo udzapatsidwa kwa anthu amene adzabereka chipatso chake. 44 Amene agwa pa mwalawu adzadukaduka, ndipo amene udzamugwere udzamuthudzula.”
45 Akulu a ansembe ndi Afarisi atamva mafanizo a Yesu, anadziwa kuti ankanena iwo. 46 Pamenepo anafuna njira yoti amugwirire, koma anaopa gulu la anthu chifukwa anthu onse ankakhulupirira kuti Iye anali mneneri.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.