Beginning
Malo Atsopano a Nyumba ya Mulungu
40 Kumayambiriro a chaka cha 25, cha ukapolo wathu, tsiku la khumi lamwezi, patapita zaka khumi ndi zinayi mzinda wa Yerusalemu utawonongedwa, pa tsiku lomwelo dzanja la Yehova linali pa ine ndipo Iye anapita nane ku Yerusalemu. 2 Mʼmasomphenyawo Yehova ananditenga ndi kupita nane ku dziko la Israeli ndipo anandiyika pa phiri lalitali kwambiri, moti ndinaona ngati mzinda. 3 Atandifikitsa kumeneko ndinaona munthu wonyezimira ngati mkuwa. Iye anali atayima pa chipata ndipo mʼdzanja lake munali chingwe cha nsalu yabafuta ndi ndodo yoyezera. 4 Munthuyo anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, penyetsetsa ndipo umvetse bwinobwino. Uyikepo mtima wako pa zonse zimene ndikukuonetsa pakuti anakubweretsa kuno kuti uwone zimenezi. Tsono ukawawuze Aisraeli zonse zimene uzione.”
Chipata Chakummawa
5 Ine ndinaona khoma litazungulira mbali zonse za Nyumba ya Mulungu. Mʼdzanja la munthuyo munali bango lopimira limene kutalika kwake kunali kwa mamita atatu. Atayeza chipupacho anapeza kuti kuchindikira kwake kunali mamita atatu, ndiponso kutalika kwake kunalinso mamita atatu.
6 Anapita ku chipata chakummawa. Anakwera pa makwerero a nyumbayo, nayeza chiwundo choyamba cha chipatacho; kutalika kwake kunali mamita atatu. 7 Kudutsa chiwundo choyambachi, panali zipinda za alonda zisanu ndi chimodzi, zitatu kudzanja lamanja, zitatu kudzanja lamanzere. Chilichonse chinali cha mamita atatu mulitali mwake, chimodzimodzinso mulifupi mwake. Mipata ya pakati pa zipindazo inali ya mamita awiri ndi theka. Ndipo chiwundo cha pa chipata pafupi ndi khonde lapachipata, chinali mamita atatu.
8 Ndipo iye anayeza khonde la chipata ndipo chinali cha mamita atatu. 9 Anayeza khonde ndipo linali mamita anayi. Mphuthu zake zinali mita imodzi kuchindikira kwake. Khonde lamʼkati lapachipata linali kumapeto kwenikweni pafupi ndi Nyumba ya Mulungu.
10 Mʼkati mwa chipata chakummawa munali zipinda za alonda zitatu mbali iliyonse. Zitatu zonsezo zinali zofanana, ndipo khonde la pakati pa zipindazo linali lofanana. 11 Kenaka anayeza chipata cholowera; mulifupi mwake munali mamita asanu ndipo mulitali mwake munali mamita asanu ndi limodzi ndi theka. 12 Kutsogolo kwa chipinda chilichonse cha alonda kunali khoma lalifupi lotalika theka la mita, ndipo mbali iliyonse ya zipinda za alondazo inali yotalika mamita atatu. 13 Ndipo anayeza kutalika kwa mulifupi mwa chipata cholowera, kuchokera ku khoma lakumbuyo la chipinda chimodzi mpaka ku khoma la chipinda china; kuchokera ku chitseko mpaka ku chitseko china. Kutalika kwake kunali mamita khumi ndi awiri ndi theka. 14 Anayezanso khonde lamʼkati ndipo linali la mamita makumi atatu. Ndipo mozungulira khondelo munali bwalo. Muyesowu sukuphatikiza khonde loyangʼanana ndi bwalo. 15 Kuchokera pa chipata cholowera mpaka ku mapeto a khonde la chipata, kutalika kwake kunali mamita 27. 16 Makoma a zipinda ndiponso makoma a pakati pa zipindazo anali ndi mazenera. Khonde lamʼkati linalinso ndi mazenera mʼkati mwake. Pa makoma onsewo anajambulapo zithunzi za kanjedza.
Bwalo la Kunja
17 Kenaka munthuyo anandilowetsa mʼbwalo lakunja, ndipo ndinaona zipinda zina ndi msewu wa miyala wozungulira bwalo lonse. Zipinda zonse zinali makumi atatu ndipo zinkayangʼana msewuwo. 18 Utali wa mulifupi mwa msewuwo unkayenda mamita 27 kufanana ndi utali wa chipata cholowera. Uwu unali msewu wa mʼmunsi. 19 Tsono, anayeza kutalika kwa bwalo kuyambira chipata cholowera choyamba mpaka polowera pa chipata chakunja cha bwalo la mʼkati. Kutalika kwake kunali mamita makumi asanu.
Chipata Chakumpoto
20 Kenaka munthuyo anayeza mulitali ndi mulifupi mwa chipata chimene chimayangʼana kumpoto, chotulukira kunja. 21 Zipinda za alonda zimene zinalipo zitatu mbali iliyonse, makoma ake ndi khonde zinali ndi muyeso wofanana ndi wachipata choyamba chija. Kutalika kwake kunali mamita 27 ndipo mulifupi mwake munali mamita 13. 22 Mipata yake, khonde lake ndi zojambula za kanjedza zinali ndi miyeso yofanana ndi za chipata chakummawa. Chipatacho chinali ndi makwerero asanu ndi awiri ndipo kotsirizira kwa chipatacho kunali khonde. 23 Panalinso chipata cholowera ku bwalo lamʼkati chofanana ndi chakummawa chimene chimayangʼanana ndi chipata chakumpoto, chofanana ndi cha mbali ya kummawa. Anachiyeza kuchokera ku chipata china mpaka ku chipata china. Kutalika kwake kunali mamita makumi asanu.
Chipata Chakummwera
24 Ndipo munthuyo anapita nane ku mbali yakummwera ndipo ndinaona chipata chakummwera. Iye anayeza mphuthu zake ndi khonde ndipo zinali ndi miyeso yofanana ndi ya zina zija. 25 Mʼzipinda za chipata cholowera chimenechi ndi mʼkhonde lake munali mipata yofanana ndi ya mʼzipinda zina. Mulitali mwake munali mamita 27, mulifupi mwake munali mamita 13. 26 Chipatacho chinali ndi makwerero asanu ndi awiri ndi khonde kotsirizira kwake. Chipindacho chinali ndi zojambula za kanjedza ku mbali zonse za makoma. 27 Bwalo lamʼkati linalinso ndi chipata kummwera. Munthuyo analiyeza kuchokera ku chipata chimenechi mpaka ku chipata chakunja. Kutalika kwake kunali mamita makumi asanu.
Zipata Zolowera ku Bwalo la Mʼkati
28 Ndipo munthu uja anandilowetsa mʼbwalo lamʼkati kudzera ku chipata chakummwera. Anayeza chipatachi ndipo chinali chofanana ndi zinzake zija. 29 Zipinda zake za alonda, makoma ake ndi khonde lake zinali zofanana ndi zina zija. Chipata cholowera ndi khonde lake zinali ndi mipata mʼmbali zonse. Mulitali mwake munali mamita 27 ndipo mulifupi munali mamita 13. 30 (Khonde lililonse la makonde atatu a zipata zolowera bwalo lamʼkati aja linali la mamita ozungulira mʼbwalo lamʼkati anali mamita 13 mulitali mwake, mamita awiri ndi theka mulifupi mwake). 31 Khonde lake linayangʼanana ndi bwalo lakunja. Pa mphuthu pake anajambulapo zithunzi za kanjedza mbali zonse ziwiri, ndipo linali ndi makwerero asanu ndi atatu.
32 Kenaka munthuyo anapita nane ku bwalo la mʼkati mbali ya kummawa, ndipo anayeza chipata cholowera; chinali chofanana ndi zinzake zina zija. 33 Zipinda zake za alonda, makoma ake ndi khonde lake zinali zofanana ndi zina zija. Chipata cholowera ndi khonde lake chinali ndi mipata mʼmbali zonse. Mulitali mwake munali mamita 27 ndipo mulifupi mwake munali mamita 13. 34 Khonde lake linayangʼanana ndi bwalo lakunja. Pa mphuthu pake anajambulapo zithunzi za kanjedza mbali zonse ziwiri, ndipo linali ndi makwerero asanu ndi atatu.
35 Kenaka anapita nane ku chipata chakumpoto ndipo anachiyeza. Chinali chofanana ndi zina zija. 36 Zipinda zake za alonda, makoma ake ndiponso khonde lake zinali zofanana ndi zina zija, ndipo chinalinso ndi mipata mbali zonse ziwiri. Mulitali mwake munali mamita 27 ndipo mulifupi mwake munali mamita 13. 37 Khonde lake limayangʼanana ndi bwalo lakunja. Pa mphuthu zake anajambulapo zithunzi za kanjedza mbali zonse ziwiri, ndipo linali ndi makwerero asanu ndi atatu.
Zipinda Zokonzeramo Nsembe
38 Panali chipinda ndipo khomo lake linali pafupi ndi khonde la chipata cholowera chamʼkati. Mʼchipinda mʼmenemo ankatsukira nyama ya nsembe yopsereza. 39 Pa khonde la chipatacho panali matebulo awiri, lina kuno lina uko. Ankapherapo nsembe zopsereza, nsembe zopepesera machimo ndi nsembe zopepesera kupalamula. 40 Panali matebulo anayi, awiri a iwo anali kunja kwa khoma la khonde pafupi ndi makwerero olowera pa chipata chakumpoto ndi awiri enawo anali mbali inayo ya makwerero. 41 Choncho ku mbali imodzi ya chipata kunali matebulo anayi, ndiponso ku mbali inayo kunali matebulo anayi. Onse pamodzi anali matebulo asanu ndi atatu. Pa matebulopo ankapherapo nyama za nsembe zopsereza. 42 Matebulo anayiwa anali a miyala yosema. Lililonse mulitali mwake linali la masentimita 75, mulifupi mwake linali la masentimita 75, ndipo msinkhu wake unali wa masentimita makumi asanu. Pa matebulopo amayikapo zipangizo zophera nsembe zopsereza ndi nsembe zina. 43 Choncho pa matebulopo ankayikapo nyama za nsembe zopsereza. Mbedza zitatu zazitali ngati chikhatho amazikoleka pa makoma pozungulira ponse.
Zipinda za Ansembe
44 Munthu uja anapita nane mʼkati mwa bwalo ndipo ndinaona zipinda ziwiri. Chimodzi chinali pafupi ndi chipata chakumpoto kuyangʼana kummwera ndi china chinali pafupi ndi chipata chakummwera kuyangʼana kumpoto. 45 Munthuyo anandiwuza kuti, “Chipinda chimene chikuyangʼana kummwera ndi cha ansembe amene amayangʼanira Nyumba ya Mulungu, 46 ndipo chipinda chimene chikuyangʼana kumpoto ndi cha ansembe amene amayangʼanira guwa lansembe. Amenewa ndiwo ana a Zadoki, ndipo ndi okhawo mwa zidzukulu za Levi amene ayenera kutumikira pamaso pa Yehova mʼNyumba ya Mulungu.”
47 Kenaka munthuyo anayeza bwalo; linali lofanana mbali zonse kutalika kwake, mulitali mwake munali mamita 53, ndipo mulifupi mwake munali mamita 53. Ndipo guwa lansembe linali kutsogolo kwa Nyumba ya Mulungu.
Nyumba ya Mulungu
48 Munthuyo anapita nane pa khonde la Nyumba ya Mulunguyo. Anayeza mphuthu za khondelo ndipo zinali mamita awiri ndi theka mbali zonse. Mulifupi mwa chipatacho munali mamita asanu ndi awiri ndipo mulifupi mwa makoma ake munali mamita awiri mbali zonse. 49 Mulitali mwa khonde munali mamita khumi, mulifupi mwake munali mamita asanu ndi limodzi kuchokera kutsogolo mpaka kumbuyo. Panali makwerero khumi, ndipo mbali zonse kunali nsanamira.
41 Ndipo munthuyo anapita nane mʼchipinda chopatulika cha Nyumba ya Mulungu ndipo anayeza khonde lake; mulifupi mwa khondelo munali mamita atatu mbali iliyonse kutalika kwake. 2 Mulifupi mwa khomo munali motalika mamita asanu. Makoma a mbali zonse anali a mamita awiri ndi theka mulifupi mwake. Anayezanso kutalika kwa chipinda chopatulika chija ndipo mulitali mwake munali motalika mamita makumi awiri ndi mulifupi mwake munali mamita khumi.
3 Kenaka munthuyo anakalowa mʼkati ndipo anayeza khonde la pa khomo; khondelo linali mita imodzi mulifupi mwake. Mulifupi mwa khondelo munali mamita atatu. 4 Ndiponso anayeza kutalika kwa chipinda chopatulika chenichenicho. Mulitali mwake munali mamita khumi, ndipo mulifupi mwake munali mamita khumi. Munthuyo anandiwuza kuti, “Ichi ndicho chipinda chopatulika kwambiri.”
5 Tsono munthuyo anayeza khoma la Nyumba ya Mulungu; kuchindikira kwake kunali mamita atatu. Panalinso zipinda zina kuzungulira Nyumba ya Mulungu ndipo chilichonse chinali cha mamita awiri mulifupi wake. 6 Zipindazo zinali zitatu zosanjikizana. Chigawo chilichonse chinali ndi zipinda makumi atatu. Pa makoma a Nyumba ya Mulungu panali zochirikiza zipindazo kuti zisatsamire khoma la Nyumba ya Mulungu. 7 Zipinda za mʼmbalizo zinkapita zikulirakulira pomakwera chipinda ndi chipinda potsata kukulirakulira kwa zochirikiza za zipinda zija. Pambali pa Nyumba ya Mulungu panali makwerero okwerera pamwamba, kuchokera chigawo chapansi kudzera chapakati, mpaka kukafika pamwamba.
8 Ndinaona chiwundo kuzungulira Nyumba ya Mulungu. Chinapanga maziko a zipindazo ndipo chinali cha mamita atatu. 9 Khoma lakunja la zipindazo linali la mamita awiri ndi theka kuchindikira kwake. Pakati pa chiwundocho 10 ndi zipinda za Nyumba ya Mulungu panali bwalo limeneli la mamita khumi kupingasa kwake kuzungulira Nyumba yonse ya Mulungu. 11 Zitseko za zipinda zamʼmbalizo zinali zotsekulira ku chiwundo. Chitseko chimodzi chinkayangʼana kumpoto ndipo china chinkayangʼana kummwera. Chiwundo chosamangapo kanthu chinali mamita awiri ndi theka kukula kwake kuzungulira ponseponse.
12 Nyumba imene inali chakummwera moyangʼanana ndi bwalo la Nyumba ya Mulungu inali mamita 35 mulifupi mwake. Khoma la nyumbayo linali mamita awiri ndi theka kuchindikira kwake kuzungulira ponseponse, ndipo mulitali mwake linali mamita 45.
13 Ndipo munthuyo anayeza Nyumba ya Mulungu ndipo mulitali mwake inali mamita makumi asanu. Nyumbayo ndi makoma ake, zonse zinali za mamita makumi asanu. 14 Kumaso kwa Nyumba ya Mulungu chakummawa kwa bwalolo mulifupi mwake munali mamita makumi asanu.
15 Kenaka anayeza kutalika kwa nyumba yoyangʼanana ndi bwalo chakumadzulo kwa Nyumba ya Mulungu, kuphatikizapo njira zamʼkati ku mbali iliyonse. Kutalika kwake kunali mamita makumi asanu.
Chipinda chachikulu cha Nyumba ya Mulungu, chimene chili chamʼkati, khonde lamʼkati loyangʼanana ndi bwalo, 16 mazenera ndi maferemu ake, zonsezi zinali zokutidwa ndi matabwa. Pamwamba moyangʼanana ndi chiwundo, Nyumba ya Mulungu inakutidwa ndi matabwa kuyambira pansi mpaka ku mazenera, (mazenerawo anali okutidwa), 17 pamwamba pa khomo lolowera ku malo opatulika amʼkati komanso kuzungulira makoma onse kunja ndi mʼkati, 18 anajambulapo zithunzi za kerubi mmodzi atakhala pakati pa kanjedza muwiri. Kerubi aliyense anali ndi nkhope ziwiri: 19 imodzi inali nkhope ya munthu yoyangʼana kanjedza mbali imodzi, ndi ina inali nkhope ya mkango yoyangʼana kanjedza mbali ina. Zinajambulidwa kuzungulira Nyumba ya Mulungu yonse. 20 Motero kuyambira pansi mpaka pamwamba pa khomo komanso pa makoma onse a chipinda chachikulu cha Nyumba ya Mulungu, anajambula zithunzi za akerubi ndi kanjedza pa makoma onse a malo opatulika.
21 Mphuthu za chipinda chachikulu cha Nyumba ya Mulungu kutalika kwake mbali zonse kunali kofanana. Ndipo kumaso kwa malo opatulika kunali chinthu china chooneka ngati 22 guwa lansembe la matabwa. Msinkhu wake unali mita imodzi ndi theka, mulitali mwake munali mita imodzi, mulifupi mwake munalinso mita imodzi. Mphuthu zake, tsinde lake ndi mbali zonse zinali za matabwa. Munthuyo anandiwuza kuti, “Tebulo limeneli ndilo limakhala pamaso pa Yehova.” 23 Chipinda chachikulu chija chinali ndi zitseko ziwiri. Malo opatulika aja analinso ndi zitseko ziwiri. 24 Chitseko chilichonse chinali ndi zigawo ziwiri zopatukana. 25 Ndipo pa zitsekopo anajambulipo zithunzi za akerubi ndi kanjedza monga zomwe anajambulapo pa makoma. Kunja kwake kunali ngati denga lamatabwa pamwamba pa khonde lamʼkati. 26 Pa mbali zonse za khonde lamʼkatilo panali mazenera, ndipo pa makoma ake onse anajambulapo zithunzi za kanjedza.
Zipinda za Ansembe
42 Pambuyo pake munthuyo anapita nane ku bwalo lakunja chakumpoto ndipo anafika nane ku zipinda zoyangʼanana ndi bwalo la Nyumba ya Mulungu ndi nyumba ina yakumpoto. 2 Nyumba yakumpotoyi mulitali mwake munali mamita makumi asanu, mulifupi mwake munali mamita 25. 3 Panali midadada iwiri, umodzi umayangʼanana ndi bwalo lamʼkati la mamita khumi, winawo umayangʼanana ndi bwalo lakunja. Midadada iwiriyi inali ya nyumba zitatu zosanjikana ndipo imayangʼanana. 4 Kumaso kwa zipindazo kunali njira yamʼkati, mulifupi mwake munali mamita asanu, mulitali mwake munali mamita makumi asanu. Makomo ake analoza chakumpoto. 5 Zipinda zammwamba zinali zazifupi mʼmimbamu kupambana zipinda zamʼmunsi ndi zipinda zapakati chifukwa njira zake zinatenga malo ambiri. 6 Popeza zipinda zinali zosanjikizana katatu ndipo zinalibe nsanamira monga za mabwalo, motero zipinda zamʼmwamba zinali zochepa kuyerekeza ndi zipinda zapansi ndi zipinda zapakati. 7 Panali khoma lakunja lomwe limatsatana ndi zipindazo kutsogolo kwake pambali pabwalo lakunja, kutalika kwake kunali mamita 25. 8 Zipinda za mʼmbali mwa bwalo lakunja mulitali mwake munali mamita 25. Koma zomwe zinali mʼmbali mwa Nyumba ya Mulungu, mulitali mwake munali mamita makumi asanu. 9 Pansi pa zipinda zimenezi panali khomo chakummawa kuchokera ku bwalo lakunja kumene khoma lake linkayambira.
10 Mbali yakummwera kuyangʼanana ndi bwalo ndi nyumbayo kunali zipinda zina. 11 Kumaso kwa zipindazi kunali njira. Zipindazi mulitali mwake, mulifupi mwake ndiponso maonekedwe ake onse zinali zofanana ndi zipinda zoyangʼana zakumpoto zija. Makomo ndi zitseko zake zinalinso zofanana 12 ndi makomo a zipinda zakummwera. Kunali khomo mʼmbali ya kummawa kumene ankalowerako. Kunalinso khoma logawa zipinda.
13 Ndipo munthuyo anandiwuza kuti, “Zipinda zakumpoto ndi zakummwera zoyangʼanana ndi bwalo la Nyumba ya Mulungu ndi zoyera. Mʼmenemo ansembe amene amakhala pafupi ndi Yehova amadyeramo zopereka zopatulika kwambiri. Mʼmenemo adzayikamo zopereka zopatulika kwambiri, zopereka za chakudya, nsembe zopepesera machimo ndi nsembe zopepesera kupalamula, poti malowo ndi opatulika. 14 Pamene ansembe alowa ku malo opatulikawa, asatuluke kupita ku bwalo lakunja popanda kusiya momwemo zovala zimene anavala potumikira zija, pakuti zovalazi ndi zopatulika. Avale kaye zovala zina ndipo akhoza kufika kwa anthu.”
15 Munthuyo atamaliza kuyeza zimene zinali mʼkati mwa Nyumba ya Mulungu, anatuluka nane pa chipata chakummawa ndi kuyeza bwalo lonse. 16 Anayeza mbali yakummawa ndi ndodo yake yoyezera; kutalika kwake kunali mamita 250. 17 Anayeza mbali ya kumpoto ndi ndodo yake; kutalika kwake kunali mamita 250. 18 Munthuyo anayeza mbali yakummwera; kutalika kwake kunali mamita 250 atayeza ndi ndodo yake. 19 Kenaka anatembenukira ku mbali ya kumadzulo ndi kuyeza ndi ndodo yake; kutalika kwake kunali mamita 250 atayeza ndi ndodo yake. 20 Motero anayeza mbali zonse zinayi. Panali khoma lozungulira bwalolo mulitali mwake munali mamita 250 ndipo mulifupi mwake munalinso mamita 250. Khomalo linali lolekanitsa zinthu zoyera ndi zinthu wamba.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.