Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Beginning

Read the Bible from start to finish, from Genesis to Revelation.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Ezekieli 9-12

Opembedza Mafano Aphedwa

Pambuyo pake Yehova anandiyankhula mofuwula kuti, “Bwerani pafupi, inu odzalanga mzindawu, aliyense ali ndi chida chake mʼmanja.” Ndipo ndinaona anthu asanu ndi mmodzi akubwera kuchokera ku chipata chakumtunda chimene chimaloza kumpoto, aliyense ali ndi chida choopsa cha nkhondo mʼdzanja lake. Pagulu pawopa panali munthu wovala chovala chabafuta, atatenga zolembera pambali pake. Iwo analowa ndi kuyima pambali pa guwa lamkuwa.

Tsono ulemerero wa Mulungu wa Israeli unakwera kuchokera pamwamba pa akerubi, pamene unali, ndipo unafika pa chiwundo cha Nyumba ya Mulungu. Pamenepo Yehova anayitana munthu amene anavala chovala chabafuta uja amene anatenga zolembera pambali pake ndipo anamuwuza kuti, “Pita mu mzinda wonse wa Yerusalemu ndi kuyika chizindikiro pamphumi pa anthu amene akumva chisoni ndi kulira chifukwa cha zinthu zonse zonyansa zimene zikuchitika mu mzindamo.”

Kenaka ndinamva Yehova akuwuza anthu ena aja kuti, “Mutsateni mu mzinda wonse ndipo mukakanthe aliyense mopanda kumvera chisoni kapena chifundo. Mukaphe kotheratu anthu okalamba, anyamata ndi atsikana, makanda ndi akazi koma musakakhudze wina aliyense amene ali ndi chizindikiro. Muyambire ku Nyumba yanga yopatulika.” Motero iwo anayamba ndi akuluakulu amene anali kutsogolo kwa Nyumba ya Mulungu.

Ndipo Yehova anawawuza kuti, “Ipitsani Nyumba ya Mulungu ndipo mudzaze mabwalo ake ndi anthu akufa. Pitani.” Choncho iwo anapita nayamba kupha anthu mu mzinda monse. Pamene iwo ankapha anthu, ine ndinatsala ndekha. Tsono ndinadzigwetsa chafufumimba ndi kufuwula kuti, “Aa, Ambuye Yehova! Kodi mwawakwiyiratu anthu a ku Yerusalemu motero kuti mudzawononga kotheratu anthu onse otsala ku Israeli?”

Iye anandiyankha kuti, “Tchimo la Aisraeli ndi Yuda ndi lalikulu kwambiri; dziko ladzaza ndi zophana ndipo mu mzinda mwadzaza ndi zosalungama. Iwo akunena kuti, ‘Yehova walisiya dziko lake; Yehova sakuona.’ 10 Choncho sindidzawamvera chisoni kapena kuwaleka, koma Ine ndidzawalanga potsata zochita zawo.”

11 Ndipo munthu wovala chovala chabafuta uja atatenga zolembera pambali pake anadzafotokozera Yehova kuti, “Ndachita monga munandilamulira.”

Ulemerero Uchoka ku mʼNyumba ya Mulungu

10 Ine nditayangʼana ku thambo limene lili pamwamba pa mitu ya akerubi ndinangoona chinthu chooneka ngati mpando waufumu wa mwala wa safiro. Tsono Yehova anawuza munthu wovala chovala chabafuta uja kuti, “Pita pakati pa mikombero kunsi kwa akerubi. Udzaze manja ako ndi makala oyaka amene ali pakati pa akerubiwo ndipo uwawaze mu mzinda.” Iye anachita zimenezi ine ndikuona.

Apa akerubiwo anali atayima mbali ya kummwera kwa Nyumba ya Mulungu pamene munthuyo ankalowa. Tsono mtambo unadzaza bwalo lamʼkati. Ndipo ulemerero wa Yehova unachoka pamwamba pa akerubi ndipo unafika ku chiwundo cha Nyumba ya Mulungu. Mtambo unadzaza Nyumba ya Mulungu, ndipo kuwala kwa ulemerero wa Yehova kunadzaza bwalolo. Phokoso la mapiko a akerubi limamveka mpaka ku bwalo lakunja, monga momwe linamvekera liwu la Mulungu Wamphamvuzonse akamayankhula.

Kenaka Yehova analamula munthu wovala chovala chabafuta uja kuti, “Pala moto pakati pa mikombero, pakati pa akerubi.” Munthu uja anapitadi nakayima pa mbali pa mkombero umodzi. Ndipo mmodzi wa akerubi anatambalitsa dzanja lake mpaka pa moto umene unali pakati pawo. Iye anapalako motowo ndipo anapatsa munthu wovala chovala chabafuta uja. Tsono iye anawulandira natuluka. Ndiye kuti kunsi kwa mapiko akerubi kumaoneka zinthu zooneka ngati manja a munthu.

Ine nditayangʼanitsitsa ndinaona mikombero inayi pambali pa akerubi. Pambali pa kerubi aliyense panali mkombero umodzi; mikomberoyo inkanyezimira ngati miyala yokongola ya krizoliti. 10 Maonekedwe a mikombero inayi ija anali ofanana. Mkombero uliwonse umaoneka ngati mkombero wolowana ndi unzake. 11 Poyenda akerubiwo, amapita mbali iliyonse ya mbali zinayizo kumene akerubiwo amayangʼana. Mikomberoyo simatembenuka pamene akerubiwo ankayenda. Kulikonse kumene mutu walunjika nʼkumene ankapita popanda kutembenuka. 12 Matupi awo onse, misana yawo, manja awo ndi mapiko awo zinali ndi maso okhaokha, monganso mʼmene inalili mikombero yawo inayi ija. 13 Ine ndinamva mikombero ikutchedwa kuti, “mikombero yakamvuluvulu.” 14 Kerubi aliyense anali ndi nkhope zinayi. Nkhope yoyamba inali ya Kerubi, nkhope yachiwiri inali ya munthu, nkhope yachitatu inali ya mkango ndipo nkhope yachinayi inali ya chiwombankhanga.

15 Tsono akerubi aja anawuluka. Izi zinali zamoyo zija zimene ndinaziona ku mtsinje wa Kebara. 16 Pamene akerubi ankayenda, nayonso mikombero ya mʼmbali mwawo inkayenda. Akerubiwo ankati akatambasula mapiko awo kuti auluke mikombero sinkachoka mʼmbali mwawo. 17 Akerubiwo ankati akayima, mikombero inkayimanso. Ngati akerubiwo auluka, mikomberoyo inkapita nawo chifukwa mzimu wa zamoyozo ndiwo unkayendetsa mikomberoyo.

18 Pamenepo ulemerero wa Yehova unachoka pa chiwundo cha Nyumba ya Mulungu ndi kukakhala pamwamba pa akerubi. 19 Ine ndikuona akerubi, anatambasula mapiko awo ndi kuwuluka. Pamene ankapita, mikombero inapita nawo pamodzi. Akerubi anakayima pa khomo la chipata cha kummawa cha Nyumba ya Yehova. Tsono ulemerero wowala wa Mulungu wa Israeli unali pamwamba pawo.

20 Izi ndizo zamoyo ndinaziona pansi pa Mulungu wa Israeli ku mtsinje wa Kebara, ndipo ndinazindikira kuti anali akerubi. 21 Kerubi aliyense anali ndi nkhope zinayi ndi mapiko anayi, ndipo kunsi kwa mapiko awo kunali chinthu chimene chimaoneka ngati manja a munthu. 22 Nkhope zawo zinali zofanana ndi zomwe ndinaziona ku mtsinje wa Kebara. Kerubi aliyense amayenda molunjika.

Chiweruzo pa Atsogoleri a Israeli

11 Pamenepo Mzimu wa Mulungu unandinyamula ndi kubwera nane ku chipata cha kummawa cha Nyumba ya Yehova. Kumeneko pa khomo la chipata panali anthu 25, ndipo ndinaona pakati pawo atsogoleri awa: Yaazaniya mwana wa Azuri ndi Pelatiya mwana wa Benaya. Yehova anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, awa ndi anthu amene akukonza zoyipa ndi kupereka malangizo oyipa mu mzindamo. Iwo amawuza anthu kuti, ‘Nthawi sinafike yoti timange Nyumba? Mzindawu uli ngati mʼphika umene uli pa moto ndipo ife tili ngati nyama mu mʼphikamo. Choncho iwe mwana wa munthu, unenere mowadzudzula. Nenera ndithu.’ ”

Ndipo Mzimu wa Yehova unandigwera ndipo unandiwuza kuti, “Unene kuti zimene akunena Yehova ndi izi. Iye akuti. ‘Izi ndi zimene mukunena, Inu Aisraeli, koma Ine ndikudziwa zimene zili mu mtima mwanu.’ Mwapha anthu ambiri mu mzinda muno ndipo mwadzaza misewu yake ndi mitembo.

“Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova akuti, ‘Mitembo imene mwayiponya mʼmisewuyo ndiyo nyama ndipo mzinda uno ndiwo mʼphika, koma Ine ndidzakuthamangitsanimo. Inu mumaopa lupanga, koma lupangalo ndi limene ndidzakubweretsereni, akutero Ambuye. Ine ndidzakuthamangitsani mu mzinda ndipo ndidzakuperekani mʼdzanja la alendo kuti akulangeni. 10 Mudzaphedwa ndi lupanga ndipo ndidzakulangani mpaka kumalire a Israeli. Pamenepo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova. 11 Mzinda uno sudzakhala ngati mʼphika wokutetezani ndipo simudzakhalanso ngati nyama ya mʼmenemo. Ndidzakulangani mpaka kumalire a Israeli. 12 Ndipo inu mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova. Inu simunatsatire malangizo anga kapena kusunga malamulo anga koma mwakhala mukutsata zochita za mitundu ina ya anthu imene yakuzungulirani.’ ”

13 Tsono pamene ndinkanenera, Pelatiya mwana wa Benaya anafa. Pomwepo ndinadzigwetsa pansi chafufumimba ndipo ndinafuwula ndi mawu aakulu kuti “Mayo, Ambuye Yehova! Kodi mudzawatheratu Aisraeli onse otsala?”

14 Yehova anayankhula nane kuti, 15 “Anthu okhala ku Yerusalemu akuwanena abale ako, anthu a ku ukapolo, onse a banja la Israeli, kuti, ‘Anthu onse amene anatengedwa ukapolo ali kutali ndi Yehova. Dziko lanu Yehova anatipatsa kuti likhale lathulathu.’ ”

Mulungu Alonjeza za Kubwerera kwa Israeli

16 “Nʼchifukwa chake nena kwa anzako a ku ukapolo kuti, ‘Ambuye Yehova akuti: Ine ndinawatumiza kutali pakati pa anthu a mitundu ina. Ndinawabalalitsa ku mayiko ambiri. Komabe ndakhala ndikuwasunga ku mayiko kumene anapitako!’

17 “Nʼchifukwa chake uwawuze zimene Ine Ambuye Yehova ndikunena kuti, Ndidzawasonkhanitsa kuchokera kwa anthu a mitundu inayo ndi kuwasonkhanitsira pamodzi kuchokera ku mayiko kumene ndinawabalalitsirako. Pambuyo pake ndidzawapatsa dziko la Israeli.

18 “Akadzalowa mʼdzikomo adzachotsa mafano awo onse oyipa ndi onyansa. 19 Ndidzawapatsa mtima watsopano ndipo ndidzayika mzimu watsopano mwa iwo. Ndidzachotsa mtima wowuma ngati mwala mwa iwo, ndipo ndidzawapatsa mtima wofewa ngati mnofu. 20 Motero adzatsata malamulo anga ndipo adzasunga mosamala malamulo anga. Adzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wawo. 21 Koma kunena za amene akupembedza mafano oyipa ndi onyansa, ndidzawalanga chifukwa cha zimene achita. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.”

22 Tsono akerubi aja anatambasula mapiko awo kuyamba kuwuluka, mikombero ili mʼmbali mwawo. Ulemerero wa Mulungu wa Israeli unali pamwamba pawo. 23 Ulemerero wa Yehova unakwera ndi kusiya mzindawo ndipo unakayima pa phiri cha kummawa kwake kwa mzindawo. 24 Pambuyo pake Mzimu wa Mulungu unandinyamula ndi kukandifikitsa. Zimenezi zinkachitika mʼmasomphenya monga mmene Mzimu wa Mulungu unkandionetsera.

Kenaka masomphenya amene ndinkawaonawo anayamba kuzimirira. 25 Ndipo ndinafotokozera akapolowo zonse zimene Yehova anandionetsa.

Chifaniziro cha Otengedwa Ukapolo

12 Yehova anayankhula nane kuti, “Iwe mwana wa munthu, ukukhala pakati pa anthu owukira, iwowo maso openyera ali nawo, koma sakuona ndipo makutu omvera ali nawo, koma sakumva chifukwa choti ndi anthu owukira.

“Choncho, iwe mwana wa munthu, longedza katundu wako wopita naye ku ukapolo. Unyamuke nthawi yamasana iwo akuona. Uchite ngati wanyamuka kuchoka kumene ukukhala kupita ku dziko lachilendo iwowo akuona. Mwina adzamvetsetsa, paja ndi anthu aupandu. Utulutse katundu wako wopita naye ku ukapolo nthawi ya masana iwo akuona. Ndipo nthawi ya madzulo, iwo akuona, uchoke monga ngati ukupita ku ukapolo. Iwo akuona, ubowole pa khoma ndipo utulutsirepo katundu wako. Usenze katundu wako pa phewa iwo akuona, ndipo upite kunja ku mdima. Uphimbe nkhope yako kuti usaone pansi, pakuti ndakusandutsa iwe chizindikiro chochenjeza Aisraeli.”

Choncho ine ndinachita monga momwe anandilamulira. Nthawi yamasana ndinatulutsa zinthu zanga nditazimanga ngati ndikupita ku ukapolo. Ndipo nthawi yamadzulo ndinabowola khoma ndi manja anga. Pamene chisisira chinkayamba, ndinasenza katundu wanga pa phewa kutuluka naye iwo akuona.

Mmawa mwake Yehova anandiyankhula nati: “Iwe mwana wa munthu, kodi anthu aupandu a Israeli sanakufunse kuti ukuchita chiyani?

10 “Uwawuze kuti, ‘zimene ndikunena Ine Ambuye Wamphamvuzonse ndi izi: Uthengawu ndi wonena za kalonga wa ku Yerusalemu pamodzi ndi banja lonse la Israeli amene akukhala kumeneko.’ 11 Uwawuze kuti, ‘Ndiwe chizindikiro chowachenjeza.’

“Zidzakuchitikirani monga momwe zakuchitikira iwemu. Iwo adzatengedwa kupita ku ukapolo.”

12 “Kalonga wawo adzatenga katundu wake nʼchisisira nʼkunyamuka. Adzatulukira pa bowo limene anthu anabowola pa khoma. Adzaphimba nkhope yake kuti asaone kumene akupita. 13 Ndidzayala ukonde wanga pa iye ndi kumukola mu msampha wanga. Ndidzabwera naye ku Babuloni, dziko la Akaldeya, koma sadzaliona dzikolo, ndipo adzafera kumeneko. 14 Ine ndidzabalalitsa kumbali zonse zinayi onse okhala naye pafupi, ndiwo omuthandiza ake pamodzi ndi ankhondo ake. Ndidzawalondola ndi lupanga losolola.

15 “Iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ndikadzawamwaza pakati pa anthu a mitundu ina ndi kuwabalalitsira ku mayiko ena. 16 Koma ndidzasiyako ena pangʼono amene adzapulumuke ku lupanga, njala ndi mliri, kuti akafotokoze ntchito zawo zonse zonyansa pakati pa anthu achilendo kumene akupitako. Pamenepo adzadziwa kuti ndine Yehova.”

17 Pambuyo pake Yehova anandiyankhulanso nati, 18 “Iwe mwana wa munthu, uzinjenjemera ukamadya chakudya chako, ndipo uzinthunthumira ndi mantha ukamamwa madzi ako. 19 Uwawuze anthu a mʼdzikomo kuti izi ndi zimene Ambuye Wamphamvuzonse akunena za anthu okhala mu Yerusalemu ndi dziko la Israeli: Iwo adzadya chakudya chawo ndi mantha ndi kumwa madzi awo ndi nkhawa. Zonse za mʼdziko lawo zidzalandidwa chifukwa cha ziwawa za anthu onse okhala mʼmenemo. 20 Mizinda imene ili ndi anthu idzasakazika ndipo dziko lidzasanduka chipululu. Pamenepo inu mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”

21 Yehova anayankhulanso nane kuti, 22 “Iwe mwana wa munthu, kodi mwambi umene ukunenedwa mu Israeli ndi wotani: ‘Masiku akupita koma masomphenya onse sakukwaniritsidwa?’ 23 Choncho uwawuze anthuwo kuti, ‘Ine Ambuye Yehova ndidzawuthetsa mwambi umenewu ndipo sadzawunenanso mu Israeli.’ Uwawuze kuti, ‘masiku ayandikira oti zonse zimene ndinanena mʼmasomphenya zichitikedi. 24 Pakuti masiku amenewo sikudzakhalanso masomphenya abodza kapena kuwombeza kwa chinyengo pakati pa anthu a Israeli. 25 Koma Ine Ambuye ndidzayankhula chimene ndikufuna, ndipo chidzachitikadi, osachedwa ayi. Pakuti mʼmasiku anu omwe ano, inu anthu opanduka, ndidzakwaniritsa chilichonse chimene ndidzanena. Ndikutero Ine Yehova.’ ”

26 Yehova anandiyankhula nati: 27 “Iwe mwana wa munthu, Aisraeli akunena kuti, ‘masomphenya amene ukuona sadzachitika kwa zaka zambiri. Iwo akuti ukulosa za zinthu zimene zidzachitika ku tsogolo kwambiri.’

28 “Choncho uwawuze kuti, ‘zimene Ine Ambuye Yehova ndikunena ndi izi: Zonena zanga sizidzachedwanso; chilichonse chimene ndikunena chidzachitikadi. Ndikutero Ine Yehova.’ ”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.