Beginning
Chizindikiro cha Chiweruzo
5 Tsiku lina Yehova anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, tsopano tenga lupanga lakuthwa ndipo uligwiritse ntchito ngati lumo lometera. Umete tsitsi ndi ndevu zako. Kenaka utenge sikelo ndipo ugawe tsitsilo patatu. 2 Kuzinga mzinda kuja kukatha, chimodzi cha zigawo zitatu za tsitsilo uchitenthe pakati pa mzinda. Chigawo chachiwiri uchiduledule ndi lupanga, poyenda muzungulire mzinda wonsewo. Chigawo chachitatu uchimwazire ku mphepo, ndidzachitsata nditasolola lupanga. 3 Koma utengeko tsitsi pangʼono, ulimange mu mpindiro wa mkanjo wako. 4 Pa tsitsi limeneli utapepo lina, uliponye pa moto ndi kulitentha. Moto udzayambira pamenepo mpaka ku nyumba yonse ya Israeli.”
5 Ambuye Yehova akunena kuti, “Uyu ndi Yerusalemu amene ndamuyika pakati pa mitundu ya anthu, ndipo mayiko onse amuzungulira. 6 Koma anthu a Yerusalemu aphwanya malamulo anga pochita zoyipa kuposa anthu a mitundu ina. Iwo anandipandukira kupambana anthu ena amene awazungulira. Iwo anakana malamulo anga ndipo sanasunge malangizo anga.
7 “Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova akuti: Popeza mwakhala osamvera kupambana anthu a mitundu ina amene akuzungulirani, popeza simunatsate malamulo anga kapena kusunga malangizo anga, mʼmalo mwake mwakhala mukutsata makhalidwe a anthu a mitundu ina amene akuzungulirani.
8 “Tsono Ambuye Yehova akuti: Ine mwini ndikutsutsana nawe, Yerusalemu, choncho Ine ndidzakulangani. Ine ndidzakulangani anthu a mitundu ina akuona. 9 Chifukwa cha ntchito zanu zonyansa ndidzakulangani ndi chilango chimene sindinakulangeni nacho nʼkale lomwe ndipo sindidzakulangani ndi chofanana nacho mʼtsogolomo. 10 Tsono pakati panu makolo adzadya ana awo, ndipo ana adzadya makolo awo. Ndidzakulanga ndipo otsala onse ndidzawabalalitsa ku mphepo zonse zinayi. 11 Ndithu, pali Ine, akutero Ambuye Yehova Wamoyo, pakuti mwayipitsa Nyumba yanga ndi mafano ano oyipa ndi miyambo yanu yonyansa, Inenso ndidzakulangani. Sindidzakulekererani kapena kukumverani chisoni. 12 Chimodzi mwa zigawo zitatu za anthu ako chidzafa ndi mliri, kapena chidzawonongeka ndi njala; chigawo china chidzaphedwa ndi lupanga kunja kwa mzinda, ndipo chigawo china ndidzachibalalitsira ku mphepo zonse zinayi pochita kuchithamangitsa.
13 “Ndi mmene udzachitire mkwiyo wanga. Ndikadzatsiriza kuwalanga, pamenepo mtima wanga udzakhala pansi. Adzadziwa kuti Ine Yehova ndinawayankhula mwa nsanje ndikadzawalanga.
14 “Ndidzakusandutsa iwe bwinja ndi chinthu chonyozeka pakati pa anthu a mitundu ina amene akuzungulira, ndi kwa onse odutsapo 15 Udzakhala chinthu chonyozeka ndi chonyogodoledwa. Udzakhala chenjezo ndi chinthu choopsa kwa anthu a mitundu ina amene akuzungulira ndikadzakulanga mokwiya ndi mwaukali ndi kugamula mlandu wako mokwiya. Ine Yehova ndayankhula. 16 Pamene ndidzakulasa ndi njala yolasa ngati mivi yoopsa ndi yosakaza ndidzatero nʼcholinga choti ndikuwonongeni. Ndidzagwetsa njalayo pa iwe mowirikiza pochepetsa chakudya chako cha tsiku ndi tsiku. 17 Ndidzatumiza njala ndi zirombo za kuthengo, ndipo zidzakulanda ana ako. Mliri ndi kuphana zidzakhala pakati pako, ndipo ndidzakubweretsera nkhondo. Ine Yehova ndayankhula.”
Uneneri Wotsutsa Mapiri a Israeli
6 Yehova anandipatsa uthenga uwu kuti, 2 “Iwe mwana wa munthu, yangʼana ku mapiri a Israeli; yankhula nawo modzudzula 3 kuti, ‘Inu mapiri a ku Israeli, imvani mawu a Ambuye Yehova. Iye akuwuza mapiri, magomo, mitsinje ndi zigwa kuti: Ine ndizakuthirani nkhondo ndipo ndidzawononga nyumba zanu mʼmene mukupembedzeramo mafano. 4 Maguwa anu ansembe adzagumulidwa ndipo maguwa anu ofukizira lubani adzaphwanyidwa; ndipo ndidzapha anthu anu pamaso pa mafano anu. 5 Ine ndidzagoneka mitembo ya Aisraeli pamaso pa mafano awo, ndipo ndidzamwaza mafupa anu mozungulira maguwa anu ansembe. 6 Konse kumene mumakhala, mizinda yanu idzasanduka bwinja. Nyumba zanu zopembedzera mafano zidzagumulidwa kotero kuti maguwa anu adzawonongedwa ndi kusakazidwa, mafano anu adzaphwanyidwa ndi kuwonongedwa. Maguwa anu ofukizirapo lubani adzagwetsedwa pansi ndipo zonse zimene munapanga zidzatheratu. 7 Anthu anu adzaphedwa pakati panu, ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.’
8 “Komabe ndidzasiya ena pangʼono opulumuka ku nkhondo. Iwowa ndidzawamwazira ku mayiko ena pakati pa anthu a mitundu ina. 9 Pamenepo opulumuka mwa inu adzandikumbukira ku mayiko kumene anatengedwa ukapolo. Ndidzawamvetsa chisoni chifukwa cha kusakhulupirika kwawo ndi kundipandukira kuja ndiponso chifukwa kuti anayika mtima wawo pa mafano. Choncho adzachita okha manyazi chifukwa cha zoyipa zimene ankachita ndi miyambo yonyansa imene ankatsata. 10 Ndipo iwo adzadziwa kuti ndine Yehova ndi kuti sindinkawaopseza chabe pamene ndinanena kuti ndidzawawononga.
11 “Ambuye Yehova akuti: Womba mʼmanja mwako ndipo uponde mapazi ako pansi mwamphamvu ndipo ufuwule kuti, ‘Mayo!’ chifukwa cha zonyansa ndi zoyipa zonse zimene Aisraeli achita, pakuti adzaphedwa ndi lupanga, njala ndi mliri. 12 Amene ali kutali adzafa ndi mliri, ndipo amene ali pafupi adzafa pa nkhondo, ndipo amene adzapulumuke ndi kusaphedwa adzafa ndi njala. Kotero ndidzakwaniritsa ukali wanga pa iwo. 13 Ndipo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pamene anthu awo adzagona atafa pakati pa mafano awo mozungulira maguwa awo ansembe, pamwamba pa magomo ndi mapiri onse, pansi pa mtengo uliwonse watambalala ndi wa thundu uliwonse wamasamba ambiri, kumalo kumene ankapereka nsembe zonunkhira kwa mafano awo onse. 14 Choncho ndidzawalanga ndi mkono wanga ndi kusandutsa dziko kukhala bwinja. Dziko lonse kumene akukhala kuyambira ku chipululu mpaka ku mzinda wa Ribula ndidzalisandutsa bwinja. Pamenepo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”
Chimaliziro Chafika
7 Yehova anandipatsa uthenga uwu kuti, 2 “Iwe mwana wa munthu, Ine Ambuye Yehova ndikuwuza dziko la Israeli kuti:
“Chimaliziro! Chimaliziro chafika
ku ngodya zinayi za dziko.
3 Chimaliziro chili pa iwe tsopano.
Mkwiyo wanga ndidzawuthira pa iwe.
Ndidzakuweruza molingana ndi machitidwe ako
ndi kukulanga chifukwa cha zonyansa zako.
4 Ine sindidzakumvera chisoni
kapena kukuleka.
Ndidzakulanga ndithu chifukwa cha ntchito zako zoyipa
komanso chifukwa cha miyambo yako yonyansa imene ili pakati pako.
Pamenepo udzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”
5 “Zimene ndikunena Ine Ambuye Yehova ndi izi:
“Chiwonongeko! Chiwonongeko chimene sichinamvekepo!
Taona chikubwera!
6 Chimaliziro chafika!
Chimaliziro chafika!
Chiwonongeko chakugwera.
Taona chafika!
7 Inu anthu okhala mʼdziko,
chiwonongeko chakugwerani.
Nthawi yafika, tsiku layandikira; tsiku la chisokonezo osati la chimwemwe pa mapiri.
8 Ine ndili pafupi kukukwiyirani,
ndipo ukali wanga udzathera pa iwe;
Ine ndidzakuweruza molingana ndi machitidwe ako
ndiponso ndidzakulanga chifukwa cha miyambo yako yonyansa.
9 Ine sindidzakumvera chisoni
kapena kukuleka.
Ndidzakulanga malingana ndi ntchito zako
ndiponso chifukwa cha miyambo yako yonyansa pakati pako.
‘Pamenepo udzadziwa kuti Ine Yehova ndine amene ndimakantha.’
10 “Taona, tsikulo!
Taona, lafika!
Chiwonongeko chako chabwera.
Ndodo yaphuka mphundu za maluwa.
Kudzitama kwaphuka.
11 Chiwawa chasanduka ndodo
yowakwapulira chifukwa cha kuyipa kwawo.
Palibe mwa anthu amenewo amene adzatsale.
Palibe ndi mmodzi yemwe mwa unyinji wawo.
Palibiretu ndipo sipadzapezeka
munthu wowalira maliro.
12 Nthawi yafika!
Tsiku layandikira!
Munthu wogula asakondwere
ndipo wogulitsa asamve chisoni,
popeza ukali wanga uli pa gulu lonse.
13 Wogulitsa sadzazipezanso zinthu
zimene anagulitsa kwa wina
chinkana onse awiri akanali ndi moyo,
pakuti chilango chidzagwera onsewo
ndipo sichingasinthike.
Chifukwa cha machimo awo, palibe aliyense
amene adzapulumutsa moyo wake.
14 “Lipenga lalira,
ndipo zonse zakonzeka.
Koma palibe ndi mmodzi yemwe amene akupita ku nkhondo,
pakuti mkwiyo wanga uli pa gulu lonse.
15 Ku bwalo kuli kumenyana
ndipo mʼkati muli mliri ndi njala.
Anthu okhala ku midzi
adzafa ndi nkhondo.
Iwo okhala ku mizinda
adzafa ndi mliri ndi njala.
16 Onse amene adzapulumuka
ndi kumakakhala ku mapiri,
azidzalira ngati nkhunda za ku zigwa.
Aliyense azidzabuwula chifukwa cha machimo ake.
17 Dzanja lililonse lidzalefuka,
ndipo bondo lililonse lidzalobodoka ngati madzi.
18 Iwo adzavala ziguduli
ndipo adzagwidwa ndi mantha.
Adzakhala ndi nkhope zamanyazi
ndipo mitu yawo adzameta mpala.
19 “Iwo adzataya siliva wawo mʼmisewu
ndipo golide wawo adzakhala chinthu chonyansa.
Siliva ndi golide wawo
sizidzatha kuwapulumutsa
pa tsiku la ukali wa Yehova.
Chuma chawochi sichidzawathandiza kuthetsa njala,
kapena kukhala okhuta,
pakuti ndicho chinawagwetsa mʼmachimo.
20 Iwo ankanyadira zodzikongoletsera zawo zamakaka
ndipo ankazigwiritsa ntchito kupanga mafano awo onyansa ndi zonyansa zawo zina.
Nʼchifukwa chake Ine ndidzazisandutsa
kukhala zowanyansa.
21 Ndidzazipereka kwa alendo kuti azifunkhe.
Anthu oyipa a dziko lapansi adzazilanda
ndi kudziyipitsa.
22 Ine ndidzawalekerera anthuwo
ndipo adzayipitsa malo anga apamtima.
Adzalowamo ngati mbala
ndi kuyipitsamo.
23 “Konzani maunyolo,
chifukwa dziko ladzaza ndi anthu opha anzawo
ndipo mzinda wadzaza ndi chiwawa.
24 Ndidzabweretsa mitundu ya anthu oyipitsitsa
kuti idzalande nyumba zawo.
Ndidzathetsa kunyada kwa anthu amphamvu
pamene anthu akunja adzalowa mʼmalo awo achipembedzo ndi kuyipitsamo.
25 Nkhawa ikadzawafikira
adzafunafuna mtendere koma osawupeza.
26 Tsoka lidzatsatana ndi tsoka linzake,
ndipo mphekesera idzatsatana ndi mphekesera inzake.
Iwo adzayesa kufuna masomphenya kuchokera kwa mneneri.
Adzasowa ansembe owaphunzitsa malamulo,
ndipo anthu akuluakulu sadzakhalanso ndi uphungu.
27 Mfumu idzalira,
kalonga adzagwidwa ndi mantha.
Manja a anthu a mʼdzikomo azidzangonjenjemera ndi mantha.
Ine ndidzawalanga molingana ndi machitidwe awo,
ndipo ndidzawaweruza molingana ndi momwe anaweruzira anzawo.
Choncho adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”
Kupembedza Mafano Mʼnyumba ya Mulungu
8 Tsiku lachisanu la mwezi wachisanu ndi chimodzi, mʼchaka chachisanu ndi chimodzi, ndinakhala mʼnyumba mwanga pamodzi ndi akuluakulu a ku Yuda. Tsono mphamvu za Ambuye Yehova zinandifikira. 2 Nditayangʼana ndinangoona chinthu chooneka ngati munthu. Kuchokera pamene pamaoneka ngati chiwuno chake kumatsika mʼmunsi anali ngati moto, ndipo kuchokera mʼchiwuno kukwera mmwamba amaoneka mowala ngati mkuwa wonyezimira. 3 Iye anatambasula chinthu chooneka ngati dzanja ndipo anagwira tsitsi la pamutu panga. Nthawi yomweyo Mzimu unandikweza mlengalenga. Tsono ndikumachita ngati ndikuona Mulungu kutulo, Mzimu uja unapita nane ku Yerusalemu nundiyika pa khomo la chipata chamʼkati choyangʼana kumpoto. Kumeneko kunali fano limene limaputa mkwiyo wa Mulungu. 4 Kumeneko ndinaona ulemerero wa Mulungu wa Israeli ngati momwe ndinaonera mʼmasomphenya mʼchigwa muja.
5 Tsono Yehova anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, tayangʼana kumpoto.” Choncho ndinayangʼana kumpoto ndipo ndinaona pa khomo la chipata pafupi ndi guwa lansembe ndinaona fano loputa mkwiyo wa Mulungu lija.
6 Ndipo Yehova anandifunsa kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi ukuona zimene akuchitazi, zonyansa zazikulu zimene Aisraeli akuchita kuno, zinthu zondichotsa Ine kumalo anga opatulika? Koma iwe udzaona zinthu zimene zili zonyansa kwambiri.”
7 Kenaka Iye anandipititsa ku khomo lolowera ku bwalo la Nyumba ya Mulungu. Nditayangʼanitsitsa ndinangoona dzenje pa khomapo. 8 Yehova anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, tsopano bowola pa khomapo.” Ndinabowoladi pa khomapo ndipo ndinapezapo khomo.
9 Ndipo Yehova anandiwuza kuti, “Lowa, ndipo ona zinthu zonyansa zimene akuchita pamenepa.” 10 Motero Ine ndinalowa ndi kuyangʼana, ndipo ndinaona pa makoma onse zithunzi za zinthu zosiyanasiyana zokwawa pansi, za nyama zonyansa ndiponso za mafano onse amene Aisraeli ankapembedza. 11 Patsogolo pa zimenezi panayima akuluakulu makumi asanu ndi awiri a Aisraeli, ndipo Yaazaniya mwana wa Safani anali atayima pakati pawo. Aliyense wa iwo anali ndi chofukizira lubani mʼdzanja lake ndipo utsi wa fungo lokoma la lubani unkafuka.
12 Tsono Yehova anandifunsa kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi waona zimene akuluakulu a Aisraeli akuchita mu mdima, aliyense akupembedza fano lakelake mʼnyumbamo? Iwo akuti, ‘Yehova sakutiona; Yehova walisiya dziko!’ 13 Iye anandiwuzanso kuti, ‘Iwe udzawaonanso akuchita zinthu zonyansa kwambiri.’ ”
14 Kenaka anapita nane pa khomo la ku khomo la chipata cha Nyumba ya Mulungu choyangʼana kumpoto, ndipo kumeneko ndinaona akazi ena atakhala pansi, akulira mulungu wawo wotchedwa Tamuzi. 15 Yehova anandifunsa kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi ukuziona zimenezi? Iwe udzaona zinthu zimene zili zonyansa kwambiri kuposa izi.”
16 Kenaka Iye anapita nane mʼkati mwa bwalo la Nyumba ya Yehova. Kumeneko ku khomo lolowera ku Nyumba ya Yehova pakati pa khonde ndi guwa lansembe, panali amuna 25. Anafulatira Nyumba ya Mulungu wa Yehova ndipo nkhope zawo zinaloza kummawa, ndipo ankapembedza dzuwa choyangʼana kummawa.
17 Yehova anandifunsa kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi waziona zimenezi? Kodi nʼchinthu chopepuka kuti anthu a ku Yuda azichita zonyansa zimene akuchitazi pano? Kodi afike mpaka pomafalitsa za ndewu mʼdziko lonse? Iwotu akuwutsa ukali wanga. Akundipsetsa mtima ndi zochita zawo! 18 Choncho Ine ndidzawalanga ndili wokwiya. Sindidzawamvera chisoni kapena kuwaleka. Ngakhale atandifuwulira mʼmakutu mwanga sindidzawamvera.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.