Beginning
Zolengedwa za Moyo ndi Ulemerero wa Yehova
1 Tsiku lachisanu la mwezi wachinayi, chaka cha makumi atatu, ine ndinali pakati pa amʼndende mʼmbali mwa mtsinje wa Kebara. Tsono kumwamba kunatsekuka ndipo ndinaona maonekedwe a Mulungu mʼmasomphenya.
2 Pa tsiku lachisanu la mwezi, chaka chachisanu Yehoyakini ali mʼndende, 3 Yehova anayankhula ndi wansembe Ezekieli, mwana wa Buzi, mʼmbali mwa mtsinje wa Kebara mʼdziko la Ababuloni. Dzanja la Yehova linali pa iye kumeneko.
4 Ndinayangʼana ndipo ndinangoona mphepo yamkuntho ikubwera kuchokera kumpoto. Panali mtambo waukulu wozunguliridwa ndi kuwala ndipo moto unali lawilawi kuchokera mu mtambowo. Pakati pa motowo pankaoneka ngati mkuwa wonyezimira. 5 Mʼkatikati mwa motowo munali zinthu zinayi zamaonekedwe a nyama. Thupi lawo limaoneka ngati la munthu 6 koma chilichonse chinali ndi nkhope zinayi ndiponso mapiko anayi. 7 Miyendo yake inali yowongoka; mapazi ake anali a ziboda ngati phazi la mwana wangʼombe. Ndipo zibodazo zinkawala ngati mkuwa wonyezimira. 8 Mʼmunsi mwa mapiko awo kumbali zonse zinayi, nyamazo zinali ndi manja a munthu. Zonse zinayi zinali ndi nkhope ndi mapiko, 9 ndipo mapiko awowo anakhudzana. Chilichonse chimapita molunjika kutsogolo; sizimatembenuka pamene zimayenda.
10 Nkhope zawo zimaoneka motere: Chilichonse chinali ndi nkhope ya munthu, ndipo mbali ya kumanja chilichonse chinali ndi nkhope zinayi zosiyana motere: nkhope ya munthu, nkhope ya mkango ku dzanja lamanja, nkhope ya ngʼombe ku dzanja lamanzere, ndipo kumbuyo kwake nkhope ya chiwombankhanga. 11 Ndi mʼmene zinalili nkhope zawo. Mapiko awo anali otambasukira mmwamba. Chamoyo chilichonse chinali ndi mapiko awiri okhudzana ndi mapiko a chinzake. Chinalinso ndi mapiko ena awiri ophimbira thupi lake. 12 Zamoyozo zinkayenda molunjika kutsogolo. Kulikonse kumene mzimu umazitsogolera kupita, nazonso zimapita kumeneko, osatembenuka pamene zikupita. 13 Pakati pa zamayozo panali chinthu chooneka ngati makala oyaka kapena miyuni yoyaka. Moto umayendayenda pakati pa zamayozo; wowala kwambiri, ndipo mphenzi zimatuluka pakati pawo. 14 Zamoyozo zinkathamanga uku ndi uko ngati kungʼanima kwa mphenzi.
15 Pamene ndinali kuyangʼana zamoyozo, ndinangoona mikombero ndipo pansi pambali pa chamoyo chilichonse panali mkombero umodzi. 16 Maonekedwe a mikomberoyo anali ngati mwala wonyezimira. Mikombero yonse inali yofanana ndipo mapangidwe awo anali ngati wongolowanalowana. 17 Mikombero ija poyenda inkatha kupita mbali iliyonse yomwe zamoyozo zinayangʼana popanda kutembenuka. 18 Marimu a mikomberoyo anali aatali ndi ochititsa mantha ndipo marimu onse anayi anali ndi maso ponseponse.
19 Zamoyozo zinkati zikamayenda, mikomberoyo imayendanso mʼmbali mwake; ndipo zamoyozo zinkati zikamakwera mmwamba, mikomberoyo imakweranso. 20 Kulikonse kumene mzimu wake unkazitsogolera, zamoyozo zinkapita komweko. Ndipo mikombero ija inkapita nawo pamodzi popeza kuti mzimu wa zamoyozo ndiwo umayendetsa mikombero ija. 21 Zamoyo zija zinkati zikamayenda mikombero imayendanso. Zamoyozo zimati zikayima, nayonso mikombero inkayima. Zamoyozo zinkati zikawuluka, mikomberonso imawuluka nazo pamodzi chifukwa mzimu wa zamoyo zija ndiwo umayendetsa mikombero ija.
22 Pamwamba pa mitu ya zamoyozo panali chinthu chonga thambo, lowala ndipo kunyezimira kwake ngati galasi loyangʼanitsa ku dzuwa, loyalidwa pamwamba pa mitu yake. 23 Zamoyozo zinatambalitsa mapiko ake mʼmunsi mwa thambo lija, mapiko ake ena kumakhudzana, mapiko awiri kumaphimba thupi lake. 24 Pamene zamoyo zimayenda ndimamva phokoso la mapiko ake, ngati mkokomo wa madzi ambiri, ngati liwu la Wamphamvuzonse, ngati phokoso la gulu lankhondo. Zimati zikayima zinkagwetsa mapiko ake.
25 Ndipo panamveka mawu kuchokera pamwamba pa thambo la pa mitu ya zamoyo zija. Nthawi iyi nʼkuti zamoyozo zitayima ndi kugwetsa pansi mapiko ake. 26 Pamwamba pa thambo la pa mitu yake panali chinthu chimene chimaoneka ngati mpando waufumu wopangidwa ndi mwala wa safiro, ndipo pamwamba pa mpando waufumuwo panali chinthu chooneka ngati munthu. 27 Ndinaona kuti mmwamba mwa chiwuno chake munali ngati chitsulo chowala konsekonse ngati moto. Mʼmunsi mwa chiwuno chake munalinso ngati moto wokhawokha. Kuwala kwa mphamvu kunamuzungulira munthuyo. 28 Kuwalako kunali ndi maonekedwe a utawaleza mʼmitambo tsiku limene kwagwa mvula.
Umu ndi mmene ulemerero wa Yehova umaonekera. Pamene ndinawuona ndinagwa pansi ndipo ndinamva mawu akundiyankhula.
Kuyitanidwa kwa Ezekieli
2 Iye anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, imirira kuti ndiyankhule nawe.” 2 Pamene ankayankhula nane, Mzimu wa Mulungu unalowa mwa ine ndipo unandiyimiritsa, ndipo ndinamva Iye akundiyankhula.
3 Iye anati, “Iwe mwana wa munthu, Ine ndikukutuma kwa Aisraeli, mtundu wa anthu owukira umene wandiwukira Ine; Iwo ndi makolo awo akhala akundiwukira Ine mpaka lero lino. 4 Ndikukutuma kwa anthu okanika ndiponso nkhutukumve. Ndikukutuma kuti akawawuze zimene Ine Ambuye Yehova ndikunena. 5 Kaya akamva kaya sakamvera, pakuti iwo ndi anthu opanduka, komabe adzadziwa kuti mneneri ali pakati pawo. 6 Tsono iwe mwana wa munthu, usachite nawo mantha kapena kuopa zimene azikanena. Usachite mantha, ngakhale minga ndi mkandankhuku zikuzinge ndipo ukukhala pakati pa zinkhanira. Usachite mantha ndi zimene akunena kapena kuopsedwa ndi nkhope zawo, popeza anthuwa ndi awupandu. 7 Ukawawuze ndithu mawu anga, kaya akamva kaya sakamva. Paja anthuwa ndi awupandu. 8 Koma iwe mwana wa munthu, mvetsera zimene ndikukuwuza. Usakhale wowukira ngati iwowo. Tsono yasama pakamwa pako kuti udye chimene ndikukupatsa.”
9 Nditayangʼana ndinangoona dzanja litaloza ine, litagwira mpukutu wolembedwa. 10 Anawufunyulura pamaso panga. Mpukutu wonse unali wolembedwa kuseri nʼkuseri. Ndipo mawu amene analembedwa mʼmenemo anali a madandawulo, maliro ndi matemberero.
3 Tsono Mulungu anandiwuza kuti, “Mwana wa munthu, idya chimene ndikukupatsachi. Idya kenaka upite ukayankhule ndi Aisraeli.” 2 Choncho ndinayasama ndipo anandipatsa mpukutuwo kuti ndidye.
3 Kenaka Iye anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, idya mpukutu umene ndikukupatsa kuti ukhute.” Choncho ndinadya, ndipo unkatsekemera ngati uchi mʼkamwa mwanga.
4 Pamenepo Iye anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, pita tsopano kwa Aisraeli ndipo ukawawuze mawu anga. 5 Sindikukutuma kwa anthu oyankhula chiyankhulo chachilendo ndi chovuta, koma kwa Aisraeli. 6 Sindikukutuma kwa mitundu yambiri ya anthu oyankhula chiyankhulo chachilendo ndi chovuta, amene mawu ake sungawamvetse. Ndithu ndikanakutuma kwa iwowa, bwenzi iwo atakumvera. 7 Koma Aisraeli sadzakumvera chifukwa iwo sakufuna kumvera Ine. Paja Aisraeli onse ndi okanika ndiponso a mtima wowuma. 8 Tsono ine ndakhwimitsa nkhope yako mofanana ndi nkhope zawo. Ndalimbitsanso mutu wako mofanana ndi mitu yawo. 9 Ine ndidzakusandutsa wolimba ngati mwala wa dayimondi umene uposa thanthwe lina lililonse kulimba kwake. Usachite nawo mantha kapena kuopsedwa nawo. Paja anthuwa ndi awupandu.”
10 Anatinso, “Iwe mwana wa munthu, umvetsetse bwino zimene ndikukuwuzazi ndipo mawu angawa uwasunge bwino mu mtima mwako. 11 Tsopano upite kwa Aisraeli anzako amene ali ku ukapolo ndipo ukayankhule nawo. ‘Kaya akamvera kaya sakamvera,’ koma uzikawawuza kuti, Ambuye Wamphamvuzonse akuti zakutizakuti.”
12 Pamenepo Mzimu unandinyamula ndipo kumbuyo kwanga ndinamva liwu lamphamvu ngati chivomerezi chachikulu, lonena kuti, “Utamandike ulemerero wa Yehova kumene Iye amakhala!” 13 Phokoso ndinkalimvalo linali la kugundana kwa mapiko a zamoyo ndiponso phokoso la mikombero ya pambali pake ija, limene linkamveka ngati chivomerezi chachikulu. 14 Mzimu wa Yehova unandikweza ndi kundinyamula ndipo ndinachokapo ndili wowawidwa ndi wonyuka mu mtima. Ndipo dzanja la Yehova linali pa ine mwa mphamvu. 15 Choncho ndinafika kwa amene anali mu ukapolo ku Telabibu pafupi ndi mtsinje wa Kebara. Ndinakhala pansi pakati pawo masiku asanu ndi awiri, ndili wothedwa nzeru kwambiri.
Chenjezo kwa Israeli
16 Atatha masiku asanu ndi awiriwo, Yehova anandiwuza kuti, 17 “Iwe mwana wa munthu, Ine ndakuyika kuti ukhale mlonda wa Aisraeli. Uziti ukamva mawu anga, ndiye uzikawachenjeza. 18 Ndikawuza munthu woyipa kuti, ‘Iwe udzafa ndithu,’ koma iwe osamuchenjeza kapena kumuyankhula kuti aleke njira zake zoyipa ndi kuti akhale ndi moyo, munthu woyipayo adzafa mu uchimo wake, koma Ine ndidzakuyimba mlandu chifukwa cha imfa yake. 19 Koma ukamuchenjeza munthu woyipa koma iye osatembenuka mtima kuleka zoyipa zake kapena kusiya njira zake zoyipa, munthuyo adzafa chifukwa cha uchimo wake koma iwe udzapulumutsa moyo wako.
20 “Ngati munthu wolungama asiya chilungamo chake ndi kuchita uchimo ndipo Ine nʼkumuyika mʼzoopsa, munthuyo adzafa ndithu. Popeza iwe sunamuchenjeze, adzafadi chifukwa cha tchimo ndipo chilungamo chake sichidzakumbukiridwa, koma ndidzakuyimba mlandu chifukwa cha imfa yake. 21 Koma ngati umuchenjeza munthu wolungama kuti asachimwe ndipo iye nʼkuleka kuchimwa adzakhala ndi moyo ndithu chifukwa anamvera chenjezo, ndipo iwe udzapulumutsa moyo wako.”
22 Nthawi ina dzanja la Yehova linali pa ine ndipo anandiwuza kuti, “Nyamuka upite ku chigwa, kumeneko ndikayankhula nawe.” 23 Choncho ndinanyamuka kupita ku chigwa. Ndipo ndinaona ulemerero wa Yehova kumeneko, ngati ulemerero umene ndinaona mʼmbali mwa mtsinje wa Kebara ndipo ndinagwa pansi chafufumimba.
24 Koma Mzimu wa Mulungu unalowa mwa ine ndipo unandiyimiritsa. Tsono Yehova anandiyankhula nati: “Pita, kadzitsekere mʼnyumba mwako. 25 Ndipo iwe mwana wa munthu, adzakumanga ndi zingwe motero kuti sudzatha kuyendanso pakati pa anthu. 26 Ndidzamatirira lilime lako kukhosi, kotero kuti udzakhala chete wosatha kuwadzudzula, chifukwa iwo ndi anthu aupandu. 27 Koma pamene ndidzayankhula kwa iwe, ndidzatsekula pakamwa pako ndipo udzawawuza kuti, ‘Ambuye Yehova akuti zakutizakuti.’ Aliyense wofuna kumva amve ndipo wokana kumva, muleke akane; pakuti iwo ndi anthu opanduka.”
Chionetsero cha Kuzingidwa kwa Yerusalemu
4 Mulungu anati, “Iwe mwana wa munthu, tsopano tenga njerwa, uliyike pamaso pako ndipo ujambulepo chithunzi cha mzinda wa Yerusalemu. 2 Ndipo uwuzinge mzindawo motere: uwumangire nsanja zowuzinga, uwumbire mitumbira ya nkhondo, uwumangire misasa ya nkhondo ndipo uyike zida zogumulira kuzungulira mzindawo. 3 Kenaka utenge chiwaya chachitsulo uchiyike ngati khoma lachitsulo pakati pa iwe ndi mzindawo. Uyangʼanitsitse mzindawo ndipo udzakhala wozingidwa ndi nsanja za nkhondo. Choncho umangire nsanja zankhondo. Chimenechi chidzakhala chizindikiro kwa Aisraeli.
4 “Tsono iwe ugonere kumanzere kwako ndipo ndidzayika pa iwe tchimo la Aisraeli. Iwe udzasenza tchimolo masiku onse amene udzagonere mbali imeneyo. 5 Ine ndakuyikira masiku okwana 390 malingana ndi zaka za machimo awo. Umu ndi mmene udzasenzere machimo a Aisraeli.
6 “Utatha zimenezo udzagonerenso mbali ya kudzanja lamanja, ndipo udzasenza machimo a anthu a ku Yuda masiku makumi anayi, tsiku lililonse kuyimira chaka chimodzi. 7 Tsono udzayangʼanitsitse nsanja za nkhondo zozinga. Dzanja la mkanjo wako utalikwinya ndi dzanja lako utakweza, udzalosere modzudzula Yerusalemu. 8 Ine ndidzakumanga ndi zingwe kotero kuti sudzatha kutembenukira uku ndi uku mpaka utatsiriza masiku akuzingidwa ako.
9 “Tsono tenga tirigu ndi barele, nyemba ndi mphodza, mapira ndi mchewere; ndipo uyike zonsezi mʼmbale imodzi ndipo upange buledi wako. Uzidya pa masiku 390 amene udzakhala ukugonera mbali imodzi. 10 Uyeze theka la kilogalamu la chakudyacho kuti uzidya tsiku lililonse kamodzi kokha. 11 Uyezenso zikho ziwiri zamadzi ndipo uzimwa tsiku ndi tsiku. 12 Uzidya chakudya chako ngati momwe amadyera keke ya barele. Uzidzaphika chakudyacho anthu akuona pogwiritsa ntchito ndowe ya munthu ngati nkhuni.” 13 Yehova anati, “Chimodzimodzi anthu a Israeli adzadya chakudya chodetsedwa ku mayiko achilendo kumene Ine ndidzawapirikitsira.”
14 Koma ine ndinati, “Zisatero, Ambuye Yehova! Ine sindinadziyipitsepo pa zachipembedzo. Kuyambira ubwana wanga mpaka tsopano, sindinadyepo kanthu kalikonse kopezeka katafa kapena kophedwa ndi zirombo za kutchire. Palibe nyama yodetsedwa pa zachipembedzo imene inalowa pakamwa panga.”
15 Iye anati, “Chabwino, ndidzakulola kuti uphike buledi wako ndi ndowe za ngʼombe mʼmalo mwa ndowe za munthu.”
16 Pambuyo pake anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, anthu a ku Yerusalemu ndidzawachepetsera chakudya. Anthuwo adzadya chakudya chochita kuyeza ndipo azidzadya mwa nkhawa. Azidzamwanso madzi ochita kuyeza ndiponso mwa mantha. 17 Ndidzachita zimenezi kuti adzasowe chakudya ndi madzi. Choncho adzachita nkhawa akumapenyana ndipo adzatheratu ndi kuwonda chifukwa cha machimo awo.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.