Beginning
Arekabu
35 Yehova anayankhula ndi Yeremiya nthawi ya ulamuliro wa Yehoyakimu mwana wa Yosiya mfumu ya Yuda, kuti: 2 “Pita ku banja la Arekabu ndipo ukawayitane kuti abwere mʼchipinda chimodzi cha Nyumba ya Yehova ndipo akafika uwapatse vinyo kuti amwe.”
3 Choncho ndinakatenga Yaazaniya (mwana wa Yeremiya winanso amene anali mwana wa Habaziniya), abale ake, ana ake onse aamuna ndi banja lonse la Arekabu. 4 Ndinabwera nawo ku Nyumba ya Yehova, ku chipinda cha ophunzira a mneneri Hanani mwana wa Igidaliya, munthu wa Mulungu. Chipinda chimenechi chinali pafupi ndi chipinda cha akuluakulu, chimene chinali pamwamba pa chipinda cha Maaseya mwana wa Salumu, mlonda wa pa khomo. 5 Kenaka ndinayika mabotolo odzaza ndi vinyo ndi zikho zake pamaso pa Arekabu ndipo ndinawawuza kuti, “Imwani vinyoyu.”
6 Koma iwo anayankha kuti, “Ife sitimwa vinyo, chifukwa kholo lathu Yehonadabu mwana wa Rekabu anatilamula kuti, ‘Inuyo ngakhale zidzukulu zanu, musadzamwe vinyo mpaka kalekale. 7 Musadzamange nyumba kapena kufesa mbewu, kapena kulima minda ya mpesa; musadzakhale ndi zinthu zimenezi. Mʼmalo mwake muzidzakhale mʼmatenti. Mukadzatero mudzakhala nthawi yayitali mʼdziko limene mukukhalamo.’ 8 Ife takhala tikumvera zonse zimene kholo lathu Yehonadabu mwana wa Rekabu anatilamula. Ife ngakhale akazi athu kapena ana athu aamuna ndi aakazi sitinamwepo vinyo 9 kapena kumanga nyumba kuti tizikhalamo kapenanso kukhala ndi minda ya mpesa, minda ina iliyonse kapena mbewu. 10 Koma takhala mʼmatenti ndipo tamvera kwathunthu chilichonse chimene kholo lathu Yehonadabu anatilamula. 11 Koma pamene Nebukadinezara mfumu ya Babuloni anathira nkhondo dziko lino, ife tinati, ‘Tiyeni tichoke, tipite ku Yerusalemu kuti tithawe magulu ankhondo a Akasidi ndi Aaramu.’ Kotero ife takhala tikukhala mu Yerusalemu.”
12 Yehova anayankhulanso ndi Yeremiya kuti, 13 “Iyeyu, Yehova Mulungu wa Israeli anawuza Yeremiya kuti: Pita ukawawuze anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu kuti, ‘Kodi simungatengeko phunziro ndi kumvera mawu anga?’ akutero Yehova. 14 ‘Yehonadabu mwana wa Rekabu analamula ana ake kuti asamwe vinyo ndipo lamulo limeneli alisunga. Mpaka lero lino iwo samwa vinyo, chifukwa akumvera lamulo la kholo lawo. Koma Ine ndakhala ndikuyankhula nanu kawirikawiri kukuchenjezani, koma inu simunandimvere Ine. 15 Kawirikawiri ndakhala ndikutumiza atumiki anga, aneneri, kwa inu. Iwo akhala akukuwuzani kuti, ‘Aliyense wa inu asiye ntchito zake zoyipa ndi kukonza makhalidwe ake; musatsatire milungu ina ndi kumayitumikira. Pamenepo mudzakhala mʼdziko limene ndinakupatsani ndi makolo anu.’ Komabe inu simunasamale zimenezi kapena kundimvera Ine. 16 Zidzukulu za Yehonadabu mwana wa Rekabu zakhala zikumvera lamulo limene kholo lawo anazilamula, koma inuyo simunandimvere Ine.
17 “Nʼchifukwa chake Yehova Mulungu Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti, ‘Ndidzagwetsera pa Yuda ndi pa onse okhala mu Yerusalemu masautso onse amene ndinakonza chifukwa sanandimvere. Ndinawayitana koma iwo sanayankhe.’ ”
18 Yeremiya anawuza banja la Arekabu mawu onse a Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, kuti, “Munamvera lamulo la kholo lanu Yehonadabu ndipo mwatsatira malangizo ake onse ndi kuchita chilichonse chimene anakulamulani.” 19 Tsono Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti, “Yehonadabu mwana wa Rekabu sadzasowa munthu wonditumikira Ine nthawi zonse.”
Yehoyakimu Atentha Buku la Yeremiya
36 Chaka chachinayi cha Yehoyakimu mwana wa Yosiya mfumu ya Yuda, Yehova anayankhula ndi Yeremiya kuti, 2 “Tenga buku ndipo ulembemo mawu onse amene ndayankhula nawe otsutsa Israeli, Yuda ndi mitundu yonse ya anthu, kuyambira nthawi imene ndinayamba kuyankhula nawe pa nthawi ya ulamuliro wa Yosiya mpaka lero lino. 3 Mwina mwake anthu a ku Yuda adzamva za zoopsa zonse zimene ndakonza kuti ndiwachitire, ndipo munthu aliyense adzatembenuka ndi kusiya ntchito zake zoyipa. Motero ndidzawakhululukira zoyipa zawo ndi machimo awo.”
4 Tsono Yeremiya anayitana Baruki mwana wa Neriya. Baruki analemba mʼbuku mawu onse amene Yeremiya ankamuwuza, mawu amene Yehova anamuwuza Yeremiya. 5 Kenaka Yeremiya anawuza Baruki kuti, “Ine andiletsa kupita ku Nyumba ya Mulungu. 6 Tsono iwe upite ku Nyumba ya Yehova pa tsiku losala kudya ndipo ukawerenge mawu a Yehova ochokera mʼbukumu amene ndinakulembetsa anthu onse akumva. Ukawawerengere anthu onse a ku Yuda amene amabwera ku Nyumba ya Mulungu kuchokera ku mizinda yawo. 7 Mwina mwake adzapempha kwa Yehova ndipo aliyense adzatembenuka ndi kusiya makhalidwe ake oyipa pakuti mkwiyo ndi ukali wa Yehova pa anthu awa ndi woopsa kwambiri.”
8 Baruki mwana wa Neriya anachita zonse zimene mneneri Yeremiya anamuwuza kuti achite. Mʼnyumba ya Yehova, iye anawerenga mawu a Yehova ochokera mʼbukulo. 9 Pa mwezi wachisanu ndi chinayi wa chaka chachisanu cha Yehoyakimu mwana wa Yosiya mfumu ya Yuda, anthu onse a mu Yerusalemu ndi onse amene anabwera kumeneko kuchokera ku mizinda ya Yuda, anapangana za kusala kudya kuti apepese Yehova. 10 Atayima pa chipinda cha Gemariya mwana wa mlembi Safani, chimene chinali mʼbwalo lapamwamba, pafupi ndi Chipata Chatsopano cholowera ku Nyumba ya Yehova, Baruki anawerenga mawu onse a Yeremiya amene anali mʼbuku muja kwa anthu onse amene anali ku Nyumba ya Yehova.
11 Mikaya mwana wa Gemariya, mwana wa Safani, atamva mawu onse a Yehova ochokera mʼbukumo, 12 anapita ku nyumba ya mfumu nakalowa ku chipinda cha mlembi. Akuluakulu, mlembi Elisama, Delaya mwana wa Semaya, Elinatani mwana wa Akibori, Gemariya mwana wa Safani, Zedekiya mwana wa Hananiya pamodzi ndi akuluakulu ena onse, anali atasonkhana kumeneko. 13 Tsono Mikaya anawafotokozera mawu onse amene anamva pamene Baruki ankawerenga buku lija anthu onse akumva. 14 Pambuyo pake akuluakulu onsewo anatuma Yehudi mwana wa Netaniya, mwana wa Selemiya, mwana wa Kusi, kwa Baruki kukamuwuza kuti, “Bwera ndi buku limene unawerenga kwa anthu.” Ndipo Baruki mwana wa Neriya anapita nalo bukulo kwa anthuwo. 15 Iwo anati, “Khala pansi, ndipo tiwerengere bukuli.”
Ndipo Baruki anawawerengera. 16 Atamva mawu onsewo, anayangʼanana mwa mantha ndipo anamuwuza Baruki kuti, “Ndithudi tikafotokozera mfumu mawu onsewa.” 17 Tsono anamufunsa Baruki kuti, “Tatiwuze, unalemba bwanji mawu onsewa? Kodi ndi Yeremiya anakulembetsa zimenezi?”
18 Baruki anayankha kuti, “Inde, ndi Yeremiya amene anandiwuza mawu onsewa, ndipo ine ndinawalemba ndi utoto mʼbukumu.”
19 Kenaka akuluakuluwo anamuwuza Baruki kuti, “Iweyo ndi Yeremiya, pitani mukabisale. Munthu aliyense asadziwe kumene muli.”
20 Atayika bukulo mʼchipinda cha mlembi Elisama, analowa mʼbwalo, napita kwa mfumu ndi kukayifotokozera zonse. 21 Itamva zimenezi mfumu inatuma Yehudi kuti akatenge bukulo, ndipo Yehudi anakalitenga ku chipinda cha mlembi Elisama ndipo anawerengera mfumu pamodzi ndi akuluakulu ake amene anali naye. 22 Unali mwezi wachisanu ndi chinayi ndipo mfumu inali mʼnyumba ya pa nyengo yozizira, ikuwotha moto umene anasonkha. 23 Yehudi ankati akawerenga masamba atatu kapena anayi a bukulo, mfumu inkawangʼamba ndi mpeni ndi kuwaponya pa moto ndipo anapitiriza kuchita zimenezi mpaka buku lonse linapsa. 24 Mfumu pamodzi ndi omutumikira ake onse amene anamva mawu onsewa sanachite mantha kapena kungʼamba zovala zawo. 25 Ngakhale kuti Elinatani, Delaya, ndi Gemariya anapempha mfumu kuti isatenthe bukulo, mfumuyo sinawamvere. 26 Mʼmalo mwake, mfumu inalamula Yerahimeeli mwana wake, Seraya mwana wa Azirieli ndi Selemiya mwana wa Abideeli kuti agwire mlembi Baruki ndi mneneri Yeremiya. Koma pamenepo nʼkuti Yehova atawabisa.
27 Mfumu itatentha buku limene linali ndi mawu amene Yeremiya anamulembetsa Baruki, Yehova anayankhula ndi Yeremiya kuti, 28 “Tenganso buku lina ndipo ulembe mawu onse amene anali mʼbuku loyamba lija, limene Yehoyakimu analitentha. 29 Ndiponso akamuwuze Yehoyakimu mfumu ya Yuda kuti, ‘Yehova akuti: Iwe unatentha buku lija ndipo unati: Nʼchifukwa chiyani unalemba kuti mfumu ya ku Babuloni idzabwera ndithu kudzawononga dziko lino ndi kupha anthu pamodzi ndi nyama zomwe?’ 30 Nʼchifukwa chake kunena za Yehoyakimu mfumu ya Yuda Yehova akuti sipadzaoneka munthu wina wolowa mʼmalo mwake pa mpando wa Davide. Akadzafa mtembo wake udzaponyedwa kunja ndipo udzakhala pa dzuwa masana, ndi pachisanu chowundana usiku. 31 Ndidzamulanga pamodzi ndi ana ake ndiponso omutumikira ake chifukwa cha zoyipa zawo; ndidzagwetsa pa iwo ndi pa onse amene akukhala mu Yerusalemu ndiponso pa anthu a ku Yuda masautso onse amene ndinawanena, chifukwa sanamvere.”
32 Choncho Yeremiya anatenga buku lina napatsa mlembi Baruki mwana wa Neriya, ndipo Yeremiya anamulembetsa mawu onse amene anali mʼbuku limene Yehoyakimu mfumu ya Yuda anatentha. Ndipo anawonjezerapo mawu ambiri monga omwewo.
Atsekera Yeremiya Mʼndende
37 Nebukadinezara mfumu ya Babuloni, inakhazika pa mpando waufumu Zedekiya mwana wa Yosiya kukhala mfumu ya Yuda. Iye analowa mʼmalo mwa Yehoyakini mwana wa Yehoyakimu. 2 Koma Zedekiya kapena atumiki ake ngakhalenso anthu a mʼdzikomo sanasamalire mawu a Yehova amene anayankhula kudzera mwa mneneri Yeremiya.
3 Tsono Zedekiya anatuma Yehukali mwana wa Selemiya ndi wansembe Zefaniya mwana wa Maseya kwa mneneri Yeremiya ndi uthenga uwu: “Chonde tipempherereni kwa Yehova Mulungu wathu.”
4 Nthawi imeneyinso nʼkuti Yeremiya ali ndi ufulu woyenda pakati pa anthu chifukwa anali asanaponyedwe mʼndende. 5 Nthawi imeneyinso nʼkuti gulu lankhondo la Farao litatuluka mʼdziko la Igupto. Ndipo Ababuloni amene anali atazinga Yerusalemu atamva zimenezi, anachoka ku Yerusalemuko.
6 Tsono Yehova anawuza mneneri Yeremiya kuti, 7 “Uyiwuze mfumu ya Yuda imene inakutuma kuti udzapemphe nzeru kwa ine kuti Ine Yehova, Mulungu wa Israeli ndikuti, gulu lankhondo la Farao limene linatuluka kuti lidzakuthandize lidzabwerera kwawo ku Igupto. 8 Ndipo Ababuloni adzabwerera kudzathira nkhondo mzinda uno. Iwo adzawugonjetsa ndi kuwutentha.
9 “Yehova akuti: Musadzinyenge, nʼkumaganiza kuti, ‘Ndithu Ababuloni adzatisiya.’ Ndithudi sadzakusiyani! 10 Ngakhale mutagonjetsa gulu lonse lankhondo la Ababuloni limene likukuthirani nkhondo ndipo mʼmatenti mwawo ndikutsala anthu ovulala okhaokha, amenewo adzabwera ndi kudzatentha mzinda uno.”
11 Gulu lankhondo la Ababuloni litaleka kuthira nkhondo mzinda wa Yerusalemu chifukwa choopa gulu lankhondo la Farao, 12 Yeremiya ananyamuka kuchoka ku Yerusalemu ndi kumapita ku dziko la Benjamini kuti akalandire gawo lake la minda ya makolo ake. 13 Koma atafika pa Chipata cha Benjamini, mkulu wa alonda amene dzina lake linali Iriya mwana wa Selemiya, mwana wa Hananiya, anagwira mneneri Yeremiyayo ndipo anati, “Iwe ukuthawira kwa Ababuloni!”
14 Yeremiya anati, “Zimenezo si zoona! Ine sindikuthawira kwa Ababuloni.” Koma Iriya sanamumvere. Mʼmalo mwake anagwira Yeremiya nʼkupita naye kwa akuluakulu. 15 Akuluakuluwo anamupsera mtima Yeremiya ndipo anamukwapula ndi kumuyika mʼnyumba ya mlembi Yonatani, imene anayisandutsa ndende.
16 Yeremiya anayikidwa mʼndende ya pansi pa nthaka, kumene anakhalako nthawi yayitali. 17 Kenaka Mfumu Zedekiya inatuma anthu kuti akayitane Yeremiya ndipo anabwera naye ku nyumba ya mfumu. Atafika mfumu inamufunsa mwamseri kuti, “Kodi pali mawu ena amene Yehova wakuwuza?”
Yeremiya anayankha kuti, “Inde. Inu mfumu mudzaperekedwa kwa mfumu ya ku Babuloni.”
18 Pamenepo Yeremiya anafunsa Mfumu Zedekiya kuti, “Kodi ndakulakwirani chiyani inuyo kapena akuluakulu anu kapenanso anthu awa, kuti mundiyike mʼndende? 19 Kodi ali kuti aneneri anu amene anakuloserani kuti, ‘Mfumu ya ku Babuloni sidzakuthirani nkhondo pamodzi ndi dziko lino’? 20 Koma tsopano, mbuye wanga mfumu, chonde tamverani. Loleni ndinene pempho langa pamaso panu: Musandibwezere ku nyumba ya mlembi Yonatani, kuopa kuti ndingakafere kumeneko.”
21 Tsono Mfumu Zedekiya analamula kuti Yeremiya asungidwe mʼbwalo la alonda. Ankamupatsa buledi tsiku ndi tsiku amene ankamugula kwa ophika buledi. Anapitiriza kutero mpaka buledi yense anatha mu mzindamo. Choncho Yeremiya anapitirira kukhala mʼbwalo la alonda.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.