Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Beginning

Read the Bible from start to finish, from Genesis to Revelation.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Yeremiya 14-17

Chilala, Njala, Lupanga

14 Awa ndi mawu amene Yehova anamuwuza Yeremiya onena za chilala:

“Yuda akulira,
    mizinda yake ikuvutika;
anthu ake adzigwetsa pansi mwachisoni,
    kulira kwa Yerusalemu kwakula.
Anthu awo wolemekezeka akutuma antchito awo kuti akatunge madzi.
    Apita ku zitsime
    osapezako madzi.
Choncho amabwerera ndi mitsuko yopanda madzi.
    Amanyazi ndi othedwa nzeru
    adziphimba kumaso.
Popeza pansi pawumiratu
    chifukwa kulibe madzi,
alimi ali ndi manyazi
    ndipo amphimba nkhope zawo.
Ngakhale mbawala yayikazi
    ikusiya mwana wake wakhanda ku thengo
    chifukwa kulibe msipu.
Mbidzi zikuyima pa zitunda zopanda kanthu
    nʼkumapuma wefuwefu ngati nkhandwe;
maso awo achita chidima
    chifukwa chosowa msipu.”

Anthu akuti, “Ngakhale machimo athu akutitsutsa,
    koma Inu Yehova chitanipo kanthu chifukwa cha dzina lanu.
Pakuti kusakhulupirika kwathu nʼkwakukulu;
    ife takuchimwirani.
Inu Yehova amene Aisraeli amakukhulupirirani
    ndi amene mumawapulumutsa pa nthawi ya masautso,
chifukwa chiyani mukukhala ngati mlendo mʼdziko muno?
    Chifukwa chiyani muli ngati wapaulendo amene akungogona tsiku limodzi?
Chifukwa chiyani muli ngati munthu amene wadzidzimutsidwa,
    kapena ngati wankhondo amene alibe mphamvu yopulumutsa?
Komabe Inu Yehova, muli pakati pathu,
    ndipo tikudziwika ndi dzina lanu;
    musatitaye ife!”

10 Zimene Yehova akunena za anthuwa ndi izi:

“Iwo amakonda kuyendayenda kwambiri;
    samatha kudziretsa.
Nʼchifukwa chake Ine Yehova sindingawalandire,
    ndipo tsopano ndidzakumbukira zoyipa zawo
    ndi kuwalanga chifukwa cha machimo awo.”

11 Kenaka Yehova anandiwuza kuti, “Usawapempherere anthu awa kuti zinthu ziwayendere bwino. 12 Ngakhale asale zakudya, Ine sindidzamva kulira kwawo; ngakhale apereke nsembe zopsereza ndi chopereka cha chakudya, sindidzazilandira. Mʼmalo mwake, ndidzawapha ndi lupanga, njala ndi mliri.”

13 Koma ine ndinati, “Aa, Ambuye Yehova, aneneri amawawuza anthuwo kuti, sadzaphedwa ndi lupanga kapena kuvutika ndi njala. Koma kuti Inu mudzawapatsa mtendere wokhawokha pamalo pano.”

14 Ndipo Yehova anandiwuza kuti, “Ndi zabodza kuti aneneriwa akunenera mʼdzina langa. Ine sindinawatume kapena kuwasankha kapenanso kuyankhula nawo. Iwo amakuwuzani zinthu zabodza zomwe amati anaziona mʼmasomphenya, kapena pogwiritsa ntchito mawula achabechabe. Zimene amayankhula ndi zongopeka mʼmutu mwawo. 15 Nʼchifukwa chake Ine Yehova ndikuti aneneri amenewa akulosera mʼdzina langa pamene Ine sindinawatume. Iwo amati simudzafa pa nkhondo kapena ndi njala mʼdziko muno. Koma tsono ndi iwowo, aneneriwa amene adzafe pa nkhondo kapena ndi njala. 16 Ndipo anthu amene anawaloserawo adzaponyedwa mʼmisewu ya mu Yerusalemu atafa ndi njala ndi lupanga. Sipadzapezeka wowayika mʼmanda popeza iwowo, akazi awo, ana awo aamuna, onse adzakhala atafa. Ine ndidzawagwetsera chilango chowayenera.

17 “Awuze mawu awa:

“ ‘Maso anga akugwetsa misozi kosalekeza
    usana ndi usiku;
chifukwa anthu anga okondedwa
    apwetekeka kwambiri,
    akanthidwa kwambiri.
18 Ndikapita kuthengo,
    ndikuona amene aphedwa ndi lupanga;
ndikapita mu mzinda,
    ndikuona amene asakazidwa ndi njala.
Ngakhale aneneri pamodzi
    ndi ansembe onse atengedwa.’ ”

19 Kodi anthu a ku Yuda mwawakana kwathunthu?
    Kodi mtima wanu wanyansidwa nawo anthu a ku Ziyoni?
Chifukwa chiyani mwatikantha chotere
    kuti sitingathenso kuchira?
Ife tinayembekezera mtendere
    koma palibe chabwino chomwe chabwera,
tinayembekezera kuchira
    koma panali kuopsezedwa kokhakokha.
20 Inu Yehova, ife tikuvomereza kuyipa kwathu
    ndiponso kulakwa kwa makolo athu;
    ndithu ife tinakuchimwiranidi.
21 Musatikane kuopa kuti dzina lanu linganyozedwe;
    musanyoze mpando wanu waufumu waulemerero.
Kumbukirani pangano lanu ndi ife
    ndipo musachiphwanye.
22 Mwa milungu yachabechabe ya anthu a mitundu ina,
    kodi pali mulungu amene angagwetse mvula?
Ife chikhulupiriro chathu chili pa Inu,
    popeza Inu nokha ndinu Yehova Mulungu wathu
    amene mukhoza kuchita zimenezi.

15 Kenaka Yehova anandiwuza kuti, “Ngakhale Mose ndi Samueli akanayima pamaso panga kupempherera anthu awa, Ine sindikanawachitira chisoni. Achotseni ndipo ndisawaonenso! Aleke apite! Ndipo ngati akufunsa iwe kuti, ‘Kodi tipite kuti?’ uwawuze kuti, ‘Yehova akuti,

“ ‘Oyenera kufa adzafa;
oyenera kufa ndi lupanga adzafa ndi lupanga;
oyenera kufa ndi njala adzafa ndi njala;
oyenera kupita ku ukapolo adzapita ku ukapolo.’

“Ine ndidzawatumizira mitundu inayi ya zinthu zowononga,” akutero Yehova, “lupanga lowapha, agalu owaluma, mbalame zamumlengalenga ndiponso zirombo zoti ziwadye ndi kuwawononga. Ndidzawasandutsa kukhala chinthu chonyansa kwa anthu a maufumu onse a dziko lapansi chifukwa cha zimene Manase mwana wa Hezekiya mfumu ya Yuda anachita mu Yerusalemu.

“Kodi adzakumvera chisoni ndani, Yerusalemu?
    Kodi adzakulira ndani?
    Kodi ndani amene adzapatuka kufunsa za moyo wako?
Inu mwandikana Ine,” akutero Yehova.
    “Inu mukubwererabe mʼmbuyo.
Choncho Ine ndidzakukanthani.
    Ndatopa ndi kukuchitirani chifundo.
Ine ndidzakubalalitsani kukuchotsani mʼmizinda ya mʼdzikomo
    monga mmene amachitira ndi mankhusu popeta ndi lichero.
Anthu anga ndinawaliritsa ndi kuwawononga
    chifukwa sanasinthe makhalidwe awo oyipa.
Ndinachulukitsa amayi awo amasiye
    kupambana mchenga wa kunyanja.
Amayiwo ndinawawonongera ana awo aamuna
    dzuwa lili pamutu.
Mwadzidzidzi ndinawagwetsera
    kuwawa mtima ndi mantha.
Mayi wa ana asanu ndi awiri wakomoka
    ndipo akupuma wefuwefu.
Dzuwa lake lalowa ukanali usana;
    anamuchititsa manyazi ndipo wathedwa nzeru.
Otsala ndidzawapereka mʼmanja mwa adani awo
    kuti awaphe ndi lupanga,”
            akutero Yehova.

10 Kalanga ine, amayi pakuti munandibereka ine,
    munthu amene ndikutsutsana ndi kulimbana ndi anthu pa dziko lonse!
Ine sindinakongoze kapena kukongola kanthu,
    komatu aliyense akunditemberera.

11 Yehova anati,

“Ndithudi, Ine ndidzakulanditsa kuti upeze bwino.
    Ndithudi, adani ako adzakupempha pa nthawi ya tsoka
    ndi ya mavuto awo.

12 “Palibe munthu amene angathe kudula chitsulo,
    makamaka chitsulo chochokera kumpoto chosakaniza ndi mkuwa.
13 Anthu ako ndi chuma chako
    ndidzazipereka kwa ofunkha popanda malipiro,
chifukwa cha machimo anu onse
    a mʼdziko lanu lonse.
14 Ndidzakusandutsani akapolo a adani anu
    mʼdziko limene inu simulidziwa,
chifukwa mkwiyo wanga wayaka ngati moto
    umene udzakutenthani.”

15 Ine ndinati, “Inu Yehova, mumadziwa zonse;
    kumbukireni ndi kundisamalira.
    Ndilipsireni anthu ondizunza.
Ndilezereni mtima musandilande moyo wanga.
    Onani momwe ndi kuvutikira chifukwa cha Inu.
16 Munandiyankhula ndipo mawu anu ndinawalandira bwino.
    Mawu anu anandipatsa chimwemwe ndipo mtima wanga unasangalala.
Paja ine, Yehova Mulungu Wamphamvuzonse,
    ndimadziwika ndi dzina lanu.
17 Sindinakhale nawo mʼgulu la anthu amadyera,
    sindinasangalale nawo anthu amenewo.
Ndinakhala ndekha chifukwa choti dzanja lanu linali pa ine
    ndipo munadzaza mu mtima mwanga ndi mkwiyo.
18 Nanga nʼchifukwa chiyani mavuto anga sakutha?
    Bwanji chilonda changa sichikupola?
Kodi inu mudzakhala ngati mtsinje wowuma nthawi yachilimwe,
    kapena ngati kasupe wopanda madzi?”

19 Tsono Yehova anandiyankha kuti,

“Ukabwerera kwa Ine, ndidzakulandiranso
    ndipo udzakhalanso mtumiki wanga.
Ngati udzayankhula mawu oyenera osati achabechabe,
    udzakhalanso mneneri wanga.
Anthu adzabwera kwa iwe
    ndipo sipadzafunika kuti iwe upite kwa iwo.
20 Ndidzakusandutsa ngati khoma lolimba
    ngati mkuwa kwa anthu awa.
Adzalimbana nawe
    koma sadzakugonjetsa,
pakuti Ine ndili nawe
    kukulanditsa ndi kukupulumutsa,”
            akutero Yehova.
21 “Ndidzakupulumutsa mʼdzanja la anthu oyipa
    ndipo ndidzakuwombola kwa anthu ankhanza.”

Tsiku la Masautso

16 Kenaka Yehova anandiwuza kuti, “Usadzakwatire ndi kubereka ana aamuna kapena aakazi malo ano pakuti ana aamuna ndi ana aakazi obadwira mʼdziko muno, komanso amayi awo ndi abambo awo amene anabereka anawo mʼdziko muno, adzafa ndi nthenda zoopsa. Sadzawalira maliro kapena kuyikidwa mʼmanda koma adzakhala ngati ndowe zotayikira pansi. Ena adzaphedwa ku nkhondo ndipo ena adzafa ndi njala. Mitembo yawo idzakhala chakudya cha mbalame zamlengalenga ndi zirombo zakuthengo.”

Yehova akuti, “Usalowe mʼnyumba ya maliro; usapite kukalira maliro kapena kukapepesa, chifukwa Ine ndawachotsera madalitso anga, chikondi changa ndi chifundo changa.” Akuluakulu ndi angʼonoangʼono omwe adzafa mʼdziko muno. Sadzayikidwa mʼmanda kapena kuliridwa, ndipo palibe amene adzaonetse chisoni podzichekacheka kapena kumeta tsitsi lake chifukwa cha iwo. Palibe amene adzapereka chakudya kutonthoza amene akulira maliro, ngakhale kuti womwalirayo ndi abambo ake kapena amayi ake.

“Ndipo usalowe mʼnyumba mmene muli madyerero, nʼkukhala pansi ndi kudya ndi kumwa nawo. Pakuti Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akunena kuti, ‘Pa nthawi yanu, inu mukuona ndidzathetsa mawu achimwemwe ndi achisangalalo ndiponso mawu a mkwati ndi mkwatibwi pa malo ano.’

10 “Ukawawuza anthu awa zinthu zonsezi akakufunsa kuti, ‘Chifukwa chiyani Yehova wanena kuti tsoka lalikulu lotere lidzatigwere? Kodi talakwa chiyani? Kodi tamuchimwira tchimo lotani Yehova Mulungu wathu?’ 11 Pamenepo ukawawuze kuti, ‘Nʼchifukwa chakuti makolo anu anandisiya Ine,’ akutero Yehova, ‘ndi kutsatira milungu ina, kuyitumikira ndi kuyipembedza. Iwo anandisiya Ine ndipo sanasunge lamulo langa. 12 Komanso inu munachimwa kwambiri kupambana makolo anu. Aliyense wa inu akutsatira zoyipa ndi mtima wake wokanikawo mʼmalo mondimvera Ine. 13 Choncho Ine ndidzakubalalitsani mʼdziko muno ndi kukulowetsani mʼdziko limene inu ndi makolo anu simunalidziwe. Kumeneko mukatumikira milungu ina usana ndi usiku, ndipo sadzakuchitirani chifundo.’ ”

14 Yehova akuti, “Komabe masiku akubwera pamene anthu polumbira sadzatinso, ‘Pali Yehova wamoyo, amene anatulutsa Aisraeli mʼdziko la Igupto,’ 15 koma adzanena kuti, ‘Pali Yehova wamoyo, amene anatulutsa Aisraeli ku dziko lakumpoto, ndi ku mayiko onse kumene anawabalalitsirako.’ Pakuti ndidzawabwezera ku dziko limene ndinalipereka kwa makolo awo.”

16 Yehova akuti, “Koma tsopano ndidzayitana adani okhala ngati asodzi ambiri, ndipo adzawagwira ngati nsomba. Izi zitatha adani enanso okhala ngati alenje ambiri, adzawasaka pa phiri lililonse, pa chitunda chilichonse ndiponso mʼmapanga onse a mʼmatanthwe. 17 Maso anga akuona makhalidwe awo onse; sanabisike pamaso panga. Palibe tchimo limene sindikulidziwa. 18 Ndidzawalanga mowirikiza chifukwa cha kuyipa kwawo ndi tchimo lawo. Ndidzatero chifukwa ayipitsa dziko langa ndi mafano awo amene ali ngati mitembo, ndiponso adzaza cholowa changa ndi mafano awo onyansa.”

19 Inu Yehova, ndinu mphamvu yanga ndi linga langa,
    pothawirapo panga nthawi ya masautso,
anthu a mitundu yonse adzabwera kwa Inu
    kuchokera ku mathero onse a dziko lapansi ndipo adzanena kuti,
“Makolo anthu anali ndi milungu yonama,
    anali ndi mafano achabechabe amene sanawathandize.
20 Kodi anthu nʼkudzipangira milungu?
    Atati atero ndiye kuti imeneyo ikhala milungu yachabechabe.”

21 “Choncho Ine ndidzawaphunzitsa,
    kokha kano kuti adziwe
    za mphamvu yanga ndi za nyonga zanga.
Pamenepo adzadziwa kuti
    dzina langa ndi Yehova.

17 “Tchimo la Yuda lazokotedwa ndi cholembera cha chitsulo,
    lalembedwa ndi msonga ya mwala wadayimondi.
Uchimowo walembedwa pa mitima yawo
    ndiponso pa nyanga za maguwa awo.
Ngakhale ana awo amakumbukira
    maguwa awo ndi zoyimiritsa ngati zifanizo za mulungu wawo Asera,
pa tsinde la mitengo ya masamba ambiri,
    pa mapiri aatali mʼdzikomo.
Chuma chanu ndiponso katundu wanu yense
    ndidzazipereka kwa ofunkha
kuti zikhale dipo lawo
    chifukwa cha machimo
    ochitika mʼdziko lonse.
Mudzataya dziko limene ndinakupatsani
    kuti likhale cholowa chanu.
Ndidzakusandutsani akapolo otumikira adani anu
    mʼdziko limene inu simukulidziwa,
chifukwa mwabutsa mkwiyo wanga ngati moto,
    ndipo udzayaka mpaka muyaya.”

Yehova akuti,

“Ndi wotembereredwa munthu amene amadalira munthu mnzake,
    amene amatsamira pa munthu mnzake kuti amuthandize
    pamene mtima wake wafulatira Yehova.
Munthuyo adzakhala ngati chitsamba mʼchipululu;
    iye sadzapeza zabwino.
Adzakhala mʼchipululu mopanda madzi,
    mʼdziko lamchere limene munthu sangathe kukhalamo.

“Koma ndi wodala munthu amene amadalira Yehova,
    amene amatsamira pa Iye.
Adzakhala ngati mtengo wodzalidwa mʼmphepete mwa madzi
    umene umatambalitsa mizu yake mʼmbali mwa mtsinje.
Mtengowo suopa pamene kukutentha;
    masamba ake amakhala obiriwira nthawi zonse.
Suchita mantha pa chaka cha chilala
    ndipo sulephera kubereka chipatso.”

Mtima wa munthu ndi wonyenga kupambana zinthu zonse
    ndipo kuyipa kwake nʼkosachizika.
    Ndani angathe kuwumvetsa?

10 “Ine Yehova ndimafufuza mtima
    ndi kuyesa maganizo,
ndimachitira munthu aliyense molingana ndi makhalidwe ake
    ndiponso moyenera ntchito zake.”

11 Munthu amene amapeza chuma mwachinyengo
    ali ngati nkhwali imene imafungatira mazira amene sinayikire.
Pamene ali pakatikati pa moyo wake, chumacho chidzamuthera,
    ndipo potsiriza adzasanduka chitsiru.

12 Nyumba yathu yopemphereramo ili ngati mpando waufumu waulemerero
    wokhazikitsidwa pa phiri lalitali chiyambire.
13 Inu Yehova, chiyembekezo cha Israeli,
    onse amene amakusiyani adzachita manyazi.
Iwo amene amakufulatirani mayina awo adzafafanizika ngati olembedwa pa fumbi
    chifukwa anakana Yehova,
    kasupe wa madzi amoyo.

14 Inu Yehova, chiritseni, ndipo ndidzachira;
    pulumutseni ndipo ndidzapulumuka,
    chifukwa ndinu amene ndimakutamandani.
15 Anthu akumandinena kuti,
    “Mawu a Yehova ali kuti?
    Zichitiketu lero kuti tizione!”
16 Ine sindinakuwumirizeni kuti muwalange.
    Mukudziwa kuti ine sindilakalaka tsiku la tsoka.
    Zonse zimene ndinayankhula Inu mukuzidziwa.
17 Musandichititse mantha;
    ndinu pothawira panga pa tsiku la mavuto.
18 Ondizunza anga achite manyazi,
    koma musandichititse manyazi;
iwo achite mantha kwambiri,
    koma ine mundichotsere manthawo.
Tsiku la mavuto liwafikire;
    ndipo muwawononge kotheratu.

Kusunga Tsiku la Sabata

19 Yehova anandiwuza kuti, “Pita ukayime pa chipata chodzerapo anthu, chimene mafumu a ku Yuda amalowerapo ndi kutulukirapo. Ukayimenso pa zipata zina zonse za Yerusalemu. 20 Ukawawuze kuti, ‘Imvani mawu a Yehova, inu mafumu onse a ku Yuda ndi anthu onse a ku Yuda ndi inu nonse okhala mu Yerusalemu amene mumatulukira pa zipata izi.’ 21 Yehova akuti: samalani kuti pa tsiku la Sabata musanyamule katundu kapena kulowa naye pa zipata za Yerusalemu. 22 Musalowetse katundu mʼnyumba zanu kapena kugwira ntchito pa tsiku la Sabata, koma mulipatule tsiku la Sabatalo, monga ndinalamulira makolo anu. 23 Komatu iwo sanandimvere kapena kulabadira. Ndi mitima yawo yowumayo sanamvere kapena kulandira malangizo anga. 24 Yehova akuti, ‘Muzimvera Ine ndi kuleka kulowetsa kapena kutulutsa katundu pa zipata za mzinda pa tsiku la Sabata. Muzisunga tsiku la Sabata kuti likhale lopatulika posachita ntchito iliyonse pa tsikuli. 25 Mukatero ndiye mafumu anu amene akukhala pa mpando wa Davide adzatulukira pa zipata za mzindawu pamodzi ndi nduna zawo. Iwo pamodzi ndi nduna zawo azidzalowa atakwera magaleta ndi akavalo, akuperekezedwa ndi anthu a ku Yuda ndi amene amakhala mu Yerusalemu, ndipo mu mzinda muno mudzakhala anthu mpaka muyaya. 26 Anthu adzabwera kuchokera ku mizinda ya Yuda ndi ku midzi yozungulira Yerusalemu, kuchokera ku dziko la Benjamini ndi ku mapiri a kumadzulo, kuchokera ku dziko la mapiri ndi ku Negevi. Adzabwera ndi nsembe zopsereza, nsembe zaufa ndi za chakudya, nsembe za lubani ndi zopereka zachiyamiko ku nyumba ya Yehova. 27 Koma ngati simundimvera; mukapanda kusunga tsiku la Sabata kuti likhale lopatulika ndi kumanyamula katundu nʼkumalowa naye pa zipata za Yerusalemu pa tsikuli, Ine ndidzabutsa moto pa zipata za Yerusalemu. Moto umenewo udzanyeketsa nyumba zaufumu za ku Yerusalemu ndipo moto wake sudzazima.’ ”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.