Beginning
Chipembedzo Chabodza Nʼchopanda Phindu
7 Mawu amene Yehova anayankhula kwa Yeremiya ndi awa, 2 “Ima pa chipata cha Nyumba ya Yehova ndipo kumeneko ukalalikire uthenga uwu:
“ ‘Imvani mawu a Yehova, inu nonse anthu a ku Yuda amene mumalowa pa chipata ichi kudzapembedza Yehova. 3 Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti: Konzani makhalidwe anu ndi zochita zanu, ndipo ndidzakulolani kukhala pa malo ano. 4 Musamakhulupirire mawu anu achinyengo onena kuti, ‘Ino ndi Nyumba ya Yehova, Nyumba ya Yehova, Nyumba ya Yehova!’ 5 Ngati mutasinthadi makhalidwe anu ndi zochita zanu, ndi kumachitirana zolungama, 6 ngati mutaleka kuzunza mlendo, ana amasiye kapena akazi amasiye ndi kuleka kupha anthu osalakwa pa malo ano, ndipo ngati muleka kutsatira milungu ina, kuti ingakuwonongeni, 7 Ine ndidzakulolani kukhala pa malo ano, mʼdziko limene ndinapatsa makolo anu mpaka muyaya. 8 Koma onani, inu mukudalira mawu abodza amene alibe phindu.
9 “Kodi inu muziba ndi kupha, kuchita chigololo ndi kulumbira monama, kufukiza lubani kwa Baala ndi kutsatira milungu ina imene simunayidziwe, 10 ndipo kenaka nʼkubwera kudzayima pamaso panga mʼNyumba ino, Nyumba imene imadziwika ndi Dzina langa, inu nʼkumati, ‘Tapulumuka.’ Mwapulumuka kuti muzichitabe zonyansazi? 11 Kodi Nyumba ino imene imadziwika ndi Dzina langa, yasanduka phanga la anthu olanda zinthu anzawo mwachifwamba inu mukuona? Komatu ndakhala ndi kuziona zonsezi! akutero Yehova.”
12 “ ‘Pitani tsopano ku malo anga ku Silo, malo amene poyamba ankadziwika ndi Dzina langa, ndipo mukaone zimene ndinachita kumeneko chifukwa cha kuyipa kwa anthu anga Aisraeli. 13 Tsono popeza munkachita zonsezi, ngakhale Ine kukuyankhulani koma inu osamvera, kukuyitanani koma inu osayankha, 14 choncho ndidzachita pa Nyumba imene imadziwika ndi Dzina langayi, Nyumba ya Yehova imene mumayidalira, malo amene ndinapereka kwa inu ndi makolo anu, zomwe ndinachita ku Silo. 15 Ndidzakuthamangitsani pamaso panga, ngati momwe ndinachitira abale anu onse, anthu a Efereimu.’ ”
16 “Choncho iwe Yeremiya usawapempherere anthu awa ngakhale kuwapepesera kapenanso kuwapembedzera; usandidandaulire, chifukwa Ine sindidzakumvera. 17 Kodi sukuona zimene akuchita mʼmizinda ya ku Yuda ndi mʼmisewu ya ku Yerusalemu? 18 Ana akutorera nkhuni, abambo akusonkha moto, ndipo amayi akukanda ufa kuti aphike makeke oti akapereke nsembe kwa mfumukazi yazakumwamba. Iwo amathira nsembe ya zakumwa kwa milungu ina kuti andipsetse mtima. 19 Koma kodi akuvutitsa Ine? Kodi sakungodzivuta okha, ndi kudzichititsa manyazi? akutero Yehova.”
20 “Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova akuti: Ndidzatsanulira mkwiyo wanga pa Nyumba yangayi, anthu, nyama, mitengo ndi zipatso zomwe. Mkwiyowo udzakhala ngati moto wosazimitsika.
21 “Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti: Wonjezerani nsembe zanu zopsereza pa nsembe zanu zinazo ndipo mudye nyama yakeyo! 22 Pakuti pamene ndinatulutsa makolo anu ku Igupto ndi kuyankhula nawo, sindinawalamulire kuti azipereka nsembe zopsereza kapena nsembe zinazo, 23 koma ndinawalamula kuti: Mverani Ine, ndipo ndidzakhala Mulungu wanu ndipo inu mudzakhala anthu anga. Muzitsata zonse zimene ndakulamulirani, ndipo zinthu zidzakuyenderani bwino. 24 Koma anthuwo sanamvere kapena kulabadira; mʼmalo mwake anapitirira kusamvera ndi mitima yawo yoyipa. Iwo anabwerera mʼmbuyo mʼmalo mopita patsogolo. 25 Kuyambira tsiku limene makolo awo anachoka ku Igupto mpaka lero lino, ndakhala ndikuwatumizira atumiki anga, aneneri. 26 Koma anthuwo sanandimvere kapena kusamalira. Anawumitsa mitima yawo ndi kuchita zoyipa kuposa makolo awo.
27 “Ngakhale iwe uwawuze zonsezi koma sadzakumvera. Ngakhale uwayitane koma sadzakuyankha. 28 Nʼchifukwa chake udzawawuze kuti, ‘Uwu ndi mtundu wa anthu umene sunamvere Yehova Mulungu wake, wosalola kulangizidwa. Choonadi chatha; chazimirira pa milomo yawo.’
29 “Tsono meta tsitsi lako ndi kulitaya. Ulire kwambiri pa zitunda zopanda zomera, pakuti Yehova waukana ndi kuwusiya mʼbado umene wamukwiyitsawu.”
Chigwa cha Imfa
30 “Anthu a ku Yuda achita zoyipa pamaso panga, akutero Yehova. Ayimika mafano awo onyansa mʼnyumba imene imadziwika ndi Dzina langa ndipo ayipitsa. 31 Amanga nsanja yopembedzera Tofeti mʼChigwa cha Hinomu kuti apserezereko ana awo aamuna ndi aakazi. Zimenezi Ine sindinawalamulire ngakhale kuziganizira nʼkomwe. 32 Nʼchifukwa chake masiku akubwera, akutero Yehova, pamene anthu sadzawatchulanso malowo Tofeti kapena Chigwa cha Hinomu, koma adzawatchula Chigwa cha Imfa, chifukwa adzakwirira anthu akufa ku Tofeti mpaka osapezekanso malo owayika. 33 Ndipo mitembo ya anthu amenewa idzakhala chakudya cha mbalame zamlengalenga ndi zirombo zakuthengo, ndipo palibe wina amene adzazipirikitse. 34 Ndidzathetsa nyimbo zonse zachisangalalo ndi zachikondwerero mʼmizinda ya ku Yuda ndi mʼmisewu ya ku Yerusalemu. Sikudzamvekanso mawu a chikondwerero a mkwatibwi ndi mkwati pakuti dzikolo lidzasanduka chipululu.”
8 Yehova akuti, “ ‘Pa nthawi imeneyo, mafupa a mafumu ndi a akuluakulu a ku Yuda, mafupa a ansembe ndi a aneneri, ndiponso mafupa a anthu a ku Yerusalemu adzafukulidwa. 2 Adzawamwaza pa nthaka kuyangʼana dzuwa, mwezi ndi nyenyezi zonse zamlengalenga, zimene ankazikonda, kuzitumikira ndi kuzitsatira, kupemphako nzeru ndiponso kuzilambira. Mafupawo sadzawasonkhanitsa kapena kuwakwirira, koma adzakhala ngati ndowe pamwamba pa nthaka. 3 Otsala onse a mtundu woyipawu adzafuna imfa kopambana moyo kulikonse kumene ndidzawapirikitsirako, akutero Yehova Wamphamvuzonse.’ ”
Tchimo ndi Chilango Chake
4 “Tsono awuze anthuwa, ‘Yehova akuti:
“ ‘Kodi anthu akagwa sangadzukenso?
Munthu akasochera kodi sangathe kubwereranso?
5 Chifukwa chiyani nanga anthu awa akupitirirabe kuchimwa, osabwerera?
Chifukwa chiyani Yerusalemu akubwerera mʼmbuyo?
Iwo akangamira chinyengo;
akukana kubwerera.
6 Ine ndinatchera khutu kumvetsera
koma iwo sanayankhulepo zoona.
Palibe woyipa amene analapapo zoyipa zake,
nʼkumati, ‘Ine ndachita chiyani?’
Aliyense akutsatira njira yake
ngati kavalo wothamangira nkhondo.
7 Mbalame yotchedwa kakowa ija imadziwa
nthawi yake mlengalenga.
Koma nkhunda, namzeze ndi chingalu
zimadziwa nthawi yonyamukira ulendo,
koma anthu anga sadziwa
malamulo a Yehova.
8 “ ‘Inu mukunena bwanji kuti,
‘Ndife anzeru ndipo timasunga malamulo a Yehova?’
Koma ndi alembi anu
amene akulemba zabodza.
9 Anthu anzeru achita manyazi;
athedwa nzeru ndipo agwidwa.
Iwo anakana mawu a Yehova.
Nanga tsono nzeru zawo ziwapinduliranji?
10 Nʼchifukwa chake akazi awo ndidzawapereka kwa amuna ena
ndipo minda yawo ndidzayipereka kwa amene adzawagonjetse.
Kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu,
onse ali ndi khalidwe lofuna kupeza chuma mwakuba.
Aneneri pamodzi ndi ansembe omwe,
onse amachita zachinyengo.
11 Iwo amapoletsa zilonda za anthu anga
pamwamba chabe
nʼkumati, ‘Mtendere, mtendere,’
pamene palibe mtendere.
12 Kodi amachita manyazi akamachita zonyansazi?
Ayi, alibe manyazi ndi pangʼono pomwe;
iwo sadziwa nʼkugwetsa nkhope komwe.
Choncho iwo adzagwera pakati pa anzawo amene agwa kale;
adzagwa pansi tsiku limene ndidzawalanga,
akutero Yehova.
13 “ ‘Ndidzatenga zokolola zawo,
Sipadzakhalanso mphesa pa mpesa
kapena nkhuyu pa mkuyu,
ndipo masamba ake adzawuma.
Zinthu zimene ndinawapatsa
ndidzawachotsera.’ ”
14 Koma amati, “Tikukhala pano chifukwa chiyani?
Tiyeni tonse pamodzi
tithawire ku mizinda yotetezedwa
ndi kukafera kumeneko.
Pakuti Yehova Mulungu wathu watsimikiza kuti tiyenera kufa.
Watipatsa madzi aululu kuti timwe,
chifukwa tamuchimwira.
15 Tinkayembekezera mtendere
koma palibe chabwino chomwe chinachitika,
tinkayembekezera kuchira
koma tinakumana ndi zoopsa zokhazokha.
16 Kulira kwa ngʼombe zazimuna za mdani
kukumveka kuchokera ku Dani;
dziko lonse likunjenjemera
chifukwa cha kulira kwa akavalowo.
Akubwera kudzawononga dziko
ndi zonse zimene zili mʼmenemo.
Adzawononga mzinda ndi onse okhalamo.”
17 Yehova akuti, “Onani, ndikukutumizirani njoka zaululu,
mphiri zimene munthu sangathe kuzilodza,
ndipo zidzakulumani,”
18 Ndadzazidwa ndi chisoni kwambiri,
mtima wanga walefukiratu.
19 Imvani kulira kwa anthu anga
kuchokera ku dziko lakutali:
akuti, “Kodi Yehova sali ku Ziyoni?
Kodi mfumu yake sili kumeneko?”
“Chifukwa chiyani akundiputa ndi mafano awo osema,
ndi milungu yawo yachilendo?”
20 “Nthawi yokolola yapita,
chilimwe chapita,
koma sitinapulumuke.”
21 Chifukwa cha mavuto a anthu anga, ine ndikumva kuwawa;
ndikungolira ndipo mantha aakulu andigwira.
22 Kodi ku Giliyadi kulibe mankhwala ochiritsa?
Kodi kumeneko kulibe singʼanga?
Nanga chifukwa chiyani mabala
a anthu anga sanapole?
9 Aa, ndikanakonda kuti mutu wanga ukanakhala chitsime cha madzi,
ndi maso anga ngati kasupe wa misozi!
Ndikanalira usana ndi usiku
kulirira anthu anga amene aphedwa.
2 Ndani adzandipatsa malo
ogona mʼchipululu
kuti ndiwasiye anthu anga
ndi kuwachokera kupita kutali;
pakuti onse ndi achigololo,
ndiponso gulu la anthu onyenga.
3 “Amapinda lilime lawo ngati uta.
Mʼdzikomo mwadzaza
ndi mabodza okhaokha
osati zoonadi.
Amapitirirabe kuchita zoyipa;
ndipo sandidziwa Ine.”
Akutero Yehova.
4 “Aliyense achenjere ndi abwenzi ake;
asadalire ngakhale abale ake.
Aliyense amafuna kumudyera mʼbale wake masuku pa mutu.
Choncho aliyense amachitira bwenzi lake ugogodi.
5 Aliyense amamunamiza mʼbale wake
ndipo palibe amene amayankhula choonadi.
Anapazoloweza pakamwa pawo kunena zabodza;
amalimbika kuchita machimo.
6 Iwe wakhalira mʼchinyengo
ndipo ukukana kundidziwa Ine,”
akutero Yehova.
7 Nʼchifukwa chake Yehova Wamphamvuzonse akuti,
“Taonani, Ine ndidzawasungunula ngati chitsulo ndi kuwayesa.
Kodi ndingachite nawonso
bwanji chifukwa cha machimo awo?
8 Lilime lawo lili ngati muvi wakuthwa;
limayankhula zachinyengo.
Aliyense ndi pakamwa pake amayankhula mawu achikondi kwa mnansi wake,
koma mu mtima mwake amakonzekera zomuchita chiwembu.
9 Kodi ndilekerenji kuwalanga chifukwa cha zimenezi?
akutero Yehova.
‘Kodi ndisawulipsire
mtundu wotere wa anthu?’ ”
10 Ndidzakhetsa misozi ndi kulira kwamphamvu chifukwa cha mapiri
ndipo ndidzadandaula chifukwa cha msipu wa ku chipululu.
Malo onsewo awonongeka ndipo palibe amene amapitako,
ndipo sikumveka kulira kwa ngʼombe.
Mbalame zamlengalenga zathawa
ndipo nyama zakuthengo zachokako.
11 Ndipo Yehova anati, “Ndidzasandutsa Yerusalemu kukhala bwinja,
malo okhalamo ankhandwe;
ndipo ndidzawononga mizinda ya Yuda
kotero kuti palibe munthu amene adzakhalemo.”
12 Ine ndinati, “Kodi munthu wanzeru ndani woti nʼkumvetsa zimenezi? Kodi ndani amene Yehova anayankhula naye zimenezi kuti akafotokozere ena? Nʼchifukwa chiyani dziko lawonongeka ndi kusanduka chipululu, mʼmene anthu sadutsamo?”
13 Yehova anati, “Nʼchifukwa chakuti anthuwa analeka kutsata malamulo anga amene ndinawapatsa; sanandimvere kapena kuwasamala. 14 Mʼmalo mwake, anatsatira zolakwa za mʼmitima yawo; anapembedza Abaala ngati momwe makolo awo anawaphunzitsira.” 15 Tsono chimene Ine Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli ndidzachite ndi anthu amenewa ndi ichi: “Ndidzawadyetsa chakudya cha ziphe ndi kuwamwetsa madzi a ndulu. 16 Ndidzawabalalitsa pakati pa mitundu ya anthu imene iwowo kapena makolo awo sanayidziwe, ndipo ndidzawalondola ndi ankhondo mpaka nditawawononga.”
17 Yehova Wamphamvuzonse akuti,
“Tsopano ganizirani! Muyitane akazi olira mwachisoni kuti abwere;
itanani akazi odziwa kulira bwino.”
18 Anthu akuti, “Abwere mofulumira
kuti adzatilire
mpaka mʼmaso mwathu mutatuluka misozi
ndi kuti msidze zathu zinyowe ndi madzi.
19 Kulira mwachisoni kukumveka kuchokera mu Ziyoni akuti,
‘Aa! Ife tawonongeka!
Tachita manyazi kwambiri!
Tiyenera kuchoka mʼdziko lathu
chifukwa atipirikitsa mʼnyumba zathu.’ ”
20 Tsono inu amayi, imvani mawu a Yehova;
tcherani makutu anu kuti mumve mawu a Yehova.
Phunzitsani ana anu aakazi kulira mwachisoni;
aliyense aphunzitse mnzake nyimbo ya maliro.
21 Imfa yatifikira kudzera mʼmazenera athu
ndipo yalowa mʼnyumba zathu zotetezedwa;
yapha ana athu mʼmisewu,
ndi achinyamata athu mʼmabwalo.
22 Yehova anandiwuza kuti ndinene izi kuti,
“ ‘Mitembo ya anthu
idzakhala ili lambalamba ngati ndowe mʼminda,
ngati mapesi mʼmbuyo mwa wokolola,
popanda munthu woyitola.’ ”
23 Yehova akuti,
“Munthu wanzeru asanyadire nzeru zake,
kapena munthu wamphamvu kunyadira nyonga zake,
kapena munthu wolemera kunyadira chuma chake,
24 koma ngati munthu akufuna kunyadira, anyadire chinthu ichi:
kuti iye amamvetsa za Ine ndipo amandidziwa,
kuti ndine Yehova, amene ndimakonda chifundo,
chilungamo ndiponso ungwiro pa dziko lapansi.
Zimenezi ndizo ndimakondwera nazo,”
akutero Yehova.
25 “Nthawi ikubwera,” akutero Yehova, “pamene ndidzalanga onse amene anachita mdulidwe koma mu mtima sasamala nʼkomwe. 26 Ndidzalanga anthu a ku Igupto, Yuda, Edomu, Amoni, Mowabu, ndiponso onse amene amakhala kutali ku chipululu. Mitundu ina yonseyi ndi yosachita mdulidwe, ngakhalenso Aisraeli nawonso sanachite mdulidwe wa mu mtima.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.