Beginning
4 “Ngati mukufuna kubwerera, inu Aisraeli,
bwererani kwa Ine,”
akutero Yehova.
“Chotsani mafano anu onyansa pamaso panga
ndipo musasocherenso.
2 Muzilumbira mokhulupirika ndiponso mwa chilungamo
kuti, ‘Pali Yehova wamoyo.’
Mukatero anthu a mitundu ina yonse adzandipempha kuti ndiwadalitse
ndipo adzanditamanda.”
3 Zimene Yehova akunena kwa anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu ndi izi:
“Limani masala anu
musadzale pakati pa minga.
4 Dziperekeni nokha kwa Ine
kuti munditumikire ndi mtima wanu wonse,
inu anthu a ku Yuda ndi ku Yerusalemu.
Muzichita zimenezi kuopa kuti mkwiyo wanga ungabuke ngati moto ndi kukutenthani,
chifukwa cha ntchito zanu zoyipazo
popanda wina wowuzimitsa.
Adani Ochokera Kumpoto kwa Yuda
5 “Lengeza ku Yuda ndi kulalikira mu Yerusalemu kuti,
‘Lizani lipenga mʼdziko lonse!’
Ndipo fuwulani kuti,
‘Sonkhanani!
Tiyeni tithawire ku mizinda yotetezedwa!’
6 Kwezani mbendera kuyangʼana ku Ziyoni!
Musachedwe, thawani kuti mupulumuke!
Pakuti Ine ndikubweretsa chilango kuchokera kumpoto,
kudzakhala chiwonongeko choopsa.”
7 Monga mkango umatulukira mʼngaka yake
momwemonso wowononga mayiko
wanyamuka ndi kutuluka ku mbuto yake.
Watero kuti awononge dziko lanu.
Mizinda yanu idzakhala mabwinja
popanda wokhalamo.
8 Choncho valani ziguduli,
lirani ndi kubuwula,
pakuti mkwiyo waukulu wa Yehova
sunatichokere.
9 “Pa tsiku limenelo, mfumu ndi nduna zake adzataya mtima,
ansembe adzachita mantha kwambiri,
ndipo aneneri adzathedwa nzeru,”
akutero Yehova.
10 Ndipo ine ndinati, “Haa, Ambuye Yehova, ndithu munawanyenga anthu awa pamodzi ndi Yerusalemu pamene munanena kuti, ‘Mudzakhala pa mtendere,’ chonsecho lupanga lili pakhosi pathu.”
11 Nthawi imeneyo anthu awa ndi Yerusalemu adzawawuza kuti, “Mphepo yotentha yochokera ku magomo a mʼchipululu ikuwomba pa anthu anga, osati mphepo yopeta kapena yoyeretsa; 12 koma mphepo yamphamvu kwambiri yochokera kwa Ine. Tsono ndi Ineyo amene ndikuwaweruza.”
13 Taonani, adani akubwera ngati mitambo,
magaleta awo akubwera ngati kamvuluvulu,
akavalo awo ndi aliwiro kupambana chiwombankhanga.
Tsoka ilo! Tawonongeka!
14 Iwe Yerusalemu, tsuka mtima wako kuchotsa zoyipa kuti upulumuke.
Kodi maganizo ako oyipawo udzakhala nawo mpaka liti?
15 Pakuti amithenga akulalika mawu mʼdziko la Dani;
akulengeza za masautso kuchokera ku mapiri a Efereimu.
16 Iwo akuti, “Fotokozani zimenezi kwa anthu a mitundu ina,
lengezani zimenezi mu Yerusalemu kuti,
‘Ankhondo akubwera kuchokera ku dziko lakutali,
akufuwula ndi kudzazinga mizinda ya Yuda.
17 Azinga Yerusalemu ngati anthu olondera munda,
chifukwa Yerusalemu wandiwukira,’ ”
akutero Yehova.
18 “Makhalidwe anu ndi zochita zanu
zakubweretserani zimenezi.
Chimenechi ndiye chilango chanu.
Nʼchowawa kwambiri!
Nʼcholasa mpaka mu mtima!”
19 Mayo, mayo,
ndikumva kupweteka!
Aa, mtima wanga ukupweteka,
ukugunda kuti thi, thi, thi.
Sindingathe kukhala chete.
Pakuti ndamva kulira kwa lipenga;
ndamva mfuwu wankhondo.
20 Tsoka limatsata tsoka linzake;
dziko lonse lasanduka bwinja.
Mwadzidzidzi matenti athu awonongedwa,
mwa kanthawi kochepa nsalu zake zotchinga zagwetsedwa.
21 Kodi ndikhale ndikuona mbendera ya nkhondo,
ndi kumva kulira kwa lipenga mpaka liti?
22 Yehova akuti, “Anthu anga ndi zitsiru;
iwo sandidziwa.
Iwo ndi ana opanda nzeru;
samvetsa chilichonse.
Ali ndi luso lochita zoyipa,
koma sadziwa kuchita zabwino.”
23 Ndinayangʼana dziko lapansi,
ndipo linali lopanda anthu ndi lopanda kanthu;
ndinayangʼana thambo,
koma linalibe kuwala kulikonse.
24 Ndinayangʼana mapiri,
ndipo ankagwedezeka;
magomo onse ankangosunthira uku ndi uku.
25 Ndinayangʼana, ndipo sindinaone anthu;
mbalame iliyonse ya mlengalenga inali itathawa.
26 Ndinayangʼana, dziko lachonde linali litasanduka chipululu;
mizinda yake yonse inali itasanduka bwinja
pamaso pa Yehova, chifukwa cha mkwiyo wake.
27 Yehova akuti,
“Dziko lonse lidzasanduka chipululu
komabe sindidzaliwononga kotheratu.
28 Chifukwa chake dziko lapansi lidzalira
ndipo thambo lidzachita mdima,
pakuti ndayankhula ndipo sindidzafewa mtima,
ndatsimikiza ndipo sindidzabwerera mʼmbuyo.”
29 Pakumva phokoso la okwera pa akavalo ndi la anthu oponya mivi,
anthu a mʼmizinda adzathawa.
Ena adzabisala ku nkhalango;
ena adzakwera mʼmatanthwe
mizinda yonse nʼkuyisiya;
popanda munthu wokhalamo.
30 Iwe Yerusalemu, ndiwe bwinja!
Ukutanthauza chiyani kuvala zovala zofiira
ndi kuvalanso zokometsera zagolide?
Ngakhale udzikonze maso ako powapaka zokometsera,
ukungodzivuta chabe.
Zibwenzi zako zikukunyoza;
zikufuna kuchotsa moyo wako.
31 Ndikumva kulira ngati kwa mayi pa nthawi yake yobereka,
kubuwula ngati kwa mayi amene akubereka mwana wake woyamba.
Kuliraku ndi kwa anthu a mu Ziyoni, wefuwefu.
Atambalitsa manja awo nʼkumati,
“Kalanga ife! Tikukomoka.
Moyo wathu waperekedwa kwa anthu otipha.”
Palibe Munthu Wolungama
5 “Pitani uku ndi uku mʼmisewu ya Yerusalemu,
mudzionere nokha,
funafunani mʼmabwalo ake.
Ngati mungapeze munthu mmodzi
amene amachita zachilungamo ndi kufunafuna choonadi,
ndipo ndidzakhululukira mzinda uno.
2 Ngakhale anthu akulumbira kuti, ‘Pali Yehova wamoyo,’
komabe akungolumbira mwachinyengo.”
3 Inu Yehova, kodi suja mumafuna anthu onena zoona?
Inu munawakantha anthuwo, koma sanamve kupweteka;
munawaphwanya anthuwo, koma sanatengepo phunziro.
Anawumitsa mitima yawo ngati mwala
ndipo anakaniratu kulapa.
4 Ndiye ndinati, “Awa ndi amphawi chabe;
anthu ochita zopusa.
Sadziwa njira ya Yehova,
sazindikira zimene Mulungu wawo amafuna.
5 Tsono ndidzapita kwa atsogoleri
ndi kukayankhula nawo;
ndithu iwo amadziwa njira ya Yehova,
amadziwa zomwe Mulungu wawo amafuna.”
Koma ayi, iwonso anathyola goli la Yehova
ndipo anadula msinga zawo.
6 Choncho mkango wochokera ku nkhalango udzawapha,
mmbulu wochokera ku thengo udzawawononga,
kambuku adzawabisalira pafupi ndi mizinda yawo
kuti akhadzule aliyense amene adzayesera kutuluka mʼmizindamo
pakuti kuwukira kwawo ndi kwakukulu
ndipo abwerera mʼmbuyo kwambiri.
7 Yehova akuti, “Kodi ndingakukhululukireni bwanji ndi zimene mwachita?
Ana anu andisiya Ine
ndipo amapembedza milungu imene si milungu konse.
Ine ndinawapatsa zonse zimene ankasowa,
komabe iwo anachita chigololo
namasonkhana ku nyumba za akazi achiwerewere.
8 Monga amachitira akavalo onenepa akamamemesa,
aliyense wa iwo ankathamangira mkazi wa mnzake.
9 Tsono ndingaleke kuwalanga chifukwa cha zimenezi?”
akutero Yehova.
“Kodi nʼkuleka kuwulipsira
mtundu woterewu?
10 “Pitani ku minda yake ya mipesa ndi kukayiwononga,
koma musakayiwononge kotheratu.
Sadzani nthambi zake
pakuti anthu amenewa si a Yehova.
11 Nyumba ya Israeli ndi nyumba ya Yuda
onse akhala osakhulupirika kotheratu kwa Ine.”
12 Iwowa ankanama ponena za Yehova kuti,
“Yehova sangachite zimenezi!
Choyipa sichidzatigwera;
sitidzaona nkhondo kapena njala.
13 Mawu a aneneri azidzangopita ngati mphepo;
ndipo mwa iwo mulibe uthenga wa Yehova.
Choncho zimene amanena zidzawachitikira okha.”
14 Chifukwa chake Yehova Mulungu Wamphamvuzonse akuti,
“Popeza kuti anthu awa ayankhula mawu amenewa,
tsono mawu anga ndidzawasandutsa moto mʼkamwa mwako
ndipo anthu awa ndidzawasandutsa nkhuni zimene moto udzapserezeretu.
15 Inu Aisraeli,” Yehova akuti,
“Ndikukubweretserani mtundu wa anthu ochokera kutali,
ndi mtundu umene sunagonjetsedwepo,
mtundu wakalekale umene chiyankhulo chawo inu simuchidziwa,
zimene akunena inu simungazimvetse.
16 Zida zawo za nkhondo zapha anthu ambirimbiri;
onsewo ndi ankhondo amphamvu okhaokha.
17 Adzakudyerani zokolola zanu ndi chakudya chanu,
adzapha ana anu aamuna ndi aakazi;
adzakupherani nkhosa zanu ndi ngʼombe zanu,
adzawononga mpesa wanu ndi mikuyu yanu.
Ndi malupanga awo adzagwetsa
mizinda yanu yotetezedwa imene mumayidalira.
18 “Komabe pa masiku amenewo sindidzakuwonongani kotheratu,” akutero Yehova. 19 Ndipo pamene anthu adzafunsa Yehova kuti, “Chifukwa chiyani Yehova Mulungu wathu wachita zimenezi?” Iwe udzawawuze kuti, “Monga momwe mwasiyira Ine ndi kutumikira milungu yachilendo mʼdziko mwanu, momwemonso mudzatumikira anthu a mʼdzikonso lachilendo.”
20 “Lengeza izi kwa ana a Yakobo
ndipo mulalikire kwa anthu a ku Yuda kuti,
21 Imvani izi, inu anthu opusa ndi opanda nzeru,
inu amene maso muli nawo koma simupenya,
amene makutu muli nawo koma simumva.
22 Kodi simuyenera kuchita nane mantha?”
Akutero Yehova.
“Kodi simuyenera kunjenjemera pamaso panga?
Ine ndinayika mchenga kuti ukhale malire a nyanja,
malire a muyaya amene nyanjayo singadutsepo.
Mafunde angawombe motani, koma sangathe kupitirira malirewo;
mafunde angakokome motani, koma sangadutse malirewo.
23 Koma anthu awa ndi nkhutukumve ndiponso a mitima yowukira;
andifulatira ndipo andisiyiratu.
24 Sananenepo mʼmitima mwawo kuti,
‘Tiyeni tizipembedza Yehova Mulungu wathu.
Kodi suja amatipatsa pa nthawi yake mvula yachizimalupsa ndi yamasika.
Iye salephera konse kutipatsa nyengo ya kholola.’
25 Koma zolakwa zanu zalepheretsa zonsezi;
ndipo machimo anu akumanitsani zabwino.
26 “Pakati pa anthu anga pali anthu ena oyipa
amene amabisalira anzawo monga amachitira mlenje mbalame
ndiponso ngati amene amatchera misampha kuti akole anthu anzawo.
27 Nyumba zawo zadzaza ndi chuma chochipeza mwa chinyengo
ngati zikwere zodzaza ndi mbalame.
Nʼchifukwa chake asanduka otchuka ndi olemera.
28 Ndipo ananenepa ndi kukhala ndi matupi osalala.
Ntchito zawo zoyipa nʼzopanda malire;
saweruza mwachilungamo nkhani ya ana amasiye kuti iyende bwino,
sateteza ufulu wa anthu osauka.
29 Kodi Ine ndingaleke kuwalanga chifukwa cha zimenezi?
Kodi ndisawulipsire
mtundu woterewu?
Akutero Yehova.
30 “Chinthu chothetsa nzeru ndi choopsa kwambiri
chachitika mʼdzikomo:
31 Aneneri akunenera zabodza,
ndipo ansembe akuvomerezana nawo,
ndipo anthu anga akukonda zimenezi.
Koma mudzatani potsiriza?
Kuzingidwa kwa Yerusalemu
6 “Thawani, inu anthu a ku Benjamini!
Tulukani mu Yerusalemu!
Lizani lipenga ku Tekowa!
Kwezani mbendera ku Beti-Hakeremu!
Pakuti tsoka lalikulu likubwera kuchokera kumpoto,
ndipo chiwonongekocho nʼchachikulu.
2 Kodi mzinda wa Ziyoni suli ngati msipu wokongola kwambiri,
kumene abusa amafikako ndi ziweto zawo?
3 Abusa ndi nkhosa zawo adzabwera kudzalimbana nawo;
adzamanga matenti awo mowuzinga,
ndipo aliyense adzakhazika anthu ake pamalo pake.”
4 Adzanena kuti, “Konzekani kuwuthira nkhondo mzindawo!
Nyamukani, kuti tiwuthire nkhondo mzindawu masana ano.
Koma tili ndi tsoka, dzuwa lapendeka,
ndipo zithunzithunzi za kumadzulo zikunka zitalika.
5 Tsono nyamukani kuti tiwuthire nkhondo mzindawu usiku uno
ndi kuwononga malinga ake!”
6 Yehova Wamphamvuzonse akuti,
“Dulani mitengo
ndipo mumange mitumbira yankhondo kulimbana ndi Yerusalemu.
Mzinda umenewu uyenera kulangidwa;
wadzaza ndi kuponderezana.
7 Monga momwe chitsime chimatulutsira madzi
ndi mmenenso Yerusalemu amatulutsira zoyipa zake.
Chiwawa ndi chiwonongeko ndi zomwe zimamveka mu mzindamo;
nthenda yake ndi mabala ake ndimaziona nthawi zonse.
8 Iwe Yerusalemu, tengapo phunziro,
kuopa kuti chikondi changa pa iwe chingakuchokere
ndi kusandutsa dziko lako kukhala bwinja
mopanda munthu wokhalamo.”
9 Yehova Wamphamvuzonse anandiwuza kuti,
“Adani adzawakunkha ndithu anthu otsala a Israeli,
monga momwe amachitira populula mphesa.
Tsono iwe yesetsa kupulumutsa amene ungathe
monga mmene amachitira munthu wokolola mphesa.”
10 Kodi ndiyankhule ndi yani ndi kumuchenjeza?
Ndinene mawu ochenjeza kwa yani kuti amve?
Makutu awo ndi otsekeka
kotero kuti sangathe kumva.
Mawu a Yehova ndi onyansa kwa iwo;
sasangalatsidwa nawo.
11 Koma ine ndadzazidwa ndi mkwiyo wa Yehova,
ndipo ndatopa ndi kusunga mkwiyo wa Yehova.
Yehova anandiwuza kuti, “Tsono ndidzawutulutsira mkwiyo umenewu pa ana oyenda mʼmisewu
ndi pa achinyamata amene asonkhana pamodzi;
pakutinso mwamuna ndi mkazi wake adzatengedwa,
pamodzi ndi okalamba amene ali ndi zaka zochuluka.
12 Nyumba zawo adzazipereka kwa ena,
pamodzi ndi minda yawo ndi akazi awo.
Ndidzatambasula dzanja langa kukantha
anthu okhala mʼdzikomo,”
akutero Yehova.
13 “Kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu,
onse ali ndi dyera lofuna kupeza phindu mwa kuba;
aneneri pamodzi ndi ansembe omwe,
onse amachita zachinyengo.
14 Amapoletsa zilonda za anthu anga
pamwamba pokha.
Iwo amanena kuti, ‘Mtendere, mtendere,’
pamene palibe mtendere.
15 Kodi amachita manyazi akamachita zonyansazo?
Ayi, sachita manyazi ndi pangʼono pomwe;
sadziwa ndi kugwetsa nkhope komwe.
Choncho iwo adzagwera pakati pa anzawo amene agwa kale;
adzagwa pansi tsiku limene ndidzawalange,”
akutero Yehova.
16 Yehova akuti,
“Imani pa mphambano ndipo mupenye;
kumeneko ndiye kuli njira zakale,
funsani kumene kuli njira yabwino. Yendani mʼmenemo,
ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu.
Koma inu munati, ‘Ife sitidzayenda njira imeneyo.’
17 Ine ndinakupatsani alonda oti akuyangʼanireni
ndipo ndinati, ‘Imvani kulira kwa lipenga!’
koma inu munati, ‘Sitidzamvera.’
18 Nʼchifukwa chake imvani, inu anthu a mitundu ina;
yangʼanitsitsani, inu amene mwasonkhana pano,
chimene chidzawachitikire anthuwo.
19 Imvani, inu anthu okhala pa dziko lapansi,
ndikubweretsa masautso pa anthu awa.
Zimenezi ndi mphotho ya ntchito zawo.
Iwowa sanamvere mawu anga
ndipo anakana lamulo langa.
20 Kodi pali phindu lanji ngakhale mubwere ndi lubani kuchokera ku Seba,
kapena zonunkhira zina kuchokera ku dziko lakutali?
Nsembe zanu zopsereza Ine sindidzalandira;
nsembe zanu sizindikondweretsa.”
21 Choncho Yehova akuti,
“Ndidzayika zokhumudwitsa pamaso pa anthu awa.
Abambo ndi ana awo aamuna onse adzapunthwa ndi kugwa;
anansi awo ndi abwenzi awo adzawonongeka.”
22 Yehova akunena kuti,
“Taonani, gulu lankhondo likubwera
kuchokera kumpoto;
mtundu wa anthu amphamvu wanyamuka
kuchokera kumathero a dziko lapansi.
23 Atenga mauta ndi mikondo;
ndi anthu ankhanza ndi opanda chifundo.
Phokoso lawo lili ngati mkokomo wa nyanja.
Akwera pa akavalo awo
ndipo akonzekera ngati anthu ankhondo,
kudzakuthirani nkhondo anthu a ku Ziyoni.”
24 A ku Ziyoni akuti “Ife tamva mbiri yawo,
ndipo manja anthu alefukiratu.
Nkhawa yatigwira,
ndipo tikumva ululu ngati mayi pa nthawi yake yochira.
25 Musapite ku minda
kapena kuyenda mʼmisewu,
pakuti mdani ali ndi lupanga,
ndipo ponseponse anthu akuchita mantha.
26 Inu anthu anga, valani ziguduli
ndipo gubudukani pa phulusa;
lirani mwamphamvu
ngati munthu wolirira mwana wake mmodzi yekha,
pakuti mwadzidzidzi wowonongayo
adzabwera kudzatipha.
27 “Iwe Yeremiya, ndakuyika kuti ukhale choyesera zitsulo.
Uwayese anthu anga
monga ungayesere chitsulo
kuti uwone makhalidwe awo.
28 Onsewo ali ndi khalidwe lokanika ndi lowukira
ndipo akunka nanena zamiseche.
Iwo ndi olimba ngati mkuwa ndi chitsulo.
Onse amangochita zoyipa zokhazokha.
29 Moto mu mvukuto ukuyaka kwambiri;
mtovu watha kusungunuka ndi moto.
Koma ntchito yosungunulayo sikupindula
chifukwa zoyipa sizikuchokapo.
30 Iwo ali ngati siliva wotayidwa,
chifukwa Yehova wawakana.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.