Beginning
45 Yehova akuyankhula ndi wodzozedwa wake
Koresi amene anamugwira dzanja lamanja
kuti agonjetse mitundu ya anthu
ndi kuwalanda mafumu zida zawo zankhondo,
ndi kutsekula zitseko
kuti zipatazo zisadzatsekedwenso ndi ichi:
2 Ine ndidzayenda patsogolo pako,
ndi kusalaza mapiri;
ndidzaphwanya zitseko za mkuwa
ndi kuthyola mipiringidzo ya chitsulo.
3 Ndidzakupatsa chuma chobisika mu mdima,
katundu wa pamalo obisika,
kotero kuti udziwe kuti Ine ndine Yehova
Mulungu wa Israeli, amene ndakuyitana pokutchula dzina.
4 Chifukwa cha mtumiki wanga Yakobo,
chifukwa cha wosankhidwa wanga Israeli,
Ine ndakuyitana pokutchula dzina
ndipo ndakupatsa dzina laulemu
ngakhale iwe sukundidziwa Ine.
5 Ine ndine Yehova ndipo palibenso wina;
kupatula Ine palibenso Mulungu wina.
Ndidzakupatsa mphamvu,
ngakhale sukundidziwa Ine,
6 kotero kuti kuchokera kummawa mpaka kumadzulo
anthu adzadziwa kuti palibe wina koma Ine ndekha.
Ine ndine Yehova,
ndipo palibenso wina.
7 Ndimalenga kuwala ndi mdima,
ndimabweretsa madalitso ndi tsoka;
ndine Yehova, amene ndimachita zonsezi.
8 “Iwe thambo gwetsa mvula kuchokera kumwamba;
mitambo ivumbwe mivumbi ya chilungamo.
Dziko lapansi litsekuke,
ndipo chipulumutso chiphuke kuti
chilungamo chimereponso;
Ine Yehova, ndine ndalenga zimenezi.
9 “Tsoka kwa wokangana ndi mlengi wake,
ngakhale kuti ali ngati phale chabe pakati pa mapale anzake.
Kodi dongo lingafunse munthu wowumba kuti,
‘Kodi ukuwumba chiyani?’
Kodi ntchito yako inganene kuti,
‘Ulibe luso?’
10 Tsoka kwa wofunsa abambo ake kuti,
‘Kodi munabereka chiyani?’
Kapena amayi ake kuti,
‘Kodi mufuna kubereka chiyani?’
11 “Yehova
Woyerayo wa Israeli, ndiponso Mlengi wake akunena,
zokhudza zinthu zimene zikubwera ndi izi:
Kodi iwe ukundifunsa za ana anga,
kapena kundilamula pa zokhudza ntchito zanga?
12 Ndine amene ndinapanga dziko lapansi
ndikulenga munthu kuti akhalemo.
Ine ndi manja anga ndinayalika thambo;
ndimalamulira zolengedwa zonse za mlengalenga.
13 Ndine amene ndidzawutsa Koresi kuti chilungamo changa chikwaniritsidwe:
ndipo ndidzawongolera njira zake zonse.
Iye adzamanganso mzinda wanga
ndi kumasula anthu anga amene ali mu ukapolo,
wopanda kupereka ndalama kapena mphotho,
akutero Yehova Wamphamvuzonse.”
14 Yehova akuti,
“Chuma cha ku Igupto ndi chuma cha malonda cha Kusi chidzakhala chanu.
Anthu amphamvu zawo ndi athanzi a ku Seba
adzabwera kwa inu
ndipo adzakhala anthu anu;
iwo adzidzakutsatani pambuyo panu
ali mʼmaunyolo.
Adzakugwadirani
ndi kukupemphani, ponena kuti,
‘Ndithudi Mulungu ali ndi inu, ndipo palibenso wina;
palibenso mulungu wina.’ ”
15 Zoonadi inu muli ndi Mulungu wobisika
amene ali Mulungu ndi Mpulumutsi wa Israeli.
16 Onse amene amapanga mafano adzawachititsa manyazi ndi kuwanyozetsa.
Adzakhala osokonezeka maganizo.
17 Koma Yehova adzapulumutsa Israeli
ndi chipulumutso chamuyaya;
simudzachitanso manyazi kapena kunyozeka
mpaka kalekale.
18 Yehova
analenga zinthu zakumwamba,
Iye ndiye Mulungu;
amene akulenga dziko lapansi,
ndi kulikhazikitsa,
sanalipange kuti likhale lopanda kanthu,
koma analipanga kuti anthu akhalemo.
Iyeyu akunena kuti:
Ine ndine Yehova,
ndipo palibenso wina.
19 Ine sindinayankhule mwachinsinsi,
pamalo ena a mdima;
Ine sindinaziwuze zidzukulu za Yakobo kuti,
“Ndifunefuneni ku malo kopanda kanthu.”
Ine Yehova, ndimayankhula zoona;
ndikunena zolungama.
20 Yehova akuti, “Sonkhanani pamodzi ndipo mubwere;
yandikirani, inu amene munapulumuka pothawa nkhondo kwa anthu a mitundu ina.
Ndinu opanda nzeru amene mumanyamula mafano a mitengo,
amene mumapemphera kwa milungu imene singathe kupulumutsa.
21 Fotokozani mlandu wanu,
mupatsane nzeru nonse pamodzi.
Kodi ndani ananeneratu zimenezi kalekale?
Ndani anazifotokozeratu zimenezi nthawi yamakedzana?
Kodi si Ineyo Yehova?
Ndipo palibenso Mulungu wina kupatula Ine,
Mulungu wolungama ndi Wopulumutsa,
palibenso wina kupatula Ine.
22 “Tembenukirani kwa Ine kuti mupulumuke,
inu anthu onse a pa dziko lapansi,
pakuti Ine ndine Mulungu ndipo palibenso wina.
23 Ndalumbira ndekha,
pakamwa panga patulutsa mawu owona,
mawu amene sadzasinthika konse akuti,
bondo lililonse lidzagwada pamaso panga;
anthu onse adzalumbira potchula dzina langa.
24 Iwo adzanene kwa Ine kuti,
‘Chilungamo ndi mphamvu zimapezeka mwa Yehova yekha.’ ”
Onse amene anamuwukira Iye
adzabwera kwa Iye ndipo adzachita manyazi.
25 Koma mwa Yehova zidzukulu zonse za Israeli
zidzapambana ndi kupeza ulemerero.
Za Kupasuka kwa Babuloni ndi Mafano Ake
46 Beli wagwada pansi, Nebo wawerama;
nyama zonyamula katundu za nyamula milungu yawo.
Mafano awo asanduka katundu wolemera pa msana pa ngʼombe.
Asandukadi ngati katundu pa msana pa nyama zotopa.
2 Nyamazo zikuwerama ndi kufuna kugwa ndi milunguyo;
sizikutha kupulumutsa katunduyo,
izo zomwe zikupita ku ukapolo.
3 Mverani Ine, Inu nyumba ya Yakobo,
inu nonse otsala a mʼnyumba ya Israeli,
Ine ndakhala ndi kukusamalirani kuyambira mʼmimba ya amayi anu,
ndakhala ndikukunyamulani chibadwire chanu.
4 Mpaka pamene mudzakalambe ndi kumera imvi
ndidzakusamalirani ndithu.
Ndinakulengani ndipo ndidzakunyamulani,
ndidzakusamalirani ndi kukulanditsani.
5 “Kodi inu mudzandifanizira ndi yani, kapena mufananitsa ndi yani?
Kodi mudzandiyerekeza kapena kundifanizitsa ndi yani?
6 Anthu ena amakhuthula golide mʼzikwama zawo
ndipo amayeza siliva pa masikelo;
amalemba ntchito mʼmisiri wosula kuti awapangire mulungu,
kenaka iwo amagwada pansi ndikupembedza kamulunguko.
7 Amanyamula nʼkumayenda nayo milunguyo pa mapewa awo;
amayikhazika pa malo pake ndipo imakhala pomwepo.
Singathe kusuntha pamalo pakepo.
Ngakhale wina apemphere kwa milunguyo singathe kuyankha;
kapena kumupulumutsa ku mavuto ake.
8 “Kumbukirani zimenezi ndipo muchite manyazi,
Muzilingalire mu mtima, inu anthu owukira.
9 Kumbukirani zinthu zakale zinthu zamakedzana;
chifukwa Ine ndine Mulungu
ndipo palibe wina ofanana nane.
10 Ndinaneneratu zakumathero kuchokera pachiyambi pomwe.
Kuyambira nthawi yamakedzana ndinaloseratu zoti zidzachitike.
Ndikanena zimene ndifuna kuchita ndipo zimachitikadi.
Chilichonse chimene ndafuna ndimachichita.
11 Ndikuyitana chiwombankhanga kuchokera kummawa.
Ndikuyitana kuchokera ku dziko lakutali munthu amene adzakwaniritsa cholinga changa.
Zimene ndanena ndidzazikwaniritsadi;
zimene ndafuna ndidzazichitadi.
12 Ndimvereni, inu anthu owuma mtima,
inu amene muli kutali ndi chipulumutso.
13 Ndikubweretsa pafupi tsiku la chipulumutso changa;
sichili kutali.
Tsikulo layandikira
ndipo sindidzachedwa kukupulumutsani
ndi kupereka ulemerero wanga kwa Israeli.
Kugwa kwa Babuloni
47 “Tsika, ndi kukhala pa fumbi,
iwe namwali, Babuloni;
khala pansi wopanda mpando waufumu,
iwe namwali, Kaldeya
pakuti sadzakutchulanso wanthete kapena woyenera
kumugwira mosamala.
2 Tenga mphero ndipo upere ufa;
chotsa nsalu yako yophimba nkhope
kwinya chovala chako mpaka ntchafu
ndipo woloka mitsinje.
3 Maliseche ako adzakhala poyera
ndipo udzachita manyazi.
Ndidzabwezera chilango
ndipo palibe amene adzandiletse.”
4 Woyerayo wa Israeli ndiye Mpulumutsi wathu,
dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse.
5 “Khala chete, ndipo lowa mu mdima,
iwe namwali, Kaldeya;
chifukwa sadzakutchulanso
mfumukazi ya maufumu.
6 Ndinawakwiyira anthu anga,
osawasamalanso.
Ndinawapereka manja mwako,
ndipo iwe sunawachitire chifundo.
Iwe unachitira nkhanza
ngakhale nkhalamba.
7 Iwe unati, ‘Ine ndidzakhalapo nthawi zonse
ngati mfumukazi.’
Koma sunaganizire zinthu izi
kapena kusinkhasinkha za mmene ziti zidzathere.
8 “Ndipo tsopano, tamvera, iwe wongokonda zokondweretsawe,
amene ukukhala mosatekesekawe,
umaganiza mu mtima mwako kuti,
‘Ine ndi Ine, ndipo kupatula ine palibenso wina.
Sindidzakhala konse mkazi wamasiye,
ndipo ana anga sadzamwalira.’
9 Koma mʼkamphindi, ndiponso tsiku limodzi,
zinthu ziwiri izi zidzakuchitikira:
ana ako kukufera komanso kukhala mkazi wamasiye.
Zimenezi zidzakuchitikira kwathunthu
ngakhale ali ndi amatsenga ambiri
ndi mawula amphamvu.
10 Iwe unkadalira kuyipa kwako
ndipo unati, ‘Palibe amene akundiona.’
Kuchenjera ndi nzeru zako zidzakusokoneza,
choncho ukuganiza mu mtima mwako kuti,
‘Ine ndine basi, ndipo kupatula ine palibenso wina.’
11 Ngozi yayikulu idzakugwera
ndipo sudzadziwa momwe ungayipewere ndi matsenga ako.
Mavuto adzakugwera
ndipo sudzatha kuwachotsa;
chipasupasu chimene iwe sukuchidziwa
chidzakugwera mwadzidzidzi.
12 “Pitiriza tsono kukhala ndi matsenga ako,
pamodzi ndi nyanga zako zochulukazo,
wakhala ukuzigwiritsa ntchito kuyambira ubwana wako.
Mwina udzatha kupambana
kapena kuopsezera nazo adani ako.
13 Malangizo onse amene unalandira angokutopetsa basi!
Abwere patsogolopa anthu amene amatanthauzira za kumwamba kuti adzakupulumutseni.
Abwere amene amayangʼana nyenyezi, ndi kumalosera mwezi ndi mwezi
zimene ziti zidzakuchitikire.
14 Ndithudi, anthuwo ali ngati phesi;
adzapsa ndi moto.
Sangathe kudzipulumutsa okha
ku mphamvu ya malawi a moto.
Awa si makala a moto woti wina nʼkuwotha;
kapena moto woti wina nʼkuwukhalira pafupi.
15 Umu ndi mmene adzachitire amatsenga,
anthu amene wakhala ukugwira nawo ntchito
ndi kuchita nawo malonda chiyambire cha ubwana wako.
Onse adzamwazika ndi mantha,
sipadzakhala ndi mmodzi yemwe wokupulumutsa.”
Israeli ndi Nkhutukumve
48 “Mverani izi, inu nyumba ya Yakobo,
inu amene amakutchani dzina lanu Israeli,
ndinu a fuko la Yuda,
inu mumalumbira mʼdzina la Yehova,
ndi kupemphera kwa Mulungu wa Israeli,
ngakhale osati mʼchoonadi kapena mʼchilungamo.
2 Komabe inu mumadzitcha nzika za mzinda wopatulika
ndipo mumadalira Mulungu wa Israeli,
amene dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse:
3 Zimene zinachitika poyamba ndinalosera kalekale,
zinatuluka mʼkamwa mwanga ndipo ndinazilengeza;
tsono mwadzidzidzi ndinachitapo kanthu ndipo zinachitikadi.
4 Pakuti Ine ndinadziwa kuti iwe ndiwe nkhutukumve
wa nkhongo gwaa,
wa mutu wowuma.
5 Ine ndinakuwuziratu zinthu izi kalekale lomwe;
zisanachitike ndinazilengezeratu kwa iwe
kuti unganene kuti,
‘Fano langa ndilo lachita zimenezi,
kapena kuti fano langa losema ndi kamulungu kanga kachitsulo ndiwo analamula kuti zimenezi zichitike.’
6 Inu munamva zinthu zimenezi.
Kodi inu simungazivomereze?
“Kuyambira tsopano mpaka mʼtsogolo ndidzakuwuzani zinthu zatsopano
zinthu zobisika zimene simunazidziwe konse.
7 Zinthu zimenezi zikulengedwa tsopano lino, osati kalekale;
munali musanazimve mpaka lero lino.
Choncho inu simunganene kuti,
‘Zimenezi ndiye ayi, ndinazidziwa kale.’
8 Inu simunazimvepo kapena kuzidziwa;
makutu anu sanali otsekuka.
Tsono Ine ndinadziwa bwino kuti ndinu anthu achiwembu ndi kuti
chiyambire ubwana wanu munatchedwa owukira.
9 Ine ndikuchedwetsa mkwiyo wanga chifukwa cha dzina langa.
Ndikukulezerani ukali wanga kuti anthu andilemekeze.
Sindidzakuwonongani kotheratu.
10 Taonani, ndinakuyeretsani ngati siliva;
ndinakuyesani mʼngʼanjo yamasautso.
11 Chifukwa cha ulemu wanga, chifukwa cha ulemu wanga Ine ndikuchita zimenezi.
Ndingalole bwanji kuti ndinyozeke?
Ulemerero wanga sindidzawupereka kwa wina.
Kumasulidwa kwa Israeli
12 “Tamvera Ine, iwe Yakobo,
Israeli, amene ndinakuyitana:
Mulungu uja Woyamba
ndi Wotsiriza ndine.
13 Inde dzanja langa linamanga maziko a dziko lapansi,
dzanja langa lamanja linafunyulula mlengalenga.
Ndi mawu anga ndinalenga kumwamba
ndi dziko lapansi.
14 “Sonkhanani pamodzi inu nonse ndipo mvetserani:
Ndani mwa mafano anu amene analoseratu za zinthu izi?
Wokondedwa wa Yehova uja adzachita
zomwe Iye anakonzera Babuloni;
dzanja lake lidzalimbana ndi Kaldeya.
15 Ine, Inetu, ndayankhula;
ndi kumuyitana
ndidzamubweretsa ndine
ndipo adzakwaniritsa zolinga zake.
16 “Bwerani pafupi ndipo mvetserani izi:
“Kuyambira pachiyambi sindinayankhule mobisa;
pa nthawi imene zinkachitika zimenezi Ine ndinali pomwepo.”
Ndipo tsopano Ambuye Yehova wandipatsa Mzimu wake
ndi kundituma.
17 Yehova, Mpulumutsi wanu,
Woyerayo wa Israeli akuti,
“Ine ndine Yehova Mulungu wanu,
amene ndimakuphunzitsa kuti upindule,
ndimakutsogolera pa njira yoyenera kuyitsata.
18 Ngati iwe ukanangosamalira zolamulira zanga,
bwenzi mtendere wako ukanakhala ngati mtsinje,
ndi chipulumutso chako ngati mafunde a pa nyanja.
19 Zidzukulu zako zikanachuluka ngati mchenga,
ana ako akanachuluka ngati fumbi;
dzina lawo silikanachotsedwa pamaso panga
ndipo silikanafafanizidwa konse.”
20 Tulukani mʼdziko la Babuloni!
Thawani dziko la Kaldeya!
Lengezani zimenezi ndi mawu a chisangalalo
ndipo muzilalikire
mpaka kumathero a dziko lapansi;
muzinena kuti, “Yehova wawombola Yakobo mtumiki wake.”
21 Iwo sanamve ludzu pamene Yehova ankawatsogolera mʼchipululu;
anawapatsa madzi otuluka mʼthanthwe;
anangʼamba thanthwelo ndipo
munatuluka madzi.
22 “Palibe mtendere kwa anthu ochimwa,” akutero Yehova.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.