Beginning
Mtumiki wa Yehova
42 “Nayu mtumiki wanga, amene ndimamuchirikiza,
amene ndamusankha, amenenso ndimakondwera naye.
Ndayika Mzimu wanga mwa Iyeyo,
ndipo adzaweruza anthu a mitundu yonse mwachilungamo.
2 Iye sadzafuwula, sadzamveka mawu,
kapena mawu ake kumveka mʼmisewu.
3 Bango lophwanyika sadzalithyola,
ndipo moto wozilala sadzawuzimitsa.
Motero adzaonetsa kuti chilungamo ndicho choonadi;
4 sadzafowoka kapena kukhumudwa
mpaka atakhazikitsa chilungamo pa dziko lapansi,
ndi mpaka mayiko a mʼmbali mwa nyanja atafika poyembekezera malangizo ake.”
5 Yehova Mulungu
amene analenga zamlengalenga ndi kuziyalika,
amene analenga dziko lapansi ndi zonse zimene zimabereka,
amenenso amapereka mpweya kwa anthu ake okhala mʼdzikomo,
ndi moyo kwa onse oyendamo, akuti,
6 “Ine Yehova, ndakuyitana chifukwa Ine ndine wolungama;
ndikugwira dzanja ndipo
ndidzakuteteza.
Ndakupereka kukhala pangano langa kwa anthu
ndi kuwunika kwa anthu a mitundu ina.
7 Udzatsekula maso a anthu osaona,
udzamasula anthu a mʼndende
ndi kutulutsa mʼndende anthu okhala mu mdima.
8 “Ine ndine Yehova: dzina langa ndi limenelo!
Sindidzapereka ulemerero wanga kwa wina aliyense
kapena matamando anga kwa mafano.
9 Taonani, zinthu zimene ndinalosera kale zachitikadi,
ndipo ndikuwuzani zinthu zatsopano;
zinthuzo zisanaonekere
Ine ndakudziwitsani.”
Nyimbo Yotamanda Yehova
10 Imbirani Yehova nyimbo yatsopano,
mutamandeni inu okhala mʼdziko lonse lapansi,
inu amene mumayenda pa nyanja, nyanja ikokome ndi zonse zili mʼmenemo.
Inu okhala pa zilumba tamandani Yehova.
11 Chipululu ndi mizinda yake zikweze mawu awo;
midzi ya Akedara ikondwere.
Anthu a ku Sela ayimbe mwachimwemwe;
afuwule kuchokera pamwamba pa mapiri.
12 Atamande Yehova
ndipo alalike matamando ake kwa anthu apazilumba zonse.
13 Yehova adzapita ku nkhondo ngati munthu wamphamvu,
adzawutsa ukali wake ngati munthu wankhondo;
akukuwa ndiponso akufuwula mfuwu wankhondo
ndipo adzagonjetsa adani ake.
14 Yehova akuti, “Ndakhala ndili chete kwa nthawi yayitali,
ndakhala ndili phee osachita kanthu.
Koma tsopano, ngati mayi pa nthawi yochira,
ndi kubuwula ndi kupuma modukizadukiza ndipo ndili wefuwefu.
15 Ndidzawononga mapiri ndi zitunda
ndipo ndidzawumitsa zomera zawo zonse;
ndidzasandutsa mitsinje kukhala zilumba
ndipo ndidzawumitsa maiwe.
16 Ndidzatsogolera anthu osaona mʼmisewu imene sanayidziwe,
ndidzawatsogolera mʼnjira zimene sanayendepo;
ndidzasandutsa mdima wa kutsogolo kwawo kuti ukhale kuwala
ndipo ndidzasalaza malo osalala.
Zimenezi ndizo ndidzachite;
sindidzawataya.
17 Koma onse amene amadalira mafano
amene amanena kwa mafanowo kuti, ‘ndinu milungu yathu,’
ndidzawachititsa manyazi kotheratu.
Aisraeli Alephera Kuphunzira
18 “Imvani, agonthi inu;
yangʼanani osaona inu, kuti muone! 19 Ali wosaona ndani, si mtumiki wanga kodi?
Ndipo ndani ali wosamva ngati mthenga amene ndamutuma?
Kodi ndani ali wosaona ngati uja ndinachita naye pangano,
kapena wosaona ndani ngati mtumiki wa Yehova?
20 Iwe waona zinthu zambiri, koma sunazisamale;
makutu ako ndi otsekuka koma sumva kanthu.”
21 Chinamukomera Yehova
chifukwa cha chilungamo chake,
kapena lamulo lake kukhala lalikulu ndi lopambana.
22 Koma awa ndi anthu amene afunkhidwa ndi kuwalanda zinthu zawo,
onsewa anawakola mʼmaenje
kapena akuwabisa mʼndende.
Tsono asanduka chofunkha
popanda wina wowapulumutsa
kapena kunena kuti,
“Abwezeni kwawo.”
23 Kodi ndani wa inu amene adzamvetsera zimenezi
kapena kutchera khutu ndi kumva za mʼtsogolomo?
24 Ndani anapereka Yakobo kwa ofunkha,
ndi Israeli kwa anthu akuba?
Kodi si Yehova,
amene ife tamuchimwirayu?
Pakuti sanathe kutsatira njira zake;
ndipo sanamvere malangizo ake.
25 Motero anawakwiyira kwambiri,
nawavutitsa ndi nkhondo.
Anayatsa moto ponseponse mowazungulira komabe iwo sanamvetse;
motowo unawapsereza, koma iwo sanatengepo phunziro ayi.
Yehova Yekha Mpulumutsi wa Israeli
43 Koma tsopano, Yehova
amene anakulenga, iwe Yakobo,
amene anakuwumba, iwe Israeli akuti,
“Usaope, pakuti ndakuwombola;
Ndinakuyitanitsa mokutchula dzina lako, ndiwe wanga.
2 Pamene ukuwoloka nyanja,
ndidzakhala nawe;
ndipo pamene ukuwoloka mitsinje,
sidzakukokolola.
Pamene ukudutsa pa moto,
sudzapsa;
lawi la moto silidzakutentha.
3 Chifukwa Ine Yehova, Mulungu wako,
Woyera wa Israeli, ndine Mpulumutsi wako.
Ndinapereka Igupto pofuna kuti ndiwombole iwe,
ndinapereka Kusi ndi Seba mʼmalo mwa iwe.
4 Popeza kuti ndiwe wamtengowapatali wolemekezeka ndi wapamtima panga,
ndipo chifukwa ndimakukonda,
ndidzapereka anthu mʼmalo mwa iwe,
ndidzapereka mitundu ya anthu pofuna kuwombola moyo wako.
5 Usachite mantha, pakuti Ine ndili nawe;
ndidzabweretsa ana ako kuchokera kummawa,
ndipo ndidzakusonkhanitsani kuchokera kumadzulo.
6 Ndidzawuza a kumpoto kuti, ‘Amasuleni,’
ndidzawuza akummwera kuti, ‘Musawagwire.’
Bweretsani ana anga aamuna kuchokera ku mayiko akutali,
ana anga a akazi kuchokera kumalekezero a dziko lapansi;
7 onsewo amadziwika ndi dzina langa;
ndinawalenga chifukwa cha ulemerero wanga,
ndinawawumba, inde ndinawapanga.”
8 Tulutsa anthu amene ali nawo maso koma sakupenya,
anthu amene ali nawo makutu koma sakumva.
9 Mitundu yonse ya anthu isonkhane pamodzi,
anthu a mitundu ina akhale pamodzi pabwalo la milandu.
Ndani wa iwo amene ananeneratu zimenezi?
Ndani wa iwo anatifotokozerapo zinthu zakalekale?
Abweretu ndi mboni zawo kuti adzatsimikizire kuti ananena zoona,
kuti anthu ena amve ndi kunena kuti, “Ndi zoona.”
10 Yehova akunena kuti, “Inu Aisraeli ndinu mboni zanga,
ndi mtumiki wanga amene ndinakusankha,
kuti mundidziwe ndi kundikhulupirira, ndipo mudzamvetsa kuti Mulungu ndine ndekha.
Patsogolo panga sipanapangidwepo mulungu wina,
ngakhale pambuyo panga
sipadzakhalaponso wina.”
11 Akutero Yehova, “Ine, Inetu ndine Yehova,
ndipo palibe Mpulumutsi wina koma Ine ndekha.
12 Ndine amene ndinaneneratu, amene ndinakupulumutsa;
ndine, osati mulungu wina wachilendo pakati panu amene ndinalengezeratu.
Inu ndinu mboni zanga, kuti Ine ndine Mulungu,” akutero Yehova.
13 “Ine ndine Mulungu kuyambira nthawi yamakedzana, ndipo ndidzakhalabe Mulungu ku nthawi zonse.
Palibe amene angathe kuthawa mʼmanja mwanga,
ndipo chimene ndachita palibe angathe kuchisintha.”
Chifundo cha Mulungu ndi Kusakhulupirika kwa Israeli
14 Yehova akuti,
Mpulumutsi wanu, Woyerayo wa Israeli akuti,
“Chifukwa cha inu ndidzatuma gulu lankhondo kukalimbana ndi Babuloni
ndi kukupulumutsani.
Ndidzagwetsa zitseko zonse za mzindawo, ndipo kukondwa kwa anthu ake kudzasanduka kulira.
15 Ine ndine Yehova, Woyera wanu uja,
Mlengi wa Israeli. Ine ndine Mfumu yanu.”
16 Yehova
anapanga njira pa nyanja,
anapanga njira pakati pa madzi amphamvu.
17 Iye anasonkhanitsa magaleta, akavalo,
gulu lankhondo ndi asilikali amphamvu,
ndipo onse anagwa pamenepo, osadzukanso
anazimitsidwa kutheratu ngati chingwe cha nyale. Yehova ameneyu akuti,
18 “Iwalani zinthu zakale;
ndipo musaganizirenso zinthu zimene zinachitika kale.
19 Taonani, Ine ndikuchita zinthu zatsopano!
Tsopano zayamba kale kuoneka; kodi simukuziona?
Ine ndikulambula msewu mʼchipululu
ndi kupanga mitsinje mʼdziko lowuma.
20 Nyama zakuthengo, nkhandwe ndi akadzidzi
zinandilemekeza.
Ndidzayendetsa mitsinje mʼdziko lowuma
kuti ndiwapatse madzi anthu anga
osankhidwa.
21 Anthu amene ndinadziwumbira ndekha
kuti aziyimba nyimbo yotamanda Ine.
22 “Komatu simunapemphera kwa Ine, Inu a mʼbanja la Yakobo,
munatopa nane, Inu Aisraeli.
23 Simunabweretse kwa Ine nkhosa za nsembe zopsereza,
kapena kundilemekeza ndi nsembe zanu.
Ine sindinakulemetseni pomakupemphani zopereka za chakudya
kapena kukutopetsani pomakupemphani nsembe zofukiza.
24 Simunandigulire bango lonunkhira
kapena kundipatsa Ine mafuta okwanira a nsembe zanu.
Koma inu mwandilemetsa Ine ndi machimo anu
ndipo mwanditopetsa Ine ndi zolakwa zanu.
25 “Ine, Inetu, ndi amene ndimafafaniza
zolakwa zanu, chifukwa cha Ine mwini,
ndipo sindidzakumbukiranso machimo anu.
26 Mundikumbutse zakale,
ndipo titsutsane nkhaniyi pamodzi;
fotokozani mlandu wanu kuti muonetse kuti ndinu osalakwa.
27 Kholo lanu loyamba linachimwa;
ndipo Atsogoleri anu achipembedzo anandiwukira.
28 Chifukwa chake Ine ndidzanyazitsa akuluakulu a Nyumba yanu ya mapemphero,
ndipo ndidzapereka Yakobo kuti awonongedwe
ndi Israeli kuti achitidwe chipongwe.”
Israeli Wosankhidwa wa Yehova
44 Yehova akuti, “Mvera tsopano, iwe Yakobo, mtumiki wanga,
Israeli, amene ndinakusankha.
2 Yehova
amene anakupanga iwe, anakuwumba iwe mʼmimba ya amayi ako,
ndi amene adzakuthandiza iwe. Iye akuti,
Usachite mantha, iwe Yakobo, mtumiki wanga,
Yesuruni, amene ndinakusankha.
3 Pakuti ndidzathira madzi pa nthaka yowuma,
ndi kuyendetsa mitsinje mʼdziko lowuma;
ndidzatumiza Mzimu wanga pa ana anu,
ndi kutsitsa madalitso anga pa zidzukulu zanu.
4 Iwo adzakula ngati udzu wothirira bwino
ndi ngati bango lomera mʼmbali mwa mitsinje ya madzi oyenda.
5 Wina adzanena kuti, ‘Ine ndine wa Yehova;’
wina adzadzitcha yekha wa banja la Yakobo;
winanso adzalemba pa dzanja lake, ‘Wa Yehova’
ndipo adzadzitcha wa banja la Israeli.
Yehova, Osati Mafano
6 “Yehova Mfumu
ndi Mpulumutsi wa Israeli, Yehova Wamphamvuzonse akuti:
Ine ndine woyamba ndi wotsiriza;
palibenso Mulungu wina koma Ine ndekha.
7 Ndani nanga angafanane ndi Ine? Muloleni kuti ayankhule.
Muloleni andifotokozere ndi kundiyalira bwino lomwe
zimene zinachitika kuyambira pamene ndinkakhazikitsa anthu anga akalekale,
ndi ziti zimene zidzachitike;
inde, muloleni alosere zimene zikubwera.
8 Musanjenjemere, musachite mantha.
Kodi sindinakuwuzeni zimenezi ndi kuzilosera kalekale lomwe?
Inu ndinu mboni zanga. Kodi aliponso Mulungu wina kupatula Ine?
Ayi, palibe Thanthwe linanso limene sindikulidziwa.”
9 Onse amene amapanga mafano ngachabe,
ndipo milungu imene amayilemekeza ndi yopanda phindu.
Iwo amene amapembedza mafano ndi wosaona;
ndipo sazindikira kanthu. Choncho adzawachititsa manyazi.
10 Ndani amasema mulungu ndi kuwumba fano,
limene silingamupindulire?
11 Iye pamodzi ndi anzake onse adzawachititsa manyazi;
amisiri a mafano ndi anthu chabe.
Aloleni onse asonkhane ndi kuyima pabwalo la milandu;
onse adzaopsedwa ndipo adzachita manyazi.
12 Mmisiri wa zitsulo amatenga chitsulo
ndipo amachiyika pa makala amoto;
ndi dzanja lake lamphamvu
amachisula pochimenya ndi nyundo.
Pambuyo pake mʼmisiri uja amamva njala natha mphamvu;
iye samwa madzi, ndipo amalefuka.
13 Mmisiri wa matabwa nayenso amayeza mtengo ndi chingwe
ndipo amajambula chithunzi ndi cholembera;
amasema bwinobwino ndi chipangizo chake
ndipo amachiwongola bwino ndi chida chake.
Amachipanga ngati munthu,
munthu wake wokongola
kuti aliyike mʼnyumba yake yachipembedzo.
14 Amagwetsa mitengo ya mkungudza,
mwinanso amatenga mtengo wa payini kapena wa thundu
nʼkudzisankhira mtengo wabwino pakati pa mitengo ya mʼnkhalango,
ndipo amadzala mtengo wa payini ndi kuwuleka kuti ukule ndi mvula.
15 Mitengoyo munthu amachitako nkhuni;
nthambi zina amasonkhera moto wowotha,
amakolezera moto wophikira buledi
ndi mbali ina ya mtengowo amapangira mulungu ndipo amapembedza;
iye amapanga fano ndi kumaligwadira.
16 Chigawo china cha mtengowo amasonkhera moto
wowotcherapo nyama imene
amadya, nakhuta.
Iye amawotha motowo ndipo amanena kuti,
“Aa! Ndikumva kutentha; pano pali moto.”
17 Chigawo chotsala amapanga kamulungu, fano lake limenelo;
amaligwadira ndi kulipembedza.
Amapemphera kwa fanolo ndipo amanena kuti,
“Iwe ndiwe mulungu wanga, ndipulumutse.”
18 Anthu otere sadziwa kanthu, samvetsa kanthu kalikonse;
maso awo ndi omatirira ndipo sangathe kuona,
ndipo mitu yawo ndi yogontha kotero sangathe kumvetsa.
19 Palibe amene amayima nʼkulingalira.
Palibe wanzeru kapena womvetsa zinthu bwino woti nʼkunena kuti,
chigawo china cha mtengowo ndinasonkhera moto;
pa makala ake ndinaphikira buledi,
ndinawotchapo nyama ndipo ndinadya.
Chigawo chotsalachi ndipangire chinthu chonyansachi.
Kodi ndidzagwadira mtengo?
20 Munthu wotere ali ngati wodya phulusa, maganizo ake opusa amusocheretsa;
motero kuti sangathe kudzipulumutsa yekha kapena kudzifunsa kuti,
“Kodi chinthu chili mʼmanja mwangachi si chabodza?”
21 Yehova akuti, “Iwe Yakobo, kumbukira zinthu izi
popeza kuti ndiwe mtumiki wanga, iwe Israeli.
Ine ndinakupanga iwe, ndiwe mtumiki wanga;
iwe Israeli, sindidzakuyiwala.
22 Ndachotsa zolakwa zako ngati mitambo,
ndi machimo ako ngati nkhungu ya mmawa.
Bwerera kwa Ine,
popeza ndakupulumutsa.”
23 Imbani mwachimwemwe, inu zolengedwa zamlengalenga, pakuti Yehova wachita zimenezi;
fuwula, iwe dziko lapansi.
Imbani nyimbo, inu mapiri,
inu nkhalango ndi mitengo yonse,
chifukwa Yehova wawombola Yakobo,
waonetsa ulemerero wake mwa Israeli.
Anthu Adzakhalanso mu Yerusalemu
24 Yehova Mpulumutsi wanu, amene
anakuwumbani mʼmimba ya amayi anu akuti:
“Ine ndine Yehova,
amene anapanga zinthu zonse,
ndinatambasula ndekha zinthu zakuthambo,
ndinayala ndekha dziko lapansi.
25 Ndine amene ndinalepheretsa mipingo ya anthu onyenga,
ndipo ndimapusitsa owombeza mawula.
Ndimasokoneza anthu a nzeru,
ndi kuonetsa kuti nzeru zawo nʼzopusa.
26 Ndine amene ndimatsimikiza mawu a atumiki ake
ndi kukwaniritsa zimene analosera amithenga ake.
“Ndine amene ndinanena za Yerusalemu kuti mudzakhalanso anthu.
Ndinanenanso za mizinda ya Yuda kuti idzamangidwanso.
Za mabwinja awo ndinanena kuti ndidzawawutsanso.
27 Ndine amene ndinawuza nyanga yayikulu kuti, ‘Uma’
ndipo ndidzawumitsa mitsinje yako.
28 Ndine amene ndinanena kwa Koresi kuti, ‘Iye ndiye mʼbusa wanga,’
ndipo adzachita zonse zimene ndikufuna;
iye adzalamula kuti, ‘Yerusalemu amangidwenso’
ndi kuti, ‘Maziko a Nyumba ya Mulungu ayikidwenso.’ ”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.