Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Beginning

Read the Bible from start to finish, from Genesis to Revelation.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Yesaya 28-30

Tsoka kwa Efereimu

28 Tsoka ufumu wonyada wa zidakwa za ku Efereimu.
    Tsoka kwa ulemerero wake wokongola umene ukufota ngati duwa
limene lili pa mutu pa anthu
    oledzera a mʼchigwa chachonde.
Taonani, ambuye ali naye wina wamphamvu ndi nyonga.
    Iye adzabwera ngati mkuntho wamatalala ndi namondwe wowononga,
ngati madzi amphamvu osefukira a mvula yamkuntho;
    ndipo adzawagwetsa pansi mwankhanza.
Ulamuliro wa atsogoleri oledzera
    a ku Efereimu adzawuthetsa.
Ndipo ulemerero wokongola wa mzinda umene uli ngati duwa
    lofota pamutu pa anthu oledzera a mʼchigwa chachonde uja,
udzakhala ngati nkhuyu yoyambirira kupsa
    imene munthu akangoyiona amayithyola
    nthawi yokolola isanakwane.

Tsiku limenelo Yehova Wamphamvuzonse
    adzakhala ngati nkhata yaufumu,
chipewa chokongola
    kwa anthu ake otsala.
Iye adzapereka mtima
    wachilungamo kwa oweruza,
adzakhala chilimbikitso kwa
    amene amabweza adani pa zipata za mzinda.

Nawonso awa ali dzandidzandi chifukwa cha vinyo
    ndipo akusochera chifukwa cha mowa:
ansembe ndi aneneri akudzandira chifukwa cha mowa
    ndipo akusokonezeka chifukwa cha vinyo;
akusochera chifukwa cha mowa,
    akudzandira pamene akuona masomphenya,
    kupunthwa pamene akupereka chigamulo.
Pa matebulo onse pali masanzi okhaokha
    ndipo palibenso malo wopanda zonyansa.

Iwo akuti, “Kodi munthu ameneyu akufuna aphunzitse ndani?
    Uthengawu akufuna kufotokozera yani?
Ndi kwa ana amene aleka kuyamwa,
    kwa makanda ongowachotsa kumene ku bere?
10 Akuyesa kumatiphunzitsa pangʼonopangʼono
    lemba ndi lemba, mzere ndi mzere,
    phunziro ndi phunziro.
    Zonsezi akungoti apa pangʼono apa pangʼono.”

11 Mulungu adzayankhula kwa anthu ake kudzera mwa anthu aziyankhulo zachilendo, ziyankhulo zosamveka bwino.
    Mulungu adzayankhula kwa anthu awa, amene
12 anakuwuzani kuti,
    “Malo opumulira ndi ano,
otopa apumule, malo owusira ndi ano.”
    Koma inu simunamvere.
13 Choncho Yehova adzakuphunzitsani
    pangʼonopangʼono lemba ndi lemba,
    mzere ndi mzere, phunziro ndi phunziro.
    Kotero mudzayenda ndi kugwa chambuyo,
adzapweteka ndi kukodwa mu msampha
    ndipo adzakutengani ku ukapolo.

14 Nʼchifukwa chake imvani mawu a Yehova,
    inu anthu achipongwe amene mumalamulira anthu awa mu Yerusalemu.
15 Inu mumayankhula monyada kuti, “Ife tinachita pangano ndi imfa,
    ife tachita mgwirizano ndi manda.
Pamene mliri woopsa ukadzafika
    sudzatikhudza ife,
chifukwa timadalira bodza ngati pothawirapo pathu
    ndi chinyengo ngati malo anthu obisalapo.”

16 Tsono zimene Ambuye Yehova akunena ndi izi:

“Taonani, ndikuyika mwala wovomerezeka ndi amisiri
    ngati maziko mu Ziyoni,
mwala wapangodya, wamtengowapatali wopanga maziko amphamvu;
    munthu amene awukhulupirira sadzagwedezeka.
17 Ntchito zolungama zidzakhala ngati chingwe choyezera maziko ake,
    ndipo chilungamo chidzakhala chowongolera mzere;
matalala adzawononga malo anu othawirapo, amene ndi mabodza,
    ndipo madzi adzamiza malo anu obisalako.
18 Pangano limene munachita ndi imfa lidzathetsedwa;
    mgwirizano wanu ndi manda udzachotsedwa.
Pakuti mliri woopsa udzafika,
    ndipo udzakugonjetsani.
19 Ndipo ukadzangofika udzakutengani.
    Udzafika mmawa uliwonse,
    usiku ndi usana.”

Anthu akadzamvetsetsa uthenga umenewu
    adzaopsedwa kwambiri.
20 Mudzakhala ngati munthu wogona pa bedi lalifupi kwambiri kuti sangathe kutambalitsapo miyendo;
    ndiponso mudzakhala ngati munthu amene wafunda bulangeti lochepa kwambiri kuti sangathe nʼkufunda komwe.
21 Yehova adzamenya nkhondo monga anachitira ku phiri la Perazimu
    adzakalipa monga anachitira ku chigwa cha Gibiyoni;
adzagwira ntchito yake yooneka ngati yachilendo,
    ndipo zimene ati adzachite zidzakhala ngati zodabwitsa.
22 Tsopano lekani kunyoza,
    mukapanda kutero maunyolo anu adzakuthinani kwambiri;
Ambuye, Yehova Wamphamvuzonse wandiwuza kuti,
    “Ndagamula kuti ndidzawononga dziko lapansi.”

23 Tcherani khutu ndipo mumve mawu anga;
    mvetserani ndipo mumve zimene ndikunena.
24 Kodi mlimi wofuna kudzala mbewu amangokhalira kutipula kokhakokha?
    Kodi amangokhalira kugawula ndi kugalawuza kokhakokha?
25 Pamene iye wasalaza mundawo,
    kodi samafesa mawere ndi chitowe?
Kodi suja samadzala tirigu
    ndi barele mʼmizere yake,
    nadzala mchewere mʼphepete mwa mundawo?
26 Mulungu wake amamulangiza
    ndi kumuphunzitsa njira yabwino.

27 Mawere sapunthira chopunthira cha galeta lopanda mikombero,
    kapena chitowe sapuntha popondetsapo mikombero ya galeta;
mawere amapuntha ndi ndodo
    ndipo chitowe amapuntha ndi kamtengo.
28 Tirigu ayenera kusinjidwa kuti apangire buledi,
    komabe munthu samangokhalira kupuntha tiriguyo osalekeza, kuopa kuti angatekedzeke.
Ngakhale kuti amapuntha tiriguyo poyendetsapo mikombero ya galeta,
    koma akavalo ake satekedza tiriguyo.
29 Izinso zimachokera kwa Yehova Wamphamvuzonse,
    wa uphungu wodabwitsa ndi wa nzeru zopambana.

Tsoka kwa Mzinda wa Davide

29 Tsoka kwa iwe, Arieli, Arieli,
    mzinda umene Davide anakhazikitsamo zithando za nkhondo!
Papite chaka chimodzi kapena ziwiri
    ndipo masiku a zikondwerero zanu azipitirirabe ndithu.
Komatu Ine ndidzathira nkhondo Arieli
    ndipo kudzakhala kulira ndi kudandaula,
    mzindawo udzasanduka ngati ngʼanjo ya guwa lansembe.
Ine ndidzamanga misasa ya nkhondo kulimbana ndi mzindawo;
    ndidzakuzungulira ndi nsanja za nkhondo
    ndi kumanga mitumbira yanga ya nkhondo kulimbana nawe.
Utagwetsedwa pansi, iwe udzayankhula kuchokera mʼnthaka,
    mawu ako adzatuluka uli mʼfumbi,
adzamveka ngati a mzukwa.
    Mawu ako adzamveka ngati onongʼona kuchokera mʼfumbi.

Koma chigulu cha adani ako chidzasanduka chifwirimbwiti.
    Chigulu cha ankhondo achilendo chidzabalalika ngati mungu wowuluzika ndi mphepo.
Mwadzidzidzi ndi mosayembekezereka,
    Yehova Wamphamvuzonse adzabwera
ndi mabingu ndi chivomerezi ndi phokoso lalikulu,
    kamvuluvulu ndi namondwe ndi malawi a moto wonyeketsa.
Tsono chigulu chankhondo cha mitundu ina yonse chimene chikulimbana ndi mzinda wa Arieli
    nʼkumathira nkhondo mzindawo, malinga ake ndi kuwuzinga,
chigulu chonsecho chidzazimirira ngati maloto,
    gati zinthu zoziona mʼmasomphenya usiku.
Chidzakhala ngati munthu wanjala wolota akudya,
    koma podzuka ali nayobe njala;
kapena ngati munthu waludzu wolota akumwa,
    koma podzuka, ali nalobe ludzu, kummero kwake kuli gwaa.
Izi zidzachitika pamene chigulu cha nkhondo cha mitundu ina yonse
    chikunthira nkhondo Phiri la Ziyoni.

Pitirizani kuledzera ndipo mudzakhala opusa.
    Dzitsekeni mʼmaso ndipo mukhale osapenya,
ledzerani, koma osati ndi vinyo,
    dzandirani, koma osati ndi mowa.
10 Yehova wakugonetsani tulo tofa nato.
    Watseka maso anu, inu aneneri;
    waphimba mitu yanu, inu alosi.

11 Kwa inu mawu onsewa ali ngati buku lotsekedwa, ndipo ngati lipatsidwa kwa wina wodziwa kuwerenga ndi kunena kuti, “Chonde tawerengani bukuli,” iye adzati, “Sindingathe popeza ndi lomatidwa.” 12 Kapena ngati lipatsidwa kwa amene sadziwa kuwerenga ndi kunena kuti, “Chonde werenga bukuli,” iye adzayankha kuti, “Ine sindidziwa kuwerenga.”

13 Ambuye akuti,

“Anthu awa amandipembedza Ine ndi pakamwa pawo,
    ndi kundilemekeza Ine ndi milomo yawo,
    koma mitima yawo ili kutali ndi Ine.
Kundipembedza kwawo ndi kwa chiphamaso.
    Amandipembedza motsata malamulo a anthu amene anaphunzitsidwa.
14 Nʼchifukwa chakenso Ine ndidzapitirira
    kuwachitira ntchito zodabwitsa;
nzeru za anthu anzeru zidzatha,
    luntha la anthu aluntha Ine ndidzalinyoza.”
15 Tsoka kwa amene amayesetsa
    kubisira Yehova maganizo awo,
amene amachita ntchito zawo mu mdima nʼkumanena kuti,
    “Ndani amene akundiona kapena ndani akudziwa zimene ndikuchita?”
16 Inu mumazondotsa zinthu
    ngati kuti dothi lasanduka wowumba mbiya.
Kodi chinthu chopangidwa chingawuze wochipanga kuti
    “Sunandipange ndi iwe?”
Kapena mʼphika kunena kwa amene anawuwumba kuti,
    “Iwe sudziwa chilichonse?”

17 Kodi Lebanoni posachedwapa sadzasanduka munda wachonde,
    ndipo kodi munda wachondewo ngati nkhalango?
18 Tsiku limenelo anthu osamva adzamva mawu a mʼbuku,
    ndipo anthu osaona amene
    ankakhala mu mdima adzapenya.
19 Anthu odzichepetsa adzakhalanso ndi chimwemwe mwa Yehova;
    ndipo anthu osowa adzakondwa chifukwa cha Woyerayo wa Israeli.
20 Koma anthu ankhanza adzazimirira,
    oseka anzawo sadzaonekanso,
    ndipo onse okopeka ndi zoyipa adzawonongedwa.
21 Yehova adzalanga amene amasinjirira munthu kuti apezeke wolakwa,
    kapena kuphophonyetsa anthu ozenga mlandu
    ndi umboni wonama kuti osalakwa asaweruzidwe mwachilungamo.

22 Choncho Yehova amene anawombola Abrahamu, akunena kwa zidzukulu za Yakobo kuti,

“Anthu anga sadzachitanso manyazi;
    nkhope zawo sizidzagwanso ndi manyazi.
23 Akadzaona ana awo ndi
    ntchito ya manja anga pakati pawo,
adzatamanda dzina langa loyera;
    adzazindikira kuyera kwa Woyerayo wa Yakobo,
    ndipo adzachita naye mantha Mulungu wa Israeli.
24 Anthu opusa adzapeza nzeru;
    onyinyirika adzalandira malangizo.”

Tsoka kwa Mtundu Wopanduka

30 Yehova akuti, “Tsoka kwa ana ondipandukira
    amene amachita zowakomera iwo okha osati Ine,
nachita mgwirizano wawowawo
    koma osati motsogozedwa ndi Ine.
    Choncho amanka nachimwirachimwira.
Amapita ku Igupto kukapempha thandizo
    koma osandifunsa;
amathawira kwa Farao kuti awateteze,
    ku Igupto amafuna malo opulumulira.
Koma chitetezo cha Farao chidzakhala manyazi anu,
    malo a mthunzi a ku Igupto mudzachita nawo manyazi.
Ngakhale kuti nduna zawo zili ku Zowani,
    ndipo akazembe awo afika kale ku Hanesi,
aliyense wa ku Yuda adzachita manyazi
    chifukwa cha anthu opanda nawo phindu,
amene sabweretsa thandizo kapena phindu,
    koma manyazi ndi mnyozo.”

Uthenga wonena za nyama za ku Negevi:

Akazembe akuyenda mʼdziko lovuta ndi losautsa,
    mʼmene muli mikango yayimuna ndi yayikazi,
    mphiri ndi njoka zaululu.
Iwo amasenzetsa abulu ndi ngamira chuma chawo,
    kupita nazo kwa mtundu wa anthu
umene sungawathandize.
    Amapita ku Igupto amene thandizo lake ndi lachabechabe.
Nʼchifukwa chake dzikolo ndalitcha
    Rahabe chirombo cholobodoka.

Yehova anandiwuza kuti, “Tsopano pita,
    ukalembe zimenezi mʼbuku iwo akuona
ndipo lidzakhala ngati umboni wosatha
    masiku a mʼtsogolo.
Amenewa ndi anthu owukira, onama ndi
    osafuna kumvera malangizo a Yehova.
10 Iwo amawuza alosi kuti,
    ‘Musationerenso masomphenya!’
Ndipo amanena kwa mneneri kuti,
    ‘Musatinenerenso zoona,’
mutiwuze zotikomera,
    munenere za mʼmutu mwanu.
11 Patukani pa njira ya Yehova,
    lekani kutsata njira ya Yehova;
ndipo tisamvenso mawu
    a Woyerayo uja wa Israeli!”

12 Nʼchifukwa chake Woyerayo wa Israeli akunena kuti,

“Popeza inu mwakana uthenga uwu,
    mumakhulupirira zopondereza anzanu
    ndipo mumadalira kuchita zoyipa,
13 choncho tchimo linalo lidzakhala ngati mingʼalu
    pa khoma lalitali ndi lopendama
    limene linagwa mwadzidzidzi ndi mwamsangamsanga.
14 Lidzaphwanyika ngati mbiya
    imene yanyenyekeratu,
mwakuti pakati pake sipadzapezeka phale ngakhale
    lopalira moto mʼngʼanjo
    kapena lotungira madzi mʼchitsime.”

15 Zimene Ambuye Yehova, Woyerayo wa Israeli ananena ndi izi:

“Ngati mubwerera ndi kupuma mudzapulumuka,
    ngati mukhala chete ndi kukhulupirira mudzakhala amphamvu,
    koma inu munakana zimenezi.
16 Inu mukuti, ‘Ayi ife tidzathawa,
    tidzakwera pa akavalo aliwiro.’
Zoonadi kuti mudzakwera pa akavalo aliwiro,
    koma okuthamangitsani adzakhalanso aliwiro.
17 Anthu 1,000 mwa inu adzathawa
    poona mdani mmodzi;
poona adani asanu okha
    nonsenu mudzathawa.
Otsala anu
    adzakhala ngati mbendera pa phiri,
    ndi ngati chizindikiro cha pa chulu.”

18 Komatu Yehova akufunitsitsa kuti akukomereni mtima,
    iye ali wokonzeka kuti akuchitireni chifundo.
Pakuti Yehova ndi Mulungu wachilungamo.
    Ndi odala onse amene amakhulupirira Iye!

19 Inu anthu a ku Ziyoni, amene mukhala mu Yerusalemu simudzaliranso. Mulungu adzakukomerani mtima pamene adzamva kulira kwanu kopempha thandizo! Ndipo akadzamva, adzakuyankhani. 20 Ngakhale Ambuye adzakulowetseni mʼmasautso, aphunzitsi anu sadzakhala kakasi; inu mudzawaona ndi maso anuwo. 21 Ngati mudzapatukira kumanja kapena kumanzere, mudzamva mawu kumbuyo kwanu woti, “Njira ndi iyi; yendani mʼmenemo.” 22 Pamenepo mudzawononga mafano anu okutidwa ndi siliva ndiponso zifanizo zanu zokutidwa ndi golide; mudzawataya ngati zinthu zonyansa ndipo mudzati, “Zichoke zonsezi!”

23 Yehova adzakugwetseraninso mvula pa mbewu zanu zimene mukadzale mʼnthaka, ndipo chakudya chimene mudzakolole chidzakhala chabwino ndi chochuluka. Tsiku limenelo ngʼombe zanu zidzadya msipu wochuluka. 24 Ngʼombe ndi abulu amene amalima mʼmunda adzadya chakudya chamchere, chopetedwa ndi foloko ndi fosholo. 25 Pa tsiku limene adani anu adzaphedwa ndi nsanja zawo kugwa, mitsinje ya madzi idzayenda pa phiri lililonse lalikulu ndi pa phiri lililonse lalingʼono. 26 Mwezi udzawala ngati dzuwa, ndipo kuwala kwa dzuwa kudzawonjezereka kasanu nʼkawiri, ngati kuwala kwa tsiku limodzi. Yehova adzamanga mabala a anthu ake ndi kupoletsa zilonda zimene Iye anachititsa polanga anthu ake.

27 Taonani, Yehova akubwera kuchokera kutali,
    ndipo mkwiyo wake ndiwonyeka ndi chiweruzo chake chidzakhala chopweteka.
Iye wayankhula mwaukali kwambiri,
    ndipo mawu ake ali ngati moto wonyeka.
28 Mpweya wake uli ngati mtsinje wosefukira,
    wa madzi ofika mʼkhosi.
Iye adzasefa anthu a mitundu ina ndi sefa wosakaza;
    Iye akuyika zitsulo mʼkamwa mwa anthu a mitundu ina ngati akavalo,
    kuti ziwasocheretse.
29 Ndipo inu mudzayimba
    mokondwa monga mumachitira usiku pa chikondwerero chopatulika.
Mudzasangalala
    ngati anthu oyimba zitoliro
popita ku phiri la Yehova,
    thanthwe la Israeli.
30 Anthu adzamva liwu la ulemerero la Yehova
    ndipo adzaona dzanja lake likutsika pa iwo
ndi mkwiyo woopsa, pamodzi ndi moto wonyeketsa,
    mphenzi, namondwe ndi matalala.
31 Asiriya adzaopa liwu la Yehova,
    ndipo Iye adzawakantha ndi ndodo.
32 Yehova akamadzalanga adani ake ndi ndodo,
    anthu ake adzakhala akuvina nyimbo
zoyimbira matambolini ndi azeze,
    Yehova ndiye ati adzamenyane ndi Asiriyawo.
33 Malo otenthera zinthu akonzedwa kale;
    anakonzera mfumu ya ku Asiriya.
Dzenje la motolo ndi lozama ndi lalikulu,
    ndipo muli nkhuni zambiri;
mpweya wa Yehova,
    wangati mtsinje wa sulufule,
    udzayatsa motowo pa nkhunizo.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.