Beginning
Zapansipano Nʼzopandapake
1 Mawu a Mlaliki, mwana wa Davide, mfumu ya ku Yerusalemu:
2 “Zopandapake! Zopandapake!”
atero Mlaliki.
“Zopandapake kotheratu!
Zopandapake.”
3 Kodi munthu amapindulanji pa ntchito zake zonse
zimene amasautsidwa nazo pansi pano?
4 Mibado imabwera ndipo mibado imapita,
koma dziko lapansi limakhalapobe nthawi zonse.
5 Dzuwa limatuluka ndipo dzuwa limalowa
ndipo limapita mwamsanga kumene limatulukira.
6 Mphepo imawombera cha kummwera
ndi kukhotera cha kumpoto;
imawomba mozungulirazungulira,
kumangobwererabwerera komwe yachokera.
7 Mitsinje yonse imakathira ku nyanja,
koma nyanjayo sidzaza;
kumene madziwo amachokera,
amabwereranso komweko.
8 Zinthu zonse ndi zotopetsa,
kutopetsa kwake ndi kosaneneka.
Maso satopa ndi kuona
kapena khutu kukwaniritsidwa ndi kumva.
9 Zomwe zinalipo kale zidzakhalaponso,
zomwe zinachitika kale zidzachitikanso.
Ndiye kuti chatsopano palibiretu pansi pano.
10 Kodi chilipo chinthu chimene wina anganene kuti,
“Taona! Ichi ndiye chatsopano?”
Chinalipo kale, kalekale;
chinalipo ife kulibe.
11 Anthu akale sakumbukiridwa,
ngakhale amene adzabwera mʼtsogolomu
sadzakumbukiridwa ndi iwo
amene adzabwere pambuyo pawo.
Nzeru Nʼzopandapake
12 Ine, Mlalikine, ndinali mfumu ya Israeli mu Yerusalemu. 13 Ndinayika mtima wanga pophunzira ndi kufunafuna mwa nzeru zinthu zonse zimene zimachitika pansi pa thambo. Ndi ntchito yolemetsa ndithu imene Mulungu anayipereka kwa anthu! 14 Ine ndaona zinthu zonse zochitika pansi pano; zinthu zonsezo ndi zopandapake, nʼkungodzivuta chabe.
15 Chinthu chokhota sichingathe kuwongoledwa;
chimene palibe sichingathe kuwerengedwa.
16 Ine ndinaganiza mu mtima mwanga, “Taona, ine ndakula ndi kukhala wa nzeru zochuluka kupambana aliyense amene analamulirapo Yerusalemu ndisanabadwe; ndaphunzira nzeru zochuluka ndi luntha.” 17 Ndipo ndinadzipereka kuti ndithe kumvetsa kuti nzeru nʼchiyani, misala nʼchiyani, uchitsiru nʼchiyani, koma ndinazindikira ichi, kuti kuteronso nʼkungodzivuta chabe.
18 Pakuti nzeru zochuluka zimabweretsa chisoni chochulukanso:
chidziwitso chochuluka, zowawa zochulukanso.
Zosangalatsa Nʼzopandapake
2 Ine ndinaganiza mu mtima mwanga, “Tsopano ndiyese zosangalatsa kuti ndipeze zomwe ndi zabwino.” Koma izi zinaonekanso kuti ndi zopandapake. 2 “Kuseka,” ndinati, “imeneyo ndi misala. Ndipo kodi chisangalalo chimabweretsa phindu lanji?” 3 Ndinayesa kudzisangalatsa ndi vinyo, koma umenewu unali uchitsiru, pamenepo nʼkuti maganizo anga akutsogozedwa ndi nzeru. Ine ndinkati mwina kapena njira yotero nʼkukhala yopambana, imene anthu amatsata pofuna kusangalala pa masiku owerengeka a moyo wawo.
4 Ndinagwira ntchito zikuluzikulu: Ndinadzimangira nyumba ndi kuwoka mipesa. 5 Ndinalima madimba ndi minda yamitengo; ndipo ndinadzalamo mitengo ya zipatso za mitundu yonse. 6 Ndinakumba mayiwe osungiramo madzi woti ndizithirira minda ya mitengo yodzalidwa ija. 7 Ndinagula akapolo aamuna ndi akapolo aakazi, ndiponso ndinali ndi akapolo ena omwe anabadwira mʼnyumba mwanga. Ndinalinso ndi ngʼombe ndi nkhosa zambiri kupambana aliyense mu Yerusalemu amene analipo ndisanabadwe. 8 Ndinadzikundikira siliva ndi golide, ndiponso chuma chochokera kwa mafumu ndi madera awo. Ndinali ndi amuna ndi akazi oyimba ndiponso azikazi; zinthu zokondweretsa mtima wa munthu. 9 Ndinali munthu wotchuka kupambana wina aliyense mu Yerusalemu amene analipo ndisanabadwe. Mu zonsezi nzeru zanga zinali nane.
10 Sindinadzimane chilichonse chimene maso anga anachifuna;
mtima wanga sindinawumane zokondweretsa.
Mtima wanga unakondwera ndi ntchito yanga yonse,
ndipo iyi ndiyo inali mphotho ya ntchito zanga zonse zolemetsa.
11 Koma pamene ndinayamba kuyangʼanayangʼana zonse zimene ndinachita ndi manja anga,
ndi zimene ndinazivutikira kuti ndizipeze,
zonsezi zinali zopandapake; kungodzivuta chabe,
palibe chomwe ndinapindula pansi pano.
Nzeru ndi Uchitsiru Nʼzopandapake
12 Kenaka maganizo anga anayamba kulingalira zakuti nzeru nʼchiyani,
komanso kuti misala ndi uchitsiru nʼchiyani.
Kodi munthu wodzalowa ufumu tsopanoyo angachite chiyani
choposa chimene chinachitidwa kale?
13 Ndinaona kuti nzeru ndi yopambana uchitsiru,
monga momwe kuwala kumapambanira mdima.
14 Munthu wanzeru amayenda maso ali patsogolo,
pamene chitsiru chimayenda mʼchimbulimbuli;
koma ndinazindikira kuti chomwe
chimawachitikira onsewo ndi chimodzi.
15 Pamenepo ndinalingalira mu mtima mwanga,
“Zochitikira chitsiru zidzandichitikiranso ine.
Nanga tsono phindu langa nʼchiyani pakukhala wanzeru?”
Ndinati mu mtima mwanga,
“Ichinso ndi chopandapake.”
16 Pakuti munthu wanzeru, pamodzinso ndi chitsiru sadzakumbukiridwa nthawi yayitali;
mʼmasiku amʼtsogolo awiriwo adzayiwalika.
Mmene chimafera chitsiru ndi mmenenso amafera wanzeru!
Kugwira Ntchito Nʼkopandapake
17 Kotero ndinadana nawo moyo chifukwa ntchito zimene zimagwiridwa pansi pano ndi zosautsa kwa ine. Ntchito zonsezo ndi zopandapake, nʼkungodzivuta chabe. 18 Ine ndinadana nazo ntchito zonse zimene ndinazigwira pansi pano, chifukwa ndinayenera kudzazisiyira wina amene adzalowa mʼmalo mwanga. 19 Ndipo ndani amadziwa kuti munthu ameneyo adzakhala wanzeru kapena chitsiru? Komabe munthuyo adzakhala wolamulira zonse zimene ndinazichita pansi pano mwa nzeru zanga. Izinso ndi zopandapake. 20 Motero ndinayamba kutaya mtima chifukwa cha ntchito zonse zimene ndinazivutikira pansi pano. 21 Pakuti munthu atha kugwira ntchito yake mwanzeru, chidziwitso ndi luntha, ndipo kenaka nʼkusiyira wina amene sanakhetserepo thukuta. Izinso ndi zopandapake ndiponso tsoka lalikulu. 22 Kodi munthu amapindulanji pa ntchito zonse zolemetsa ndi zodetsa nkhawa zimene amazichita pansi pano? 23 Masiku ake onse amakhala achisoni, ntchito yake imakhala yovuta; ngakhale usiku womwe, mtima wake supumula. Izinso ndi zopandapake.
24 Kwa munthu palibe chabwino china kuposa kudya, kumwa ndi kukondwerera ntchito zake. Izinso ndaona kuti ndi zochokera kwa Mulungu, 25 pakuti popanda Iye, ndani angadye ndi kupeza chisangalalo? 26 Munthu amene amakondweretsa Mulungu, Mulunguyo amamusandutsa wanzeru, wozindikira ndi wachisangalalo, koma wochimwa, Mulungu amamupatsa ntchito yosonkhanitsa ndi kusunga chuma kuti adzachipereke kwa amene Mulunguyo amakondwera naye. Izinso ndi zopandapake, nʼkungodzivuta chabe.
Chilichonse Chili ndi Nthawi
3 Chinthu chilichonse chili ndi nthawi yake,
ndi nyengo yake yomwe anayika Mulungu:
2 Nthawi yobadwa ndi nthawi yomwalira,
nthawi yodzala ndi nthawi yokolola.
3 Nthawi yakupha ndi nthawi yochiritsa,
nthawi yogwetsa ndi nthawi yomanga.
4 Nthawi yomva chisoni ndi nthawi yosangalala,
nthawi yolira maliro ndi nthawi yovina.
5 Nthawi yotaya miyala ndi nthawi yokundika miyala,
nthawi yokumbatirana ndi nthawi yoleka kukumbatirana.
6 Nthawi yofunafuna ndi nthawi yoleka kufunafuna,
nthawi yosunga ndi nthawi yotaya.
7 Nthawi yongʼamba ndi nthawi yosoka,
nthawi yokhala chete ndi nthawi yoyankhula.
8 Nthawi yokondana ndi nthawi yodana,
nthawi ya nkhondo ndi nthawi ya mtendere.
9 Kodi wantchito amapeza phindu lanji pa ntchito yake yolemetsa? 10 Ine ndinaona chipsinjo chimene Mulungu anayika pa anthu. 11 Iye anapanga chinthu chilichonse kuti chikhale chabwino pa nthawi yake. Anayika nzeru zamuyaya mʼmitima ya anthu; komabe anthuwo sangathe kuzindikira zomwe Mulungu wachita kuyambira pa chiyambi mpaka chimaliziro. 12 Ine ndikudziwa kuti palibenso kanthu kabwino kwa anthu kopambana kusangalala ndi kuchita zabwino pamene ali ndi moyo. 13 Ndi mphatso ya Mulungu kwa munthu kuti azidya, azimwa ndi kumakondwera ndi ntchito zake zolemetsa. 14 Ndikudziwa kuti chilichonse chimene Mulungu amachita chidzakhala mpaka muyaya; palibe zimene zingawonjezedwe kapena kuchotsedwa. Mulungu amazichita kuti anthu azimuopa.
15 Chilichonse chimene chilipo chinalipo kale,
ndipo chimene chidzakhalapo chinalipo poyamba;
Mulungu amabwezanso zakale zimene zinapita kuti zichitikenso.
16 Ndipo ndinaona chinthu chinanso pansi pano:
ku malo achiweruzo, kuyipa mtima kuli komweko,
ku malo achilungamo, kuyipa mtima kuli komweko.
17 Ndinalingalira mu mtima mwanga kuti;
“Mulungu adzaweruza
olungama pamodzi ndi oyipa omwe,
pakuti anayika nthawi yochitikira chinthu chilichonse,
nthawi ya ntchito iliyonse.”
18 Ndinalingaliranso kuti, “Kunena za anthu, Mulungu amawayesa ndi cholinga choti awaonetse kuti iwo ali ngati nyama. 19 Zimene zimachitikira munthu, zomwezonso zimachitikira nyama; chinthu chimodzi chomwecho chimachitikira onse: Monga munthu amafa momwemonso nyama imafa. Zonsezi zimapuma mpweya umodzimodzi omwewo; munthu saposa nyama. Zonsezi ndi zopandapake. 20 Zonse zimapita kumodzimodzi; zonsezi zimachokera ku fumbi, ndipo zimabwereranso ku fumbi komweko. 21 Kodi ndani amene amadziwa ngati mzimu wa munthu umakwera kumwamba, ndipo mzimu wa nyama umatsikira kunsi kwa dziko?”
22 Kotero ndinaona kuti palibe chinthu chabwino kwa munthu kuposa kuti munthu azisangalala ndi ntchito yake, pakuti ichi ndiye chake chenicheni. Pakuti ndani amene angamubweretse kuti adzaone zimene zidzamuchitikira iye akadzamwalira?
Matsoka ndi Mavuto a Moyo Uno
4 Ndinayangʼananso ndi kuona chipsinjo chimene chimachitika pansi pano:
ndinaona misozi ya anthu opsinjika,
ndipo iwo alibe owatonthoza;
mphamvu zinali ndi anthu owapsinjawo
ndipo iwonso analibe owatonthoza.
2 Ndipo ndinanena kuti akufa,
amene anafa kale,
ndi osangalala kuposa amoyo,
amene akanalibe ndi moyo.
3 Koma wopambana onsewa
ndi amene sanabadwe,
amene sanaone zoyipa
zimene chimachitika pansi pano.
4 Ndipo ndinazindikira kuti ntchito zonse zolemetsa ndiponso ntchito zonse zaluso zimachitika chifukwa choti wina akuchitira nsanje mnzake. Izinso ndi zopandapake, nʼkungodzivuta chabe.
5 Chitsiru chimangoti manja ake lobodo
ndi kudzipha chokha ndi njala.
6 Nʼkwabwino kukhala ndi dzanja limodzi lodzaza uli pa mtendere,
kuposa kukhala ndi manja awiri odzaza uli pa mavuto,
ndipo uku nʼkungodzivuta chabe.
7 Ndinaonanso chinthu china chopanda phindu pansi pano:
8 Panali munthu amene anali yekhayekha;
analibe mwana kapena mʼbale.
Ntchito yake yolemetsa sinkatha,
ndipo maso ake sankakhutitsidwa ndi chuma chake.
Iye anadzifunsa kuti, “Kodi ntchito yosautsayi ndikuyigwirira yani?
Nanga nʼchifukwa chiyani ndikudzimana chisangalalo?”
Izinso ndi zopandapake,
zosasangalatsa!
9 Kukhala awiri nʼkwabwino kuposa kukhala wekha,
chifukwa ntchito ya anthu awiri ili ndi phindu:
10 Ngati winayo agwa,
mnzakeyo adzamudzutsa.
Koma tsoka kwa munthu amene agwa
ndipo alibe wina woti amudzutse!
11 Komanso ngati anthu awiri agona malo amodzi, adzafunditsana.
Koma nanga mmodzi angadzifunditse yekha?
12 Munthu mmodzi angathe kugonjetsedwa,
koma anthu awiri akhoza kudziteteza.
Chingwe cha maulusi atatu sichidukirapo.
Kutukuka Nʼkopandapake
13 Wachinyamata wosauka koma wanzeru aposa mfumu yokalamba koma yopusa imene simvanso malangizo. 14 Wachinyamatayo angathe kuchokera ku ndende ndi kudzakhala mfumu, kapena angathe kubadwa wosauka mʼdziko la mfumuyo. 15 Ndipo ndinaona kuti iwo onse amene anakhala ndi moyo ndi kuyenda pansi pano anatsatira wachinyamatayo, amene anatenga malo a mfumu. 16 Mfumu ikhoza kulamulira anthu osawerengeka, komabe itamwalira, palibe amene adzayamikire zomwe mfumuyo inachita. Izinso ndi zopandapake, nʼkungozivuta chabe.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.