Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Beginning

Read the Bible from start to finish, from Genesis to Revelation.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Miyambo 27-29

27 Usamanyadire za mawa,
    pakuti sudziwa zimene zidzachitike pa tsikulo.

Munthu wina akutamande, koma osati wekha;
    mlendo akakutamanda, ndiponi koma osati ndi pakamwa pako.

Mwala ndi wolemera ndipo mchenganso ndi wolemera kwambiri,
    koma makani a chitsiru ndi oposa zonsezo kulemera kwake.

Mkwiyo umadzetsa nkhanza ndipo kupsa mtima kumachititsa zoopsa.
    Koma nsanje imachita zoopsa zopambana.

Kudzudzula munthu poyera nʼkwabwino
    kuposa chikondi chobisika.

Munthu amene amakukonda ngakhale akupweteke zili bwino,
    koma mdani wako amakupsompsona mwachinyengo.

Iye amene wakhuta amayipidwa ndi chisa cha uchi,
    koma kwa munthu wanjala ngakhale chimene chili chowawa chimamukomera.

Munthu amene wasochera ku nyumba kwake,
    ali monga mbalame imene yasochera pa chisa chake.

Mafuta ndi zonunkhira zimasangalatsa mtima,
    ndipo kukoma mtima kwa bwenzi kwagona pa malangizo ake.

10 Usasiye bwenzi lako ndiponso bwenzi la abambo ako,
    ndipo usapite ku nyumba ya mʼbale wako pamene wakumana ndi mavuto;
    mnzako wokhala naye pafupi amaposa mʼbale wako wokhala kutali.

11 Mwana wanga, khala wanzeru, ndipo ukondweretse mtima wanga;
    pamenepo ine ndidzatha kuyankha aliyense amene amandinyoza.

12 Munthu wochenjera akaona choopsa amabisala,
    koma munthu wopusa amangopitirira ndipo amakumana ndi mavuto.

13 Utenge chovala cha munthu amene waperekera mlendo chikole;
    ngati chigwiriro chifukwa waperekera chikole mlendo wosadziwika.

14 Ngati munthu apatsa mnzake moni mofuwula mmamawa kwambiri,
    anthu adzamuyesa kuti akutemberera.

15 Mkazi wolongolola ali ngati
    mvula yamvumbi.
16 Kumuletsa mkazi wotereyu zimenezi zili ngati kuletsa mphepo
    kapena kufumbata mafuta mʼdzanja.

17 Chitsulo chimanoledwa ndi chitsulo chinzake,
    chomwechonso munthu amanoledwa ndi munthu mnzake.

18 Amene amasamalira mtengo wamkuyu adzadya zipatso zake,
    ndipo iye amene amasamalira mbuye wake adzalandira ulemu.

19 Monga momwe nkhope imaonekera mʼmadzi,
    chomwechonso mtima wa munthu umadziwika ndi ntchito zake.

20 Manda sakhuta,
    nawonso maso a munthu sakhuta.

21 Siliva amasungunulira mu uvuni ndipo golide mʼngʼanjo,
    chomwechonso munthu amadziwika ndi zomwe akudzitamandira nazo.

22 Ngakhale utakonola chitsiru mu mtondo
    ndi musi ngati chimanga,
    uchitsiru wakewo sudzachoka.

23 Uzidziwe bwino nkhosa zako momwe zilili.
    Kodi usamalire bwino ziweto zako?
24 Paja chuma sichikhala mpaka muyaya,
    ndipo ufumu sukhala mpaka mibado yonse.
25 Pamene udzu watha, msipu nʼkumera;
    ndipo atatuta udzu wa ku mapiri,
26 ana ankhosa adzakupatsani chovala
    ndipo pogulitsa mbuzi mudzapeza ndalama yogulira munda.
27 Mudzakhala ndi mkaka wambuzi wambiri
    kuti muzidya inuyo ndi banja lanu
    ndi kudyetsa antchito anu aakazi.
28 Munthu woyipa amathawa ngakhale palibe wina womuthamangitsa,
    koma wolungama ndi wolimba mtima ngati mkango.

Pamene mʼdziko muli kuwukirana, dzikolo limakhala ndi olamulira ambiri,
    koma anthu omvetsa ndi odziwa zinthu bwino ndiwo angakhazikitse bata mʼdzikolo nthawi yayitali.

Munthu wosauka amene amapondereza osauka anzake
    ali ngati mvula yamkuntho imene imawononga mbewu mʼmunda.

Amene amakana malamulo amatamanda anthu oyipa,
    koma amene amasunga malamulo amatsutsana nawo.

Anthu oyipa samvetsa za chiweruzo cholungama,
    koma amene amafuna kuchita zimene Yehova afuna amachimvetsetsa bwino.

Munthu wosauka wa makhalidwe abwino
    aposa munthu wolemera wa makhalidwe okhotakhota.

Amene amasunga malamulo ndi mwana wozindikira zinthu,
    koma amene amayenda ndi anthu adyera amachititsa manyazi abambo ake.

Amene amachulukitsa chuma chake polandira chiwongoladzanja chochuluka
    amakundikira chumacho anthu ena, amene adzachitira chifundo anthu osauka.

Wokana kumvera malamulo
    ngakhale pemphero lake lomwe limamunyansa Yehova.

10 Amene amatsogolera anthu olungama kuti ayende mʼnjira yoyipa
    adzagwera mu msampha wake womwe,
    koma anthu opanda cholakwa adzalandira cholowa chabwino.

11 Munthu wolemera amadziyesa kuti ndi wanzeru,
    koma munthu wosauka amene ali ndi nzeru zodziwa zinthu amamutulukira.

12 Pamene olungama apambana pamakhala chikondwerero chachikulu;
    koma pamene anthu oyipa apatsidwa ulamuliro, anthu amabisala.

13 Wobisa machimo ake sadzaona mwayi,
    koma aliyense amene awulula ndi kuleka machimowo, adzalandira chifundo.

14 Ndi wodala munthu amene amaopa Yehova nthawi zonse,
    koma amene aumitsa mtima wake adzagwa mʼmavuto.

15 Ngati mkango wobuma kapena chimbalangondo cholusa
    ndi mmenenso amakhalira munthu woyipa akamalamulira anthu osauka.

16 Wolamulira amene samvetsa zinthu ndiye amakhala wankhanza
    koma amene amadana ndi phindu lopeza mwachinyengo adzakhala ndi moyo wautali.

17 Munthu amene wapalamula mlandu wopha munthu
    adzakhala wothawathawa mpaka imfa yake;
    wina aliyense asamuthandize.

18 Amene amayenda mokhulupirika adzapulumutsidwa
    koma amene njira zake ndi zokhotakhota adzagwa mʼdzenje.

19 Amene amalima mʼmunda mwake adzakhala ndi chakudya chochuluka,
    koma amene amangosewera adzakhala mʼmphawi.

20 Munthu wokhulupirika adzadalitsika kwambiri,
    koma wofuna kulemera mofulumira adzalangidwa.

21 Kukondera si kwabwino,
    ena amachita zolakwazo chifukwa cha kachidutswa ka buledi.

22 Munthu wowumira amafunitsitsa kulemera
    koma sazindikira kuti umphawi udzamugwera.

23 Amene amadzudzula mnzake potsiriza pake
    mnzakeyo adzamukonda kwambiri, kupambana amene amanena mawu oshashalika.

24 Amene amabera abambo ake kapena amayi ake
    namanena kuti “kumeneko sikulakwa,”
    ndi mnzake wa munthu amene amasakaza.

25 Munthu wadyera amayambitsa mikangano,
    koma amene amadalira Yehova adzalemera.

26 Amene amadzidalira yekha ndi chitsiru,
    koma amene amatsata nzeru za ena adzapulumuka.

27 Amene amapereka kwa osauka sadzasowa kanthu,
    koma amene amatsinzina maso ake adzatembereredwa kwambiri.

28 Pamene anthu oyipa apatsidwa ulamuliro anthu amabisala,
    koma anthu oyipa akawonongeka olungama amapeza bwino.
29 Munthu amene amawumitsabe khosi lake atadzudzulidwa kwambiri,
    adzawonongeka mwadzidzidzi popanda chomuchiritsa.

Anthu olungama akamalamulira mʼdziko anthu amakondwa,
    koma ngati dziko lilamulidwa ndi anthu oyipa mtima anthu amadandaula.

Munthu amene amakonda nzeru amasangalatsa abambo ake,
    koma woyenda ndi akazi achiwerewere amasakaza chuma chake.

Mfumu imalimbitsa dziko poweruza mwachilungamo,
    koma mfumu imene imawumiriza anthu kuti ayipatse mphatso imawononga dziko.

Munthu woshashalika mnzake,
    akudziyalira ukonde mapazi ake.

Munthu woyipa amakodwa ndi machimo ake,
    koma wochita chilungamo amayimba lokoma.

Munthu wolungama amasamalira anthu osauka,
    koma woyipa salabadira zimenezi.

Anthu onyoza atha kuwutsa ziwawa mu mzinda,
    koma anthu anzeru amaletsa ukali.

Ngati munthu wanzeru atsutsana ndi chitsiru,
    chitsirucho chimachita phokoso ndi kumangoseka ndipo sipakhala mtendere.

10 Anthu okhetsa magazi amadana ndi munthu wangwiro
    koma anthu olungama amasamalira moyo wake.

11 Munthu wopusa amaonetsa mkwiyo wake,
    koma munthu wanzeru amadzigwira.

12 Ngati wolamulira amvera zabodza,
    akuluakulu ake onse adzakhala oyipa.

13 Munthu wosauka ndi munthu wopondereza anzake amafanana pa kuti:
    Yehova ndiye anawapatsa maso onsewa.

14 Ngati mfumu iweruza osauka moyenera,
    mpando wake waufumu udzakhazikika nthawi zonse.

15 Ndodo ndi chidzudzulo zimapatsa nzeru
    koma mwana womulekerera amachititsa amayi ake manyazi.

16 Oyipa akamalamulira zoyipa zimachuluka,
    koma anthu olungama adzaona kugwa kwa anthu oyipawo.

17 Umulange mwana wako ndipo adzakupatsa mtendere
    ndi kusangalatsa mtima wako.

18 Ngati uthenga wochokera kwa Yehova supezeka anthu amangochita zofuna zawo;
    koma wodala ndi amene amasunga malamulo.

19 Munthu wantchito sangalangizidwe ndi mawu okha basi;
    ngakhale awamvetse mawuwo sadzatha kuchitapo kanthu.

20 Ngakhale munthu wa uchitsiru nʼkuti ndiponi popeza chikhulupiriro chilipo
    kuposa munthu wodziyesa yekha kuti ndi wanzeru poyankhula.

21 Ngati munthu asasatitsa wantchito wake kuyambira ali mwana,
    potsirizira adzapeza kuti wantchitoyo wasanduka mlowachuma wake.

22 Munthu wamkwiyo amayambitsa mikangano,
    ndipo munthu waukali amachita zolakwa zambiri.

23 Kunyada kwa munthu kudzamutsitsa,
    koma munthu wodzichepetsa amalandira ulemu.

24 Woyenda ndi munthu wakuba ndi mdani wa moyo wake womwe;
    amalumbira koma osawulula kanthu.

25 Kuopa munthu kudzakhala ngati msampha,
    koma aliyense amene amadalira Yehova adzatetezedwa.

26 Anthu ambiri amafunitsitsa kuti wolamulira awakomere mtima,
    koma munthu amaweruzidwa mwachilungamo ndi thandizo la Yehova basi.

27 Anthu olungama amanyansidwa ndi anthu achinyengo;
    koma anthu oyipa amanyansidwa ndi anthu a mtima wowongoka.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.