Beginning
Za Mkazi Wachigololo
7 Mwana wanga, mvera mawu anga;
usunge bwino malamulo angawa.
2 Utsate malamulo anga ndipo udzakhala ndi moyo;
samala malangizo angawa monga uchitira ndi maso ako.
3 Uchite ngati wawamangirira pa zala zako,
ndiponso ngati kuti wawalemba pa mtima pako.
4 Nzeru uyiwuze kuti, “Iwe ndiwe mlongo wanga,”
ndipo khalidwe lomvetsa bwino zinthu ulitchule kuti, “Bwenzi langa lapamtima.”
5 Zidzakuteteza kwa mkazi wachigololo
ndiponso zidzakuthandiza kusamvera mawu oshashalika a mkazi wachilendo.
6 Tsiku lina pa zenera la nyumba yanga
ndinasuzumira pa zenera.
7 Ndinaona pakati pa anthu opusa,
pakati pa anyamata,
mnyamata wina wopanda nzeru.
8 Iye ankayenda njira yodutsa pafupi ndi nyumba ya mkaziyo,
kuyenda molunjika nyumba ya mkaziyo.
9 Inali nthawi yachisisira madzulo,
nthawi ya usiku, kuli mdima.
10 Ndipo mkaziyo anadzakumana naye,
atavala ngati munthu wachiwerewere wa mtima wonyenga.
11 (Mkaziyo ndi wolongolola ndiponso nkhutukumve,
iye ndi wosakhazikika pa khomo.
12 Mwina umupeza pa msewu, mwina umupeza pa msika,
ndipo amadikirira munthu pa mphambano iliyonse).
13 Tsono amagwira mnyamatayo ndi kupsompsona
ndi nkhope yake yopanda manyazi amamuwuza kuti,
14 “Ndinayenera kupereka nsembe zachiyanjano.
Lero ndakwaniritsa malumbiro anga.
15 Choncho ndinabwera kudzakumana nawe;
ndinkakufunafuna ndipo ndakupeza!
16 Pa bedi panga ndayalapo
nsalu zosalala zokongola zochokera ku Igupto.
17 Pa bedi panga ndawazapo zonunkhira
za mure, mafuta onunkhira a aloe ndi sinamoni.
18 Bwera, tiye tikhale malo amodzi kukondwerera chikondi mpaka mmawa;
tiye tisangalatsane mwachikondi!
19 Mwamuna wanga kulibe ku nyumbako;
wapita ulendo wautali:
20 Anatenga thumba la ndalama
ndipo adzabwera ku nyumba mwezi ukakhwima.”
21 Ndi mawu ake onyengerera amamukakamiza mnyamatayo;
amukopa ndi mawu ake oshashalika.
22 Nthawi yomweyo chitsiru chimamutsatira mkaziyo
ngati ngʼombe yopita kukaphedwa,
monga momwe mbawala ikodwera mu msampha,
23 mpaka muvi utalasa chiwindi chake,
chimakhala ngati mbalame yothamangira mʼkhwekhwe,
osadziwa kuti moyo wake uwonongeka.
24 Tsono ana inu, ndimvereni;
mvetsetsani zimene ndikunena.
25 Musatengeke mtima ndi njira za mkazi ameneyu;
musasochere potsata njira zake.
26 Paja iye anagwetsa anthu ambiri;
wapha gulu lalikulu la anthu.
27 Nyumba yake ndi njira yopita ku manda,
yotsikira ku malo a anthu akufa.
Nzeru Ikuyitana
8 Kodi nzeru sikuyitana?
Kodi nzeru yomvetsa zinthu sinakweze mawu ake?
2 Nzeru imayima pa zitunda mʼmbali mwa njira,
imayima pa mphambano ya misewu.
3 Imafuwula pafupi ndi zipata zolowera mu mzinda,
pa makomo olowera imafuwula kuti,
4 Inu anthu, ndikuyitana inu;
ndikuyitanatu anthu onse.
5 Inu amene simudziwa kanthunu khalani ochenjera;
inu amene ndi opusa, khalani ndi mtima womvetsa zinthu.
6 Mverani, pakuti ndikukuwuzani zinthu zofunika kwambiri;
ndatsekula pakamwa panga ndipo payankhula zolungama.
7 Pakamwa panga pamayankhula zoona
ndimanyansidwa ndi kuyankhula zoyipa.
8 Mawu onse a pakamwa panga ndi olungama;
mʼmawu angawo mulibe zokhotakhota kapena zopotoka.
9 Kwa anthu ozindikira, mawu anga onse ndi woona;
kwa anthu amene ali ndi nzeru zomvetsa zinthu, mawu angawo ndi okhoza.
10 Landirani malangizo anga mʼmalo mwa siliva,
nzeru zomvetsa zinthu mʼmalo mwa golide wabwino.
11 Paja nzeru ndi yabwino kwambiri kuposa miyala yamtengowapatali,
ndipo zonse zimene ungazifune sizingafanane ndi nzeru.
12 Ine nzeru, ndimakhala pamodzi ndi kuchenjera.
Ine ndimadziwa zinthu ndiponso ndimalingalira zinthu bwino.
13 Kuopa Yehova ndiko kudana ndi zoyipa.
Ine ndimadana ndi kunyada, kudzitama,
kuchita zoyipa, ndiponso kuyankhula zonyenga.
14 Ndine mwini uphungu ndi maganizo abwino;
ndili ndi nzeru yomvetsa zinthu ndiponso mphamvu.
15 Ndine amene ndimathandiza mafumu kulamulira.
Ndimawathandiza olamulira kukhazikitsa malamulo olungama.
16 Ndine amene ndimathandiza akalonga polamula.
Ndinenso amene ndimathandiza akuluakulu onse kulamulira bwino dziko.
17 Ndimakonda amene amandikonda,
ndipo amene amandifunafuna amandipeza.
18 Ine ndili ndi chuma ndi ulemu,
chuma ndi kupindula pa ntchito kokhazikika.
19 Chipatso changa ndi chabwino kuposa golide, ngakhale golide wosalala;
zimene ine ndimabereka zimaposa siliva wabwino kwambiri.
20 Ndimachita zinthu zolungama.
Ine sindipatuka mʼnjira za chilungamo.
21 Ndimapereka chuma kwa amene amandikonda
ndi kudzaza nyumba zawo zosungiramo chuma.
22 “Yehova anandilenga ine nzeru monga ntchito yake yoyamba.
Mwa ntchito zake zakalekale yoyamba ndinali ine.
23 Ndinapangidwa kalekalelo,
pachiyambi penipeni dziko lapansi lisanalengedwe.
24 Nyanja, akasupe odzaza ndi madzi,
zonsezi kulibe pamene ine ndinkabadwa.
25 Mapiri asanakhazikitsidwe pa malo awo,
mapiri angʼonoangʼono asanakhalepo, ine ndinali nditabadwa kale,
26 lisanalengedwe dziko lapansi ndi minda yake;
lisanalengedwe dothi loyamba la dziko lapansi.
27 Ine ndinalipo pamene Yehova ankakhazikitsa mlengalenga,
pamene ankalemba malire a nyanja yozama,
28 pamene anakhazikitsa mitambo ya mlengalenga
ndi kukhazikitsa akasupe a madzi ozama,
29 pamene anayikira nyanja malire
kuti madzi asadutse malirewo,
ndiponso pamene ankayika malire a dziko lapansi.
30 Tsono ine ndinali pambali pake ngati mmisiri;
ndikumukondweretsa tsiku ndi tsiku,
kusangalala nthawi zonse pamaso pake.
31 Ndinkasangalala ndi dziko lake lonse
ndiponso kumakondwera nawo anthu onse.”
32 “Ndiye tsono ana inu, ndimvereni;
odala anthu amene amasunga njira zanga.
33 Mverani malangizo anga kuti mukhale ndi nzeru;
musanyozere mawu anga.
34 Wodala munthu amene amandimvera,
amene amakhala pa khomo panga tsiku ndi tsiku,
kudikirira pa chitseko changa.
35 Paja aliyense amene apeza ine wapeza moyo
ndipo Yehova amamukomera mtima.
36 Koma amene alephera kundipeza, amadzipweteka yekha;
onse amene amandida amakonda imfa.”
Za Nzeru ndi Uchitsiru
9 Nzeru inamanga nyumba yake;
inayimika nsanamira zake zisanu ndi ziwiri.
2 Inapha ziweto zake ndipo yasakaniza vinyo wake;
inasakaniza vinyo wake ndi kuyala tebulo lake.
3 Nzeruyo inatuma adzakazi ake,
kuti akakhale pamwamba penipeni pa mzinda ndi kukalengeza kuti,
4 “Aliyense amene ali munthu wamba, abwere kuno!”
Kwa onse opanda nzeru inkanena kuti,
5 “Bwerani, dzadyeni chakudya changa
ndipo dzamweni vinyo amene ndakonza.
6 Lekani zopusa zanu kuti mukhale ndi moyo;
yendani njira ya nzeru yomvetsa zinthu.”
7 Aliyense amene amayesa kukonza munthu wonyoza amadziputira minyozo;
aliyense amene amadzudzula munthu woyipa amadetsa mbiri yake.
8 Usadzudzule munthu wonyoza kuti angadzadane nawe;
dzudzula munthu wanzeru ndipo adzakukonda.
9 Ukalangiza munthu wanzeru ndiye adzapitirira kukhala wanzeru;
ukaphunzitsa munthu wolungama ndiye adzawonjezera kuphunzira kwake.
10 Kuopa Yehova ndiye chiyambi cha nzeru;
kudziwa Woyerayo ndiko kukhala womvetsa bwino zinthu.
11 Chifukwa cha ine nzeru, masiku ako adzachuluka,
ndipo zaka za moyo wako zidzawonjezeredwa.
12 Ngati ndiwe wanzeru, nzeru yakoyo idzakupindulitsa;
ngati ndiwe wonyoza ena, udzavutika wekha.
13 Uchitsiru ndi mkazi waphokoso,
wopulikira ndiponso wosadziwa zinthu.
14 Iye amakhala pa mpando, pa khomo la nyumba yake,
pamalo aatali a mu mzinda,
15 kuti aziyitana anthu ongodutsa,
amene akunka nayenda njira zawo.
16 Amati, “Onse amene ndi anthu wamba abwere kuno,”
ndipo kwa wopanda nzeru amati,
17 “Madzi akuba ndiye amatsekemera;
chakudya chodya mobisa ndi chokoma!”
18 Koma amunawo sadziwa kuti akufa ali kale komweko,
ndi kuti alendo ake alowa kale mʼmanda akuya.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.