Beginning
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Pempho.
70 Fulumirani Mulungu kundipulumutsa;
Yehova bwerani msanga kudzandithandiza.
2 Iwo amene akufunafuna moyo wanga
achititsidwe manyazi ndi kusokonezedwa;
onse amene akukhumba chiwonongeko changa
abwezedwe mopanda ulemu.
3 Onse amene akunena kwa ine kuti, “Aha, aha,”
abwerere chifukwa cha manyazi awo.
4 Koma onse amene akufunafuna Inu
akondwere ndi kusangalala mwa Inu;
iwo amene amakonda chipulumutso chanu
nthawi zonse anene kuti, “Mulungu akuzike!”
5 Koma ine ndine wosauka ndi wosowa;
bwerani msanga kwa ine Inu Mulungu.
Inu ndinu thandizo langa ndi momboli wanga;
Inu Yehova musachedwe.
71 Mwa Inu Yehova ine ndathawiramo;
musalole kuti ndichititsidwe manyazi.
2 Mundilanditse ndi kundipulumutsa mwa chilungamo chanu,
mutchere khutu lanu ndi kundipulumutsa.
3 Mukhale thanthwe langa lothawirapo,
kumene ine nditha kupita nthawi zonse;
lamulani kuti ndipulumuke,
pakuti Inu ndinu thanthwe langa ndi linga langa.
4 Landitseni Inu Mulungu wanga, kuchoka mʼdzanja la oyipa,
kuchoka mʼdzanja la oyipa ndi anthu ankhanza.
5 Pakuti Inu mwakhala chiyembekezo changa, Inu Ambuye Wamphamvuzonse,
chilimbikitso changa kuyambira ndili mwana.
6 Kuyambira pamene ndinabadwa, ndakhala ndikudalira Inu;
Inu munanditulutsa mʼmimba mwa amayi anga,
ndipo ndidzakupembedzani nthawi zonse.
7 Ine ndakhala chinthu chodabwitsa kwa anthu ambiri
koma Inu ndinu wonditchinjiriza wamphamvu.
8 Pakamwa panga padzaza ndi matamando anu,
kulengeza ulemerero wanu tsiku lonse.
9 Musanditaye pamene ndakalamba;
musandisiye pamene mphamvu zanga zatha.
10 Pakuti adani anga ayankhula motsutsana nane;
iwo amene amadikira kuti andiphe amapangana pamodzi.
11 Iwo amati, “Mulungu wamusiya;
mutsatireni ndi kumugwira,
pakuti palibe amene adzamupulumutse.”
12 Musakhale kutali ndi ine Inu Mulungu,
bwerani msanga, Inu Mulungu wanga; thandizeni.
13 Ondineneza anga awonongeke mwa manyazi,
iwo amene akufuna kundipweteka
avale chitonzo ndi manyazi.
14 Koma ine ndidzakhala ndi chiyembekezo mwa Inu nthawi zonse,
ndidzakutamandani mowirikizawirikiza.
15 Pakamwa panga padzafotokoza za chilungamo chanu,
za chipulumutso chanu tsiku lonse,
ngakhale sindikudziwa muyeso wake.
16 Ndidzabwera ndi kulengeza za machitidwe amphamvu zanu Inu Ambuye Wamphamvuzonse.
Ndidzalengeza chilungamo chanu, chanu chokha.
17 Kuyambira ubwana wanga, Inu Mulungu mwakhala mukundiphunzitsa,
ndipo mpaka lero ine ndikulengeza za ntchito zanu zodabwitsa
18 Ngakhale pamene ndakalamba ndipo imvi zili mbuu
musanditaye Inu Mulungu,
mpaka nditalengeza mphamvu zanu
kwa mibado yonse yakutsogolo.
19 Mphamvu zanu ndi kulungama kwanu zimafika mpaka kumwambamwamba.
Ndani wofanana nanu Inu Mulungu,
amene mwachita zazikulu?
20 Ngakhale mwandionetsa mavuto
ambiri owawa,
mudzabwezeretsanso moyo wanga;
kuchokera kunsi kwa dziko lapansi,
mudzandiukitsanso.
21 Inu mudzachulukitsa ulemu wanga
ndi kunditonthozanso.
22 Ndidzakutamandani ndi zeze
chifukwa cha kukhulupirika kwanu Mulungu,
ndidzayimba matamando kwa Inu ndi pangwe,
Inu Woyera wa Israeli.
23 Milomo yanga idzafuwula ndi chimwemwe
pamene ndidzayimba matamando kwa Inu
amene mwandiwombola.
24 Lilime langa lidzafotokoza za ntchito zanu zachilungamo
tsiku lonse,
pakuti iwo amene amafuna kundipweteka
achititsidwa manyazi ndi kusokonezedwa.
Salimo la Solomoni.
72 Patsani mwana wa mfumu nzeru zanu zoweruzira mwa chilungamo,
Inu Mulungu mupatseni mwana wa mfumu chilungamo chanu.
2 Iye adzaweruza anthu anu mwachilungamo,
anthu anu ozunzika mosakondera.
3 Mapiri adzabweretsa chuma kwa anthu anu,
timapiri tidzabweretsa zipatso zachilungamo.
4 Iye adzateteza ozunzika pakati pa anthu
ndi kupulumutsa ana a anthu osowa;
adzaphwanya ozunza anzawo.
5 Adzakhala ndi moyo pa mibado yonse,
nthawi zonse pamene dzuwa ndi mwezi zikuwala.
6 Iye adzakhala kugwa kwa mvula pa minda yolimidwa
ngati mivumbi yothirira dziko lapansi.
7 Mʼmasiku a munthu wolungama adzakhazikika;
chuma chidzachuluka mpaka mwezi utaleka kuwala.
8 Iye adzalamulira kuchokera ku nyanja ina mpaka ku nyanja ina
ndiponso kuchokera ku mtsinje mpaka ku malekezero a dziko lapansi.
9 Mafuko a mʼchipululu adzawerama pamaso pake
ndipo adani ake adzanyambita fumbi.
10 Mafumu a ku Tarisisi ndi a ku zilumba zakutali
adzabweretsa mitulo kwa iye,
mafumu a ku Seba ndi Seba
adzapereka mphatso kwa iyeyo.
11 Mafumu onse adzamuweramira
ndipo mitundu yonse idzamutumikira.
12 Pakuti iye adzawombola wosowa amene akulira,
wozunzika amene alibe wina womuthandiza.
13 Iye adzachitira chifundo anthu ofowoka ndi anthu osowa
ndi kupulumutsa osowa ku imfa.
14 Iye adzalanditsa iwo ku mazunzo ndi chiwawa
pakuti magazi awo ndi amtengo wapatali pamaso pake.
15 Iye akhale ndi moyo wautali;
golide ochokera ku Seba apatsidwe kwa iye.
Anthu amupempherere nthawi zonse
ndi kumudalitsa tsiku lonse.
16 Mulole kuti tirigu achuluke mʼdziko lonse;
pamwamba pa mapiri pakhale tirigu.
Zipatso zake zichuluke ngati za ku Lebanoni;
zichuluke ngati udzu wakuthengo
17 Dzina lake likhazikike kwamuyaya,
lipitirire kukhala monga momwe limakhalira dzuwa.
Mitundu yonse idzadalitsika kudzera mwa iye
ndipo iwo adzamutcha iye wodala.
18 Matamando akhale kwa Yehova Mulungu, Mulungu wa Israeli
amene Iye yekha amachita ntchito zodabwitsa.
19 Matamando akhale ku dzina lake laulemerero kwamuyaya
dziko lonse lapansi lidzaze ndi ulemerero wake.
Ameni ndi Ameni.
20 Uku ndiko kumaliza kwa mapemphero a Davide mwana wa Yese.
BUKU LACHITATU
Masalimo 73–89
Salimo la Asafu.
73 Mulungu ndi wabwino ndithu kwa Israeli,
kwa iwo amene ndi oyera mtima.
2 Koma kunena za ine, mapazi anga anali pafupi kuterereka;
ndinatsala pangʼono kugwa.
3 Pakuti ndinkachitira nsanje odzitamandira,
pamene ndinaona mtendere wa anthu oyipa.
4 Iwo alibe zosautsa;
matupi awo ndi athanzi ndi amphamvu.
5 Saona mavuto monga anthu ena;
sazunzika ngati anthu ena onse.
6 Nʼchifukwa chake kunyada kuli monga mkanda wa mʼkhosi mwawo;
amadziveka chiwawa.
7 Mʼmitima yawo yokhota mumachokera zolakwa;
zoyipa zochokera mʼmaganizo awo sizidziwa malire.
8 Iwowo amanyogodola ndi kumayankhula zoyipa;
mwa kudzikuza kwawo amaopseza ena nʼkumati, “Tikuponderezani.”
9 Pakamwa pawo pamayankhula monyoza Mulungu kumwamba
ndipo lilime lawo limayenda pa dziko lapansi.
10 Nʼchifukwa chake anthu awo amapita kwa iwowo
ndi kumwa madzi mochuluka.
11 Iwo amati, “Kodi Mulungu angadziwe bwanji?
Kodi Wammwambamwamba angadziwe kalikonse?”
12 Umu ndi mmene oyipa alili;
nthawi zonse ali pabwino ndipo chuma chawo chimachulukirachulukira.
13 Ndithudi ine ndawusunga pachabe mtima wanga woyera;
pachabe ndasamba mʼmanja mwanga mwa kusalakwa kwanga.
14 Tsiku lonse ndapeza mavuto;
ndakhala ndi kulangidwa mmawa uliwonse.
15 Ndikanati, “Ndidzayankhula motere,”
ndikanachita chosakhulupirika kwa ana anu.
16 Pamene ndinayesa kuti ndimvetse zonsezi,
zinandisautsa kwambiri
17 kufikira nditalowa mʼmalo opatulika a Mulungu;
pamenepo ndinamvetsa mathero awo.
18 Zoonadi Inu munawayika pa malo woterera;
Mumawagwetsa pansi kuti awonongeke.
19 Mwamsangamsanga iwo amawonongedwa,
amasesedwa kwathunthu ndi mantha!
20 Monga loto pamene wina adzuka,
kotero pamene Inu muuka, Inu Ambuye,
mudzawanyoza ngati maloto chabe.
21 Pamene mtima wanga unasautsidwa
ndi kuwawidwa mu mzimu mwanga,
22 ndinali wopusa ndi wosadziwa;
ndinali chirombo chopanda nzeru pamaso panu.
23 Komabe ineyo ndili ndi Inu nthawi zonse;
mumandigwira dzanja langa lamanja.
24 Inu mumanditsogolera ndi malangizo anu
ndipo pambuyo pake mudzanditenga ku ulemerero.
25 Kodi kumwamba ndili ndi yani kupatula Inu?
Ndipo dziko lapansi lilibe chilichonse chimene ndimachilakalaka koposa Inuyo.
26 Thupi ndi mtima wanga zitha kufowoka,
koma Mulungu ndiye mphamvu ya mtima wanga
ndi cholandira changa kwamuyaya.
27 Iwo amene ali kutali ndi Inu adzawonongeka;
Inu mumawononga onse osakhulupirika pamaso panu.
28 Koma kunena za Ine ndi kwabwino kukhala pafupi ndi Mulungu.
Ndatsimikiza kuti Ambuye Yehova ndiwo pothawirapo panga
ndipo ndidzalalika ntchito zanu zonse.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.