Beginning
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.
21 Inu Yehova, mfumu ikusangalala mu mphamvu yanu,
chimwemwe chake nʼchachikuludi pa kupambana kumene mumapereka!
2 Inu mwayipatsa zokhumba za mtima wake
ndipo simunayimane zopempha za pa milomo yake.
Sela
3 Inu munayilandira ndi madalitso ochuluka
ndipo munayiveka chipewa chaufumu chagolide weniweni pa mutu wake.
4 Iye anakupemphani moyo, ndipo munamupatsa
masiku ochuluka kwamuyaya.
5 Kudzera mʼzigonjetso zimene munapereka, ulemerero wake ndi waukulu;
Inu mwapereka pa iyo ulemerero ndi ufumu.
6 Zoonadi Inu mwayipatsa madalitso amuyaya,
Inu mwayipatsa chisangalalo ndi chimwemwe chimene chili pamaso panu.
7 Pakuti mfumu imadalira Yehova;
kudzera mʼchikondi chake chosatha cha Wammwambamwamba,
iyo sidzagwedezeka.
8 Dzanja lanu lidzayimitsa adani anu onse;
dzanja lanu lamanja lidzagwira adani anu.
9 Pa nthawi ya kuonekera kwanu
mudzawasandutsa ngʼanjo yamoto yotentha.
Mu ukali wake Yehova adzawameza,
ndipo moto wake udzawatha.
10 Inu mudzawononga ana awo pa dziko lapansi,
zidzukulu zawo pakati pa anthu.
11 Ngakhale iwo akukonzereni chiwembu mwa kuchenjera kwawo
sadzapambana;
12 pakuti mudzawapirikitsa ndipo adzaonetsa misana yawo
pamene mudzawaloza ndi mivi yanu.
13 Mukwezeke Inu Yehova mʼmphamvu yanu,
ife tidzayimba nyimbo ndi kutamanda mphamvu yanu.
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Monga mwa “Mbawala yayikazi ya Mmawa.” Salimo la Davide.
22 Mulungu wanga, Mulungu wanga, nʼchifukwa chiyani mwandisiya?
Chifuwa chiyani simukundithandiza ndi pangʼono pomwe?
Nʼchifukwa chiyani simukumva mawu a kudandaula kwanga?
2 Inu Mulungu wanga, ine ndimalira masana, koma simuyankha,
usikunso, ndipo sindikhala chete.
3 Inu ndinu Woyera, wokhala pa mpando waufumu;
ndinu matamando a Israeli.
4 Pa inu makolo athu anadalira;
iwo anadalira ndipo Inu munawapulumutsa.
5 Analirira kwa inu ndipo munawapulumutsa.
Iwo anakhulupirira Inu ndipo simunawakhumudwitse.
6 Koma ine ndine nyongolotsi osati munthu,
wosekedwa ndi wonyozedwa ndi anthu onse.
7 Onse amene amandiona amandiseka;
amandiyankhulira mawu achipongwe akupukusa mitu yawo kunena kuti
8 “Iyeyu amadalira Yehova,
musiyeni Yehovayo amulanditse.
Musiyeni Yehova amupulumutse
popeza amakondwera mwa Yehovayo.”
9 Komabe Inu ndinu amene munandibadwitsa, munanditulutsa mʼmimba mwa amayi anga.
Munachititsa kuti ndizikudalirani
ngakhale pa nthawi imene ndinkayamwa.
10 Chibadwire ine ndinaperekedwa kwa Inu;
kuchokera mʼmimba mwa amayi anga Inu mwakhala muli Mulungu wanga.
11 Musakhale kutali ndi ine,
pakuti mavuto ali pafupi
ndipo palibe wina wondipulumutsa.
12 Ngʼombe zazimuna zandizungulira;
ngʼombe zazimuna zamphamvu za ku Basani zandizinga.
13 Mikango yobangula pokadzula nyama,
yatsekula kwambiri pakamwa pawo kulimbana nane.
14 Ine ndatayika pansi ngati madzi
ndipo mafupa anga onse achoka mʼmalo mwake.
Mtima wanga wasanduka phula;
wasungunuka mʼkati mwanga.
15 Mphamvu zanga zauma ngati phale,
ndipo lilime langa lamamatira ku nsagwada;
mwandigoneka mʼfumbi la imfa.
16 Agalu andizungulira;
gulu la anthu oyipa landizinga.
Alasa manja ndi mapazi anga.
17 Ine nditha kuwerenga mafupa anga onse;
anthu amandiyangʼanitsitsa ndi kundidzuma.
18 Iwo agawana zovala zanga pakati pawo
ndi kuchita maere pa zovala zangazo.
19 Koma Inu Yehova, musakhale kutali;
Inu mphamvu yanga, bwerani msanga kuti mudzandithandize.
20 Pulumutsani moyo wanga ku lupanga,
moyo wanga wopambanawu ku mphamvu ya agalu.
21 Ndilanditseni mʼkamwa mwa mikango;
pulumutseni ku nyanga za njati.
22 Ine ndidzalengeza dzina lanu kwa abale anga;
ndidzakutamandani mu msonkhano.
23 Inu amene mumaopa Yehova mutamandeni!
Inu zidzukulu zonse za Yakobo, mulemekezeni!
Muopeni mwaulemu, inu zidzukulu zonse za Israeli!
24 Pakuti Iye sanapeputse kapena kunyoza
kuvutika kwa wosautsidwayo;
Iye sanabise nkhope yake kwa iye.
Koma anamvera kulira kwake kofuna thandizo.
25 Ndidzakutamandani pa msonkhano waukulu chifukwa cha zimene mwandichitira.
Ndidzakwaniritsa lonjezo langa pamaso pa amene amaopa Inu.
26 Osauka adzadya ndipo adzakhuta;
iwo amene amafunafuna Yehova adzamutamanda.
Mitima yanu ikhale ndi moyo mpaka muyaya!
27 Malekezero onse a dziko lapansi
adzakumbukira Yehova ndi kutembenukira kwa Iye,
ndipo mabanja a mitundu ya anthu
adzawerama pamaso pake,
28 pakuti ulamuliro ndi wake wa Yehova
ndipo Iye amalamulira anthu a mitundu yonse.
29 Anthu olemera onse a dziko lapansi adzachita phwando ndi kulambira;
onse amene amapita ku fumbi adzagwada pamaso pake;
iwo amene sangathe kudzisunga okha ndi moyo.
30 Zidzukulu zamʼtsogolo zidzamutumikira Iye;
mibado ya mʼtsogolo idzawuzidwa za Ambuye.
31 Iwo adzalengeza za chilungamo chake
kwa anthu amene pano sanabadwe
pakuti Iye wachita zimenezi.
Salimo la Davide.
23 Yehova ndiye mʼbusa wanga, sindidzasowa kanthu.
2 Amandigoneka pa msipu wobiriwira,
amanditsogolera ku madzi akumwa abwino,
3 amatsitsimutsa moyo wanga.
Amanditsogolera mʼnjira zachilungamo
chifukwa cha dzina lake.
4 Ngakhale ndiyende
mʼchigwa cha mdima wakuda bii,
sindidzaopa choyipa,
pakuti Inu muli ndi ine;
chibonga chanu ndi ndodo yanu
zimanditonthoza.
5 Mumandikonzera chakudya
adani anga akuona.
Mumadzoza mutu wanga ndi mafuta;
chikho changa chimasefukira.
6 Zoonadi, zokoma ndi chikondi chosasinthika zidzanditsata
masiku onse a moyo wanga,
ndipo ndidzakhala mʼNyumba ya Yehova
kwamuyaya.
Salimo la Davide.
24 Dziko lapansi ndi la Yehova ndi zonse zimene zili mʼmenemo,
dziko ndi onse amene amakhala mʼmenemo;
2 pakuti Iye ndiye anayika maziko ake pa nyanja
ndi kulikhazika pamwamba pa madzi.
3 Ndani angakwere phiri la Yehova?
Ndani angathe kuyima pa malo ake opatulika?
4 Iye amene ali ndi mʼmanja moyera ndi mtima woyera,
amene sapereka moyo wake kwa fano
kapena kulumbira mwachinyengo.
5 Iyeyo adzalandira madalitso kwa Yehova
ndipo Mulungu mpulumutsi wake adzagamula kuti alibe mlandu.
6 Umenewo ndiwo mʼbado wa amene amafunafuna Yehova;
amene amafunafuna nkhope yanu, Inu Mulungu wa Yakobo.
Sela
7 Tukulani mitu yanu inu zipata;
tsekukani, inu zitseko zakalekalenu,
kuti Mfumu yaulemerero ilowe.
8 Kodi Mfumu yaulemereroyo ndani?
Yehova Wamphamvuzonse,
Yehova ndiye wamphamvu pa nkhondo.
9 Tukulani mitu yanu, inu zipata;
tsekukani, inu zitseko zakalekalenu,
kuti Mfumu yaulemerero ilowe.
10 Kodi Mfumu yaulemereroyo ndani?
Yehova Wamphamvuzonse,
Iye ndiye Mfumu yaulemerero.
Sela
Salimo la Davide.
25 Kwa Inu Yehova, ndipereka moyo wanga.
2 Ndimadalira Inu Mulungu wanga.
Musalole kuti ndichite manyazi
kapena kuti adani anga andipambane.
3 Aliyense amene amayembekezera kwa Ambuye
sadzachititsidwa manyazi
koma achinyengo ndiwo adzachititsidwe manyazi
ndipo sadzakhala ndi chodzitetezera.
4 Ndidziwitseni njira zanu Inu Yehova,
phunzitseni mayendedwe anu;
5 tsogolereni mʼchoonadi chanu ndi kundiphunzitsa,
pakuti Inu ndinu Mulungu mpulumutsi wanga,
ndipo chiyembekezo changa chili mwa Inu tsiku lonse.
6 Kumbukirani Inu Yehova chifundo ndi chikondi chanu chachikulu,
pakuti ndi zakalekale.
7 Musakumbukire machimo a ubwana wanga
ndi makhalidwe anga owukira;
molingana ndi chikondi chanu ndikumbukireni ine,
pakuti Inu Yehova ndinu wabwino.
8 Yehova ndi wabwino ndi wolungama;
choncho Iye akulangiza ochimwa mʼnjira yake.
9 Amatsogolera odzichepetsa kuti achite zolungama
ndipo amawaphunzitsa njira zake.
10 Njira zonse za Yehova ndi zachikondi ndi zokhulupirika
kwa iwo amene amasunga zofuna za pangano lake.
11 Chifukwa cha dzina lanu, Inu Yehova,
khululukireni mphulupulu zanga, ngakhale kuti ndi zochuluka.
12 Tsono ndani munthu amene amaopa Yehova?
Yehova adzamulangiza njira yoti ayitsate.
13 Iye adzakhala pa ulemerero masiku ake onse,
ndipo zidzukulu zake zidzalandira dziko ngati cholowa chawo.
14 Yehova amawulula chinsinsi chake kwa iwo amene amamuopa;
amawulula pangano lake kwa iwowo.
15 Maso anga ali pa Yehova nthawi zonse,
pakuti ndi Iye yekha amene adzawonjola mapazi anga mu msampha.
16 Tembenukirani kwa ine ndipo mundikomere mtima,
pakuti ndili ndekhandekha ndipo ndikuzunzika.
17 Masautso a mu mtima mwanga achulukirachulukira;
masuleni ku zowawa zanga.
18 Penyani mazunzo anga ndi zovuta zanga
ndipo mufafanize machimo anga onse.
19 Onani mmene adani anga achulukira
ndi momwe chidani chawo ndi ine chakulira.
20 Tetezani moyo wanga ndi kundilanditsa;
musalole kuti ndichite manyazi,
pakuti ndimathawira kwa Inu.
21 Kukhulupirika ndi kulungama kwanga kunditeteze,
chifukwa chiyembekezo changa chili mwa Inu.
22 Wombolani Israeli Inu Mulungu,
ku mavuto ake onse!
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.