Beginning
Yuda ndi Tamara
38 Pa nthawi imeneyi, Yuda anasiyana ndi abale ake napita kukakhala ndi munthu wina wa ku Adulamu wotchedwa Hira. 2 Kumeneko, Yuda anaona mwana wamkazi wa munthu wina wa Chikanaani wotchedwa Suwa. Anamukwatira nagona naye malo amodzi. 3 Iye anatenga pathupi, nabala mwana wamwamuna amene anamutcha Eri. 4 Anatenganso pathupi nabala mwana wa mwamuna ndipo anamutcha Onani. 5 Anaberekanso mwana wina wamwamuna ndipo anamutcha Sela. Ameneyu anabadwa Yuda ali ku Kezibi.
6 Yuda anamupezera mkazi mwana wake woyamba uja Eri, ndipo dzina la mkaziyo linali Tamara. 7 Koma ntchito zoyipa za Eri, mwana wachisamba wa Yuda zinayipira Yehova. Choncho Mulungu anamulanga ndi imfa.
8 Pamenepo Yuda anati kwa Onani, “Kwatira mkazi wamasiye wa mʼbale wako. Ulowe chokolo kuti mʼbale wako akhale ndi mwana.” 9 Koma Onani anadziwa kuti mwanayo sadzakhala wake. Choncho nthawi zonse pamene amagona naye mkaziyo, ankatayira umuna pansi kuti asamuberekere mwana mʼbale wake. 10 Zimene ankachitazi zinayipira Yehova. Choncho anamulanganso ndi imfa.
11 Kenaka Yuda anati kwa mpongozi wake Tamara, “Bwererani ku nyumba ya abambo anu ndi kukhala kumeneko ngati wamasiye mpaka mwana wanga Sela atakula.” Ananena izi chifukwa ankaopa kuti Sela angafenso ngati abale ake aja. Choncho Tamara anapita kukakhala ku nyumba ya abambo ake.
12 Patapita nthawi yayitali, Batishua, mkazi wa Yuda anamwalira. Yuda atatha kulira maliro a mkazi wake, anapita, iyeyu pamodzi ndi bwenzi lake Hira, Mwadulamu uja, ku Timna kumene ankameta nkhosa zawo.
13 Tamara atamva kuti apongozi ake akupita ku Timna kukameta nkhosa, 14 iye anavula zovala zake za umasiye, nadziphimba nkhope ndi nsalu kuti asadziwike, ndipo anakhala pansi pa chipata cha ku Enaimu popita ku Timna. Tamara anachita izi chifukwa anaona kuti ngakhale Selayo anali atakula tsopano, iye sanaperekedwe kuti amulowe chokolo.
15 Yuda atamuona anangomuyesa mkazi wadama chabe, chifukwa anadziphimba nkhope. 16 Tsono anapita kwa mkaziyo pamphepete pa msewu paja nati, “Tabwera ndigone nawe.” Apa Yuda sankadziwa kuti mkazi uja anali mpongozi wake.
Ndiye mkazi uja anamufunsa Yuda nati, “Mudzandipatsa chiyani kuti ndigone nanu?”
17 Iye anati, “Ndidzakutumizira kamwana kambuzi ka mʼkhola mwanga.”
Mkaziyo anayankha kuti, “Chabwino, ndavomera, koma mungandipatse chikole mpaka mutanditumizira mbuziyo?”
18 Iye anati, “Ndikupatse chikole chanji?”
Mkaziyo anayankha, “Mundipatse mphete yanuyo, chingwe chanucho pamodzi ndi ndodo imene ili mʼdzanja lanulo.” Choncho anazipereka kwa iye nagona naye ndipo anatenga pathupi. 19 Kenaka Tamara anachoka, navula nsalu anadziphimba nayo ija, navalanso zovala zake za umasiye zija.
20 Tsono Yuda anatuma bwenzi lake Mwadulamu uja ndi kamwana kambuzi kaja kuti akapereke kwa mkazi wadama uja, ndi kuti akatero amubwezere chikole chake chija. Koma atafika sanamupezepo. 21 Anawafunsa anthu a komweko, “Kodi mkazi wadama uja amene ankakhala pambali pa msewu wa ku Enaimu, ali kuti?”
Iwo anayankha, “Sipanakhalepo mkazi wa dama aliyense pano.”
22 Choncho anabwerera kwa Yuda nati, “Sindinamupeze mkazi uja. Kuwonjeza apo, anthu a kumeneko amati, ‘Sipanakhalepo mkazi wadama pano.’ ”
23 Pamenepo Yuda anati, “Mulekeni atenge zinthuzo zikhale zake, kuopa kuti anthu angatiseke. Ine sindinalakwe, ndinamutumizira kamwana kambuzika, koma simunamupeze.”
24 Patapita miyezi itatu, Yuda anawuzidwa kuti, “Mpongozi wanu Tamara anachita zadama, ndipo zotsatira zake nʼzakuti ali ndi pathupi.”
Yuda anati, “Kamutulutseni ndipo mukamutenthe kuti afe!”
25 Akumutulutsa, iye anatuma mawu kwa apongozi ake. Anati, “Ndili ndi pathupi pa munthu amene ndi mwini wake wa zinthu izi. Taziyangʼanitsitsani, kodi mwini wa khoza, chingwe ndi ndodo yoyenderayi ndi yani?”
26 Yuda anazizindikira zinthuzo ndipo anati, “Uyu ndi wolungama kuposa ine, chifukwa sindinamupereke kwa mwana wanga Sela.” Ndipo Yuda sanagone nayenso.
27 Pamene Tamara nthawi inamukwanira yoti abeleke, mʼmimbamo munali mapasa. 28 Pamene ankabereka, mmodzi wa iwo anatulutsa dzanja lake. Choncho mzamba anatenga kawulusi kofiira nakamangirira pa mkono pa mwanayo nati, “Uyu ndiye anayamba kubadwa.” 29 Koma pamene anabweza mkonowo, mʼbale wake anabadwa ndipo mzamba anati, “Wachita kudziphotcholera wekha njira chonchi!” Ndipo anamutcha Perezi. 30 Pambuyo pake mʼbale wake amene anali ndi ulusi wofiira pa mkono wake uja anabadwa ndipo anapatsidwa dzina lakuti Zera.
Yosefe ndi Mkazi wa Potifara
39 Tsopano Yosefe anatengedwa kupita ku Igupto. Potifara Mwigupto amene anali mmodzi wa akuluakulu a Farao ndiponso mkulu wa asilikali olonda ku nyumba kwa Farao, anagula Yosefe kwa Aismaeli amene anapita naye kumeneko.
2 Koma Yehova anali ndi Yosefe ndipo zake zonse zimayenda bwino. Iye ankakhala mʼnyumba ya mbuye wake wa ku Igupto. 3 Mbuye wake anaona kuti Yehova anali naye Yosefe ndi kuti pa chilichonse chimene anachita Yehova ankaonetsetsa kuti achite bwino. 4 Potifara anakondwera ndi Yosefe chifukwa cha matumikiridwe ake. Choncho anamusandutsa woyangʼanira nyumba yake ndi zonse za mʼnyumba yake. 5 Kuchokera pa nthawi imene anamuyika kukhala woyangʼanira wa nyumbayo ndi zonse za mʼnyumbamo, Yehova anadalitsa nyumba ya Mwiguptoyo chifukwa cha Yosefe. Madalitso a Yehova anali pa chilichonse chimene Potifara anali nacho, za mʼnyumba komanso za ku munda. 6 Choncho anasiyira mʼmanja mwa Yosefe chilichonse chomwe anali nacho, kotero kuti samadandaula ndi chilichonse kupatula chakudya chimene ankadya.
Tsopano Yosefe anali wa thupi labwino ndi wokongola. 7 Patapita kanthawi, mkazi wa mbuye wake anayamba kusirira Yosefe nati, “Bwanji ugone nane!”
8 Koma iye anakana namuwuza kuti, “Inu mukuona kuti mbuye wanga sadandaula ndi kena kalikonse mʼnyumba muno, ndipo chawo chilichonse anachiyika mʼmanja mwanga. 9 Motero kuti palibe wina wamkulu kuposa ine mʼnyumba muno. Ndipo palibe chilichonse chimene mbuye wanga sanachipereke kwa ine kupatula inuyo, chifukwa ndinu mkazi wake. Tsono ndingachite bwanji choyipa choterechi ndi kuchimwira Mulungu?” 10 Ndipo ngakhale kuti iye anayankhula mawu omwewa ndi Yosefe tsiku ndi tsiku, Yosefe sanalole kugona naye ngakhale kukhala naye pafupi.
11 Tsiku lina Yosefe analowa mʼnyumbamo kukagwira ntchito zake, ndipo munalibe wina aliyense wantchito mʼnyumbamo. 12 Mkazi uja anamugwira mkanjo Yosefe nati, “Tiye ugone nane!” Koma Yosefe anasiya mkanjo wake mʼmanja mwa mkaziyo nathawira kunja kwa nyumba.
13 Pamene mkazi uja anaona kuti Yosefe wamusiyira mkanjo wake mʼmanja mwake nathawira kunja kwa nyumba, 14 iye anayitana antchito ake a mʼnyumba nati, “Taonani mwamuna wanga anabwera ndi Mhebri uyu mʼnyumba muno kuti adzagone nane. Iyeyu analowa ku chipinda kwanga kuti adzagone nane ndipo ine ndinakuwa kwambiri. 15 Atandimva ndikukuwa, anandisiyira mkanjo wakewu nʼkuthawira kunja.”
16 Tsono mkazi wa Potifara uja anasunga mkanjowo mpaka mbuye wake wa Yosefe atabwera ku nyumba. 17 Tsono anamuwuza nkhaniyi nati: “Wantchito Wachihebri amene munatibweretsera uja anabwera kuti adzagone nane. 18 Koma pamene ndinakuwa, iye anandisiyira mkanjo wake nathawira kunja.”
19 Mbuye wake wa Yosefe atamva nkhani imene mkazi wake anamuwuza kuti, “Ndi zimene anandichitira wantchito wanu,” anapsa mtima kwambiri. 20 Tsono iye anatenga Yosefe namuyika mʼndende mmene ankasungiramo amʼndende a mfumu.
Ndipo Yosefe anakhala mʼndendemo 21 koma Yehova anali naye, ndipo anamuonetsa kukoma mtima kwake, kotero kuti woyangʼanira ndende anakondwera ndi Yosefe. 22 Choncho woyangʼanira ndende uja anamuyika Yosefe kukhala woyangʼanira onse amene anayikidwa mʼndende. Ndiponso anamupatsa udindo woyangʼanira zonse zochitika mʼndendemo. 23 Woyangʼanira ndende uja sankayangʼaniranso china chilichonse chimene chinali mu ulamuliro wa Yosefe, chifukwa Yehova anali ndi Yosefe. Ndipo Yehova anaonetsetsa kuti chilichonse chimene Yosefe ankachita chimuyendere bwino.
Yosefe Amasulira Maloto a Amʼndende Anzake
40 Patapita nthawi, woperekera zakumwa ndi wopanga buledi a ku nyumba kwa mfumu ya ku Igupto analakwira mbuye wawoyo. 2 Farao anapsa mtima ndi akuluakulu awiriwa, 3 ndipo anakawatsekera mʼndende, nakawayika mʼmanja mwa mkulu wa asilikali olonda ku nyumba kwa mfumu kuja, mʼndende momwe Yosefe ankasungidwamo. 4 Mkulu wa alonda aja anawapereka mʼmanja mwa Yosefe, ndipo iye anawasamalira.
Iwo anakhala mʼndendemo kwa kanthawi. 5 Usiku wina, aliyense wa anthu awiriwa, wopereka zakumwa pamodzi ndi wopanga buledi wa ku nyumba ya mfumu ya ku Igupto aja, amene ankasungidwa mʼndende, analota maloto. Malotowo anali ndi tanthauzo lake.
6 Mmawa wake, Yosefe atabwera, anaona kuti nkhope zawo zinali zakugwa. 7 Choncho anafunsa akuluakulu a kwa Farao amene anali naye mʼndende muja kuti, “Bwanji nkhope zanu zili zachisoni lero?”
8 Iwo anayankha, “Tonse awiri talota maloto, koma palibe wotitanthauzira malotowo.”
Pamenepo Yosefe anawawuza kuti, “Ndi Mulungu yekha amene amapereka matanthauzo a maloto. Uzeni ine maloto anu.”
9 Choncho mkulu wa operekera zakumwa uja anamuwuza Yosefe maloto ake. Anati, “Mʼmaloto anga ndinaona mtengo wa mpesa, 10 unali ndi nthambi zitatu. Mpesawo utangophukira, unachita maluwa ndipo maphava ake anabereka mphesa zakupsa. 11 Chikho cha Farao chinali mʼmanja mwanga, ndipo ndinatenga mphesa, kupsinyira mu chikho cha Farao ndi kuchipereka mʼmanja mwake.”
12 Yosefe anati kwa iye, “Tanthauzo lake ndi ili: Nthambi zitatuzo ndi masiku atatu. 13 Pakangopita masiku atatu, Farao adzakutulutsa muno. Udzaperekera zakumwa kwa Farao monga momwe umachitira poyamba. 14 Koma zako zikakuyendera bwino, udzandikumbukire ndi kundikomera mtima. Chonde ukandipepesere kwa Farao kuti anditulutse muno. 15 Popezatu ine anangochita mondiba kubwera nane kuno kuchokera ku dziko la Ahebri, ndipo ngakhale kunoko, ine sindinalakwe kali konse kuti ndizipezeka mʼdzenje muno.”
16 Mkulu wa opanga buledi ataona kuti Yosefe wapereka tanthauzo labwino, anati kwa Yosefe, “Inenso ndinalota nditasenza nsengwa zitatu za buledi. 17 Mu nsengwa yapamwamba munali zakudya zamitundumitundu za Farao, koma mbalame zimadya zakudyazo.”
18 Yosefe anati, “Tanthauzo lake ndi ili: nsengwa zitatuzo ndi masiku atatu. 19 Pakangotha masiku atatu Farao adzakutulutsa muno koma adzakupachika. Ndipo mbalame zidzadya mnofu wako.”
20 Tsono tsiku lachitatulo linali lokumbukira kubadwa kwa Farao, ndipo anawakonzera phwando akuluakulu ake onse. Anatulutsa mʼndende mkulu wa operekera zakumwa ndi mkulu wa ophika buledi, ndipo anawayimiritsa pamaso pa nduna zake. 21 Tsono Farao anamubwezera mkulu wa operekera zakumwa uja pa udindo wake, kotero kuti anayamba kuperekeranso zakumwa kwa Farao, 22 koma mkulu wa ophika buledi anamupachika, mofanana ndi mmene Yosefe anatanthauzira maloto.
23 Koma mkulu wa operekera zakumwa uja sanamukumbukire Yosefe ndipo anamuyiwaliratu.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.