Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Beginning

Read the Bible from start to finish, from Genesis to Revelation.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Ahebri 7-10

Za Melikizedeki Mkulu wa Ansembe

Melikizedeki ameneyu anali mfumu ya ku Salemu, ndiponso wansembe wa Mulungu Wammwambamwamba. Anakumana ndi Abrahamu pamene ankabwerera kuchokera ku nkhondo atagonjetsa mafumu aja, Melikizedeki anakumana naye namudalitsa. Ndipo Abrahamu anamupatsa chakhumi cha zonse anafunkha. Choyamba dzina la Melikizedeki likutanthauza, “Mfumu ya chilungamo,” kenakanso, “Mfumu ya Salemu,” kutanthauza, “Mfumu ya mtendere.” Alibe abambo kapena mayi, alibe chiyambi kapena chitsiriziro cha moyo wake. Iye ali ngati Mwana wa Mulungu ndipo akupitirira kukhala wansembe wamuyaya.

Mukuona tsono kuti munthuyo anali wamkulu ndithu, pakuti Abrahamu kholo lathu anamupatsa chakhumi cha zimene anafunkha. Tsono lamulo likuti, ana a Levi amene amakhala ansembe azilandira chakhumi kuchokera kwa Aisraeli, abale awo ngakhale kuti abale awowo ndi ochokera kwa Abrahamu. Melikizedeki sanali wochokera kwa Levi, komabe analandira chakhumi kuchokera kwa Abrahamu nadalitsa Abrahamuyo amene analandira malonjezo a Mulungu. Mosakayika konse, munthu amene amadalitsa ndi wamkulu kuposa amene akudalitsidwayo. Ansembe amene amalandira chakhumi amafa, choncho Melikizedeki ndi wamkulu kuwaposa iwo chifukwa Malemba amamuchitira umboni kuti ndi wamoyo. Wina angathe kunena kuti Levi, amene amalandira chakhumi, anapereka chakhumicho kudzera mwa Abrahamu, 10 chifukwa pamene Melikizedeki anakumana ndi Abrahamu nʼkuti Levi ali mʼthupi la kholo lake.

Yesu Wofanana ndi Melikizedeki

11 Kukanatheka kukhala wangwiro mwa unsembe wa Levi, pakuti Malamulo anapatsidwa kwa anthu mwa unsembe wa Levi, nʼchifukwa chiyani panafunikanso wansembe wina kuti abwere, wofanana ndi Melikizedeki, osati Aaroni? 12 Pakuti pamene unsembe usintha, malamulonso amayenera kusintha. 13 Ambuye athu Yesu, amene mawuwa akunena za Iye, anali wa fuko lina, ndipo palibe aliyense wochokera fuko lakelo amene anatumikira pa guwa lansembe. 14 Pakuti nʼzodziwika bwino kuti Ambuye athu anachokera fuko la Yuda. Kunena za fuko limeneli, Mose sananenepo kanthu za ansembe. 15 Ndipo zimene tanenazi zimamveka bwino ngati tiona kuti pafika wansembe wina wofanana ndi Melikizedeki. 16 Yesu sanakhale wansembe chifukwa cha malamulo monga mwa mabadwidwe ake koma mwamphamvu ya moyo wosatha. 17 Pakuti Mulungu anamuchitira umboni kuti,

“Iwe ndi wansembe wamuyaya,
    monga mwa dongosolo la unsembe wa Melikizedeki.”

18 Choncho lamulo loyamba lachotsedwa chifukwa linali lofowoka ndi lopanda phindu. 19 Tsono Malamulo sangathe kusandutsa chilichonse kukhala changwiro, koma mʼmalo mwake mwalowa chiyembekezo chabwino, chimenechi timayandikira nacho kwa Mulungu.

20 Izi sizinachitiketu wopanda lumbiro. Ena ankakhala ansembe popanda lumbiro. 21 Koma Yesu ankakhala wansembe ndi lumbiro pamene Mulungu anati,

“Ambuye analumbira
    ndipo sangasinthe maganizo ake,
‘Iwe ndi wansembe wamuyaya.’ ”

22 Chifukwa cha lumbiroli, Yesu wakhala Nkhoswe ya Pangano lopambana.

23 Tsono ansembe akale aja analipo ambiri, popeza imfa imawalepheretsa kupitiriza ntchitoyi. 24 Koma Yesu popeza ndi wamuyaya, unsembe wake ndi wosatha. 25 Chifukwa chake Iye amapulumutsa kwathunthu amene amabwera kwa Mulungu kudzera mwa Iyeyo. Iye ali ndi moyo nthawi zonse kuti adziwapempherera iwo.

26 Uyu ndi Mkulu wa ansembe amene tikumufuna chifukwa ndi woyera, wopanda choyipa kapena chodetsa chilichonse, wosiyana ndi anthu ochimwa, ndiponso wokwezedwa kuposa zonse zakumwambaku. 27 Kusiyana ndi akulu a ansembe ena aja, Yesu sanafunike kupereka nsembe tsiku ndi tsiku poyamba chifukwa cha machimo ake, ndipo kenaka chifukwa cha machimo a anthu ena. Iye anadzipereka nsembe chifukwa cha machimo awo kamodzi kokha pamene anadzipereka yekha. 28 Pakuti lamulo limasankha anthu amene ndi ofowoka kukhala akulu a ansembe; koma lumbiro, lomwe linabwera pambuyo pa lamulo, linasankha Mwana, amene anapangidwa kukhala wangwiro kwamuyaya.

Mkulu wa Ansembe wa Pangano Latsopano

Fundo yayikulu pa zimene tikunenazi ndi iyi: Tili naye ife Mkulu wa ansembe, amene anakhala ku dzanja lamanja la mpando waufumu wa Mulungu Waulemerero kumwamba. Ndipo akutumikira mʼmalo opatulika, mu Tenti yeniyeni yoyikidwa ndi Ambuye, osati ndi munthu.

Mkulu wa ansembe aliyense amasankhidwa kuti azipereka mphatso ndi nsembe kwa Mulungu, ndipo kunali koyenera kuti wansembe wathunso akhale nʼkanthu kopereka. Ngati iye akanakhala pa dziko lapansi, sakanakhala wansembe pakuti alipo kale anthu amene amapereka mphatso zolembedwa mʼMalamulo. Iwo amatumikira pamalo opatulika amene ndi chithunzi ndi chifanizo cha zimene zili kumwamba. Ichi ndi chifukwa chake Mose anachenjezedwa pamene anali pafupi kumanga Tenti: “Uwonetsetse kuti wapanga zonse monga momwe ndikukuonetsera pa phiri pano.” Koma Yesu analandira utumiki wopambana kuposa wawo monga Iyenso ali Nkhoswe ya pangano lopambana kuposa lakale lija, chifukwa pangano latsopano lakhazikika pa malonjezano opambana kwambiri.

Ngati pangano loyamba lija likanakhala langwiro, sipakanafunikanso lina mʼmalo mwake. Koma Mulungu anapeza zolakwika pakati pa anthu ndipo anati,

“Masiku akubwera,” akutero Yehova,
    “pamene ndidzachita pangano latsopano
ndi Aisraeli
    ndiponso nyumba ya Yuda.
Silidzakhala ngati pangano
    limene ndinachita ndi makolo awo,
pamene ndinawagwira padzanja
    nʼkuwatulutsa ku Igupto
chifukwa iwo sanasunge pangano langa lija
    ndipo Ine sindinawasamalire,
            akutero Ambuye.
10 Tsono ili ndi pangano ndidzapangane ndi nyumba ya Israeli:
    Atapita masiku amenewa, akutero Ambuye,
Ine ndidzayika malamulo anga mʼmaganizo mwawo,
    ndi kulemba mʼmitima mwawo.
Ine ndidzakhala Mulungu wawo,
    ndipo iwo adzakhala anthu anga.
11 Sipadzafunikanso wina kuti aphunzitse mnzake,
    kapena munthu kuphunzitsa mʼbale wake, kunena kuti, udziwe Ambuye
chifukwa onse adzandidziwa,
    kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu.
12 Pakuti Ine ndidzawakhululukira zoyipa zawo,
    ndipo sindidzakumbukiranso machimo awo.”

13 Ponena kuti, pangano “latsopano” Mulungu wapanga pangano loyamba lija kukhala lotha ntchito, ndipo chilichonse chimene chayamba kutha ntchito ndi kukalamba, chili pafupi kuchokeratu.

Kupembedza mʼTenti ya Dziko Lapansi

Pangano loyamba lija linali ndi malamulo okhudza chipembedzo, ndi malo opembedzeramo omangidwa ndi anthu. Anthu ankamanga chihema. Mʼchipinda choyamba munali choyikapo nyale, tebulo ndi buledi woperekedwa kwa Mulungu. Chipinda chimenechi chinkatchedwa Malo Opatulika. Kuseri kwa chinsalu chotchinga chachiwiri kunkatchedwa Malo Opatulika kwambiri. Mʼmenemo munali guwa lansembe lagolide lofukizirapo lubani. Munalinso Bokosi la Chipangano lokutidwa ndi golide. Mʼbokosimo munali mʼphika wagolide mʼmene ankasungiramo mana ndi ndodo ya Aaroni imene inaphuka ija, ndiponso miyala ya pangano. Pamwamba pa bokosilo panali zifanizo za angelo otchedwa akerubi aulemerero, ataphimba chivundikiro cha bokosilo chimene chinali malo okhululukirapo machimo. Koma nʼzosatheka tsopano kufotokoza zinthu mwatsatanetsatane.

Zinthu zonsezi zitakonzedwa, ansembe ankalowamo mʼchipinda choyamba chija nthawi ndi nthawi kumatumikiramo. Koma Mkulu wa ansembe yekha ndiye ankalowa chipinda chachiwiri chija kamodzi kokha pa chaka. Iye sankalowamo wopanda magazi. Magaziwo ankapereka nsembe kwa Mulungu chifukwa cha iye mwini ndiponso chifukwa cha machimo a anthu amene ankachita mosazindikira. Mwa njira imeneyi Mzimu Woyera ankaonetsa kuti njira yolowera ku malo opatulika inali isanaonetsedwe pamene Chihema choyamba chinali chilipo. Zimenezi nʼzofanizira chabe, ndipo zinkalozera nthawi ino, kusonyeza kuti mphatso ndi nsembe zimene zinkaperekedwa sizinkachotsa chikumbumtima cha wopembedzayo. 10 Inali nkhani ya zakudya, ya zakumwa ndi ya miyambo yosiyanasiyana ya masambidwe. Anali malamulo akunja kokha mpaka pa nthawi imene anakonzanso zonse mwatsopano.

Magazi a Yesu

11 Koma Khristu atafika monga Mkulu wa ansembe wa zinthu zokoma zimene zilipo tsopano, Iye analowa mʼChihema chachikulu ndiponso changwiro chimene sichinamangidwe ndi munthu, ndiye kuti sichili pansi pano. 12 Iye sanalowemo ndi magazi ambuzi yayimuna, ana angʼombe amphongo, koma analowa Malo Opatulika kamodzi kokha ndi magazi ake, atatikonzera chipulumutso chosatha. 13 Ngati magazi ambuzi yayimuna, angʼombe yayimuna ndi phulusa la mwana wangʼombe wamkazi zimati zikawazidwa pa odetsedwa zimawayeretsa kotero kuti amakhala oyeretsedwa ku thupi, 14 nʼkoposa kotani magazi a Khristu, amene mwa Mzimu wamuyaya anadzipereka yekha kwa Mulungu kukhala nsembe yopanda chilema. Iye adzayeretsa chikumbumtima chathu pochotsa ntchito za imfa, kuti ife titumikire Mulungu wamoyo.

15 Pa chifukwa chimenechi Khristu ndi mʼkhalapakati wa pangano latsopano, kuti iwo amene anayitanidwa alandire chuma chamuyaya, pakuti Iye tsopano anafa ngati dipo lomasula iwo ku machimo amene anachita ali pansi pa pangano loyamba lija.

16 Ngati munthu alemba pangano losiyira ena chuma, pafunika kutsimikiza kuti wolemba panganolo wamwaliradi, 17 chifukwa pangano lotere limakhala ndi mphamvu ngati wolembayo wamwalira. Siligwira ntchito pamene wolembayo ali ndi moyo. 18 Nʼchifukwa chake pangano loyamba lija silinachitike popanda kukhetsa magazi. 19 Mose atawawuza anthu onse malamulo, anatenga magazi a ana angʼombe amphongo ndi ambuzi yayimuna pamodzi ndi madzi, ubweya wofiira ndiponso chitsamba chotchedwa hisope, ndi kuwaza pa buku ndi anthu onse. 20 Iye anati, “Awa ndi magazi a pangano limene Mulungu wakulamulirani kuti mulisunge.” 21 Momwemonso Mose anawaza magazi pa Chihema chija ndiponso pa zipangizo zonse zogwiritsa ntchito pa chipembedzo. 22 Monga mwa malamulo titha kunena kuti, pafupifupi zinthu zonse zimayeretsedwa ndi magazi ndipo popanda kukhetsa magazi palibe kukhululukidwa machimo.

23 Tsono panafunika kuti zinthu zingofanizira zenizeni za kumwamba, ziyeretsedwe ndi nsembe zimenezi, koma zinthu za kumwamba zenizenizo kuti ziyeretsedwe panafunika nsembe zina zoposa zimenezo. 24 Pakuti Khristu sanalowe mʼmalo opatulika omangidwa ndi anthu amene anali chifaniziro cha malo enieniwo. Iye analowa kumwamba kwenikweniko kuti azionekera pamaso pa Mulungu chifukwa cha ife. 25 Iye sanalowe kumwamba kuti azikadziperekanso nsembe kachiwiri monga momwe mkulu wa ansembe ankachitira chaka ndi chaka ku Malo Opatulika kwambiri ndi magazi amene sanali ake. 26 Zikanatero bwenzi Khristu atamva zowawa kambirimbiri chilengedwere cha dziko lapansi. Koma tsopano anaoneka kamodzi kokha chifukwa cha onse pa nthawi yotsiriza kuti achotse tchimo podzipereka yekha nsembe. 27 Popeza kunayikika kwa munthu kufa kamodzi ndipo kenaka kuweruzidwa, 28 momwemonso Khristu anadzipereka nsembe kamodzi kokha kuchotsa machimo a anthu ambiri. Ndipo Iye adzaonekanso kachiwiri, osati kudzachotsa tchimo, koma kudzapereka chipulumutso kwa amene akumudikira.

Yesu Nsembe ya Anthu Onse

10 Malamulo ndi chithunzithunzi cha zinthu zabwino zimene zikubwera, osati madalitso enieniwo. Pa chifukwa chimenechi sizingatheke konse kuti nsembe zimodzimodzi, zoperekedwa kawirikawiri, kosalekeza ndi chaka ndi chaka, kuti nʼkusandutsa angwiro amene amabwera kudzapembedza. Ngati zikanamatero iwowo akanasiya kupereka nsembezo. Pakuti opembedzawo akanamayeretsedwa kamodzi kokha, sibwenzi chikumbumtima chawo chikuwatsutsabe chifukwa cha machimo awo. Koma nsembezo zimawakumbutsa anthuwo machimo awo chaka ndi chaka. Chifukwa nʼkosatheka kuti magazi angʼombe yayimuna ndi mbuzi yayimuna achotse machimo.

Nʼchifukwa chake Khristu atabwera pa dziko lapansi anati,

“Simunafune nsembe kapena zopereka,
    koma thupi munandikonzera.
Simunakondwere nazo nsembe zopsereza
    ndi nsembe zopereka chifukwa cha tchimo.
Tsono, Ine ndinati, ‘Ndili pano Ine,
    Inu Mulungu, ndabwera kudzachita zimene mukufuna monga zinalembedwa mʼMalemba.’ ”

Poyamba Iye anati, “Nsembe kapena zopereka zopsereza ndi nsembe zopereka chifukwa cha tchimo, Inu simunazifune kapena kukondwera nazo.” Ngakhale kuti Malamulo ndiye amanena kuti ziperekedwe. Pamenepo Iye anati, “Ndili pano Ine, ndabwera kudzachita zimene mukufuna.” Khristu anachotsa nsembe zoyamba zija kuti mʼmalo mwake ayikemo nsembe za mtundu wachiwiri. 10 Chifukwa chakuti Yesu Khristu anachita zimene Mulungu anafuna kuti achite, ndife oyeretsedwa ndi nsembe ya thupi lake, limene analipereka kamodzi kokha.

11 Wansembe aliyense amayimirira tsiku ndi tsiku nʼkutumikira, ndipo amapereka nsembe imodzimodzi mobwerezabwereza, nsembe zimene sizingathe kuchotsa machimo. 12 Koma pamene wansembe uyu anapereka kamodzi kokha nsembe imodzi yokha chifukwa cha machimo, Iye anakhala pansi ku dzanja lamanja la Mulungu. 13 Kumeneko akudikira tsono kuti Mulungu asandutse adani ake kukhala chopondapo mapazi ake. 14 Chifukwa cha nsembe imodzi Iye anasandutsa angwiro kwamuyaya iwo amene akuwayeretsa.

15 Mzimu Woyera nayenso akuchitira umboni za zimenezi kwa ife. Poyamba Iye anati,

16 “Ili ndi pangano limene ndidzachita nawo
    atapita masiku amenewo,” akutero Yehova.
“Ndidzayika malamulo anga mʼmitima mwawo,
    ndipo ndidzawalemba mʼmaganizo mwawo.”

17 Ndipo akutinso:

“Sindidzakumbukiranso konse
    machimo awo ndi zolakwa zawo.”

18 Ndipo pamene machimo akhululukidwa, sipafunikanso nsembe yoperekedwa chifukwa cha machimowo.

Kulimbika Mtima ndi Kupirira pa Chikhulupiriro

19 Ndipo tsono abale, molimba mtima timalowa mʼMalo Opatulika kwambiri chifukwa cha magazi a Yesu. 20 Iye anatitsekulira njira yatsopano ndi yamoyo kudutsa chinsalu chotchinga, chimene ndi thupi lake. 21 Ndiponso tili ndi wansembe wamkulu woyangʼanira nyumba ya Mulungu. 22 Tsono tiyeni tiyandikire kwa Mulungu ndi mtima woona ndi wodzaza ndi chikhulupiriro. Popeza mitima yathu yayeretsedwa, ndi yopanda chikumbumtima chotitsutsa, ndiponso matupi athu asambitsidwa ndi madzi woyera. 23 Tiyeni tigwiritsitse mosagwedezeka zimene timaziyembekezera ndi kuzivomereza, pakuti amene anatilonjezayo ndi wokhulupirika. 24 Tiziganizira mmene tingalimbikitsirane wina ndi mnzake pokondana ndi kuchita ntchito zabwino. 25 Tiyeni tisaleke kusonkhana kwathu pamodzi monga mmene ena amachitira, koma tizilimbikitsana makamaka poona kuti tsiku la Ambuye layandikira.

26 Ngati ife tipitirira kuchimwa mwadala pamene tikudziwa choona, palibenso nsembe ina imene ingaperekedwe chifukwa cha machimo athuwo. 27 Koma kumangodikira kokha ndi mantha chiweruzo ndiponso moto woopsa umene udzawononga adani a Mulungu 28 Aliyense amene amakana malamulo a Mose amaphedwa popanda nʼchifundo chomwe, malingana pali mboni ziwiri kapena zitatu. 29 Koposa kotani nanga ululu wachilango chimene adzalandire munthu amene amapeputsa Mwana wa Mulungu, amene amayesa magazi a pangano, amene anamuyeretsa, kukhala chinthu chodetsedwa, ndi kunyoza Mzimu wachisomo? 30 Pakuti timadziwa amene anati, “Kubwezera chilango nʼkwanga; ndidzawalanga ndine.” Iye anatinso, “Ambuye adzaweruza anthu ake.” 31 Nʼchinthu choopsa kugwa mʼmanja a Mulungu wamoyo.

32 Kumbukirani masiku akale aja mutangowunikiridwa chatsopano, pa nthawi imeneyi munapirira zowawa zambiri. 33 Nthawi zina ankakunyozani pagulu ndi kukuzunzani. Nthawi zina munkamva zowawa pamodzi ndi amene ankasautsidwa chotere. 34 Munkawamvera chisoni amene anali mʼndende ndiponso munkalola mokondwera kuti akulandeni katundu wanu chifukwa munkadziwa kuti muli nacho chuma choposa ndi chosatha.

35 Tsono musataye kulimbika mtima kwanuko pakuti mudzalandira nako mphotho yayikulu. 36 Nʼkofunika kuti mupirire kuti pamene muchita chifuniro cha Mulungu mudzalandire zimene Iye analonjeza. 37 Pakuti nʼkanthawi kochepa chabe,

Iye amene akubwera adzabwera ndipo sadzachedwa ayi.
38 Koma wolungama wangayo adzakhala ndi moyo mwachikhulupiriro.
    Ndipo ngati iye abwerera mʼmbuyo chifukwa cha mantha,
    Ine sindidzakondwera naye.

39 Koma ife sindife amodzi a iwo obwerera mʼmbuyo mwa mantha ndi owonongedwa, koma ndife amodzi a amene akukhulupirira ndi wopulumutsidwa.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.