Beginning
Mulungu ndi Mafano
10 Inu Aisraeli, imvani zimene Yehova akunena. 2 Yehova akuti,
“Musatsatire makhalidwe a anthu a mitundu ina
kapena kuchita mantha ndi zizindikiro zamlengalenga,
ngakhale anthu a mitundu ina amachita nazo mantha.
3 Pakuti miyambo ya mitundu inayo ndiyachabechabe.
Iwo amakadula mtengo ku nkhalango
ndipo mmisiri amawusema ndi sompho.
4 Amakongoletsa chosemacho ndi siliva ndi golide;
kenaka amachikhomerera ndi misomali
kuti chisagwedezeke.
5 Mafano awo ali ngati mtengo wakanjedza woopsezera mbalame mʼmunda wa minkhaka.
Mafanowo sangathe nʼkuyankhula komwe
ndipo ayenera kunyamulidwa
popeza sangathe nʼkuyenda komwe.
Musachite nawo mantha
popeza sangathe kukuchitani choyipa
ndiponso alibe mphamvu yochitira chabwino chilichonse.”
6 Palibe wofanana nanu, Inu Yehova;
Inu ndinu wamkulu,
ndipo dzina lanu lili ndi mphamvu yayikulu.
7 Ndani amene angaleke kukuopani,
inu Mfumu ya mitundu ya anthu?
Chimenechi ndicho chokuyenerani.
Pakati pa anthu anzeru onse komanso mafumu onse
a mitundu ya anthu,
palibe wina wofanana nanu.
8 Onsewo ndi opusa ndi opanda nzeru;
malangizo awo amawatenga kuchokera kwa mafano achabechabe opanga ndi mitengo.
9 Siliva wosula amabwera naye kuchokera ku Tarisisi
ndipo golide amachokera naye ku Ufazi.
Mafanowo ndi ntchito ya anthu aluso ndi odziwa kuzokota golide.
Tsono mafanowo amawaveka zovala za mtundu wamtambo ndi pepo.
Yonseyo ndi ntchito ya anthu a luso.
10 Koma Yehova ndiye Mulungu woona;
Iyeyo ndiye Mulungu wamoyo, Mfumu yamuyaya.
Akakwiya, dziko limagwedezeka;
anthu a mitundu ina sangathe kupirira ukali wakewo.
11 “Awuze anthu awa kuti, ‘Milungu iyi, imene sinalenge dziko lakumwamba ndi dziko lapansi, idzawonongeka pa dziko lapansi ndi pansi pa thambo.’ ”
12 Koma Mulungu analenga dziko lapansi ndi mphamvu zake;
Iye anapanga dziko lonse ndi nzeru zake
ndipo anayala thambo mwaluso lake.
13 Iye akayankhula, kumamveka mkokomo wamadzi akumwamba;
Iyeyo amabweretsa mitambo kuchokera ku malekezero a dziko lapansi.
Amabweretsa mphenzi pamodzi ndi mvula
ndi kutulutsa mphepo yamkuntho kumalo kumene osungirako.
14 Anthu onse ndi opusa ndiponso opanda nzeru;
mmisiri aliyense wosula golide akuchita manyazi ndi mafano ake.
Mafano akewo ndi abodza;
alibe moyo mʼkati mwawo.
15 Mafanowo ndi achabechabe, zinthu zosekedwa nazo.
Pamene anthuwo azidzaweruzidwa, mafanowo adzawonongedwa.
16 Koma Yehova amene ndi Cholowa cha Yakobo sali ngati mafanowo.
Iyeyu ndi Mlengi wa zinthu zonse
kuphatikizapo Israeli, mtundu umene anawusankha kuti ukhale anthu ake.
Dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse.
Chiwonongeko Chikubwera
17 Sonkhanitsani katundu wanu,
inu amene mukukhala mʼlinga la ankhondo.
18 Pakuti Yehova akuti,
“Tsopano Ine ndidzachotsa anthu onse
amene akukhala mʼdziko lino;
adzakhala pa mavuto
mpaka adzamvetsa.”
19 Aliyense ankangoti, “Mayo ine, chifukwa cha kupweteka kwanga!
Chilonda changa nʼchachikulu!”
Koma ine ndinkaganiza kuti, “Ndithu, ili ndi vuto langa basi,
choncho ndingolipirira.”
20 Tenti yanga yawonongeka,
zingwe zake zonse zaduka.
Ana anga andisiya ndipo kulibenso.
Palibenso amene adzandimangire tenti,
kapena kufunyulula nsalu yake.
21 Abusa ndi opusa
ndipo sanapemphe nzeru kwa Yehova;
choncho palibe chimene anapindula
ndipo nkhosa zawo zonse zabalalika.
22 Tamvani! kukubwera mphekesera,
phokoso lalikulu la gulu la a ankhondo likumveka kuchokera kumpoto!
Lidzasandutsa bwinja mizinda ya ku Yuda,
malo okhala nkhandwe.
Pemphero la Yeremiya
23 Inu Yehova, ndikudziwa kuti moyo umene munthu ali nawo si wake;
munthuyo sangathe kuwongolera mayendedwe ake.
24 Inu Yehova, langizeni, komatu mwachilungamo,
osati ndi mkwiyo wanu,
mungandiwononge kotheratu.
25 Tsanulirani ukali wanu pa mitundu ya anthu amene sakudziwani,
ndiye kuti mitundu ya anthu amene satama pa dzina lanu mopemba.
Iwo aja anasakaza Yakobo;
amusakaza kotheratu
ndipo awononga dziko lake.
Pangano Liphwanyidwa
11 Yehova anayankhula ndi Yeremiya kuti, 2 “Imvani mawu a pangano ili, ndipo uwawuze anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu. 3 Awuze kuti Yehova, Mulungu wa Israeli akuti ‘adzakhala wotembereredwa munthu amene samvera mawu a pangano ili. 4 Awa anali mawu amene ndinalamulira makolo anu nditawatulutsa mu Igupto, kuchoka mʼngʼanjo yamoto.’ Ine ndinati, ‘Mverani Ine ndi kuchita chilichonse chimene ndakulamulirani. Mukatero mudzakhala anthu anga ndi Ine ndidzakhala Mulungu wanu. 5 Tsono Ine ndidzakwaniritsa lumbiro lomwe ndinalumbira kwa makolo anu kuti ndidzawapatsa dziko loyenda mkaka ndi uchi,’ dziko lomwe inu lero mukukhalamo.”
Tsono Ine ndinayankha kuti, “Ameni, Yehova.”
6 Yehova anandiwuza kuti, “Lengeza mawu onsewa mʼmizinda yonse ya ku Yuda ndi mʼmisewu ya mu Yerusalemu: ‘Mverani mawu a pangano ili ndi kuzitsatira. 7 Kuyambira nthawi imene ndinatulutsa makolo anu ku Igupto mpaka lero, ndakhala ndi kuwachenjeza kawirikawiri kuti, ‘Mverani Ine.’ 8 Koma sanamvere kapena kulabadirako. Aliyense anawumirira kuchita zoyipa za mʼmitima yawo. Ngakhale ndinawalamulira kuti asunge pangano langa koma iwo sanasunge. Choncho ndinawalanga monga ndinaneneramo.’ ”
9 Kenaka Yehova anandiwuza kuti, “Anthu a ku Yuda ndi ku Yerusalemu andiwukira. 10 Abwereranso ku machimo a makolo awo, amene anakana kumvera mawu anga. Akutsata milungu ina ndi kumayitumikira. Aisraeli ndi Ayuda aphwanya pangano limene ndinachita ndi makolo awo. 11 Choncho Yehova akuti, ‘Ndidzawagwetsera mavuto amene sadzatha kuwalewa. Ngakhale adzandilirire, sindidzawamvera. 12 Anthu a mʼmizinda ya Yuda ndi anthu a ku Yerusalemu adzapita ndi kukalirira milungu imene ankayifukizira lubani, koma milunguyo sidzawathandiza ndi pangʼono pomwe mavuto akadzafika. 13 Iwe Yuda, uli ndi milungu yochuluka ngati chiwerengero cha mizinda yako; chiwerengero cha maguwa ansembe amene umafukizirapo lubani kwa Baala chili ngati misewu ya mu Yerusalemu.’
14 “Tsono iwe Yeremiya usawapempherere anthu amenewa ngakhale kuwadandaulira kapena kuwapepesera, chifukwa sindidzawamvera akadzandiyitana pa nthawi ya mavuto awo.
15 “Kodi anthu anga okondedwa akudzachita chiyani mʼNyumba yanga?
Kodi suja iwowa amachita zoyipa zambiri?
Kodi mungathe kupulumuka,
tsoka osakugwerani
chifukwa cha nsembe zanuzo?”
16 Kale Yehova ankakutchani mtengo wa olivi wa masamba obiriwira,
wokhala ndi zipatso zokongola.
Koma tsopano adzawutentha
ndi mkuntho wamkokomo
ndipo nthambi zake zidzapserera.
17 Yehova Wamphamvuzonse, amene anakudzalani, walamula kuti mavuto akugwereni. Inu a banja la Yuda ndi a banja la Israeli munachitira Yehova zoyipa ndi kumukwiyitsa pamene munkapereka nsembe zanu kwa Baala.
Amuchitira Chiwembu Yeremiya
18 Yehova anandiwululira ndipo ndinadziwa. Iye anatsekula maso anga kuti ndione chiwembu chawocho. 19 Ndinali ngati mwana wankhosa wofatsa amene akupita naye kukamupha; sindinkadziwa kuti chiwembu chimene ankakonzekeracho chinkaloza ine. Iwo amati:
“Tiyeni timuphe
munthu ameneyu
kuti dzina lake lisadzakumbukiridwenso.”
20 Koma, Inu Yehova Wamphamvuzonse, Inu amene mumaweruza molungama
ndi kuyesa mitima ndi maganizo,
lolani kuti ine ndione kuti mwawalipsira,
pakuti mlandu wanga ndawupereka mʼmanja mwanu.
21 “Nʼchifukwa chake Yehova akunena za anthu a ku Anatoti amene akufuna kuwononga moyo wako namanena kuti, ‘Usanenere mʼdzina la Yehova, ukatero ife tidzakupha ndi manja athu,’ 22 koma Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Ine ndidzawalanga. Achinyamata awo adzaphedwa ndi lupanga, ana awo aamuna ndi aakazi adzafa ndi njala. 23 Sipadzakhala otsala ndi mmodzi yemwe, chifukwa ndidzalanga anthu a ku Anatoti chikadzafika chaka chawo cha chilango.’ ”
Madandawulo a Yeremiya
12 Yehova, Inu mumakhala wokhoza nthawi zonse
ndikati nditsutsane nanu.
Komabe ndikufuna kuyankhula nanu za mlandu wanga.
Chifukwa chiyani anthu oyipa zinthu zimawayendera bwino?
Chifukwa chiyani anthu achinyengo amakhala pabwino?
2 Inu munawadzala ndipo anamera mizu;
amakula ndi kubereka zipatso.
Dzina lanu limakhala pakamwa pawo nthawi zonse,
koma mitima yawo imakhala kutali ndi Inu.
3 Koma Inu Yehova, ine mumandidziwa;
mumandiona ndipo mumayesa zolingalira zanga.
Akokeni anthu oyipawo ngati nkhosa zokaphedwa!
Ayikeni padera mpaka tsiku loti akaphedwe!
4 Kodi dziko lidzakhala likulirabe mpaka liti
ndipo udzu mʼmunda uliwonse udzakhalabe ofota mpaka liti?
Nyama ndi mbalame kulibiretu
chifukwa anthu amene amakhalamo ndi oyipa.
Iwo amati:
“Yehova sangathe kuona ntchito zathu.”
Yankho la Mulungu
5 Yehova anayankha kuti, “Ngati kukutopetsa kuthamanga pamodzi ndi anthu
nanga ungapikisane bwanji ndi akavalo?
Ngati ukupunthwa ndi kugwa pa malo abwino,
udzatha bwanji kuthamanga mʼnkhalango
za ku Yorodani?
6 Ngakhale abale ako
ndi anansi akuwukira,
onsewo amvana zokuyimba mlandu.
Usawakhulupirire,
ngakhale ayankhule zabwino ndi iwe.
7 “Ine ndawasiya anthu anga;
anthu amene ndinawasankha ndawataya.
Ndapereka okondedwa anga
mʼmanja mwa adani awo.
8 Anthu amene ndinawasankha
asanduka ngati mkango wa mʼnkhalango.
Akundibangulira mwaukali;
nʼchifukwa chake Ine ndikudana nawo.
9 Anthu anga amene ndinawasankha
asanduka ngati mbalame yolusa yamawangamawanga
imene akabawi ayizinga.
Pitani, kasonkhanitseni nyama zakuthengo.
Mubwere nazo kuti zidzadye mbalameyo.
10 Abusa ambiri anawononga munda wanga wa mpesa,
anapondereza munda wanga;
munda wanga wabwino uja
anawusandutsa chipululu.
11 Unawusandutsadi chipululu.
Ukanali wokhawokha chomwecho ukundilirira Ine.
Dziko lonse lasanduka chipululu
chifukwa palibe wolisamalira.
12 Anthu onse owononga abalalikira
ku zitunda zonse za mʼchipululu.
Yehova watuma ankhondo ake
kudzawatha kuyambira kumalire ena a dziko mpaka ku malire enanso a dziko,
ndipo palibe amene adzakhale pa mtendere.
13 Anthu anafesa tirigu koma anatuta minga;
anadzitopetsa kugwira ntchito koma osapeza phindu lililonse.
Choncho mudzachita manyazi ndi zokolola zanu
chifukwa cha mkwiyo wa Yehova.”
14 “Anthu oyipa oyandikana ndi anthu anga Aisraeli, akuwalanda Aisraeliwo dziko, cholowa chimene ndinawapatsa. Nʼchifukwa chake ndidzawachotsa mʼdziko limenelo, ndipo ndidzachotsa banja la Yuda pakati pawo. 15 Komabe nditawachotsa, ndidzawachitiranso chifundo, ndipo ndidzabwezera aliyense cholowa chake ndi dziko lake. 16 Ndipo ngati iwo adzaphunzira bwino njira za anthu anga ndi kulumbira mʼdzina langa, namanena kuti, ‘Pali Yehova wamoyo,’ monga iwo anaphunzitsira anthu anga kulumbira mʼdzina la Baala, Ine ndidzawakhazikitsa pakati pa anthu anga. 17 Koma ngati mtundu wina uliwonse sudzamvera, Ine ndidzawuchotsa ndi kuwuwonongeratu,” akutero Yehova.
Lamba Womanga Mʼchiwuno
13 Yehova anandiwuza kuti, “Pita kagule lamba wansalu yosalala ndipo ukavale mʼchiwuno mwako, koma usakamuviyike mʼmadzi.” 2 Choncho ndinakagula lambayo, monga momwe anandiwuzira Yehova, ndipo ndinamanga mʼchiwuno mwanga.
3 Kenaka Yehova anandiyankhulanso kachiwiri kuti, 4 “Tenga lamba amene unagula ndi kuvala mʼchiwuno mwako uja. Tsono pita ku mtsinje wa Yufurate ndipo ukamubise lambayo mʼmingʼalu ya mʼmatanthwe.” 5 Ndipo ndinapitadi ndi kukabisa lambayo ku Yufurate, monga anenera Yehova.
6 Patapita masiku ambiri Yehova anandiwuzanso kuti, “Pitanso ku Yufurate ndipo ukatenge lamba amene ndinakuwuza kuti ukamubise kumeneko.” 7 Choncho ndinapita ku Yufurate kukafukula lambayo ndi kumuchotsa pamalo pamene ndinamubisa, koma nthawi imeneyi nʼkuti lambayo atawonongeka kotheratu ndipo analibenso ntchito.
8 Pamenepo Yehova anandiwuza kuti, 9 “Izi ndi zimene ine ndikunena: ‘Umu ndi mmene ndidzawonongere zimene akunyadira kwambiri a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu. 10 Anthuwa ndi oyipa. Iwo akana kumvera mawu anga. Mʼmalo mwake amawumirira kutsata milungu ina, kuyitumikira ndi kuyipembedza. Anthu amenewa adzakhala ngati lamba wopanda ntchitoyu. 11 Monga momwe lamba amakanirira mʼchiwuno cha munthu, momwemonso ndinakonza kuti nyumba yonse ya Israeli ndi nyumba yonse ya Yuda indikangamire Ine kuti akhale anthu anga, kuti azitamanda dzina langa ndi kulemekeza Ine. Koma iwo sanamvere,’ akutero Yehova.
Zikopa Zothiramo Vinyo
12 “Awuze anthuwo kuti, ‘Yehova Mulungu wa Israeli akuti: Mtsuko uliwonse adzawudzaza ndi vinyo.’ Ndipo ngati iwo anena kwa iwe kuti, ‘Kodi ngati ife sitikudziwa kuti mtsuko uliwonse udzadzazidwa ndi vinyo?’ 13 Tsono iwe uwawuze kuti, Yehova akuti ‘Ine ndidzaledzeretsa anthu onse okhala mʼdziko muno, kuyambira mafumu amene amakhala pa mpando waufumu wa Davide, ansembe, aneneri, pamodzi ndi anthu onse amene akukhala mu Yerusalemu. 14 Ndidzawagundanitsa mitu kuti aphwanyane okhaokha ngati mitsuko, makolo ndi ana awo, akutero Yehova. Sindidzawamvera chisoni kapena kuwachitira chifundo kapena kukhudzidwa nawo kuti ndileke kuwawononga.’ ”
Yuda Adzapita ku Ukapolo
15 Imvani inu Aisraeli ndipo tcherani khutu,
musadzitukumule,
pakuti ndi Yehova amene akuyankhula.
16 Lemekezani Yehova Mulungu wanu
asanagwetse mdima,
mapazi anu asanayambe kupunthwa
mʼchisisira chamʼmapiri.
Asanasandutse kuwala
mukuyembekezerako kukhala
mdima wandiweyani.
17 Koma ngati simumvera,
ndidzalira kwambiri
chifukwa cha kunyada kwanu.
Mʼmaso mwanga
mwadzaza ndi misozi yowawa
chifukwa nkhosa za Yehova zatengedwa ukapolo.
18 Uza mfumu pamodzi ndi amayi ake kuti,
“Tsikani pa mipando yaufumuyo,
pakuti zipewa zanu zaufumu zokongolazo
zagwa pansi.”
19 Mizinda ya ku Negevi yatsekedwa
ndipo palibe wina woti nʼkuyitsekula.
Yuda yense watengedwa kupita ku ukapolo,
watengedwa yense ukapolo.
20 Tukula maso ako kuti uwone
amene akubwera kuchokera kumpoto.
Kodi nkhosa zimene anakusungitsa zili kuti,
nkhosa zanu zokongola zija?
21 Kodi udzanena chiyani pamene [Yehova] adzakuyikira
anthu amene unkanena kuti ndi abale ako akukugonjetsa ndi kukulamulira?
Kodi sudzamva zowawa
ngati za mayi pa nthawi yake yochira?
22 Ndipo ngati udzadzifunsa kuti,
“Kodi zimenezi zandichitikira chifukwa chiyani?”
Ndi chifukwa cha machimo anu ambiri
kuti zovala zanu zingʼambike
ndiponso kuti akuchitireni nkhanza.
23 Kodi wa dziko la Kusi nʼkusintha khungu lake,
kapena kambuku kusintha mawanga ake?
Inunso amene munazolowera kuchita
zoyipa simungathe kusintha.
24 “Ine ndidzakumwazani ngati mankhusu
amene amawuluka ndi mphepo ya ku chipululu.
25 Limeneli ndiye gawo lanu,
chilango chimene ndakukonzerani
chifukwa chondiyiwala Ine
ndi kutumikira milungu yabodza,
akutero Yehova.
26 Ine ndidzakwinya zovala zanu mpaka ku maso
kuti umaliseche wanu uwonekere.
27 Ndaona zonyansa zanu: zigololo zanu, kutchetcherera kwanu
ndi ziwerewere zanu,
zochitika pa mapiri ndi mʼminda.
Tsoka iwe Yerusalemu!
Udzakhala wosayeretsedwa
pa zachipembedzo mpaka liti?”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.