Beginning
Kulangidwa Kwa Babuloni
13 Uthenga onena za Babuloni umene Yesaya mwana wa Amozi anawulandira:
2 Kwezani mbendera yankhondo pa phiri loti see,
muwafuwulire ankhondo;
muwakodole kuti adzalowe pa zipata
za anthu olemekezeka.
3 Ine Yehova, ndalamulira ankhondo anga;
ndasonkhanitsa ankhondo anga kuti akhale zida zanga zolangira
amene amadzikuza ndi chipambano changa.
4 Tamvani phokoso ku mapiri,
likumveka ngati phokoso la gulu lalikulu la anthu!
Tamvani phokoso pakati pa maufumu,
ngati kuti mitundu ya anthu ikusonkhana pamodzi!
Yehova Wamphamvuzonse akukhazika asilikali ake mokonzekera
kuchita nkhondo.
5 Iwo akuchokera ku mayiko akutali,
kuchokera kumalekezero a dziko
Yehova ali ndi zida zake za nkhondo
kuti adzawononge dziko la Babuloni.
6 Lirani mofuwula, pakuti tsiku la Yehova layandikira;
lidzabwera ngati chiwonongeko chochokera kwa Wamphamvuzonse.
7 Zimenezi zinafowoketsa manja onse,
mtima wa munthu aliyense udzachokamo.
8 Anthu adzagwidwa ndi mantha aakulu,
zowawa ndi masautso zidzawagwera;
adzamva zowawa zonga amamva mayi pobereka.
Adzayangʼanana mwamantha,
nkhope zawo zikufiira ngati malawi amoto.
9 Taonani, tsiku la Yehova likubwera,
tsiku lopanda chisoni, lawukali ndi lamkwiyo;
kudzasandutsa dziko kuti likhale chipululu
ndi kuwononga anthu ochimwa a mʼmenemo.
10 Nyenyezi zakumwamba ndiponso zonse zamlengalenga
sizidzaonetsa kuwala kwawo.
Dzuwa lidzada potuluka,
ndipo mwezi sudzawala konse.
11 Ndidzalanga dziko lonse chifukwa cha zolakwa zake,
anthu oyipa ndidzawalanga chifukwa cha machimo awo.
Ndidzathetsa kunyada kwa odzikuza,
ndipo ndidzatsitsa kudzitukumula kwa anthu ankhanza.
12 Ndidzasandutsa anthu kukhala ovuta kupeza kuposa mmene amasowera golide wabwino.
Iwo sazidzapezekapezeka kuposa mmene amasowera golide wa ku Ofiri.
13 Tsono ndidzagwedeza miyamba
ndipo dziko lapansi lidzachoka pa maziko ake.
Izi zidzachitika chifukwa cha ukali wa Wamphamvuzonse
pa tsiku la mkwiyo wake woopsa.
14 Ngati mbawala zosakidwa,
ngati nkhosa zopanda wozikusa,
munthu aliyense adzabwerera kwa anthu akwawo,
aliyense adzathawira ku dziko lake.
15 Aliyense amene atadzapezeke ndi kugwidwa
adzaphedwa momubaya ndi lupanga.
16 Ana awo akhanda adzaphwanyidwa iwo akuona;
nyumba zawo zidzafunkhidwa ndipo akazi awo adzagwiriridwa.
17 Taona, Ine ndidzadzutsa Amedi amene safuna siliva
ndipo sasangalatsidwa ndi golide,
kuti amenyane ndi Ababuloni.
18 Adzapha anyamata ndi mauta awo;
sadzachitira chifundo ana
ngakhale kumvera chisoni ana akhanda.
19 Babuloni, ufumu wake ndi waulemerero kuposa mafumu onse.
Anthu ake amawunyadira.
Koma Yehova adzawuwononga
ngati mmene anawonongera Sodomu ndi Gomora.
20 Anthu sadzakhalamonso
kapena kukhazikikamo pa mibado yonse;
palibe Mwarabu amene adzayimike tenti yake,
palibe mʼbusa amene adzawetamo ziweto zake.
21 Koma nyama zakuthengo ndizo zidzakhale kumeneko,
nyumba zake zidzadzaza ndi nkhandwe;
mu mzindamo muzidzakhala akadzidzi,
ndipo atonde akuthengo azidzalumphalumphamo.
22 Mu nsanja zake muzidzalira afisi,
mʼnyumba zake zokongola muzidzalira nkhandwe.
Nthawi yake yayandikira
ndipo masiku ake ali pafupi kutha.
14 Yehova adzachitira chifundo Yakobo;
adzasankhanso Israeli
ndi kuwalola kuti akhalenso mʼdziko lawo.
Alendo adzabwera kudzakhala nawo
ndi kudziphatika okha kukhala ngati a mʼnyumba ya Yakobo.
2 Anthu a mitundu ina adzaperekeza a Israeli
ku dziko lawo.
Tsono Aisraeli adzasandutsa anthu a mitundu ina aja
kukhala antchito awo aamuna ndi aakazi mʼdziko la Yehova.
Ndiye kuti Aisraeli adzasandutsa akapolo anthu amene kale anali ambuye awo.
Iwo adzasandutsa akapolo anthu amene kale ankawalamulira ndi kuwazunza.
3 Yehova akadzakupumitsani ku zowawa ndi mavuto, ndiponso kuntchito yakalavulagaga imene ankakugwiritsani, 4 mudzayankhula monyogodola mfumu ya Babuloni kuti,
Wopsinja uja watha!
Ukali wake uja watha!
5 Yehova wathyola chikwapu cha anthu oyipa,
Iye waphwanya ndodo ya olamulira.
6 Mfumu ya ku Babuloni inkakantha mitundu ya anthu mwaukali
powamenya kosalekeza,
Iyo inkagonjetsa anthu a mitundu ina mwaukali
ndikuwazunza kosalekeza.
7 Koma tsopano mayiko onse ali pa mpumulo ndi pa mtendere;
ndipo akuyimba mokondwa.
8 Ngakhale mitengo ya payini ndi mikungudza ya ku Lebanoni
ikuyimba za iwe mokondwa ndipo ikuti,
“Chigwetsedwere chako pansi,
palibe wina anabwera kudzatigwetsa.”
9 Ku manda kwatekeseka
kuti akulandire ukamabwera;
mizimu ya anthu akufa, aja amene anali atsogoleri
a dziko lapansi, yadzutsidwa.
Onse amene anali mafumu a mitundu ya anthu
ayimiritsidwa pa mipando yawo.
10 Onse adzayankha;
adzanena kwa iwe kuti,
“Iwenso watheratu mphamvu ngati ife;
Iwe wafanana ndi ife.”
11 Ulemerero wako wonse walowa mʼmanda,
pamodzi ndi nyimbo za azeze ako;
mphutsi zayalana pogona pako
ndipo chofunda chako ndi nyongolotsi.
12 Wagwa pansi bwanji kuchoka kumwamba,
iwe nthanda, mwana wa mʼbandakucha!
Wagwetsedwa pansi pa dziko lapansi,
Iwe amene unagonjetsapo mitundu ya anthu!
13 Mu mtima mwako unkanena kuti,
“Ndidzakwera mpaka kumwamba;
ndidzakhazika mpando wanga waufumu
pamwamba pa nyenyezi za Mulungu;
ndidzakhala pa mpando waufumu pa phiri losonkhanirako,
pamwamba penipeni pa phiri la kumpoto.
14 Ndidzakwera pamwamba pa mitambo;
ndidzafanana ndi Wammwambamwamba.”
15 Koma watsitsidwa mʼmanda
pansi penipeni pa dzenje.
16 Anthu akufa adzakupenyetsetsa
nadzamalingalira za iwe nʼkumati,
“Kodi uyu ndi munthu uja anagwedeza dziko lapansi
ndi kunjenjemeretsa maufumu,
17 munthu amene anasandutsa dziko lonse chipululu,
amene anagwetsa mizinda yake
ndipo sankalola kuti anthu ogwidwa abwerere kwawo?”
18 Mafumu onse a mitundu ya anthu akugona mwaulemu
aliyense mʼmanda akeake.
19 Koma iwe watayidwa kunja kwa manda ako,
ngati nthambi yowola ndi yonyansa.
Mtembo wako waphimbidwa ndi anthu ophedwa;
amene anabayidwa ndi lupanga,
anatsikira mʼdzenje lamiyala
ngati mtembo woponderezedwa.
20 Sudzayikidwa nawo mʼmanda mwaulemu,
chifukwa unawononga dziko lako
ndi kupha anthu ako.
Zidzukulu za anthu oyipa
sizidzakumbukika nʼpangʼono pomwe.
21 Konzani malo woti muphere ana ake aamuna
chifukwa cha machimo a makolo awo;
kuti angadzuke ndi kulanda dziko lapansi
ndi kulidzaza dziko lonselo ndi mizinda yawo.
22 Yehova Wamphamvuzonse akuti,
“Ine ndidzathira nkhondo mzinda wa Babuloni.
Ndidzachotseratu mu Babuloni dzina lake ndi onse otsaliramo.
Ndiye kuti sipadzakhala ana kapena zidzukulu,”
akutero Yehova.
23 “Ndidzawusandutsa mzindawo malo okhalamo anungu
ndiponso dambo lamatope;
ndidzawusesa ndi tsache lowononga,”
akutero Yehova Wamphamvuzonse.
Za Kulangidwa kwa Asiriya
24 Yehova Wamphamvuzonse walumbira kuti,
“Ndithudi, monga ndaganizira ndidzachitadi choncho,
ndipo monga momwe ndatsimikizira zidzakhala momwemo ndithu.
25 Ndidzawawononga Asiriya mʼdziko langa;
ndidzawapondereza ndi mapazi pa mapiri anga;
ndidzachotsa goli lawo pa anthu anga,
ndipo ndidzachotsa katundu wawo pa mapewa awo.”
26 Izi ndizo ndakonza kuti zichitike pa dziko lonse lapansi,
ndatambasula dzanja pa anthu a mitundu yonse.
27 Pakuti Yehova Wamphamvuzonse watsimikiza, ndipo ndani angamuletse?
Dzanja lake latambasulidwa ndipo ndani angalibweze?
Za Kulangidwa kwa Afilisti
28 Uthenga uwu unabwera chaka chimene mfumu Ahazi anamwalira:
29 Musakondwere inu Afilisti nonse
kuti Asiriya amene anali ngati ndodo yokukanthani anathedwa;
chifukwa kuchokera ku njoka yomweyi (mfumu ya Aasiriya) mudzatuluka mphiri,
ndipo chipatso chake chidzakhala njoka yaliwiro ndiponso yaululu.
30 Osaukitsitsa adzapeza chakudya
ndipo amphawi adzakhala mwamtendere.
Koma anthu ako ndidzawawononga ndi njala,
ndipo njalayo idzapha ngakhale opulumuka ako.
31 Lirani kwambiri, anthu a pa chipata! Fuwulani kwambiri, anthu a mu mzinda!
Njenjemerani ndi mantha, inu Afilisti nonse!
Mtambo wa utsi ukuchokera kumpoto,
ndipo palibe wamantha pakati pa ankhondo ake.
32 Kodi tidzawayankha chiyani
amithenga a ku Filisitiya?
“Yehova wakhazikitsa Ziyoni,
ndipo mu mzinda wakewu, anthu ozunzika apeza populumukira.”
Za Kulangidwa kwa Mowabu
15 Uthenga wonena za Mowabu:
Popeza kuti mu usiku umodzi wokha mzinda wa Ari wa ku Mowabu wawonongedwa,
wawonongedwa pa usiku umodzi wokha.
Mzinda wa Kiri wawonongedwa,
wawonongedwa pa usiku umodzi wokha.
2 Anthu a ku Diboni akupita ku nyumba ya milungu yawo,
akupita ku malo awo achipembedzo kukalira;
anthu a ku Mowabu akulirira mofuwula mzinda wa Nebo ndi wa Medeba.
Mutu uliwonse wametedwa mpala,
ndipo ndevu zonse zametedwa.
3 Mʼmisewu akuvala ziguduli;
pa madenga ndi mʼmabwalo
aliyense akulira mofuwula,
misozi ili pupupu.
4 Anthu a ku Hesiboni ndi Eleali akulira mofuwula,
mawu awo akumveka mpaka ku Yahazi.
Kotero asilikali a ku Mowabu akulira mofuwula,
ndipo ataya mtima.
5 Inenso ndikulirira Mowabu;
chifukwa othawa nkhondo ake akupita akulira ku chikweza cha Luluti mpaka ku Zowari
ndi Egilati-Selisiya
akupita akulira ku chikweza cha Luhiti,
Akulira mosweka mtima
pa njira yopita ku Horonaimu;
akulira mosweka mtima chifukwa cha chiwonongeko chawo.
6 Madzi a ku Nimurimu aphwa
ndipo udzu wauma;
zomera zawonongeka
ndipo palibe chomera chobiriwira chatsala.
7 Kotero kuti chuma chomwe anachipeza ndi kuchisunga,
achitenga kuti awoloke nacho chigwembe cha Misondozi.
8 Kulira kwawo kukumveka mʼdziko lonse la Mowabu;
kulira kwawo kosweka mtima kukumveka
mpaka ku Egilaimu ndi Beeri-Elimu.
9 Madzi a ku Dimoni afiira ndi magazi,
komabe ndidzabweretsa zina zambiri pa Dimoni,
mkango woti udzagwire aliyense othawa mu Mowabu
ndi aliyense wotsala mʼdzikomo.
16 Anthu a ku Mowabu
atumiza mphatso za ana ankhosa onenepa,
kuchokera ku Sela kudutsa chipululu
mpaka kukafika ku phiri la Ziyoni.
2 Monga momwe mbalame zimawulukira uku ndi uku
akazimwaza mʼchisa,
momwemonso akazi a ku Mowabu
akuyendayenda ku madooko a Arinoni.
3 Amowabu aja anawuza a ku Yuda kuti,
“Tiwuzeni chochita, gamulani zoti tichite.
Inu mutiteteze kwa adani anthu.
Mukhale ngati mthunzi wathu dzuwa lili pa liwombo.
Mutibise,
musatipereke ife othawa nkhondo kwa adani athu.
4 Lolani kuti anthu othawa nkhondo a ku Mowabu azikhala pakati panu;
mukhale populumukira pawo kwa wowonongayo.”
Nthawi idzafika ndipo wozunzayo sadzakhalaponso,
kuwononga kudzaleka;
waukaliyo adzachoka mʼdzikomo.
5 Mpando waufumu udzakhazikitsidwa mwachikondi;
mmodzi mwa zidzukulu za Davide adzakhalapo mokhulupirika.
Iyeyo poweruza adzatsata chilungamo
ndipo adzalimbikitsa kuchita zachilungamo.
6 Tinamva kuti Mowabu anadzikuza kwambiri.
Kunyada kwawo
ndi kunyogodola kwawo ndi kudzitama kwawo,
zonse ndi zopanda phindu.
7 Nʼchifukwa chake Amowabu akulira kwambiri;
iwo akulirira dziko lawo.
Akubuma momvetsa chisoni
chifukwa cha makeke a mphesa a ku Kiri Hareseti.
8 Minda ya ku Hesiboni yauma,
minda ya mpesa ya ku Sibina yaguga.
Atsogoleri a mitundu ina anapondaponda
minda ya mpesa wabwino,
imene nthambi zake zinakafika ku Yazeri,
mpaka kutambalalira ku chipululu.
Mizu yake inakafika
mpaka ku tsidya la nyanja.
9 Kotero Ine ndikulira, monga mmene akulirira anthu a ku Yazeri,
chifukwa cha minda ya mpesa ya ku Sibima.
Inu anthu a ku Hesiboni, inu anthu a ku Eleali,
ndikukunyowetsani ndi misozi!
Mwalephera kupeza zokolola,
chifukwa cha nkhondo imene inawononga zokolola zonse.
10 Chimwemwe ndi chisangalalo zalekeka ku minda yanu ya zipatso;
palibe amene akuyimba kapena kufuwula mʼminda ya mpesa;
palibe amene akupsinya vinyo ku malo opsinyira mphesa,
pakuti ndathetsa kufuwula.
11 Chifukwa chake moyo wanga ukulira ngati pangwe kulirira Mowabu,
mtima wanga ukubuwula chifukwa cha Kiri Hareseti.
12 Ngakhale anthu a ku Mowabu
apite ku malo awo achipembedzo
koma amangodzitopetsa ndi kutaya nthawi chabe
chifukwa sizidzatheka.
13 Awa ndi mawu amene Yehova wayankhula kale zokhudza Mowabu. 14 Koma tsopano Yehova akuti, “Zisanathe zaka zitatu, potsata mʼmene munthu waganyu amawerengera, ulemerero wa Mowabu udzakhala utatheratu ndipo anthu ake ambiri adzakhala atawonongeka, ndipo opulumuka ake adzakhala ochepa ndi ofowoka.”
Uthenga Wotsutsa Damasiko
17 Uthenga wonena za Damasiko:
“Taonani, mzinda wa Damasiko sudzakhalanso mzinda,
koma udzasanduka bwinja.
2 Mizinda ya Aroeri idzakhala yopanda anthu
ndipo idzakhala ya ziweto, zimene zidzagona pansi
popanda wina woziopseza.
3 Ku Efereimu sikudzakhalanso linga,
ndipo ku Damasiko sikudzakhalanso ufumu;
Otsalira a ku Siriya adzachotsedwa ulemu
monga anthu a ku Israeli,”
akutero Yehova Wamphamvuzonse.
4 “Tsiku limenelo ulemerero wa Yakobo udzazimirira;
ndipo chuma chake chidzasanduka umphawi.
5 Israeli adzakhala ngati munda wa tirigu
umene anatsiriza kukolola.
Adzakhalanso ngati munda wa mʼchigwa cha Refaimu
anthu atatha kukunkha ngala za tirigu.
6 Komabe Aisraeli ochepa okha ndiwo ati adzatsale
monga mʼmene zimatsalira zipatso ziwiri kapena zitatu pa nthambi ya pamwamba penipeni
kapena zipatso zisanu pa nthambi za mʼmunsi
mwa mtengo wa olivi akawugwedeza,”
akutero Yehova, Mulungu wa Israeli.
7 Tsiku limenelo anthu adzayangʼana Mlengi wawo
ndipo adzatembenukira kwa Woyerayo wa Israeli.
8 Iwo sadzakhulupiriranso maguwa ansembe,
ntchito ya manja awo,
ndipo sadzadaliranso mitengo ya mafano a Asera,
ndiponso maguwa ofukizirapo lubani amene manja awo anapanga.
9 Tsiku limenelo mizinda yawo yamphamvu, imene anasiya chifukwa cha Aisraeli, idzakhala ngati malo osiyidwa kuti awirire ndi kumera ziyangoyango. Ndipo yonse idzakhala mabwinja.
10 Inu mwayiwalatu Mulungu Mpulumutsi wanu;
simunakumbukire Thanthwe, linga lanu.
Choncho, ngakhale munadzala mbewu zabwino,
ndi kuyitanitsa kunja mitengo ya mpesa,
11 nimuyembekeza kuti zikule tsiku lomwelo
ndi kuphukira maluwa mmawa mwake,
komabe zimenezi sizidzakupindulirani
pa tsiku la mavuto.
12 Aa, mkokomo wa anthu a mitundu yambiri,
akusokosa ngati kukokoma kwa nyanja!
Aa, phokoso la anthu a mitundu ina,
akusokosa ngati mkokomo wa madzi amphamvu!
13 Ngakhale ankhondo a mitundu ina akubwera ndi mkokomo ngati wa madzi ambiri,
koma adzathawira kutali Mulungu akadzawadzudzula.
Yehova adzawapirikitsa ngati mankhusu owuluka ndi mphepo pa phiri,
ndi ngati fumbi la kamvuluvulu asanayambe.
14 Pofika nthawi yamadzulo zoopsa zidzayamba kuchitika,
ndipo zidzakhala zitatha pofika mmawa.
Izi ndizo zidzachitikire anthu otilanda zinthu,
gawo la amene amatibera zinthu zathu.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.