Menu
Bible Gateway Plus logo
Bible Gateway logo
account
Read Scripture without ads. Study with fewer distractions with Bible Gateway Plus.
Bible Gateway Plus logo
Bible Gateway logo
Read Scripture without ads. Try Bible Gateway Plus.
  • Read
    • Reading Plans
    • Advanced Search
    • Available Versions
    • Audio Bibles
  • Study
    • Scripture Engagement
    • More Resources
  • News
  • Explore
    • Newsletters
    • Devotionals
    • Bible Gateway App
    • Bible Audio App
    • Take a Tour
  • Store
    • Bibles
    • Deals
    • More
  • Bible Gateway Plus
CCL
Version
Bible Books Bible Books
CCL
Version
Read
Study
News
Explore
Store
Bible Gateway Plus
Light Mode Dark Mode
Font Size
Log In show menu
Previous Next
Print PrintSettingsSettingsShare ShareParallelParallelExpandExpandCollapse

Yoswa 18  Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Kugawa kwa Madera Otsala a Dziko

18 Atagonjetsa dziko lonse Aisraeli anasonkhana ku Silo ndipo anayimikako tenti ya msonkhano. 2 Koma pa nthawiyo nʼkuti mafuko asanu ndi awiri a Aisraeli asanalandire cholowa chawo.

3 Ndipo Yoswa anati kwa Aisraeli, “Kodi mudikira mpaka liti kuti mulowe ndi kulanda dziko limene Yehova Mulungu wa makolo anu wakupatsani? 4 Sankhani amuna atatu kuchokera ku fuko lililonse ndipo ine ndidzawatuma kuti akayendere dzikolo ndi kukalilembera bwino kuti ndiligawe kukhala lawo. Akatero, abwererenso kwa ine. 5 Aligawe dzikolo mʼzigawo zisanu ndi ziwiri; fuko la Yuda lidzakhale ndi dziko lake la kummwera ndi nyumba ya Yosefe ikhalebe mʼdziko lawo la kumpoto. 6 Mudzalembe mawu ofotokoza za zigawo zisanu ndi ziwiri za dzikolo, ndi kubwera nawo kwa ine. Tsono ineyo ndidzakuchitirani maere pamaso pa Yehova Mulungu wanu. 7 Alevi asakhale ndi dziko pakati panu, chifukwa gawo lawo ndi kutumikira Yehova pa ntchito ya unsembe. Ndipo Gadi, Rubeni ndi theka la fuko la Manase analandira kale cholowa chawo kummawa kwa Yorodani. Mose mtumiki wa Yehova ndiye anawapatsa.”

8 Anthuwo akupita kukalembera dzikolo, Yoswa anawalangiza kuti, “Pitani mukayendere ndi kulembera dzikolo. Kenaka mukabwere kwa ine, ndidzakuchitirani maere kuno ku Silo pamaso pa Yehova.” 9 Ndipo anthu anachoka ndi kukayendera dziko lonse. Iwo analemba bwinobwino mʼbuku za dzikolo, mzinda ndi mzinda. Analigawa magawo asanu ndi awiri, ndipo anabwerera kwa Yoswa ku misasa ya ku Silo. 10 Pambuyo pake Yoswa anawachitira maere ku Silo pamaso pa Yehova, ndipo fuko lililonse la Israeli analigawira dziko lake.

Dziko la Benjamini

11 Maere anagwera mabanja a fuko la Benjamini. Dziko limene anapatsidwa linali pakati pa fuko la Yuda ndi fuko la Yosefe:

12 Mbali ya kumpoto malire awo anayambira ku Yorodani nalowera chakumpoto kwa matsitso a ku Yeriko kulowera cha kumadzulo kwa dziko la ku mapiri ndi kukafika ku chipululu cha Beti-Aveni. 13 Kuchokera kumeneko malirewo analoza ku Luzi nadutsa mʼmbali mwa mapiri kummwera kwa Luzi (ndiye Beteli) ndipo anatsika mpaka ku Ataroti Adari, ku mapiri a kummwera kwa Beti-Horoni wa Kumunsi.

14 Ndipo malirewo analowanso kwina, analunjika kummwera kuchokera kumadzulo kwake kwa phiri loyangʼanana ndi Beti-Horoni, mpaka ku mzinda wa Kiriyati Baala (ndiye Kiriati Yearimu), mzinda wa anthu a fuko la Yuda. Amenewa ndiye anali malire a mbali ya kumadzulo.

15 Malire a kummwera anayambira mʼmphepete mwenimweni mwa Kiriati Yearimu napita kumadzulo mpaka kukafika ku akasupe a Nefitowa. 16 Malire anatsikira mʼmphepete mwa phiri loyangʼanana ndi chigwa cha Beni Hinomu, kumpoto kwa chigwa cha Refaimu. Anapitirira kutsikira ku chigwa cha Hinomu kummwera kwa chitunda cha Ayebusi mpaka ku Eni Rogeli. 17 Kenaka anakhotera kumpoto kupita ku Eni-Semesi, kupitirira mpaka ku Geliloti amene amayangʼanana ndi pokwera pa Adumimu. Kenaka malire anatsikira ku Mwala wa Bohani, mwana wa Rubeni. 18 Anabzola cha kumpoto kwa chitunda cha Beti Araba ndi kutsikabe mpaka ku chigwa cha Yorodani. 19 Anabzolanso cha kumpoto kwa chitunda cha Beti-Hogila kukafika cha kumpoto ku gombe la Nyanja ya Mchere kumene mtsinje wa Yorodani umathirirako, cha kummwera kwenikweni. Awa anali malire a kummwera.

20 Yorodani ndiye anali malire a mbali ya kummawa.

Awa anali malire a dziko limene mabanja a fuko la Benjamini analandira.

21 Mabanja a fuko la Benjamini anali ndi mizinda iyi;

Yeriko, Beti-Hogila, Emeki Kezizi, 22 Beti-Araba, Zemaraimu, Beteli 23 Avimu, Para, Ofiri, 24 Kefari-Amoni, Ofini ndi Geba, mizinda khumi ndi awiri ndi midzi yake

25 Panalinso Gibiyoni, Rama, Beeroti, 26 Mizipa, Kefira, Moza 27 Rekemu, Iripeeli, Tarala, 28 Zera Haelefu, mzinda wa Ayebusi (ndiye kuti Yerusalemu) Gibeya ndi Kiriati, mizinda 14 ndi midzi yake.

Limeneli ndilo dziko limene mabanja a fuko la Benjamini analandira kuti likhale lawo.

Next
Yoswa 17
Yoswa 19
Next
dropdown
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.

Bible Gateway Plus logo
Bible Gateway logo

Font Size

Font Size

Dark Mode

Light Mode Dark Mode

About

  • About
  • Learn About the Bible
  • Statement of Faith
  • Mobile App
  • Store
  • Blog
  • Newsroom
  • Support Us

Help

  • FAQs
  • Tutorials
  • Use Bible Gateway on Your Site
  • Advertise with us
  • Contact us
  • Privacy policy
  • California Privacy Rights
  • Do Not Sell My Personal Information
  • Site: Terms of use
  • Widget: Terms of use

Our Network

  • FaithGateway
  • StudyGateway
  • ChurchSource
  • HarperCollins Christian Publishing
  • Grupo Nelson
  • Editorial Vida
  • Thomas Nelson
  • WestBow Press
  • Zondervan
  • MasterLectures

Social

  • Facebook
  • Instagram
  • Pinterest
  • TikTok
  • X
  • YouTube

Preferences

  • Versión en español
  • Preferences
  • Classic Bible Gateway
Sign Up for Bible Gateway: News & Knowledge
Get weekly Bible news, info, reflections, and deals in your inbox.

By submitting your email address, you understand that you will receive email communications from Bible Gateway, operated by HarperCollins Christian Publishing, 501 Nelson Pl, Nashville, TN 37214 USA, including commercial communications and messages from partners of Bible Gateway. You may unsubscribe from Bible Gateway’s emails at any time. If you have any questions, please review our Privacy Policy or email us at privacy@biblegateway.com.

Preferences

  • Versión en español
  • Preferences
  • Classic Bible Gateway