Menu
Bible Gateway Plus logo
Bible Gateway logo
account
Welcome to the new Bible Gateway. Take a quick tour and see what’s new.
Bible Gateway Plus logo
Bible Gateway logo
Finding your way around? Take the tour.
  • Read
    • Reading Plans
    • Advanced Search
    • Available Versions
    • Audio Bibles
  • Study
    • Scripture Engagement
    • More Resources
  • News
  • Explore
    • Newsletters
    • Devotionals
    • Bible Gateway App
    • Bible Audio App
    • Take a Tour
  • Store
    • Bibles
    • Deals
    • More
  • Bible Gateway Plus
CCL
Version
Bible Books Bible Books
CCL
Version
Read
Study
News
Explore
Store
Bible Gateway Plus
Light Mode Dark Mode
Font Size
Log In show menu
Previous Next
Print PrintSettingsSettingsShare ShareParallelParallelExpandExpandCollapse

Yobu 7  Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 “Kodi munthu sakhala ndi ntchito yowawa pa dziko lapansi?
    Kodi masiku ake sali ngati munthu waganyu?
2 Monga ngati kapolo wolakalaka mthunzi wa nthawi yamadzulo,
    kapena ngati munthu waganyu woyembekezera malipiro ake,
3 choncho ine ndapatsidwa nthawi yongovutika pachabe,
    ndiponso usiku wamasautso wapatsidwa kwa ine.
4 Ndikamagona ndimaganiza kuti, ‘Kodi kucha liti?’
    Usikuwo umatalika ndipo sindigona tulo mpaka mmawa.
5 Thupi langa ladzala mphutsi ndi zipsera,
    khungu langa langʼambika ndipo likutuluka mafinya.

6 “Masiku anga ndi othamanga kupambana makina wolukira nsalu,
    ndipo amatha wopanda chiyembekezo.
7 Inu Mulungu kumbukirani kuti moyo wanga uli ngati mpweya;
    sindidzaonanso masiku achisangalalo.
8 Amene akundiona tsopano akundiona;
    mudzandifunafuna koma sindidzapezekanso.
9 Monga mtambo umazimirira ndi kukanganuka,
    momwemonso munthu amene walowa mʼmanda sabwerera.
10 Iye sadzabweranso ku nyumba kwake
    ndipo onse omudziwa adzamuyiwala.

11 “Nʼchifukwa chake ine sindidzakhala chete;
    ndidzayankhula mopsinjika mtima,
    ndidzadandaula mowawidwa mtima.
12 Kodi ine ndine nyanja kapena chirombo chamʼnyanja
    kuti inu mundiyikire alonda?
13 Pamene ndikuganiza kuti ndidzapeza chitonthozo pa bedi panga
    ndipo pogona panga padzachepetsa madandawulo anga,
14 ngakhale nthawi imeneyo mumandiopseza ndi maloto
    ndi kundichititsa mantha ndi masomphenya,
15 kotero kuti ndimalakalaka kudzikhweza kapena kufa,
    kupambana kupirira zowawa zimene ndikuzimva mʼthupi mwanga.
16 Ine ndatopa nawo moyo wanga; sindingakonde kukhala moyo nthawi zonse.
    Ndisiyeni ndekha pakuti moyo wanga ulibe tanthauzo.

17 “Kodi munthu nʼchiyani kuti muzimuganizira chotere,
    kuti muzisamala zochita zake,
18 kuti muzimusanthula mmawa uliwonse
    ndi kumamuyesa nthawi yonse?
19 Kodi simudzaleka kumandizonda
    kuti ndipezeko mpata wopumula?
20 Ngati ine ndachimwa, ndachita chiyani kwa Inu,
    Inu wopenyetsetsa anthu?
Chifukwa chiyani mwachititsa kuti ndikhale ngati choponyera chandamale chanu?
    Kodi ndasanduka katundu wolemera kwa Inu?
21 Chifukwa chiyani simukundikhululukira zolakwa zanga
    ndi kundichotsera machimo anga?
Pakuti posachedwa ndilowa mʼmanda;
    mudzandifunafuna ine koma simudzandionanso.”

Next
Yobu 6
Yobu 8
Next
dropdown
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.

Bible Gateway Plus logo
Bible Gateway logo

Font Size

Font Size

Dark Mode

Light Mode Dark Mode

About

  • About
  • Learn About the Bible
  • Statement of Faith
  • Mobile App
  • Store
  • Blog
  • Newsroom
  • Support Us

Help

  • FAQs
  • Tutorials
  • Use Bible Gateway on Your Site
  • Advertise with us
  • Contact us
  • Privacy policy
  • California Privacy Rights
  • Do Not Sell My Personal Information
  • Site: Terms of use
  • Widget: Terms of use

Our Network

  • FaithGateway
  • StudyGateway
  • ChurchSource
  • HarperCollins Christian Publishing
  • Grupo Nelson
  • Editorial Vida
  • Thomas Nelson
  • WestBow Press
  • Zondervan
  • MasterLectures

Social

  • Facebook
  • Instagram
  • Pinterest
  • TikTok
  • X
  • YouTube

Preferences

  • Versión en español
  • Preferences
  • Classic Bible Gateway
Sign Up for Bible Gateway: News & Knowledge
Get weekly Bible news, info, reflections, and deals in your inbox.

By submitting your email address, you understand that you will receive email communications from Bible Gateway, operated by HarperCollins Christian Publishing, 501 Nelson Pl, Nashville, TN 37214 USA, including commercial communications and messages from partners of Bible Gateway. You may unsubscribe from Bible Gateway’s emails at any time. If you have any questions, please review our Privacy Policy or email us at privacy@biblegateway.com.

Preferences

  • Versión en español
  • Preferences
  • Classic Bible Gateway