Add parallel Print Page Options

More of Solomon's Proverbs

25 Here are more of Solomon's proverbs, copied by scribes at the court of King Hezekiah of Judah.

We honor God for what he conceals; we honor kings for what they explain.

You never know what a king is thinking; his thoughts are beyond us, like the heights of the sky or the depths of the ocean.

Take the impurities out of silver and the artist can produce a thing of beauty. Keep evil advisers away from the king and his government will be known for its justice.

(A)When you stand before the king, don't try to impress him and pretend to be important. It is better to be asked to take a higher position than to be told to give your place to someone more important.

Don't be too quick to go to court about something you have seen. If another witness later proves you wrong, what will you do then?

If you and your neighbor have a difference of opinion, settle it between yourselves and do not reveal any secrets. 10 Otherwise everyone will learn that you can't keep a secret, and you will never live down the shame.

11 An idea well-expressed is like a design of gold, set in silver.

12 A warning given by an experienced person to someone willing to listen is more valuable than gold rings or jewelry made of the finest gold.

13 A reliable messenger is refreshing to the one who sends him, like cold water in the heat of harvest time.

14 People who promise things that they never give are like clouds and wind that bring no rain.

15 Patient persuasion can break down the strongest resistance and can even convince rulers.

16 Never eat more honey than you need; too much may make you vomit. 17 Don't visit your neighbors too often; they may get tired of you and come to hate you.

18 A false accusation is as deadly as a sword, a club, or a sharp arrow.

19 Depending on an unreliable person in a crisis is like trying to chew with a loose tooth or walk with a crippled foot.

20 Singing to a person who is depressed is like taking off a person's clothes on a cold day or like rubbing salt in a wound.

21 (B)If your enemies are hungry, feed them; if they are thirsty, give them a drink. 22 You will make them burn with shame, and the Lord will reward you.

23 Gossip brings anger just as surely as the north wind brings rain.

24 Better to live on the roof than share the house with a nagging wife.

25 Finally hearing good news from a distant land is like a drink of cold water when you are dry and thirsty.

26 A good person who gives in to someone who is evil reminds you of a polluted spring or a poisoned well.

27 Too much honey is bad for you, and so is trying to win too much praise.[a]

28 If you cannot control your anger, you are as helpless as a city without walls, open to attack.

Footnotes

  1. Proverbs 25:27 Probable text and so … praise; Hebrew unclear.

Miyambo Ina ya Solomoni

25 Iyi ndi miyambo inanso ya Solomoni, imene anthu a Hezekiya mfumu ya ku Yuda analemba.

Ulemerero wa Mulungu uli pa kubisa zinthu;
    ulemerero wa mafumu uli pa kufufuza zinthuzo.

Monga momwe kwatalikira kumwamba ndi momwe kulili kuzama kwa dziko lapansi,
    ndi momwemonso alili maganizo a mfumu kusadziwika kwake.

Chotsa zoyipa mʼsiliva
    ndipo wosula adzapanga naye ziwiya.
Chotsa munthu woyipa pamaso pa mfumu;
    ndipo ufumu wake udzakhazikika mu chilungamo.

Usamadzikuze ukakhala pamaso pa mfumu,
    ndipo usamakhale pamalo pa anthu apamwamba;
paja ndi bwino kuti mfumu ichite kukuwuza kuti, “Bwera pamwamba pano,”
    kulekana ndi kuti ikuchititse manyazi chifukwa cha wina wokuposa.

Chimene wachiona ndi maso ako,
    usafulumire kupita nacho ku bwalo la milandu
nanga udzachita chiyani pa mapeto pake
    ngati mnansi wako adzakuchititsa manyazi?

Kamba mlandu ndi mnansi wako,
    koma osawulula chinsinsi cha munthu wina
10 kuopa kuti wina akamva mawu ako adzakuchititsa manyazi
    ndipo mbiri yako yoyipa sidzatha.

11 Mawu amodzi woyankhulidwa moyenera
    ali ngati zokongoletsera zagolide mʼzotengera zasiliva.

12 Kwa munthu womvetsa bwino, kudzudzula kwa munthu wanzeru kuli ngati ndolo zagolide
    kapena chodzikongoletsera china cha golide wabwino kwambiri.

13 Wamthenga wodalirika ali ngati madzi ozizira pa nthawi yokolola
    kwa anthu amene amutuma;
    iye amaziziritsa mtima bwana wake.

14 Munthu wonyadira mphatso imene sayipereka
    ali ngati mitambo ndi mphepo yopanda mvula.

15 Kupirira ndiye kumagonjetsa mfumu,
    ndipo kufewa mʼkamwa kutha kumafatsitsa munthu wowuma mtima.

16 Ngati upeza uchi, ingodya okukwanira,
    kuopa ungakoledwe nawo ndi kuyamba kusanza.
17 Uzipita kamodzikamodzi ku nyumba ya mnzako
    ukawirikiza kupita, udzadana naye.

18 Munthu wochitira mnzake umboni wonama,
    ali ngati chibonga kapena lupanga kapena muvi wakuthwa.

19 Kudalira munthu wosankhulupirika pa nthawi ya mavuto,
    kuli ngati dzino lobowoka kapena phazi lolumala.

20 Kuyimbira nyimbo munthu wachisoni
    kuli ngati kuvula zovala pa nyengo yozizira
    kapena kuthira mchere pa chilonda.

21 Ngati mdani wako ali ndi njala, mupatse chakudya kuti adye;
    ngati ali ndi ludzu mupatse madzi kuti amwe.
22 Pochita izi, udzamusenzetsa makala a moto pa mutu pake,
    ndipo Yehova adzakupatsa mphotho.

23 Monga momwe mphepo yampoto imabweretsera mvula,
    chonchonso mjedu umadzetsa mkwiyo.

24 Nʼkwabwino kukhala pa ngodya ya denga
    kuposa kukhala mʼnyumba ndi mkazi wolongolola.

25 Mthenga wabwino wochokera ku dziko lakutali
    ali ngati madzi ozizira kwa munthu waludzu.

26 Munthu wolungama amene amagonjera munthu woyipa
    ali ngati kasupe wodzaza ndi matope kapena chitsime cha madzi oyipa.

27 Sibwino kudya uchi wambiri,
    sibwinonso kudzifunira wekha ulemu.

28 Munthu amene samatha kudziretsa
    ali ngati mzinda umene adani awuthyola ndi kuwusiya wopanda malinga.