Add parallel Print Page Options

Nsembe Yopepesera Kupalamula

“ ‘Malamulo a nsembe yopepesera kupalamula imene ndi nsembe yopatulika kwambiri ndi awa: Nsembe yopepesera machimo iziphedwa pamalo pomwe amaphera nsembe yopsereza ndipo awaze magazi ake mbali zonse za guwa. Tsono apereke mafuta ake onse: mchira wamafuta ndi mafuta amene amakuta matumbo. Aperekenso impsyo ziwiri, mafuta ake pamodzi ndi mafuta onse amene ali chamʼchiwuno, ndiponso mafuta onse amene aphimba chiwindi. Wansembe azitenthe pa guwa kuti zikhale nsembe yotentha pa moto, yoperekedwa kwa Yehova. Imeneyi ndi nsembe yopepesera tchimo lopalamula. Munthu wamwamuna aliyense wa mʼbanja la wansembe angathe kudyako nsembeyo koma adyere ku malo opatulika. Imeneyi ndi nsembe yopatulika kwambiri.

“ ‘Nsembe yopepesera tchimo lopalamula ndi yofanana ndi nsembe yoperekedwa chifukwa cha tchimo. Ndipo nsembe ziwiri zonsezi zili ndi lamulo limodzi lokha. Wansembe amene wachita mwambo wa nsembe yopepesera machimo a kupalamula atenge nyamayo ngati yake. Wansembe wopereka nsembe yopsereza ya munthu wina aliyense, atenge chikopa cha nsembe yopserezayo kuti chikhale chake. Chopereka chilichonse cha chakudya chophika mu uvuni kapena chokazinga mu mʼphika kapena mu chiwaya ndi cha wansembe amene wapereka nsembezo. 10 Ndipo chopereka china chilichonse cha chakudya chosakaniza ndi mafuta kapena chowuma, chikhale cha ana onse a Aaroni ndipo anawo achigawane mofanana.

Nsembe Yachiyanjano

11 “ ‘Malamulo a nsembe ya chiyanjano imene munthu angathe kupereka kwa Yehova ndi awa:

12 “ ‘Ngati munthuyo apereka chifukwa cha kuthokoza, apereke nsembeyo pamodzi ndi makeke wopanda yisiti, osakaniza ndi mafuta; timitanda ta buledi wopanda yisiti, topyapyala, topaka mafuta, ndiponso makeke a ufa wosalala wophikidwa bwino, wosakaniza ndi mafuta. 13 Pamodzi ndi nsembe yachiyanjano yothokozerayo abwerenso ndi makeke opangidwa ndi yisiti ngati chopereka chake. 14 Munthuyo atenge mtanda umodzi pa mtanda wa buledi wa mtundu uliwonse kuti ukhale nsembe yopereka kwa Yehova. Tsono mtanda umenewo ndi wake wa wansembe amene awaze magazi a nsembe yachiyanjano. 15 Nyama ya nsembe yachiyanjano yothokozera idyedwe pa tsiku lomwe nsembeyo yaperekedwa ndipo isatsaleko mpaka mmawa.

16 “ ‘Koma ngati nsembe yakeyo apereka chifukwa cha lumbiro kapena mwaufulu, nsembeyo adye tsiku lomwe yaperekedwalo. Koma yotsala angathe kuyidya mmawa mwake. 17 Ngati nyama ina ya nsembe yatsalabe mpaka tsiku lachitatu, imeneyo itenthedwe pa moto. 18 Ngati munthu adya nyama yachiyanjano pa tsiku lachitatu, nsembeyo sidzalandiridwa. Amene wayipereka nsembeyo Mulungu sadzamulandira ndipo nsembeyo idzakhala yonyansa pamaso pa Mulungu, yosamupindulira kanthu woperekayo.

19 “ ‘Nyama imene yakhudza chilichonse chodetsedwa, munthu asayidye, koma itenthedwe pa moto. Aliyense amene ali woyeretsedwa angathe kudya nyama inayo. 20 Koma ngati munthu wina amene ndi wosayeretsedwa adya nyama ya nsembe yachiyanjano imene ndi ya Yehova, ameneyo achotsedwe pakati pa anthu a mtundu wake. 21 Ndipo ngati munthu wina akhudza chinthu chodetsedwa, kaya chonyansa cha munthu kapena cha nyama, kapenanso chonyansa china chilichonse, ndipo kenaka nʼkudya nyama ya nsembe yachiyanjano imene ndi ya Yehova, munthu ameneyo achotsedwe pakati anthu a mtundu wake.’ ”

Za Kuletsa Kudya Mafuta ndi Magazi

22 Yehova anayankhula ndi Mose kuti, 23 “Awuze Aisraeli kuti, ‘Musadye mafuta a ngʼombe, nkhosa kapenanso mbuzi. 24 Mafuta a nyama yofa yokha, kapena mafuta a nyama yophedwa ndi zirombo akhoza kuwagwiritsa ntchito iliyonse, koma inu musadye mafuta amenewo. 25 Pakuti munthu wakudya mafuta a nyama yoperekedwa kwa Yehova ngati nsembe yotentha pa moto, ayenera kuchotsedwa pakati pa anthu a mtundu wake. 26 Ndipo kulikonse kumene mukakhale musakadye magazi a mbalame iliyonse kapena magazi a nyama iliyonse. 27 Ngati munthu aliyense adya magazi achotsedwe pakati pa anthu a mtundu wake.’ ”

Gawo la Ansembe

28 Yehova anayankhula ndi Mose kuti, 29 “Awuze Aisraeli kuti, Aliyense amene apereka nsembe yachiyanjano kwa Yehova, abwere ndi gawo la nsembeyo kwa Yehova. 30 Atenge ndi manja ake zigawo za chopereka zoyenera kuzitentha pa moto ngati chopereka kwa Yehova. Abweretse mafuta, pamodzi ndi chidale chomwe, ndipo chidalecho achiweyule kuti chikhale chopereka choweyula kwa Yehova. 31 Wansembe atenthe mafutawo pa guwa koma chidalecho chikhale cha Aaroni ndi ana ake. 32 Mumupatse wansembe ntchafu ya kumanja ya nsembe yanu yachiyanjano kuti ikhale chopereka chanu kwa iye. 33 Mwana wa Aaroni amene amapereka magazi ndi mafuta a nsembe yachiyanjano, adzitenga ntchafu ya kumanja kukhala gawo lake. 34 Choncho pa zopereka zachiyanjano za Aisraeli, Ine ndatengapo chidale chomwe amaweyula ndi ntchafu zimene amapereka nsembe ndipo ndazipereka kwa wansembe Aaroni ndi ana ake. Izi ndizo gawo lawo nthawi zonse pa zopereka za Aisraeli.”

35 Zimenezi ndi chigawo cha Aaroni ndi ana ake chotapidwa pa zopereka kwa Yehova zoti zitenthedwe pa moto zimene zinaperekedwa pa tsiku limene anapatulidwa kuti akhale ansembe otumikira Yehova. 36 Yehova ndiye analamulira kuti pa zopereka za Aisraeli azitapapo zimenezi ndi kuwapatsa ansembe ngati gawo lawo. Yehovayo analamula zimenezi pa tsiku limene ansembewo anapatulidwa ndipo anachikhazikitsa ngati lamulo la nthawi zonse.

37 Awa ndi malamulo a nsembe izi: nsembe yopsereza, nsembe yachakudya, nsembe yopepesera machimo, nsembe yopepesera kupalamula, nsembe ya mwambo wodzoza ndi nsembe yachiyanjano. 38 Malamulo amenewa Yehova anapereka kwa Mose pa Phiri la Sinai pa tsiku limene Yehova analamulira Aisraeli kuti abwere ndi zopereka za kwa Yehova, ku chipululu cha Sinai kuja.

The Guilt Offering

“‘These are the regulations for the guilt offering,(A) which is most holy: The guilt offering is to be slaughtered in the place where the burnt offering is slaughtered, and its blood is to be splashed against the sides of the altar. All its fat(B) shall be offered: the fat tail and the fat that covers the internal organs, both kidneys with the fat on them near the loins, and the long lobe of the liver, which is to be removed with the kidneys.(C) The priest shall burn them on the altar(D) as a food offering presented to the Lord. It is a guilt offering. Any male in a priest’s family may eat it,(E) but it must be eaten in the sanctuary area; it is most holy.(F)

“‘The same law applies to both the sin offering[a](G) and the guilt offering:(H) They belong to the priest(I) who makes atonement with them.(J) The priest who offers a burnt offering for anyone may keep its hide(K) for himself. Every grain offering baked in an oven(L) or cooked in a pan(M) or on a griddle(N) belongs to the priest who offers it, 10 and every grain offering, whether mixed with olive oil or dry, belongs equally to all the sons of Aaron.

The Fellowship Offering

11 “‘These are the regulations for the fellowship offering anyone may present to the Lord:

12 “‘If they offer it as an expression of thankfulness, then along with this thank offering(O) they are to offer thick loaves(P) made without yeast(Q) and with olive oil mixed in, thin loaves(R) made without yeast and brushed with oil,(S) and thick loaves of the finest flour well-kneaded and with oil mixed in. 13 Along with their fellowship offering of thanksgiving(T) they are to present an offering with thick loaves of bread made with yeast.(U) 14 They are to bring one of each kind as an offering, a contribution to the Lord; it belongs to the priest who splashes the blood of the fellowship offering against the altar. 15 The meat of their fellowship offering of thanksgiving must be eaten on the day it is offered; they must leave none of it till morning.(V)

16 “‘If, however, their offering is the result of a vow(W) or is a freewill offering,(X) the sacrifice shall be eaten on the day they offer it, but anything left over may be eaten on the next day.(Y) 17 Any meat of the sacrifice left over till the third day must be burned up.(Z) 18 If any meat of the fellowship offering(AA) is eaten on the third day, the one who offered it will not be accepted.(AB) It will not be reckoned(AC) to their credit, for it has become impure; the person who eats any of it will be held responsible.(AD)

19 “‘Meat that touches anything ceremonially unclean must not be eaten; it must be burned up. As for other meat, anyone ceremonially clean may eat it. 20 But if anyone who is unclean(AE) eats any meat of the fellowship offering belonging to the Lord, they must be cut off from their people.(AF) 21 Anyone who touches something unclean(AG)—whether human uncleanness or an unclean animal or any unclean creature that moves along the ground[b]—and then eats any of the meat of the fellowship offering belonging to the Lord must be cut off from their people.’”

Eating Fat and Blood Forbidden

22 The Lord said to Moses, 23 “Say to the Israelites: ‘Do not eat any of the fat of cattle, sheep or goats.(AH) 24 The fat of an animal found dead or torn by wild animals(AI) may be used for any other purpose, but you must not eat it. 25 Anyone who eats the fat of an animal from which a food offering may be[c] presented to the Lord must be cut off from their people. 26 And wherever you live, you must not eat the blood(AJ) of any bird or animal. 27 Anyone who eats blood(AK) must be cut off from their people.’”

The Priests’ Share

28 The Lord said to Moses, 29 “Say to the Israelites: ‘Anyone who brings a fellowship offering to the Lord is to bring part of it as their sacrifice to the Lord. 30 With their own hands they are to present the food offering to the Lord; they are to bring the fat, together with the breast, and wave the breast before the Lord as a wave offering.(AL) 31 The priest shall burn the fat on the altar,(AM) but the breast belongs to Aaron and his sons.(AN) 32 You are to give the right thigh of your fellowship offerings to the priest as a contribution.(AO) 33 The son of Aaron who offers the blood and the fat of the fellowship offering shall have the right thigh as his share. 34 From the fellowship offerings of the Israelites, I have taken the breast that is waved and the thigh(AP) that is presented and have given them to Aaron the priest and his sons(AQ) as their perpetual share from the Israelites.’”

35 This is the portion of the food offerings presented to the Lord that were allotted to Aaron and his sons on the day they were presented to serve the Lord as priests. 36 On the day they were anointed,(AR) the Lord commanded that the Israelites give this to them as their perpetual share for the generations to come.

37 These, then, are the regulations for the burnt offering,(AS) the grain offering,(AT) the sin offering, the guilt offering, the ordination offering(AU) and the fellowship offering, 38 which the Lord gave Moses(AV) at Mount Sinai(AW) in the Desert of Sinai on the day he commanded the Israelites to bring their offerings to the Lord.(AX)

Footnotes

  1. Leviticus 7:7 Or purification offering; also in verse 37
  2. Leviticus 7:21 A few Hebrew manuscripts, Samaritan Pentateuch, Syriac and Targum (see 5:2); most Hebrew manuscripts any unclean, detestable thing
  3. Leviticus 7:25 Or offering is