Add parallel Print Page Options

Yesu Acheza ndi Mayi wa ku Samariya

Yesu atazindikira kuti Afarisi amva zoti Iye ankapeza ndi kubatiza ophunzira ambiri kupambana Yohane, (ngakhale kuti Yesuyo sankabatiza, koma ophunzira ake). Iye anachoka ku Yudeya ndi kubwereranso ku Galileya.

Ndipo Iye anayenera kudutsa mu Samariya. Iye anafika mʼmudzi wa Asamariya wotchedwa Sukari, pafupi ndi malo amene Yakobo anapatsa mwana wake Yosefe. Chitsime cha Yakobo chinali pamenepo ndipo Yesu atatopa ndi ulendo anakhala pansi pambali pa chitsimecho. Nthawi inali pafupifupi ora lachisanu ndi chimodzi masana.

Mayi wa Chisamariya atabwera kudzatunga madzi, Yesu anati kwa iye, “Kodi ungandipatse madzi akumwa.” (Ophunzira ake nʼkuti atapita mʼmudzi kukagula chakudya).

Mayiyo anati kwa Iye, “Inu ndinu Myuda ndipo ine ndine Msamariya. Bwanji mukundipempha madzi akumwa?” (Popeza Ayuda ndi Asamariya sankayanjana).

10 Yesu anamuyankha kuti, “Koma iwe ukanadziwa mphatso ya Mulungu ndi Iye amene akukupempha madzi akumwa, ukanamupempha ndipo akanakupatsa madzi amoyo.”

11 Mayiyo anati, “Ambuye, Inu mulibe kanthu kotungira madzi ndipo chitsime ndi chakuya. Kodi madzi amoyowo mungawatenge kuti? 12 Kodi Inu ndinu wamkulu kuposa kholo lathu Yakobo, amene anatipatsa chitsimechi ndipo iye ankamwanso monga anachita ana ake ndi ziweto zake?”

13 Yesu anayankha kuti, “Aliyense amene amamwa madzi awa amamvanso ludzu, 14 koma aliyense amene adzamwa madzi amene Ine ndidzamupatsa sadzamvanso ludzu. Ndithudi, madzi amene ndidzamupatsa adzakhala kasupe wamadzi wotumphukira ku moyo wosatha.”

Read full chapter