Add parallel Print Page Options

Kaini ndi Abele

Adamu anagona malo amodzi ndi Hava mkazi wake ndipo mkaziyo anakhala woyembekezera nabala Kaini, ndipo anati, “Ndi thandizo la Yehova ndapeza mwana wamwamuna.” Kenaka anabereka mʼbale wake Abele.

Abele anali woweta nkhosa ndipo Kaini anali mlimi. Patapita nthawi, Kaini anatenga zipatso za ku munda nakazipereka kwa Yehova monga nsembe. Nayenso Abele anatenga ana ankhosa oyamba kubadwa pamodzi ndi mafuta ake nakazipereka ngati nsembe kwa Yehova. Yehova anakondwera ndi Abele ndi nsembe yake. Koma sanakondwere ndi Kaini ndi nsembe yake. Kotero Kaini anakwiya kwambiri ndipo nkhope yake inagwa.

Choncho Yehova anati kwa Kaini, “Chifukwa chiyani wakwiya ndipo bwanji nkhope yako yagwa? Ukanachita zabwino sindikanakulandira kodi? Koma tsopano wachita zoyipa ndipo tchimo likukudikira pa khomo pako, likufuna kukugwira; koma iwe uyenera kugonjetsa tchimolo.”

Tsiku lina Kaini anati kwa mʼbale wake Abele, “Tiye tipite ku munda.” Ndipo ali ku mundako, Kaini anawukira mʼbale wake namupha.

Ndipo Yehova anamufunsa Kaini kuti, “Ali kuti mʼbale wako Abele?”

Iye anayankha kuti, “Sindikudziwa. Kodi ine ndine wosunga mʼbale wanga?”

10 Yehova anati, “Kodi wachita chiyani? Tamvera! Magazi a mʼbale wako akulirira kwa Ine kuchokera mʼnthaka. 11 Ndipo tsopano ndiwe wotembereredwa ndipo wachotsedwa mʼdziko limene nthaka yake inatsekula pakamwa pake kulandira magazi a mʼbale wako amene unakhetsa. 12 Udzalima munda koma nthakayo sidzakupatsanso zokolola zake. Udzakhala wosakhazikika; womangoyendayenda pa dziko lapansi.”

13 Kaini anati kwa Yehova, “Chilango changa ndi chachikulu kuposera mphamvu zanga. 14 Lero mukundipirikitsa pa dziko ndi pamaso panu; ndidzakhala wosakhazikika, woyendayenda, ndipo aliyense amene adzandipeze adzandipha.”

15 Koma Yehova anamuwuza kuti, “Sizidzatero ayi; aliyense amene adzaphe Kaini adzalangidwa ndi kulipiritsidwa kasanu ndi kawiri.” Pamenepo Yehova anayika chizindikiro pa Kaini kuti aliyense womupeza asamuphe. 16 Ndipo Kaini anachoka pamaso pa Yehova nakakhala ku dziko la Nodi, kummawa kwa Edeni.

Banja la Kaini

17 Kaini anagona malo amodzi ndi mkazi wake ndipo mkaziyo anakhala woyembekezera nabala Enoki. Kaini nthawi imeneyo nʼkuti akumanga mzinda ndipo anawutcha dzina la mwana wake Enoki. 18 Enoki anabereka Iradi; Iradi anabereka Mehuyaeli, ndipo Mehuyaeli anabereka Metusela, ndipo Metusela anabereka Lameki.

19 Lameki anakwatira akazi awiri, wina dzina lake linali Ada ndi winayo dzina lake linali Zila. 20 Ada anabereka Yabala; iyeyu anali kholo la onse okhala mʼmatenti ndi oweta ziweto. 21 Dzina la mʼbale wake linali Yubala; iyeyu anali kholo la onse oyimba zeze ndi chitoliro. 22 Zila nayenso anali ndi mwana wamwamuna, dzina lake Tubala-Kaini. Iyeyu anali kholo la amisiri onse osula zida za mkuwa ndi chitsulo. Mlongo wake wa Tubala-Kaini anali Naama.

23 Lameki anawuza akazi akewo kuti,

“Ada ndi Zila, ndimvereni;
    inu akazi anga imvani mawu anga.
Ine ndinapha munthu chifukwa anandipweteka.
    Ndinapha mnyamatayo chifukwa anandimenya.
24 Ngati wopha Kaini amulipsira kasanu nʼkawiri,
    ndiye kuti wopha ine Lameki adzamulipsira kokwanira 77.”

25 Adamu anagonanso malo amodzi ndi mkazi wake, ndipo anabereka mwana wamwamuna namutcha Seti, kutanthauza kuti, “Mulungu wandipatsa mwana wina mʼmalo mwa Abele, popeza Kaini anamupha.” 26 Seti naye anali ndi mwana wa mwamuna, ndipo anamutcha Enosi.

Pa nthawi imeneyi anthu anayamba kupemphera mʼdzina la Yehova.

Caín y Abel

Adán conoció a Eva, su mujer, y ella concibió y dio a luz a Caín, y dijo: «Por la voluntad del Señor he adquirido[a] un varón.» Después dio a luz a Abel, hermano de Caín. Abel era pastor de ovejas, y Caín cultivaba la tierra. Andando el tiempo, sucedió que Caín llevó al Señor una ofrenda del fruto de la tierra. Y Abel también llevó algunos de los primogénitos de sus ovejas, de los mejores entre ellas. Y el Señor miró con agrado a Abel y a su ofrenda,(A) pero no miró con agrado a Caín ni a su ofrenda. Y Caín se enojó mucho, y decayó su semblante. Entonces el Señor le dijo a Caín:

«¿Por qué estás enojado? ¿Por qué ha decaído tu semblante? Si haces lo bueno, ¿acaso no serás enaltecido? Pero, si no lo haces, el pecado está listo para dominarte. Sin embargo, su deseo lo llevará a ti, y tú lo dominarás.»[b]

Dijo entonces Caín a su hermano Abel: «Vayamos al campo.» Y sucedió que, mientras estaban ellos en el campo, Caín se levantó contra su hermano Abel, y lo mató.(B) Y el Señor le dijo a Caín:

«¿Dónde está tu hermano Abel?»

Y él respondió:

«No lo sé. ¿Acaso soy yo el guardián de mi hermano?»

10 Y el Señor le dijo:

«¿Qué es lo que has hecho? Desde la tierra, la voz de la sangre de tu hermano me pide que le haga justicia. 11 Ahora, pues, ¡maldito serás por parte de la tierra, que abrió su boca para recibir de tus manos la sangre de tu hermano! 12 Cuando labres la tierra, no te volverá a dar su fuerza. Y andarás por la tierra errante y extranjero.»

13 Caín le dijo al Señor:

«Mi castigo es muy grande para poder soportarlo. 14 Tú me echas hoy de la tierra, y tendré que esconderme de tu presencia. Errante y extranjero andaré por la tierra, y sucederá que cualquiera que me encuentre, me matará.»

15 Pero el Señor le respondió:

«Pues cualquiera que mate a Caín será castigado siete veces.»

Y el Señor puso en Caín una señal, para que cualquiera que lo encontrara no lo matara.

16 Caín salió de la presencia del Señor y habitó en la tierra de Nod,[c] al oriente de Edén. 17 Y conoció Caín a su mujer, y ella concibió y dio a luz a Enoc. Entonces edificó una ciudad, y llamó a esa ciudad Enoc, como el nombre de su hijo. 18 Y a Enoc le nació Irad. Irad engendró a Mejuyael, Mejuyael engendró a Metusael, y Metusael engendró a Lamec. 19 Y Lamec tomó para sí dos mujeres; una de ellas se llamaba Ada; la otra, Silá. 20 Ada dio a luz a Jabal, que fue el padre de los que habitan en tiendas y crían ganados. 21 El nombre de su hermano era Jubal, que fue el padre de todos los que tocan arpa y flauta. 22 También Silá dio a luz a Tubal Caín, artífice de toda obra de bronce y de hierro; y la hermana de Tubal Caín fue Noamá.

23 Dijo entonces Lamec a sus mujeres:

«Ada y Silá, escuchen mi voz;
Mujeres de Lamec, atiendan mis palabras.
Si soy herido, mataré a un varón;
Si soy golpeado, mataré a un joven.
24 Y si Caín será vengado siete veces,
Lamec será vengado setenta veces siete.»

25 Adán conoció de nuevo a su mujer, y ella dio a luz un hijo, al que puso por nombre Set,[d] pues dijo: «Dios me ha dado otro hijo en lugar de Abel, a quien mató Caín.» 26 También a Set le nació un hijo, al que puso por nombre Enós. Desde entonces comenzó a invocarse el nombre del Señor.

Footnotes

  1. Génesis 4:1 Heb. qanah, adquirir.
  2. Génesis 4:7 O, a ti quedará sujeto.
  3. Génesis 4:16 Es decir, Errante.
  4. Génesis 4:25 Es decir, Sustitución.

Cain and Abel

Adam[a] made love to his wife(A) Eve,(B) and she became pregnant and gave birth to Cain.[b](C) She said, “With the help of the Lord I have brought forth[c] a man.” Later she gave birth to his brother Abel.(D)

Now Abel kept flocks, and Cain worked the soil.(E) In the course of time Cain brought some of the fruits of the soil as an offering(F) to the Lord.(G) And Abel also brought an offering—fat portions(H) from some of the firstborn of his flock.(I) The Lord looked with favor on Abel and his offering,(J) but on Cain and his offering he did not look with favor. So Cain was very angry, and his face was downcast.

Then the Lord said to Cain, “Why are you angry?(K) Why is your face downcast? If you do what is right, will you not be accepted? But if you do not do what is right, sin is crouching at your door;(L) it desires to have you, but you must rule over it.(M)

Now Cain said to his brother Abel, “Let’s go out to the field.”[d] While they were in the field, Cain attacked his brother Abel and killed him.(N)

Then the Lord said to Cain, “Where is your brother Abel?”(O)

“I don’t know,(P)” he replied. “Am I my brother’s keeper?”

10 The Lord said, “What have you done? Listen! Your brother’s blood cries out to me from the ground.(Q) 11 Now you are under a curse(R) and driven from the ground, which opened its mouth to receive your brother’s blood from your hand. 12 When you work the ground, it will no longer yield its crops for you.(S) You will be a restless wanderer(T) on the earth.(U)

13 Cain said to the Lord, “My punishment is more than I can bear. 14 Today you are driving me from the land, and I will be hidden from your presence;(V) I will be a restless wanderer on the earth,(W) and whoever finds me will kill me.”(X)

15 But the Lord said to him, “Not so[e]; anyone who kills Cain(Y) will suffer vengeance(Z) seven times over.(AA)” Then the Lord put a mark on Cain so that no one who found him would kill him. 16 So Cain went out from the Lord’s presence(AB) and lived in the land of Nod,[f] east of Eden.(AC)

17 Cain made love to his wife,(AD) and she became pregnant and gave birth to Enoch. Cain was then building a city,(AE) and he named it after his son(AF) Enoch. 18 To Enoch was born Irad, and Irad was the father of Mehujael, and Mehujael was the father of Methushael, and Methushael was the father of Lamech.

19 Lamech married(AG) two women,(AH) one named Adah and the other Zillah. 20 Adah gave birth to Jabal; he was the father of those who live in tents and raise livestock. 21 His brother’s name was Jubal; he was the father of all who play stringed instruments(AI) and pipes.(AJ) 22 Zillah also had a son, Tubal-Cain, who forged(AK) all kinds of tools out of[g] bronze and iron. Tubal-Cain’s sister was Naamah.

23 Lamech said to his wives,

“Adah and Zillah, listen to me;
    wives of Lamech, hear my words.
I have killed(AL) a man for wounding me,
    a young man for injuring me.
24 If Cain is avenged(AM) seven times,(AN)
    then Lamech seventy-seven times.(AO)

25 Adam made love to his wife(AP) again, and she gave birth to a son and named him Seth,[h](AQ) saying, “God has granted me another child in place of Abel, since Cain killed him.”(AR) 26 Seth also had a son, and he named him Enosh.(AS)

At that time people began to call on[i] the name of the Lord.(AT)

Footnotes

  1. Genesis 4:1 Or The man
  2. Genesis 4:1 Cain sounds like the Hebrew for brought forth or acquired.
  3. Genesis 4:1 Or have acquired
  4. Genesis 4:8 Samaritan Pentateuch, Septuagint, Vulgate and Syriac; Masoretic Text does not have “Let’s go out to the field.”
  5. Genesis 4:15 Septuagint, Vulgate and Syriac; Hebrew Very well
  6. Genesis 4:16 Nod means wandering (see verses 12 and 14).
  7. Genesis 4:22 Or who instructed all who work in
  8. Genesis 4:25 Seth probably means granted.
  9. Genesis 4:26 Or to proclaim

And Adam knew Eve his wife; and she conceived, and bare Cain, and said, I have gotten a man from the Lord.

And she again bare his brother Abel. And Abel was a keeper of sheep, but Cain was a tiller of the ground.

And in process of time it came to pass, that Cain brought of the fruit of the ground an offering unto the Lord.

And Abel, he also brought of the firstlings of his flock and of the fat thereof. And the Lord had respect unto Abel and to his offering:

But unto Cain and to his offering he had not respect. And Cain was very wroth, and his countenance fell.

And the Lord said unto Cain, Why art thou wroth? and why is thy countenance fallen?

If thou doest well, shalt thou not be accepted? and if thou doest not well, sin lieth at the door. And unto thee shall be his desire, and thou shalt rule over him.

And Cain talked with Abel his brother: and it came to pass, when they were in the field, that Cain rose up against Abel his brother, and slew him.

And the Lord said unto Cain, Where is Abel thy brother? And he said, I know not: Am I my brother's keeper?

10 And he said, What hast thou done? the voice of thy brother's blood crieth unto me from the ground.

11 And now art thou cursed from the earth, which hath opened her mouth to receive thy brother's blood from thy hand;

12 When thou tillest the ground, it shall not henceforth yield unto thee her strength; a fugitive and a vagabond shalt thou be in the earth.

13 And Cain said unto the Lord, My punishment is greater than I can bear.

14 Behold, thou hast driven me out this day from the face of the earth; and from thy face shall I be hid; and I shall be a fugitive and a vagabond in the earth; and it shall come to pass, that every one that findeth me shall slay me.

15 And the Lord said unto him, Therefore whosoever slayeth Cain, vengeance shall be taken on him sevenfold. And the Lord set a mark upon Cain, lest any finding him should kill him.

16 And Cain went out from the presence of the Lord, and dwelt in the land of Nod, on the east of Eden.

17 And Cain knew his wife; and she conceived, and bare Enoch: and he builded a city, and called the name of the city, after the name of his son, Enoch.

18 And unto Enoch was born Irad: and Irad begat Mehujael: and Mehujael begat Methusael: and Methusael begat Lamech.

19 And Lamech took unto him two wives: the name of the one was Adah, and the name of the other Zillah.

20 And Adah bare Jabal: he was the father of such as dwell in tents, and of such as have cattle.

21 And his brother's name was Jubal: he was the father of all such as handle the harp and organ.

22 And Zillah, she also bare Tubalcain, an instructer of every artificer in brass and iron: and the sister of Tubalcain was Naamah.

23 And Lamech said unto his wives, Adah and Zillah, Hear my voice; ye wives of Lamech, hearken unto my speech: for I have slain a man to my wounding, and a young man to my hurt.

24 If Cain shall be avenged sevenfold, truly Lamech seventy and sevenfold.

25 And Adam knew his wife again; and she bare a son, and called his name Seth: For God, said she, hath appointed me another seed instead of Abel, whom Cain slew.

26 And to Seth, to him also there was born a son; and he called his name Enos: then began men to call upon the name of the Lord.