Add parallel Print Page Options

Za Chilango cha Edomu

35 Yehova anandiyankhula kuti: “Iwe mwana wa munthu, yangʼana phiri la Seiri; yankhula moliyimba mlandu ndipo awawuze anthu a kumeneko kuti zimene ndikuyankhula Ine Ambuye Yehova ndi izi: Inu anthu a ku mapiri a Seiri ndikudana nanu. Ndidzatambasula dzanja langa kulimbana nanu, ndipo ndidzasandutsa dziko lanu kukhala chipululu. Mizinda yanu ndidzayisandutsa mabwinja, ndipo dziko lanu lidzasanduka chipululu. Zikadzachitika izi mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

“Munali adani a Israeli nthawi zonse, ndipo munkalola kuti Aisraeli aphedwe pa nkhondo pa nthawi ya mavuto awo, pa nthawi imene chilango chawo chinafika pachimake. Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: Pali Ine wamoyo, ndithu ndidzakukanthani. Imfa idzakulondolani. Popeza sunadane nako kukhetsa magazi, imfa idzakulondola. Phiri la Seiri ndidzalisandutsa chipululu ndipo ndidzapha onse amene amapita nabwerera kumeneko. Ndidzaza mapiri ake ndi mitembo. Ophedwa pa nkhondo adzagwera pa zitunda zanu, zigwa zanu ndi mʼmitsinje yanu yonse. Ndidzasandutsa dziko lanu kukhala chipululu mpaka muyaya, ndipo mʼmizinda yanu simudzakhalanso anthu. Zikadzachitika izi mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

10 “Inu munanena kuti, ‘Mitundu iwiri iyi ya anthu, Yuda ndi Israeli, pamodzi ndi mayiko awo omwe idzakhala yathu.’ Munanena chomwechi ngakhale kuti Ine Yehova ndinali momwemo. 11 Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: Pali Ine wamoyo, ndithu ndidzachita nanu monga munachita ndi anthu a ku Yuda ndi Israeli poonetsa mkwiyo wanu, nsanje yanu ndi chidani chanu pa iwo. Ndikadzakulangani mudzandidziwadi pakati panupo. 12 Ndipo mudzadziwa kuti Ine Yehova ndinamva mawu anu onse onyoza amene munanena molimbana ndi mapiri a Israeli. Inu munati, ‘Mapiri a Israeli asanduka bwinja, ndipo aperekedwa kwa ife kuti tiwawononge.’ 13 Mawu anu amene munayankhula monyada kundinyoza Ine ndinawamva. 14 Ine Ambuye Yehova ndikuti: Dziko lonse lapansi lidzasangalala pamene ndidzakusandutsani bwinja. 15 Monga momwe inu munasangalala pamene anthu anga Aisraeli anagwa, Inenso ndidzakuchitani chimodzimodzi. Udzasanduka bwinja, iwe Phiri la Seiri, iwe ndi dziko lonse la Edomu. Zikadzatero anthu onse adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”

A Prophecy Against Edom

35 The word of the Lord came to me: “Son of man, set your face against Mount Seir;(A) prophesy against it and say: ‘This is what the Sovereign Lord says: I am against you, Mount Seir, and I will stretch out my hand(B) against you and make you a desolate waste.(C) I will turn your towns into ruins(D) and you will be desolate. Then you will know that I am the Lord.(E)

“‘Because you harbored an ancient hostility and delivered the Israelites over to the sword(F) at the time of their calamity,(G) the time their punishment reached its climax,(H) therefore as surely as I live, declares the Sovereign Lord, I will give you over to bloodshed(I) and it will pursue you.(J) Since you did not hate bloodshed, bloodshed will pursue you. I will make Mount Seir a desolate waste(K) and cut off from it all who come and go.(L) I will fill your mountains with the slain; those killed by the sword will fall on your hills and in your valleys and in all your ravines.(M) I will make you desolate forever;(N) your towns will not be inhabited. Then you will know that I am the Lord.(O)

10 “‘Because you have said, “These two nations and countries will be ours and we will take possession(P) of them,” even though I the Lord was there, 11 therefore as surely as I live, declares the Sovereign Lord, I will treat you in accordance with the anger(Q) and jealousy you showed in your hatred of them and I will make myself known among them when I judge you.(R) 12 Then you will know that I the Lord have heard all the contemptible things you have said against the mountains of Israel. You said, “They have been laid waste and have been given over to us to devour.(S) 13 You boasted(T) against me and spoke against me without restraint, and I heard it.(U) 14 This is what the Sovereign Lord says: While the whole earth rejoices, I will make you desolate.(V) 15 Because you rejoiced(W) when the inheritance of Israel became desolate, that is how I will treat you. You will be desolate, Mount Seir,(X) you and all of Edom.(Y) Then they will know that I am the Lord.’”