Eksodo 34:1-4
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Miyala ina Yatsopano
34 Yehova anati kwa Mose, “Sema miyala iwiri yofanana ndi yoyamba ija, ndipo Ine ndidzalembapo mawu amene anali pa miyala yoyamba ija, imene unayiphwanya. 2 Ukonzeke mmamawa, ndipo ubwere ku Phiri la Sinai. Udzaonekera pamaso panga pamwamba pa phiri. 3 Palibe amene abwere nawe kapena kuoneka pena paliponse pafupi ndi phiri. Ndipo ngakhale nkhosa kapena ngʼombe zisadye mʼmbali mwa phirilo.”
4 Choncho Mose anasema miyala iwiri yofanana ndi yoyamba ija ndipo anapita ku Phiri la Sinai mmawa atanyamula miyala iwiri mʼmanja mwake monga momwe Yehova anamulamulira.
Read full chapterThe Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.