Add parallel Print Page Options

Mose Adalitsa Mafuko a Aisraeli

33 Awa ndi madalitso amene Mose, munthu wa Mulungu, anawapereka kwa Aisraeli asanafe. Iye anati:

“Yehova anabwera kuchokera ku Sinai
    ndipo anatulukira kuchokera ku Seiri;
    anawala kuchokera pa Phiri la Parani.
Iye anabwera ndi chiwunyinji cha angelo
    kuchokera kummwera, moto woyaka uli mʼdzanja mwake.
Ndithu ndinu amene mumakonda anthu anu;
    opatulika ake onse ali mʼmanja mwake.
Onse amagwada pansi pa mapazi anu
    kuchokera kwa inu amalandira malangizo,
malamulo amene Mose anatipatsa,
    chuma chopambana cha mtundu wa Yakobo.
Iye anali mfumu ya Yesuruni
    pamene atsogoleri a anthu anasonkhana,
    pamodzi ndi mafuko a Israeli.

“Lolani Rubeni akhale ndi moyo ndipo asafe,
    anthu ake asachepe pa chiwerengero.”

Ndipo ponena za Yuda anati:

“Inu Yehova, imvani kulira kwa Yuda;
    mubweretseni kwa anthu ake.
Ndi manja ake omwe adziteteze yekha.
    Inu khalani thandizo lake polimbana ndi adani ake!”

Za fuko la Alevi anati:

“Tumimu wanu ndi Urimu ndi za
    mtumiki wanu wokhulupirika.
Munamuyesa ku Masa;
    munalimbana naye ku madzi a ku Meriba.
Iye ananena za abambo ake ndi amayi ake kuti,
    ‘Sindilabadira za iwo.’
Sanasamale za abale ake
    kapena ana ake,
koma anayangʼanira mawu anu
    ndipo anateteza pangano lanu.
10 Iye amaphunzitsa Yakobo malangizo anu
    ndi malamulo anu kwa Israeli.
Amafukiza lubani pamaso panu
    ndiponso amapereka nsembe zanu zonse zopsereza pa guwa lanu.
11 Inu Yehova, dalitsani luso lake lonse
    ndipo mukondwere ndi ntchito za manja ake.
Menyani adani awo mʼchiwuno
    kanthani amene amuwukira kuti asadzukenso.”

12 Za fuko la Benjamini anati:

“Wokondedwa wa Yehova akhale mwamtendere mwa Iye,
    pakuti amamuteteza tsiku lonse,
    ndipo amene Yehova amamukonda amawusa pa mapewa ake.”

13 Za fuko la Yosefe anati:

“Yehova adalitse dziko lake
    ndi mame ambiri ochokera kumwamba
    ndiponso madzi ambiri ochokera pansi pa nthaka;
14 ndi zinthu zambiri zimene zimacha ndi dzuwa
    ndiponso ndi zokolola zabwino kwambiri zimene zimacha ndi mwezi uliwonse;
15 ndi zipatso zabwino kwambiri zochokera mʼmapiri amakedzanawa
    ndiponso zokolola zochuluka zochokera ku zitunda zakalekale;
16 ndi mphatso zabwino kwambiri zochokera pa dziko lapansi ndi zonse zimene zili mʼmenemo
    ndiponso kukoma mtima kwa Iye amene amakhala mʼchitsamba choyaka moto.
Madalitso onsewa akhale pa mutu pa Yosefe,
    wapaderadera pakati pa abale ake.
17 Ulemerero wake uli ngati ngʼombe yayimuna yoyamba kubadwa;
    nyanga zake zili ngati za njati.
Ndi nyanga zakezo adzapirikitsa anthu a mitundu ina,
    ngakhale iwo amene akukhala ku malekezero a dziko lapansi.
Nyanga zimenezi ndiye anthu miyandamiyanda a Efereimu;
    nyanga zimenezi ndiye anthu 1,000 a Manase.”

18 Za fuko la Zebuloni anati:

“Kondwera Zebuloni, pamene ukutuluka,
    ndipo iwe, Isakara, kondwera mʼmatenti ako.
19 Adzayitanira mitundu ya anthu kumapiri,
    kumeneko adzaperekako nsembe zachilungamo;
kumeneko adzadyerera zinthu zochuluka zochokera ku nyanja,
    chuma chobisika mu mchenga.”

20 Za fuko la Gadi anati:

“Wodala amene amakulitsa malire a Gadi!
    Gadi amakhala kumeneko ngati mkango,
    kukhadzula mkono kapena mutu.
21 Iye anadzisankhira dziko labwino kwambiri;
    gawo la mtsogoleri anasungira iye.
Pamene atsogoleri a anthu anasonkhana,
    anachita chifuniro cha Yehova molungama,
    ndiponso malamulo onena za Israeli.”

22 Za fuko la Dani anati:

“Dani ndi mwana wamkango,
    amene akutuluka ku Basani.”

23 Za fuko la Nafutali anati:

“Nafutali wadzaza ndi kukoma mtima kwa Yehova
    ndipo ndi wodzaza ndi madalitso ake;
    cholowa chake chidzakhala mbali ya kummwera kwa nyanja.”

24 Za fuko la Aseri anati:

“Mwana wodalitsika kwambiri ndi Aseri;
    abale ake amukomere mtima,
    ndipo asambe mapazi ake mʼmafuta.
25 Zotsekera za zipata zako zidzakhala za chitsulo ndi za mkuwa,
    ndi mphamvu zako zidzakhala ngati masiku a moyo wako.

26 “Palibe wina wofanana ndi Mulungu wa Yesuruni,
    amene amakwera pa thambo kukuthandizani
    ndiponso pa mitambo ya ulemerero wake.
27 Mulungu wamuyaya ndiye pothawirapo pathu,
    ndipo pa dziko lapansi amakusungani ndi mphamvu zosatha.
Adzathamangitsa patsogolo panu mdani wanu,
    adzanena kuti, ‘Muwonongeni!’
28 Motero Israeli adzakhala yekha mwamtendere;
    zidzukulu za Yakobo zili pa mtendere
mʼdziko la tirigu ndi vinyo watsopano,
    kumene thambo limagwetsa mame.
29 Iwe Israeli, ndiwe wodala!
    Wofanana nanu ndani
    anthu opulumutsidwa ndi Yehova?
Iye ndiye chishango ndi mthandizi wanu
    ndi lupanga lanu la ulemerero.
Adani ako adzakugonjera,
    ndipo iwe udzapondereza pansi malo awo achipembedzo.”