1 Mafumu 1-2
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Adoniya Adziyika Kukhala Mfumu
1 Mfumu Davide atakalamba sankamva kufunda ngakhale akamufunditsa mabulangeti. 2 Choncho nduna zake zinamuwuza kuti, “Tiloleni tifune namwali woti azikhala nanu ndi kumakusamalirani. Namwaliyo azigona pafupi nanu kuti mbuye wathu mfumu muzimva kufundira.”
3 Kotero anafunafuna mʼdziko lonse la Israeli mtsikana wokongola ndipo anapeza Abisagi wa ku Sunemu, nabwera naye kwa mfumu. 4 Mtsikanayo anali wokongola kwambiri ndipo ankasamalira mfumu ndi kumayitumikira, koma mfumuyo sinakhale naye malo amodzi.
5 Nthawi imeneyi Adoniya, mwana wa Hagiti, anayamba kudzitukumula ndipo anati, “Ndidzakhala mfumu ndine.” Choncho anadzikonzera galeta ndi akavalo, pamodzi ndi anthu 50 woti azithamanga patsogolo pake. 6 (Abambo ake sanalowererepo nʼkamodzi komwe ndipo sanafunsepo kuti, “Nʼchifukwa chiyani ukuchita zimenezi?” Adoniyayo anali wokongola kwambiri ndipo anali wopondana ndi Abisalomu).
7 Adoniya anagwirizana ndi Yowabu mwana wa Zeruya ndiponso Abiatara wansembe, ndipo iwowa anamuthandiza. 8 Koma Zadoki wansembe, Benaya mwana wa Yehoyada, mneneri Natani, Simei ndi Rei ndiponso asilikali amphamvu a Davide sanamutsate Adoniya uja.
9 Kenaka Adoniya anapereka nsembe za nkhosa ndi ngʼombe ndiponso ana angʼombe onenepa ku Mwala wa Zohereti kufupi ndi Eni Rogeli. Iye anayitana abale ake onse, ana aamuna a mfumu ndiponso akuluakulu onse a ku Yuda, 10 koma sanayitane mneneri Natani kapena Benaya kapenanso asilikali amphamvu a Davide ngakhalenso mʼbale wake Solomoni.
11 Pamenepo Natani anafunsa Batiseba, amayi ake a Solomoni, kuti, “Kodi simunamve kuti Adoniya, mwana wa Hagiti, walowa ufumu popanda Davide mbuye wathu kudziwa? 12 Tsopano ine ndikulangizeni inu mmene mungapulumutsire moyo wanu ndi moyo wa mwana wanu Solomoni. 13 Pitani msanga kwa Mfumu Davide ndipo mukanene kuti, ‘Mbuye wanga mfumu, kodi simunalumbire kwa ine mdzakazi wanu kuti, ‘Ndithu mwana wako Solomoni ndiye adzakhale mfumu mʼmalo mwanga, ndipo adzakhala pa mpando wanga waufumu?’ Nanga nʼchifukwa chiyani Adoniya walowa ufumu?’ 14 Pamene inu muzikayankhula ndi mfumu, ine ndidzalowa ndi kuchitira umboni mawu anuwo.”
15 Choncho Batiseba anapita nakalowa ku chipinda kukaonana ndi mfumu imene inali itakalamba kwambiri, kumene Abisagi wa ku Sunemu uja ankayisamalira. 16 Batiseba anagwada nalambira mfumu.
Mfumu inamufunsa kuti, “Kodi nʼchiyani chimene ukufuna?”
17 Iye anayankha kuti, “Mbuye wanga, inu mwini munalumbira kwa ine mdzakazi wanu mʼdzina la Yehova Mulungu wanu kuti, ‘Solomoni mwana wako ndiye adzakhale mfumu mʼmalo mwa ine, ndipo adzakhala pa mpando wanga waufumu.’ 18 Koma tsopano Adoniya ndiye walowa ufumu, ndipo inu mbuye wanga mfumu, simukuzidziwa zimenezi. 19 Ndipo wapereka nsembe ngʼombe zambiri, ana angʼombe onenepa ndi nkhosa ndi mbuzi ndipo wayitana ana anu onse, wansembe Abiatara ndiponso Yowabu mkulu wa ankhondo, koma sanayitane kapolo wanu Solomoni. 20 Mbuye wanga mfumu, maso a Aisraeli onse ali pa inu, kuti adziwe kuchokera kwa inu amene adzakhala pa mpando waufumu wa mbuye wanga mʼmalo mwanu. 21 Mukapanda kutero, mbuye wanga, mukadzangotisiya nʼkulondola kumene kunapita makolo anu, ine pamodzi ndi mwana wangayu Solomoni adzatiyesa owukira.”
22 Pamene Batiseba amayankhula ndi mfumu, mneneri Natani analowa. 23 Ndipo anthu anawuza mfumu kuti, “Kwabwera mneneri Natani.” Kotero iye anafika pamaso pa mfumu ndipo anawerama nagunditsa nkhope yake pansi.
24 Natani anafunsa kuti, “Mbuye wanga mfumu, kodi mwalengeza kuti Adoniya adzakhala mfumu mʼmalo mwanu, ndi kuti adzakhala pa mpando wanu waufumu? 25 Lero lomwe lino wakapereka nsembe ngʼombe zambiri, ana angʼombe onenepa ndiponso nkhosa ndi mbuzi. Iye wayitana ana anu onse, atsogoleri a nkhondo, ndiponso wansembe Abiatara. Panopa onsewa akudya ndi kumwa naye ndipo akunena kuti, ‘Akhale ndi moyo wautali mfumu Adoniya!’ 26 Koma ine kapolo wanu, wansembe Zadoki ndi Benaya mwana wa Yehoyada, ndiponso kapolo wanu Solomoni sanatiyitane. 27 Kodi zimenezi mbuye wanga mfumu mwazichita ndinu, osawawuza atumiki anu kuti adziwe amene adzakhale pa mpando waufumu mʼmalo mwanu?”
Davide Alonga Ufumu Solomoni
28 Pamenepo mfumu Davide anati, “Muyitaneni Batiseba.” Kotero Batiseba analowa ndipo anayimirira pamaso pa mfumu.
29 Tsono mfumu inalumbira kuti, “Pali Yehova wamoyo, amene anandipulumutsa ine ku mavuto onse, 30 ndithu ine lero ndichita zonse zimene ndinalumbira kwa Yehova Mulungu wa Israeli kuti, mwana wako Solomoni adzakhala mfumu mʼmalo mwanga ndipo adzakhala pa mpando wanga waufumu.”
31 Pamenepo Batiseba anawerama, nagunditsa mutu wake pansi nalambira mfumu, ndipo anati, “Mbuye wanga Mfumu Davide mukhale ndi moyo wautali!”
32 Mfumu Davide anati, “Ndiyitanireni wansembe Zadoki, mneneri Natani ndi Benaya mwana wa Yehoyada.” Atafika pamaso pa mfumu, 33 mfumuyo inati kwa iwo, “Tengani atumiki anga ndipo mukweze mwana wanga Solomoni pa bulu wanga ndipo mupite naye ku Gihoni. Mukalize lipenga ndi kufuwula kuti, ‘Akhale ndi moyo wautali mfumu Solomoni!’ 34 Kumeneko Zadoki wansembe ndi mneneri Natani akamudzoze kuti akhale mfumu ya Israeli. Kenaka mukalize lipenga ndi kumanena kuti ‘Akhale ndi moyo wautali Mfumu Solomoni.’ 35 Ndipo pobwera muzikamutsata pambuyo. Iyeyo akabwere kuno ndi kudzakhala pa mpando wanga waufumu ndi kudzalamulira mʼmalo mwanga. Ndamusankha kukhala wolamulira Israeli ndi Yuda.”
36 Benaya mwana wa Yehoyada anayankha mfumu kuti, “Ameni! Yehova Mulungu wa mbuye wanga mfumu akhazikitse kuti zichitike motero. 37 Monga momwe Yehova wakhalira ndi inu mbuye wanga mfumu, momwemonso akhale ndi Solomoni ndi kukhazikitsa ufumu wake kuti ukhale waukulu kuposa ufumu wa mbuye wanga Mfumu Davide!”
38 Kotero Zadoki wansembe, mneneri Natani, Benaya mwana wa Yehoyada, Akereti ndiponso Apeleti, anthu oteteza mfumu, anapita kukamukweza Solomoni pa bulu wa Mfumu Davide ndi kupita naye ku Gihoni. 39 Wansembe Zadoki anatenga nyanga ya mafuta yochokera ku malo opatulika ndi kumudzoza Solomoni. Kenaka analiza lipenga ndipo anthu onse anafuwula kuti, “Akhale ndi moyo wautali Mfumu Solomoni!” 40 Ndipo anthu onsewo anapita namutsatira pambuyo akuyimba zitoliro ndi kukondwerera kwambiri, kotero nthaka inagwedezeka chifukwa cha phokoso lawo.
41 Adoniya pamodzi ndi anthu onse oyitanidwa amene anali naye anamva zimenezi pamene ankamaliza madyerero awo. Atamva kulira kwa malipenga, Yowabu anafunsa kuti, “Kodi phokoso lonselo mu mzindamo likutanthauza chiyani?”
42 Iye akuyankhula, Yonatani mwana wa wansembe Abiatara anafika. Adoniya anati, “Lowa. Munthu wabwino ngati iwe ayenera kubweretsa nkhani yabwino.”
43 Yonatani anayankha Adoniya kuti, “Ayi ndithu, zinthu sizili bwino! Mbuye wathu Mfumu Davide walonga Solomoni ufumu. 44 Mfumu yatuma Zadoki wansembe, mneneri Natani, Benaya mwana wa Yehoyada, Akereti ndi Apeleti ku Gihoni ndipo iwo amukweza pa bulu wa mfumu, 45 ndipo Zadoki wansembe ndi mneneri Natani adzoza Solomoni ku Gihoni kuti akhale mfumu. Ndipo kuchokera kumeneko akhala akululutira, kotero kuti mu mzinda monse muli phokoso lokhalokha. Ndiyetu phokoso limene mukulimvalo. 46 Ndipo Solomoni wakhala kale pa mpando wake waufumu. 47 Kuwonjezera pamenepo, nduna za mfumu zabwera kale kudzayamika mbuye wathu Mfumu Davide, pomanena kuti, ‘Mulungu wanu atchukitse dzina la Solomoni kuposa dzina lanu ndipo ufumu wake ukule kupambana ufumu wanu!’ Ndipo mfumu inawerama niyamba kupembedza pa bedi lake, 48 inati, ‘Atamandike Yehova, Mulungu wa Israeli, amene wasankha wolowa mʼmalo mwanga ine ndikanali ndi moyo lero lino.’ ”
49 Anthu onse amene Adoniya anawayitana ananjenjemera ndi mantha, ndipo anayimirira, kenaka anamwazikana. 50 Koma Adoniya, poopa Solomoni, anapita ku Nyumba ya Mulungu nakagwira msonga za guwa lansembe. 51 Tsono Solomoni anawuzidwa kuti, “Adoniya akukuopani inu Mfumu Solomoni ndipo wagwira msonga za guwa lansembe. Iye akuti, ‘Mfumu Solomoni alumbire kuti sadzapha kapolo wake ndi lupanga.’ ”
52 Solomoni anayankha kuti, “Ngati iyeyo aonetse kuti ndi munthu wakhalidwe labwino, ngakhale tsitsi la mʼmutu mwake silidzathothoka ndi kugwera pansi, koma akapezeka kuti ali ndi khalidwe loyipa, adzafa ndithu.” 53 Pamenepo Mfumu Solomoni inatuma anthu ndipo anakamutenga paguwa paja. Adoniya anabwera ndi kudzalambira Mfumu Solomoni, ndipo Solomoni anati, “Pita ku nyumba yako.”
Davide Alangiza Solomoni
2 Davide ali pafupi kumwalira, analangiza mwana wake Solomoni kuti:
2 “Ndatsala pangʼono kupita kumene munthu wina aliyense amayenera kupitako. Tsono khala wamphamvu, uvale zilimbe, 3 ndipo uzichita zimene Yehova Mulungu wako amafuna, uziyenda mʼnjira zake, uzisunga malangizo ndi malamulo ake monga momwe zinalembedwera mʼMalamulo a Mose, kuti zonse zimene udzachite zidzakuyendere bwino kulikonse kumene udzapite. 4 Ndipo Yehova akwaniritse zimene anandilonjeza kuti, ‘Ngati zidzukulu zako zidzakhala mosamala, niziyenda mokhulupirika pamaso panga ndi mtima wawo wonse ndi moyo wawo wonse, sudzasowa munthu wokhala pa mpando waufumu wa Israeli.’
5 “Tsono iwe ukudziwanso zoyipa zimene Yowabu mwana wa Zeruya anandichitira pakupha atsogoleri awiri a ankhondo a Israeli, Abineri mwana wa Neri ndi Amasa mwana wa Yeteri. Iye anawapha ndi kukhetsa magazi nthawi ya mtendere ngati nthawi ya nkhondo, ndipo anapaka magazi amenewo pa lamba wa mʼchiwuno mwake ndi pa nsapato za ku mapazi ake. 6 Iwe uchite kwa iye molingana ndi nzeru zako, koma usalole kuti afe ndi ukalamba ndi kupita ku manda mwamtendere.
7 “Koma ana a Barizilai wa ku Giliyadi uwakomere mtima ndipo uwalole kuti akhale mʼgulu la anthu amene azidya pamodzi nawe. Pakuti anandisamalira pamene ndinkathawa mʼbale wako Abisalomu.
8 “Ndipo kumbukira kuti uli ndi Simei mwana wa Gera, wa fuko la Benjamini wochokera ku Bahurimu, amene ananditemberera koopsa tsiku limene ndimapita ku Mahanaimu. Atabwera kudzakumana nane ku Yorodani, ine ndinalumbira mʼdzina la Yehova kuti, ‘Sindidzakupha iwe ndi lupanga.’ 9 Koma tsopano usamuyese ngati munthu wosalakwa. Iwe ndiwe munthu wanzeru. Udzadziwa choti uchite naye. Ngakhale ndi wokalamba, aphedwe ndithu.”
10 Tsono Davide anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda mu Mzinda wa Davide. 11 Iyeyo nʼkuti atalamulira Israeli kwa zaka makumi anayi. Ku Hebroni analamulira zaka zisanu ndi ziwiri ndipo ku Yerusalemu analamulira zaka 33. 12 Choncho Solomoni anakhala pa mpando waufumu wa abambo ake Davide, ndipo ufumu wake unakhazikika kwambiri.
Kukhazikika kwa Ufumu wa Solomoni
13 Tsono Adoniya, mwana wa Hagiti, anapita kwa Batiseba, amayi ake a Solomoni. Batiseba anamufunsa kuti, “Kodi wabwera mwamtendere?”
Iye anayakha kuti, “Eya, ndi zamtendere.” 14 Ndipo iye anawonjezera kunena kuti, “Ndili ndi mawu oti ndiyankhule nanu.”
Batiseba anayankha kuti, “Yankhula.”
15 Tsono Adoniya anati, “Monga inu mukudziwa, ufumu unali wanga. Aisraeli onse ankayembekezera kuti ine ndidzakhala mfumu yawo. Koma zinthu zinasintha ndipo ufumu wapita kwa mʼbale wanga; pakuti wapatsa iye ufumuwu ndi Yehova. 16 Tsono ndili ndi pempho limodzi kwa inu. Musandikanize ayi.”
Batiseba anati, “Nena.”
17 Adoniya anapitiriza kunena kuti, “Chonde, inu mupemphe mfumu Solomoni kuti andipatse Abisagi wa ku Sunemu kuti akhale mkazi wanga pakuti mukapempha inu sadzakukanizani.”
18 Batiseba anayankha kuti, “Chabwino. Ndidzakuyankhulira kwa mfumu.”
19 Batiseba atapita kwa Mfumu Solomoni kukayankhula naye mʼmalo mwa Adoniya, mfumu inanyamuka kukumana naye, ndipo inaweramira amayi akewo, kenaka inakhala pa mpando wake waufumu. Iye anayitanitsa mpando wina kuti amayi ake akhalepo ndipo anakhala pansi ku dzanja lake lamanja.
20 Amayi akewo anati, “Ndikufuna ndikupempheni kanthu kakangʼono. Chonde musandikanize.”
Mfumu inayankha kuti, “Pemphani amayi, ine sindikukanizani.”
21 Ndipo amayiwo anati, “Mulole kuti Abisagi wa ku Sunemu akhale mkazi wa mʼbale wanu Adoniya.”
22 Koma Mfumu Solomoni inayankha amayi ake aja kuti, “Chifukwa chiyani mukupemphera Adoniya Abisagi wa ku Sunemu? Mungathenso kumupemphera ufumu pakuti iyeyu ndi mkulu wanga ndipo mupemphereninso wansembe Abiatara ndi Yowabu mwana wa Zeruya!”
23 Pamenepo Mfumu Solomoni inalumbira mʼdzina la Yehova kuti, “Mulungu andilange ine koopsa ngati Adoniya saphedwa chifukwa cha pempho lakeli! 24 Tsono pali Yehova wamoyo, amene anandikhazikitsa ine pa mpando waufumu wa abambo anga Davide ndi kundipatsa ufumu monga analonjezera, Adoniya aphedwa lero lomwe lino!” 25 Choncho Mfumu Solomoni inalamula Benaya mwana wa Yehoyada ndipo anakantha Adoniyayo, nafa.
26 Ndipo mfumu inati kwa Abiatara wansembe, “Pita ku Anatoti ku minda yako chifukwa ndiwe woyenera kufa, koma sindikupha tsopano, chifukwa unkanyamula Bokosi la Chipangano la Ambuye Yehova pamaso pa abambo anga Davide ndipo unazunzika limodzi ndi abambo angawo.” 27 Kotero Solomoni anachotsa Abiatara pa udindo wokhala wansembe wa Yehova, kukwaniritsa mawu a Yehova amene anayankhula za nyumba ya Eli ku Silo.
28 Yowabu atamva zimenezi anathawira ku tenti ya Yehova ndipo anakagwira msonga za guwa lansembe, popeza Yowabu ndiye anathandiza Adoniya kuwukira koma sanathandize Abisalomu. 29 Mfumu Solomoni inawuzidwa kuti Yowabu wathawira ku tenti ya Yehova ndipo ali pambali pa guwa lansembe. Tsono Solomoni analamula Benaya mwana wa Yehoyada kuti, “Pita, kamukanthe!”
30 Choncho Benaya analowa mʼtenti ya Yehova ndipo anati kwa Yowabu, “Mfumu ikuti ‘Tuluka!’ ”
Koma iye anayankha kuti, “Ayi, ine ndifera muno.”
Benaya anakafotokozera mfumu kuti, “Umu ndi mmene Yowabu wandiyankhira.”
31 Pamenepo mfumu inalamula Benaya kuti, “Kachite monga iye wanenera. Ukamukanthe ndi kumuyika mʼmanda. Ukatero udzandichotsera ine pamodzi ndi nyumba ya abambo anga mlandu wa anthu osalakwa amene Yowabu anawapha. 32 Yehova adzamubwezera zomwe anachita pokhetsa magazi, chifukwa iye anakantha ndi lupanga anthu awiri abwino ndi olungama kuposa iye, nawapha, abambo anga Davide osadziwa. Anthu awiriwo ndi Abineri mwana wa Neri, wolamulira gulu lankhondo la Israeli ndi Amasa mwana wa Yeteri, wolamulira gulu lankhondo la Yuda. 33 Magazi amene Yowabu anakhetsa akhale pamutu pake ndi pa zidzukulu zake kwamuyaya. Koma pa Davide ndi zidzukulu zake, nyumba yake ndi mpando wake waufumu pakhale mtendere wochokera kwa Yehova kwamuyaya.”
34 Choncho Benaya mwana wa Yehoyada anapita kukakantha Yowabu nʼkumupha ndipo anayikidwa mʼmanda mʼnyumba yakeyake ya ku chipululu. 35 Mfumu inayika Benaya mwana wa Yehoyada kuti akhale woyangʼanira gulu lankhondo mʼmalo mwa Yowabu ndipo inayika Zadoki kuti akhale wansembe mʼmalo mwa Abiatara.
36 Kenaka mfumu inatuma anthu kukayitana Simei ndipo inamuwuza kuti, “Udzimangire nyumba mu Yerusalemu ndipo uzikhala kumeneko, koma usatuluke mu mzinda kupita kwina kulikonse. 37 Tsiku lomwe udzatulukemo ndi kuwoloka Chigwa cha Kidroni, udziwiretu kuti udzafa ndipo magazi ako adzakhala pamutu pako.”
38 Simei anayankha mfumu kuti, “Zimene mwanenazi nʼzabwino. Kapolo wanu adzachita monga mbuye wanga mfumu mwanenera.” Choncho Simei anakhala mu Yerusalemu nthawi yayitali.
39 Koma patatha zaka zitatu, akapolo awiri a Simei anathawira kwa Akisi mwana wa Maaka, mfumu ya ku Gati, ndipo Simei anawuzidwa kuti, “Akapolo anu ali ku Gati.” 40 Atamva zimenezi, anakwera bulu wake ndipo anapita kwa Akisi ku Gati kukafunafuna akapolo ake. Choncho Simei anapita ndi kukatenga akapolo ake ku Gati ndipo anabwera nawo.
41 Solomoni atawuzidwa kuti Simei anatuluka mu Yerusalemu ndi kupita ku Gati ndipo kuti wabwerako, 42 mfumu inamuyitanitsa Simei ndipo inamufunsa kuti, “Kodi sindinakulumbiritse mʼdzina la Yehova ndi kukuchenjeza kuti, ‘Tsiku limene udzatuluka kupita kwina kulikonse, udziwe kuti udzafa’? Nthawi imeneyo iwe unandiwuza kuti, ‘Zimene mwanena nʼzabwino. Ine ndidzamvera.’ 43 Chifukwa chiyani tsono sunasunge lumbiro lako kwa Yehova? Bwanji nanga sunamvere lamulo limene ndinakuwuza?”
44 Mfumuyo inawuzanso Simei kuti, “Ukudziwa mu mtima mwakomo zoyipa zonse zimene unachitira abambo anga Davide. Tsopano Yehova akubwezera zoyipa zakozo. 45 Koma Mfumu Solomoni idzadalitsidwa ndipo mpando waufumu wa Davide udzakhazikika pamaso pa Yehova kwamuyaya.”
46 Pamenepo mfumu inalamula Benaya mwana wa Yehoyada ndipo iye anapita kukakantha Simei ndi kumupha.
Tsono ufumu unakhazikika mʼdzanja la Solomoni.
Masalimo 37
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Salimo la Davide.
37 Usamavutike chifukwa cha anthu oyipa
kapena kuchitira nsanje amene akuchita cholakwa;
2 pakuti monga udzu iwo adzafota msanga,
ngati mbewu zobiriwira adzanyala msanga.
3 Khulupirira Yehova ndipo uzichita zabwino;
khazikika mʼdziko ndi kutsata zokhulupirika.
4 Udzikondweretse wekha mwa Yehova
ndipo Iye adzakupatsa zokhumba za mtima wako.
5 Pereka njira yako kwa Yehova;
dalira Iye ndipo Iyeyo adzachita izi:
6 Iye adzachititsa chilungamo chako kuwala ngati mʼbandakucha,
chiweruzo chako ngati dzuwa la masana.
7 Khala chete pamaso pa Yehova ndipo umudikire mofatsa;
usavutike pamene anthu apambana mʼnjira zawo,
pamene iwo achita zinthu zawo zoyipa.
8 Pewa kupsa mtima ndipo tembenuka kuchoka ku ukali,
usavutike chifukwa zimenezi zimatsogolera ku zoyipa.
9 Pakuti anthu oyipa adzachotsedwa,
koma iwo amene amayembekeza mwa Yehova adzalandira dziko.
10 Kwa kanthawi oyipa sadzapezekanso;
ngakhale muwafunefune, sadzapezekanso.
11 Koma ofatsa adzalandira dziko
ndipo adzasangalala ndi mtendere waukulu.
12 Oyipa amakonza chiwembu kutsutsana ndi olungama
ndipo amawakukutira mano;
13 koma Ambuye amaseka oyipa
pakuti Iye amadziwa kuti tsiku lawo likubwera.
14 Oyipa amasolola lupanga
ndi kupinda uta
kugwetsa osauka ndi osowa,
kupha iwo amene njira zawo ndi zolungama.
15 Koma malupanga awo analasa mitima yawo yomwe,
ndipo mauta awo anathyoka.
16 Zabwino zochepa zimene olungama ali nazo
ziposa chuma cha anthu oyipa ambiri;
17 pakuti mphamvu ya oyipa idzasweka,
koma Yehova amasunga olungama.
18 Masiku a anthu osalakwa amadziwika ndi Yehova,
ndipo cholowa chawo chidzakhala mpaka muyaya.
19 Pa nthawi ya mavuto iwo sadzafota;
mʼmasiku a njala adzakhala ndi zinthu zambiri.
20 Koma oyipa adzawonongeka;
adani a Yehova adzakhala ngati kukongola kwa kuthengo,
iwo adzazimirira ngati utsi.
21 Oyipa amabwereka ndipo sabweza
koma olungama amapereka mowolowamanja.
22 Iwo amene Yehova amawadalitsa adzalandira dziko,
koma amene Iye amawatemberera adzachotsedwa.
23 Ngati Yehova akondwera ndi njira ya munthu,
amakhazikitsa mayendedwe ake;
24 ngakhale atapunthwa sadzagwa,
pakuti Yehova amamutchinjiriza ndi dzanja lake.
25 Ine ndinali wamngʼono ndipo tsopano ndakalamba
koma sindinaonepo olungama akusiyidwa
kapena ana awo akupempha chakudya.
26 Iwo ndi owolowamanja nthawi zonse ndipo amabwereketsa mwaufulu;
ana awo adzadalitsika.
27 Tembenuka kuchoka ku zoyipa ndipo chita zabwino;
pamenepo udzakhazikika mʼdziko kwamuyaya.
28 Pakuti Yehova amakonda wolungama
ndipo sadzasiya okhulupirika ake.
Iwo adzatetezedwa kwamuyaya,
koma zidzukulu za oyipa zidzachotsedwa;
29 olungama adzalandira dziko
ndipo adzakhazikikamo kwamuyaya.
30 Pakamwa pa munthu wolungama pamayankhula za nzeru,
ndipo lilime lake limayankhula zolungama.
31 Lamulo la Mulungu wake lili mu mtima mwake;
mapazi ake saterereka.
32 Oyipa amabisala kudikira olungama;
kufunafuna miyoyo yawoyo;
33 koma Yehova sadzawasiya pansi pa mphamvu yawo
kapena kuti atsutsidwe pamene abweretsedwa pa milandu.
34 Khulupirira Yehova,
ndipo sunga njira yake;
Iye adzakukweza ndipo udzalandira dziko kuti likhale lako;
udzaona anthu oyipa akuwonongeka.
35 Ine ndinaona munthu woyipa ndi munthu wopanda chifundo
akupeza bwino ngati mtengo wobiriwira pa nthaka ya makolo ake.
36 Koma sanachedwe kumwalira ndipo sanaonekenso;
ngakhale ndinamuyangʼanayangʼana, sanapezekenso.
37 Ganizira za munthu wosalakwa, yangʼanitsitsa munthu wolungama;
udzaona kuti ali ndi tsogolo labwino ndipo ali ndi zidzukulu zambiri.
38 Koma anthu ochimwa adzawonongeka;
iwowo pamodzi ndi zidzukulu zawo zomwe.
39 Chipulumutso cha olungama chimachokera kwa Yehova;
Iye ndiye linga lawo pa nthawi ya masautso.
40 Yehova amawathandiza ndi kuwalanditsa;
Iye amawalanditsa kwa oyipa ndi kuwapulumutsa,
pakuti amathawira kwa Iye.
Masalimo 71
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
71 Mwa Inu Yehova ine ndathawiramo;
musalole kuti ndichititsidwe manyazi.
2 Mundilanditse ndi kundipulumutsa mwa chilungamo chanu,
mutchere khutu lanu ndi kundipulumutsa.
3 Mukhale thanthwe langa lothawirapo,
kumene ine nditha kupita nthawi zonse;
lamulani kuti ndipulumuke,
pakuti Inu ndinu thanthwe langa ndi linga langa.
4 Landitseni Inu Mulungu wanga, kuchoka mʼdzanja la oyipa,
kuchoka mʼdzanja la oyipa ndi anthu ankhanza.
5 Pakuti Inu mwakhala chiyembekezo changa, Inu Ambuye Wamphamvuzonse,
chilimbikitso changa kuyambira ndili mwana.
6 Kuyambira pamene ndinabadwa, ndakhala ndikudalira Inu;
Inu munanditulutsa mʼmimba mwa amayi anga,
ndipo ndidzakupembedzani nthawi zonse.
7 Ine ndakhala chinthu chodabwitsa kwa anthu ambiri
koma Inu ndinu wonditchinjiriza wamphamvu.
8 Pakamwa panga padzaza ndi matamando anu,
kulengeza ulemerero wanu tsiku lonse.
9 Musanditaye pamene ndakalamba;
musandisiye pamene mphamvu zanga zatha.
10 Pakuti adani anga ayankhula motsutsana nane;
iwo amene amadikira kuti andiphe amapangana pamodzi.
11 Iwo amati, “Mulungu wamusiya;
mutsatireni ndi kumugwira,
pakuti palibe amene adzamupulumutse.”
12 Musakhale kutali ndi ine Inu Mulungu,
bwerani msanga, Inu Mulungu wanga; thandizeni.
13 Ondineneza anga awonongeke mwa manyazi,
iwo amene akufuna kundipweteka
avale chitonzo ndi manyazi.
14 Koma ine ndidzakhala ndi chiyembekezo mwa Inu nthawi zonse,
ndidzakutamandani mowirikizawirikiza.
15 Pakamwa panga padzafotokoza za chilungamo chanu,
za chipulumutso chanu tsiku lonse,
ngakhale sindikudziwa muyeso wake.
16 Ndidzabwera ndi kulengeza za machitidwe amphamvu zanu Inu Ambuye Wamphamvuzonse.
Ndidzalengeza chilungamo chanu, chanu chokha.
17 Kuyambira ubwana wanga, Inu Mulungu mwakhala mukundiphunzitsa,
ndipo mpaka lero ine ndikulengeza za ntchito zanu zodabwitsa
18 Ngakhale pamene ndakalamba ndipo imvi zili mbuu
musanditaye Inu Mulungu,
mpaka nditalengeza mphamvu zanu
kwa mibado yonse yakutsogolo.
19 Mphamvu zanu ndi kulungama kwanu zimafika mpaka kumwambamwamba.
Ndani wofanana nanu Inu Mulungu,
amene mwachita zazikulu?
20 Ngakhale mwandionetsa mavuto
ambiri owawa,
mudzabwezeretsanso moyo wanga;
kuchokera kunsi kwa dziko lapansi,
mudzandiukitsanso.
21 Inu mudzachulukitsa ulemu wanga
ndi kunditonthozanso.
22 Ndidzakutamandani ndi zeze
chifukwa cha kukhulupirika kwanu Mulungu,
ndidzayimba matamando kwa Inu ndi pangwe,
Inu Woyera wa Israeli.
23 Milomo yanga idzafuwula ndi chimwemwe
pamene ndidzayimba matamando kwa Inu
amene mwandiwombola.
24 Lilime langa lidzafotokoza za ntchito zanu zachilungamo
tsiku lonse,
pakuti iwo amene amafuna kundipweteka
achititsidwa manyazi ndi kusokonezedwa.
Masalimo 94
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
94 Inu Yehova, ndinu Mulungu wobwezera chilango,
Inu Mulungu amene mumabwezera chilango, wonetsani kuwala kwanu.
2 Nyamukani, Inu woweruza wa dziko lapansi;
bwezerani kwa odzikuza zowayenera.
3 Kodi mpaka liti anthu oyipa Inu Yehova,
mpaka liti anthu oyipa adzalumpha ndi chimwemwe?
4 Amakhuthula mawu onyada;
onse ochita zoyipa ndi odzaza ndi kudzikuza.
5 Amaphwanya anthu anu, Inu Yehova;
amapondereza cholowa chanu.
6 Amaphanso amayi a masiye ndi alendo okhala nawo mʼdziko;
amapha ana amasiye.
7 Iwo amati, “Yehova sakuona;
Mulungu wa Yakobo salabadirako.”
8 Samalani, inu anthu opanda nzeru pakati pa anthu;
zitsiru inu, kodi mudzakhala liti anzeru?
9 Kodi Iye amene anapanga khutu sangathe kumva?
Kodi Iye amene anapanga diso sangathe kuona?
10 Kodi Iye amene amalangiza mitundu ya anthu sangathenso kulanga?
Kodi Iye amene amaphunzitsa munthu angasowe nzeru?
11 Yehova amadziwa maganizo a munthu;
Iye amadziwa kuti maganizowo ndi achabechabe.
12 Wodala munthu amene Inu Yehova mumamulangiza,
munthu amene mumamuphunzitsa kuchokera mulamulo lanu;
13 mumamupumitsa pa nthawi ya mavuto,
mpaka woyipa atakumbiridwa dzenje.
14 Pakuti Yehova sadzawakana anthu ake;
Iye sadzasiya cholowa chake.
15 Chiweruzo chidzakhazikikanso pa chilungamo,
ndipo onse olungama mtima adzachitsata.
16 Ndani adzadzuka chifukwa cha ine kulimbana ndi anthu oyipa?
Ndani adzayimirira mʼmalo mwanga kulimbana ndi anthu ochita zoyipa?
17 Yehova akanapanda kundithandiza,
bwenzi nditakakhala msanga ku malo achete a imfa.
18 Ndikanena kuti, “Phazi langa likuterereka,”
chikondi chanu, Inu Yehova, chimandichirikiza.
19 Pamene nkhawa inakula mʼkati mwanga,
chitonthozo chanu chinabweretsa chimwemwe mʼmoyo mwanga.
20 Kodi mpando waufumu woyipa ungathe kugwirizana nanu
umene umabweretsa masautso chifukwa cha malamulo ake?
21 Iwo amasonkhana pamodzi kulimbana ndi wolungama
ndi kugamula kuti wosalakwa aphedwe.
22 Koma Yehova wakhala linga langa,
ndipo Mulungu ndiye thanthwe limene ndimathawirako.
23 Iye adzawabwezera chifukwa cha machimo awo
ndi kuwawononga chifukwa cha kuyipa kwawo;
Yehova Mulungu wathu adzawawononga.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.