1 Samueli 22
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Davide Apita ku Adulamu ndi ku Mizipa
22 Davide anachoka kumeneko nathawira ku phanga la Adulamu. Abale ake ndi banja lonse la abambo ake anamva izi, anapita kumene kunali Davide. 2 Ndipo aliyense amene anali pa mavuto, kapena ndi ngongole kapenanso amene anali wosakondwa anasonkhana kwa iye, ndipo iye anakhala mtsogoleri wawo. Onse pamodzi analipo amuna 400.
3 Kuchokera kumeneko Davide anapita ku Mizipa ku Mowabu ndipo anapempha mfumu ya Mowabu kuti, “Bwanji abambo ndi amayi anga akhale nanu mpaka ine nditadziwa chimene Mulungu adzachite nane?” 4 Choncho iye anawasiya kwa mfumu ya Mowabu ndipo anakhala naye nthawi yonse imene Davide ankabisala ku phanga kuja.
5 Koma mneneri Gadi anawuza Davide kuti, “Usakhale ku phanga kuno. Pita ku dziko la Yuda.” Kotero Davide anachoka ndi kupita ku nkhalango ya Hereti.
Sauli Apha Ansembe a ku Nobi
6 Tsono Sauli anamva kuti Davide ndi anthu ake apezeka. Nthawiyo nʼkuti Sauli atakhala pansi pa mtengo wa bwemba pa phiri la ku Gibeya, mkondo uli mʼdzanja lake ndi ankhondo ake atayima chomuzungulira. 7 Tsono Sauli anafunsa ankhondo ake aja kuti, “Tamverani inu anthu a fuko la Benjamini! Kodi mwana wa Yese adzakupatsani nonsenu minda ndi minda ya mpesa? Kodi nonsenu adzakuyikani kukhala atsogoleri a magulu ankhondo? 8 Mwinatu nʼchifukwa chake mwagwirizana zondichita chiwembu. Palibe amene anandiwuza pamene mwana wanga ankapanga pangano ndi mwana wa Yese. Palibe aliyense amene ankalabadirako za ine kapena kundiwuza kuti mwana wanga wautsa mtima wa wantchito wanga kuti andiwukire monga wachitira lero.”
9 Koma Doegi Mwedomu anayima pafupi ndi nduna za Sauli nati, “Ine ndinaona mwana wa Yese atabwera kwa Ahimeleki mwana wa Ahitubi ku Nobi. 10 Ahimelekiyo anafunsa kwa Yehova chomwe Davide ayenera kuchita. Iye anamupatsa zakudya ndiponso lupanga la Goliati Mfilisiti uja.”
11 Pamenepo mfumu inayitanitsa wansembe Ahimeleki mwana wa Ahitubi ndi banja lonse la abambo ake, amene anali ansembe ku Nobi. Ndipo onse anabwera kwa mfumu. 12 Sauli anati, “Tsono tamvera, mwana wa Ahitubi.”
Iye anayankha kuti, “Inde mbuye wanga.”
13 Sauli anamufunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani iwe ndi mwana wa Yese mwandiwukira ine? Wamupatsa buledi ndi lupanga. Wafunsiranso kwa Yehova zoti andiwukire ndi kundibisalira monga wachita leromu?”
14 Ahimeleki anayankha mfumu kuti, “Kodi ndani mwa ankhondo anu onse amene ali wokhulupirika monga Davide? Iye uja ndi mkamwini wa mfumu, kapitawo wa asilikali okutetezani ndiponso munthu amene amalemekezedwa mʼbanja lanu? 15 Kodi tsiku limeneli linali loyamba kuti ndimufunsire kwa Yehova? Ayi sichoncho! Mfumu musandinenere kanthu kalikonse koyipa kapena banja la abambo anga, pakuti sindikudziwa kanthu kena kalikonse ka zimenezi.”
16 Koma mfumu inati, “Iwe Ahimeleki ndi banja lonse la abambo ako mudzaphedwa ndithu.”
17 Kenaka mfumu inalamulira alonda amene anali naye kuti, “Iphani ansembe a Yehovawa chifukwa iwo akugwirizana ndi Davide. Iwo amadziwa kuti Davide ankathawa koma sanandiwuze.”
Koma antchito a mfumu aja sanasamule dzanja kuti aphe ansembe a Yehova.
18 Kotero mfumu inalamula Doegi kuti, “Uwaphe ndiwe ansembewa.” Choncho Doegi Mwedomu anapita ndi kuwapha. Tsiku limenelo iye anapha amuna 85 amene amavala efodi wa nsalu yofewa. 19 Kunena za Nobi, mzinda wa ansembe, Sauli anapha amuna ndi amayi, ana ndi makanda pamodzi ndi ngʼombe, abulu ndi nkhosa.
20 Koma Abiatara mwana wa Ahimeleki mwana wa Ahitubi anapulumuka ndi kuthawira kwa Davide. 21 Abiatara anawuza Davide kuti Sauli wapha ansembe a Yehova. 22 Ndipo Davide anati kwa Abiatara, “Tsiku lija pamene Doegi Mwedomu anali kumene kuja, ine ndimadziwa kuti salephera kukamuwuza Sauli. Ine ndi amene ndaphetsa banja lonse la abambo ako. 23 Iwe khala ndi ine, usaope munthu amene akufuna moyo wako komanso wanga. Udzatetezeka ukakhala ndi ine.”
1 Samuel 22
King James Version
22 David therefore departed thence, and escaped to the cave Adullam: and when his brethren and all his father's house heard it, they went down thither to him.
2 And every one that was in distress, and every one that was in debt, and every one that was discontented, gathered themselves unto him; and he became a captain over them: and there were with him about four hundred men.
3 And David went thence to Mizpeh of Moab: and he said unto the king of Moab, Let my father and my mother, I pray thee, come forth, and be with you, till I know what God will do for me.
4 And he brought them before the king of Moab: and they dwelt with him all the while that David was in the hold.
5 And the prophet Gad said unto David, Abide not in the hold; depart, and get thee into the land of Judah. Then David departed, and came into the forest of Hareth.
6 When Saul heard that David was discovered, and the men that were with him, (now Saul abode in Gibeah under a tree in Ramah, having his spear in his hand, and all his servants were standing about him;)
7 Then Saul said unto his servants that stood about him, Hear now, ye Benjamites; will the son of Jesse give every one of you fields and vineyards, and make you all captains of thousands, and captains of hundreds;
8 That all of you have conspired against me, and there is none that sheweth me that my son hath made a league with the son of Jesse, and there is none of you that is sorry for me, or sheweth unto me that my son hath stirred up my servant against me, to lie in wait, as at this day?
9 Then answered Doeg the Edomite, which was set over the servants of Saul, and said, I saw the son of Jesse coming to Nob, to Ahimelech the son of Ahitub.
10 And he enquired of the Lord for him, and gave him victuals, and gave him the sword of Goliath the Philistine.
11 Then the king sent to call Ahimelech the priest, the son of Ahitub, and all his father's house, the priests that were in Nob: and they came all of them to the king.
12 And Saul said, Hear now, thou son of Ahitub. And he answered, Here I am, my lord.
13 And Saul said unto him, Why have ye conspired against me, thou and the son of Jesse, in that thou hast given him bread, and a sword, and hast enquired of God for him, that he should rise against me, to lie in wait, as at this day?
14 Then Ahimelech answered the king, and said, And who is so faithful among all thy servants as David, which is the king's son in law, and goeth at thy bidding, and is honourable in thine house?
15 Did I then begin to enquire of God for him? be it far from me: let not the king impute any thing unto his servant, nor to all the house of my father: for thy servant knew nothing of all this, less or more.
16 And the king said, Thou shalt surely die, Ahimelech, thou, and all thy father's house.
17 And the king said unto the footmen that stood about him, Turn, and slay the priests of the Lord: because their hand also is with David, and because they knew when he fled, and did not shew it to me. But the servants of the king would not put forth their hand to fall upon the priests of the Lord.
18 And the king said to Doeg, Turn thou, and fall upon the priests. And Doeg the Edomite turned, and he fell upon the priests, and slew on that day fourscore and five persons that did wear a linen ephod.
19 And Nob, the city of the priests, smote he with the edge of the sword, both men and women, children and sucklings, and oxen, and asses, and sheep, with the edge of the sword.
20 And one of the sons of Ahimelech the son of Ahitub, named Abiathar, escaped, and fled after David.
21 And Abiathar shewed David that Saul had slain the Lord's priests.
22 And David said unto Abiathar, I knew it that day, when Doeg the Edomite was there, that he would surely tell Saul: I have occasioned the death of all the persons of thy father's house.
23 Abide thou with me, fear not: for he that seeketh my life seeketh thy life: but with me thou shalt be in safeguard.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.