Add parallel Print Page Options

Musakhale ngati mafumu pa amene mukuwayangʼanira, koma mukhale chitsanzo kwa gululo. Ndipo Mʼbusa wamkulu akadzaonekera, mudzalandira chipewa cha ulemerero chosafota.

Momwemonso, inu anyamata gonjerani amene ndi akulu. Inu nonse mukhale odzichepetsa kuti mutumikirane, chifukwa,

“Mulungu amatsutsana nawo odzikuza,
    koma amapereka chisomo kwa odzichepetsa.”

Choncho, mudzichepetse pamaso pa Mulungu wamphamvu, kuti pa nthawi yake adzakukwezeni.

Read full chapter