1 Mafumu 11
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Akazi a Solomoni
11 Komatu Mfumu Solomoni anakonda akazi ambiri achilendo ndipo kuwonjezera pa mwana wamkazi wa Farao, analinso ndi akazi a mitundu iyi: Amowabu, Aamoni, Aedomu, Asidoni, ndi Ahiti. 2 Akazi amenewa anali ochokera ku mitundu ija imene Yehova anawuza Aisraeli kuti, “Simuyenera kudzakwatirana nawo amenewa, chifukwa ndithu, amenewa adzatembenuza mitima yanu kuti mutsatire milungu yawo.” Komabe Solomoni anawakonda kwambiri akazi amenewa. 3 Iye anali ndi akazi 700 ochokera ku mabanja achifumu ndi azikazi 300 ndipo akaziwo anamusocheretsa. 4 Solomoni atakalamba, akazi akewo anakopa mtima wake kuti atsatire milungu ina, ndipo sanatsatire Yehova Mulungu wake ndi mtima wodzipereka, monga unalili mtima wa Davide abambo ake. 5 Pakuti iye ankapembedza Asitoreti, mulungu wamkazi wa Asidoni, ndiponso Moleki mulungu wonyansa wa Aamoni. 6 Kotero Solomoni anachita zoyipa pamaso pa Yehova. Sanatsatire Yehova kwathunthu monga anachitira Davide abambo ake.
7 Pa phiri la kummawa kwa Yerusalemu, anamanga malo opembedzerapo Kemosi, mulungu wonyansa wa Mowabu, ndiponso malo a Moleki, mulungu wonyansa wa Aamoni. 8 Iye anamangiranso malo oterewa akazi ake onse achilendo, amene amafukiza lubani ndi kumapereka nsembe kwa milungu yawo.
9 Choncho Yehova anakwiyira Solomoni chifukwa mtima wake unatembenuka kuchoka kwa Yehova Mulungu wa Israeli, amene anamuonekera kawiri konse. 10 Ngakhale kuti Yehova anamuletsa Solomoni kutsatira milungu ina, iyeyo sanamvere lamulo la Yehova. 11 Pamenepo Yehova anati kwa Solomoni, “Popeza mtima wako ndi wotere ndipo sunasunge pangano langa ndi malamulo anga amene ndinakuwuza, ndithudi, Ine ndidzawugawa ufumuwu kuwuchotsa kwa iwe ndi kuwupereka kwa mmodzi mwa atumiki ako. 12 Koma chifukwa cha Davide abambo ako, sindidzachita zimenezi iwe uli moyo. Ndidzawugawa mʼdzanja la mwana wako. 13 Komabe sindidzamulanda ufumu wonse, koma ndidzamusiyira fuko limodzi chifukwa cha mtumiki wanga Davide ndiponso chifukwa cha Yerusalemu, mzinda umene ndinawusankha.”
Adani a Solomoni
14 Ndipo Yehova anamuutsira Solomoni mdani, Hadadi Mwedomu, wochokera ku banja laufumu ku Edomu. 15 Kale pamene Davide ankachita nkhondo ndi Aedomu, Yowabu mkulu wa ankhondo, amene anapita kukakwirira Aisraeli akufa, anakantha amuna onse ku Edomu. 16 Yowabu ndi Aisraeli onse anakhala kumeneko miyezi isanu ndi umodzi mpaka anawononga amuna onse a ku Edomu. 17 Koma Hadadi akanali mwana anathawira ku Igupto pamodzi ndi akuluakulu ena a ku Edomu amene ankatumikira abambo ake. 18 Iwo ananyamuka ku Midiya ndi kupita ku Parani. Ndipo anatenga amuna ena ku Paraniko, napita nawo ku Igupto, kwa Farao mfumu ya Igupto, amene anamupatsa nyumba, malo ndiponso chakudya.
19 Farao anamukomera mtima Hadadi ndipo anamupatsa mkazi amene anali mngʼono wake wa Mfumukazi Tahipenesi. 20 Mngʼono wake wa Tahipenesi anabereka mwana wamwamuna ndipo anamutcha Genubati, amene analeredwa mʼnyumba yaufumu ndi Tahipenesi. Genubatiyo ankakhala limodzi ndi ana a Farao.
21 Ali ku Iguptoko, Hadadi anamva kuti Davide ndi Yowabu anamwalira. Pamenepo Hadadi anati kwa Farao, “Loleni ndichoke kuti ndibwerere ku dziko la kwathu.”
22 Farao anafunsa kuti, “Kodi ukusowa chiyani kuno kuti ufune kubwerera ku dziko la kwanu?”
Hadadi anayankha kuti, “Palibe chimene ndikusowa, koma loleni kuti ndichoke!”
23 Ndipo Mulungu anawutsira Solomoni mdani wina, Rezoni mwana wa Eliada, amene anali atathawa mbuye wake, Hadadezeri mfumu ya ku Zoba. 24 Iye anasonkhanitsa anthu ndipo anali mtsogoleri wa anthu owukira pamene Davide anapha ankhondo a ku Zoba. Anthu owukirawa anapita ku Damasiko, nakakhala kumeneko ndi kuyamba kulamulira. 25 Rezoni anali mdani wa Israeli pa masiku onse a Solomoni, kuwonjezera pa mavuto amene ankabweretsa Hadadi. Kotero Rezoni ankalamulira ku Aramu ndipo ankadana ndi Israeli.
Yeroboamu Awukira Solomoni
26 Yeroboamu, mwana wa Nebati anawukiranso mfumu. Iye anali mmodzi mwa akuluakulu a Solomoni wa fuko la Efereimu, wa ku Zeredi, ndipo amayi ake anali Zeruya, mkazi wamasiye.
27 Nkhani ya kuwukira kwa Yeroboamu inali yotere: Solomoni anamanga malo a chitetezo a Milo ndipo anakonza khoma logumuka la mzinda wa Davide, abambo ake. 28 Tsono Yeroboamu anali munthu wamphamvu kwambiri ndipo Solomoni ataona kuti mnyamatayo amadziwa kugwira ntchito bwino, anamuyika kukhala woyangʼanira anthu a ntchito onse a nyumba ya Yosefe.
29 Tsiku lina Yeroboamu ali pa ulendo kuchokera ku Yerusalemu, anakumana ndi mneneri Ahiya pa msewu, ndipo Ahiyayo anali atavala mwinjiro watsopano. Awiriwo anali okha kuthengoko, 30 ndipo Ahiya anagwira mwinjiro watsopano umene anavala ndi kuwungʼamba zidutswa 12. 31 Tsono iye anati kwa Yeroboamu, “Tenga zidutswa khumi, pakuti Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Taona, Ine ndidzachotsa ufumu mʼdzanja la Solomoni ndipo ndidzakupatsa iwe mafuko khumi. 32 Koma chifukwa cha mtumiki wanga Davide ndiponso mzinda wa Yerusalemu, umene ndinawusankha pakati pa mafuko a Israeli, iye adzakhala ndi fuko limodzi lokha. 33 Ndidzachita zimenezi chifukwa wandisiya Ine ndi kupembedza Asitoreti mulungu wamkazi wa Asidoni, Kemosi mulungu wa Amowabu ndiponso Moleki mulungu wa Aamoni, ndipo sanayende mʼnjira yanga, kapena kusunga mawu anga ndi malamulo anga monga anachitira Davide abambo ake.
34 “ ‘Koma sindidzalanda ufumu wonse mʼdzanja la Solomoni. Ine ndamuyika kukhala wolamulira masiku onse a moyo wake chifukwa cha mtumiki wanga Davide, amene ndinamusankha ndiponso amene anamvera malamulo anga ndi mawu anga. 35 Ndidzalanda ufumu mʼdzanja la mwana wake ndipo ndidzakupatsa iwe mafuko khumi. 36 Ndidzapereka fuko limodzi kwa mwana wake ndi cholinga choti Davide mtumiki wanga adzakhale nyale nthawi zonse pamaso panga mu Yerusalemu, mzinda umene ndinawusankha kuyikamo Dzina langa. 37 Koma kunena za iwe, ndidzakutenga ndipo udzalamulira chilichonse chimene mtima wako ukukhumba; udzakhala mfumu ya Israeli. 38 Ngati udzamvera zonse zimene ndidzakulamula ndi kuyenda mʼnjira yanga ndi kuchita zabwino pamaso panga, posunga malamulo anga ndi mawu anga monga anachitira Davide mtumiki wanga, Ine ndidzakhala nawe. Ndidzakupatsa ufumu umene udzakhala wokhazikika monga ndinamupatsira Davide, ndipo Ine ndidzakupatsa Israeli. 39 Ine ndidzalanga zidzukulu za Davide chifukwa cha zimenezi, koma osati kwamuyaya.’ ”
40 Solomoni anafunitsitsa kupha Yeroboamu, koma Yeroboamu anathawira ku Igupto, kwa Sisaki mfumu ya Igupto ndipo anakhala kumeneko mpaka Solomoni atamwalira.
Kumwalira kwa Solomoni
41 Ntchito zina za Solomoni, zonse zomwe anachita komanso za nzeru zake, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya Solomoni? 42 Solomoni analamulira Aisraeli onse mu Yerusalemu kwa zaka makumi anayi. 43 Ndipo anagona ndi makolo ake nayikidwa mʼmanda mu mzinda wa Davide abambo ake. Ndipo Rehobowamu mwana wake analowa ufumu mʼmalo ake.
1 Kungaboken 11
Svenska Folkbibeln
Salomos hustrur
11 Kung Salomo hade vid sidan om faraos dotter många andra utländska kvinnor som han älskade: moabitiskor, ammonitiskor, edomitiskor, sidoniskor och hetitiskor, 2 De hörde till folk som Herren hade talat om och sagt till Israels barn: "Ni skall inte gå in till dem, och de inte till er, eftersom de kommer att förleda era hjärtan att följa deras gudar." Till dessa höll sig Salomo och älskade dem. 3 Han hade sjuhundra furstliga gemåler och trehundra bihustrur, och dessa kvinnor förledde hans hjärta. 4 När Salomo blev gammal, förledde kvinnorna honom att följa andra gudar, så att hans hjärta inte förblev hängivet Herren, sin Gud, som hans fader Davids hjärta hade varit. 5 Salomo följde efter Astarte, sidoniernas gudinna, och Milkom, ammoniternas styggelse. 6 Salomo gjorde det som var ont i Herrens ögon och följde inte i allt efter Herren, så som hans fader David hade gjort. 7 Salomo byggde då en offerhöjd åt Kemosh, moabiternas styggelse, på berget öster om Jerusalem och likaså en åt Molok, ammoniternas styggelse. 8 På samma sätt gjorde han för alla sina utländska kvinnor, som fick tända offereld och offra åt sina gudar.
9 Herren blev vred på Salomo, därför att hans hjärta hade vänt sig bort från Herren, Israels Gud, som två gånger hade visat sig för honom. 10 Han hade givit honom befallning om denna sak: att han inte skulle följa efter andra gudar. Men han hade inte hållit vad Herren befallt. 11 Därför sade Herren till Salomo: "Eftersom det är så med dig och eftersom du inte har hållit mitt förbund och mina stadgar som jag har givit dig, skall jag rycka riket ifrån dig och ge det åt din tjänare. 12 Men för din fader Davids skull vill jag inte göra detta så länge du lever. Först ur din sons hand skall jag rycka det. 13 Dock skall jag inte rycka hela riket ifrån honom, utan en stam skall jag ge åt din son för min tjänare Davids skull, och för Jerusalems skull, som jag har utvalt."
Salomos fiender
14 Herren reste upp en motståndare[a] till Salomo. Det var edomiten Hadad som var släkt med kungen i Edom. 15 När David var i strid med Edom drog befälhavaren Joab upp för att begrava de stupade och han förgjorde alla av mankön i Edom. 16 Joab och hela Israel stannade där i sex månader till dess att han hade utrotat alla av mankön i Edom. 17 Då flydde Hadad tillsammans med några edomitiska män, som hade varit i hans fars tjänst, för att bege sig till Egypten. Hadad var då en ung pojke. 18 Sedan de brutit upp från Midjan kom de till Paran. De tog folk med sig från Paran och kom till Egypten, till farao, kungen i Egypten. Denne gav Hadad hus, underhåll och land. 19 Farao uppskattade Hadad så mycket att han till hustru gav honom en syster till sin gemål, en syster till drottning Tapenes. 20 Denna syster till Tapenes födde åt honom sonen Genubat, och Tapenes avvande honom i faraos hus. Sedan vistades Genubat i faraos hus bland faraos söner.
21 Medan Hadad var i Egypten, hörde han att David hade gått till vila hos sina fäder och att befälhavaren Joab var död. Han sade då till farao: "Låt mig fara hem till mitt land." 22 Men farao sade till honom: "Vad saknar du här hos mig, eftersom du vill fara hem till ditt land?" Men han svarade: "Ingenting, men låt mig ändå ge mig av."
23 Gud reste upp ännu en motståndare till Salomo. Det var Rezon, Eljadas son, som hade flytt från sin herre Hadadezer, kungen i Soba. 24 När David åstadkom ett blodbad bland dem, samlade denne folk omkring sig och blev ledare för ett rövarband. Dessa drog till Damaskus och slog sig ner där och gjorde sig till herrar i Damaskus. 25 Rezon var under hela Salomos livstid motståndare till Israel och gjorde landet skada, han liksom Hadad. Han var fientligt inställd till Israel, och han blev kung över Aram.
Jerobeam gör uppror mot Salomo
26 En av Salomos tjänare hette Jerobeam. Han var son till Nebat, en efraimit från Sereda, och hans mor hette Seruga och var änka. Jerobeam gjorde uppror mot kungen. 27 Orsaken till att han gjorde uppror mot kungen var denna:
Salomo byggde på Millo. Han ville täppa till öppningen i muren omkring sin fader Davids stad. 28 Jerobeam var en duglig man, och då Salomo såg att den unge mannen var driftig i sitt arbete, satte han honom över allt det arbete som Josefs hus hade att utföra. 29 Vid den tiden hände sig en gång att Jerobeam hade begivit sig ut ur Jerusalem. Då kom profeten Ahia från Silo emot honom på vägen. Profeten var klädd i en ny mantel, och de båda var ensamma på fältet. 30 Ahia tog den nya manteln, som han hade på sig och slet sönder den i tolv delar. 31 Och han sade till Jerobeam: "Tag här tio delar för din räkning. Ty så säger Herren, Israels Gud: Se, jag vill rycka riket ur Salomos hand och ge tio av stammarna åt dig. 32 Bara en stam skall han få behålla för min tjänare Davids skull och för Jerusalems skull, den stad som jag har utvalt ur alla Israels stammar. 33 Detta skall ske, därför att de har övergivit mig och tillbett Astarte, sidoniernas gudinna, Kemosh, Moabs gud, och Milkom, ammoniternas gud. De har inte gått på mina vägar och inte gjort det som är rätt i mina ögon, efter mina stadgar och föreskrifter, så som Salomos fader David gjorde. 34 Dock skall jag inte ta ifrån honom hela riket, utan jag vill låta honom vara furste så länge han lever, för min tjänare Davids skull, som jag utvalde, därför att han höll fast vid mina bud och stadgar. 35 Men jag skall ta kungadömet från hans son och ge de tio stammarna åt dig. 36 Åt hans son skall jag ge en stam, så att min tjänare David alltid har en lampa inför mitt ansikte i Jerusalem, den stad som jag har utvalt åt mig för att där fästa mitt namn. 37 Dig vill jag alltså ta och låta regera över allt vad du önskar, och du skall bli kung över Israel. 38 Om du lyder allt jag befaller dig och går på mina vägar och gör det som är rätt i mina ögon, så att du håller fast vid mina stadgar och bud, så som min tjänare David gjorde, då skall jag vara med dig och åt dig bygga ett hus som blir bestående, så som jag byggde ett hus åt David, och jag skall ge Israel åt dig. 39 Jag skall förödmjuka Davids släkt genom detta, men inte för alltid."
40 Salomo sökte efter tillfälle att döda Jerobeam, men Jerobeam stod upp och flydde till Egypten, till Sisak, kungen i Egypten, och stannade där till Salomos död.
Salomo dör
41 Vad som mer finns att säga om Salomo, om allt vad han gjorde och om hans visdom, det är skrivet i Salomos krönika. 42 Den tid Salomo regerade i Jerusalem över hela Israel var fyrtio år.[b]
43 Och Salomo gick till vila hos sina fäder och blev begravd i sin fader Davids stad. Hans son Rehabeam blev kung efter honom.
Footnotes
- 1 Kungaboken 11:14 motståndare Hebr. "satan". Så även v. 23, 25.
- 1 Kungaboken 11:42 fyrtio år Ca 970-930 f. Kr.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.
1996, 1998 by Stiftelsen Svenska Folkbibeln