1 Akorinto 3
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Mpingo ndi Atsogoleri Ake
3 Ndipo abale sindikanakuyankhulani ngati auzimu koma adziko lapansi, makanda chabe mwa Khristu. 2 Ndinakupatsani mkaka osati chakudya cholimba pakuti munali musanakonzeke kuchilandira. Zoonadi, simunakonzekebe. 3 Mukanali adziko lapansi. Pakuti pakati panu pali kaduka ndi kukangana, kodi si inu a dziko lapansi? Kodi simukuchita ngati anthu wamba? 4 Pamene wina anena kuti, “Ine ndimatsatira Paulo,” ndipo wina akuti, “Ine ndimatsatira Apolo,” Kodi si inu akunja?
5 Ndiponso kodi Apolo ndi ndani? Nanga Paulo ndi ndani? Otumikira chabe, omwe kudzera mwa iwo inu munakhulupirira monga Ambuye anawagawira aliyense ntchito yake. 6 Ine ndinadzala mbewu, Apolo anayithirira, koma Mulungu ndiye anayikulitsa. 7 Choncho kuphatikiza iye wodzala ndi iye wothirira, onse sali kanthu, koma Mulungu yekha amene amakulitsa zinthu. 8 Munthu wodzala ndi munthu wothirira ali ndi cholinga chimodzi, ndipo aliyense adzapatsidwa mphotho molingana ndi ntchito yake. 9 Pakuti ife ndife antchito anzake a Mulungu; inu ndinu munda wa Mulungu, Nyumba ya Mulungu.
10 Mwachisomo chimene Mulungu wandipatsa, ine ndinayika maziko monga mmisiri waluntha, ndipo ena akumangapo. Koma aliyense ayenera kuchenjera mmene akumangira. 11 Pakuti wina sangayikenso maziko ena oposera amene anakhazikitsidwa kale, amene ndi Yesu Khristu. 12 Ngati munthu aliyense amanga pa maziko awa pogwiritsa ntchito golide, siliva, miyala yamtengowapatali, milimo yamitengo, tsekera kapena udzu, 13 ntchito yake idzaonekera pamene Tsiku la chiweruzo lidzazionetsa poyera. Tsikulo lidzafika ndi moto, ndipo motowo ndi umene udzayesa ntchito ya munthu aliyense. 14 Ngati zimene zamangidwazo sizidzagwa, adzalandira mphotho yake. 15 Ndipo ngati zidzanyeke ndi moto, sadzalandira mphotho koma iye mwini adzapulumukabe, koma monga ngati munthu amene wapulumuka mʼmoto.
16 Kodi inu simukudziwa kuti ndinu Nyumba ya Mulungu ndipo kuti Mzimu wa Mulungu amakhala mwa inu? 17 Ngati wina aliyense awononga Nyumba ya Mulunguyo, Mulungu nayenso adzamuwononga ameneyo; popeza Nyumba ya Mulungu ndi yopatulika ndipo Nyumbayo ndi inu amene.
18 Choncho musadzinyenge. Ngati wina wa inu akuganiza kuti ndi wanzeru pa mulingo wa mʼbado uno, ayenera kukhala “wopusa” kuti athe kukhala wanzeru. 19 Pakuti nzeru ya dziko lapansi ndi yopusa pamaso pa Mulungu. Monga kwalembedwera kuti, “Iye amakola anthu ochenjera mu msampha wa kuchenjera kwawo,” 20 ndiponso, “Ambuye amadziwa kuti maganizo a wanzeru ndi opandapake.” 21 Choncho, wina asanyadire anthu chabe! Zonse ndi zanu, 22 kaya Paulo kapena Apolo kapena Kefa kapena dziko lapansi, kapena moyo, kapena imfa, kapena tsopano, kapena mʼtsogolo, zonse ndi zanu, 23 ndipo inu ndinu a Khristu, ndipo Khristu ndi wa Mulungu.
1 Corinthians 3
King James Version
3 And I, brethren, could not speak unto you as unto spiritual, but as unto carnal, even as unto babes in Christ.
2 I have fed you with milk, and not with meat: for hitherto ye were not able to bear it, neither yet now are ye able.
3 For ye are yet carnal: for whereas there is among you envying, and strife, and divisions, are ye not carnal, and walk as men?
4 For while one saith, I am of Paul; and another, I am of Apollos; are ye not carnal?
5 Who then is Paul, and who is Apollos, but ministers by whom ye believed, even as the Lord gave to every man?
6 I have planted, Apollos watered; but God gave the increase.
7 So then neither is he that planteth any thing, neither he that watereth; but God that giveth the increase.
8 Now he that planteth and he that watereth are one: and every man shall receive his own reward according to his own labour.
9 For we are labourers together with God: ye are God's husbandry, ye are God's building.
10 According to the grace of God which is given unto me, as a wise masterbuilder, I have laid the foundation, and another buildeth thereon. But let every man take heed how he buildeth thereupon.
11 For other foundation can no man lay than that is laid, which is Jesus Christ.
12 Now if any man build upon this foundation gold, silver, precious stones, wood, hay, stubble;
13 Every man's work shall be made manifest: for the day shall declare it, because it shall be revealed by fire; and the fire shall try every man's work of what sort it is.
14 If any man's work abide which he hath built thereupon, he shall receive a reward.
15 If any man's work shall be burned, he shall suffer loss: but he himself shall be saved; yet so as by fire.
16 Know ye not that ye are the temple of God, and that the Spirit of God dwelleth in you?
17 If any man defile the temple of God, him shall God destroy; for the temple of God is holy, which temple ye are.
18 Let no man deceive himself. If any man among you seemeth to be wise in this world, let him become a fool, that he may be wise.
19 For the wisdom of this world is foolishness with God. For it is written, He taketh the wise in their own craftiness.
20 And again, The Lord knoweth the thoughts of the wise, that they are vain.
21 Therefore let no man glory in men. For all things are your's;
22 Whether Paul, or Apollos, or Cephas, or the world, or life, or death, or things present, or things to come; all are your's;
23 And ye are Christ's; and Christ is God's.
1 Corinthians 3
English Standard Version
Divisions in the Church
3 But I, brothers,[a] could not address you as (A)spiritual people, but as (B)people of the flesh, as (C)infants in Christ. 2 (D)I fed you with milk, not solid food, for (E)you were not ready for it. And even now you are not yet ready, 3 for you are still of the flesh. For while there is (F)jealousy and strife among you, are you not of the flesh and behaving only in a human way? 4 For (G)when one says, “I follow Paul,” and another, “I follow Apollos,” (H)are you not being merely human?
5 What then is Apollos? What is Paul? (I)Servants through whom you believed, (J)as the Lord assigned to each. 6 (K)I planted, (L)Apollos watered, (M)but God gave the growth. 7 So (N)neither he who plants nor he who waters is anything, but only God who gives the growth. 8 He who plants and he who waters are one, and each (O)will receive his wages according to his labor. 9 For we are (P)God's fellow workers. You are God's field, (Q)God's building.
10 (R)According to the grace of God given to me, like a skilled[b] master builder I laid a (S)foundation, and (T)someone else is building upon it. Let each one take care how he builds upon it. 11 For no one can lay a (U)foundation other (V)than that which is laid, (W)which is Jesus Christ. 12 Now if anyone builds on the foundation with gold, silver, precious stones, wood, hay, straw— 13 (X)each one's work will become manifest, for the Day will disclose it, because it will be revealed (Y)by fire, and (Z)the fire will test what sort of work each one has done. 14 If the work that anyone has built on the foundation survives, (AA)he will receive a reward. 15 If anyone's work is burned up, he will suffer loss, though he himself will be saved, (AB)but only as through fire.
16 (AC)Do you not know that you[c] are God's temple and that God's Spirit dwells in you? 17 If anyone destroys God's temple, God will destroy him. For (AD)God's temple is holy, and you are that temple.
18 (AE)Let no one deceive himself. (AF)If anyone among you thinks that he is wise in this age, let him become a fool that he may become wise. 19 For (AG)the wisdom of this world is folly with God. For it is written, (AH)“He catches the wise in their craftiness,” 20 and again, (AI)“The Lord knows the thoughts of the wise, that they are futile.” 21 So (AJ)let no one boast in men. For (AK)all things are yours, 22 whether Paul or Apollos or Cephas or the world or life or death or the present or the future—all are yours, 23 and (AL)you are Christ's, and (AM)Christ is God's.
Footnotes
- 1 Corinthians 3:1 Or brothers and sisters
- 1 Corinthians 3:10 Or wise
- 1 Corinthians 3:16 The Greek for you is plural in verses 16 and 17
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.
The ESV® Bible (The Holy Bible, English Standard Version®), © 2001 by Crossway, a publishing ministry of Good News Publishers. ESV Text Edition: 2025.