出埃及記 26
Chinese Contemporary Bible (Traditional)
聖幕的做法
26 「要用十幅幔子造聖幕,這些幔子要用細麻線和藍、紫、朱紅三種顏色的毛線織成,還要用精緻的手工繡上基路伯天使。 2 每幅幔子的尺寸都一樣,長十二米、寬兩米。 3 每五幅連在一起,形成兩幅大幔子。 4 要在每幅大幔子邊緣釘上藍色的扣環, 5 每幅大幔子釘五十個,扣環要兩兩相對, 6 再做五十個金鉤,把兩幅大幔子連在一起,成為聖幕。
7 「要用山羊毛織十一幅幔子作聖幕的罩棚, 8 每幅長十三米、寬兩米。十一幅幔子的尺寸都要一樣。 9 然後,你們要把五幅連成一大幅,其餘六幅連成一大幅,第六幅要在聖幕前疊起來。 10 要在這兩幅幔子的邊緣各釘上五十個扣環, 11 再做五十個銅鉤,把這兩幅大幔子扣在一起,成為一個完整的罩棚。 12 鋪罩棚所剩下來的半幅幔子要垂到聖幕後面。 13 兩旁餘下的幔子可垂在聖幕的兩邊,每邊長五十釐米,蓋著聖幕。 14 罩棚上面要蓋一層染成紅色的公羊皮,再蓋一層海狗皮做頂蓋。
15 「要用皂莢木做支撐聖幕的木板, 16 每塊木板長四米,寬六十六釐米。 17 每塊木板要有兩個接榫,好連接在一起。聖幕的所有木板都要這樣。 18 聖幕的南面要有二十塊木板, 19 在這些木板下面要造四十個帶凹槽的銀底座,每塊木板下面兩個,用來套在木板的兩個接榫上。 20 聖幕北面也要有二十塊木板, 21 這些木板下面也要裝上四十個帶凹槽的銀底座,每塊木板下面有兩個銀底座。 22 聖幕後面,就是西面,要有六塊木板。 23 聖幕後面的兩個拐角要各有兩塊木板, 24 木板的下端連於底座[a],頂端用一個環固定。兩個拐角都要這樣做。 25 這樣,兩端便共有八塊木板,每塊木板下面各有兩個帶凹槽的銀底座,一共有十六個銀底座。
26-27 「要用皂莢木做橫閂,聖幕左右兩邊及後面的牆板上要各有五根橫閂, 28 攔腰固定牆板的那根橫閂要從這端貫穿到那端。 29 所有的木板和橫閂都要包上金,並要在木板上造金環,用來穿橫閂。 30 要照著我在山上所指示你的樣式,把聖幕支搭起來。
造至聖所的條例
31 「要用細麻線和藍色、紫色、朱紅色的線織成一幅幔子,上面用精緻的手工繡上基路伯天使。 32 要把這幅幔子掛在四根包金的皂莢木柱上,木柱上面有金鉤,木柱立在四個帶凹槽的銀底座上面。 33 要把整幅幔子掛在木柱的金鉤上,把約櫃抬進幔子裡。這幔子把聖幕分為兩個部分,幔子裡面是至聖所,外面是聖所。 34 要把施恩座放在至聖所裡面的約櫃上。 35 桌子要放在幔子的外面、聖所的北面,燈臺放在南面,跟桌子相對。 36 要用細麻線和藍色、紫色、朱紅色的線繡製聖幕的門簾。 37 要用皂莢木做五根掛門簾的柱子,柱子包上金,上面要有金鉤,並要為柱子造五個帶凹槽的銅底座。
Footnotes
- 26·24 「連於底座」或譯「是雙層的」。
Exodus 26
King James Version
26 Moreover thou shalt make the tabernacle with ten curtains of fine twined linen, and blue, and purple, and scarlet: with cherubims of cunning work shalt thou make them.
2 The length of one curtain shall be eight and twenty cubits, and the breadth of one curtain four cubits: and every one of the curtains shall have one measure.
3 The five curtains shall be coupled together one to another; and other five curtains shall be coupled one to another.
4 And thou shalt make loops of blue upon the edge of the one curtain from the selvedge in the coupling; and likewise shalt thou make in the uttermost edge of another curtain, in the coupling of the second.
5 Fifty loops shalt thou make in the one curtain, and fifty loops shalt thou make in the edge of the curtain that is in the coupling of the second; that the loops may take hold one of another.
6 And thou shalt make fifty taches of gold, and couple the curtains together with the taches: and it shall be one tabernacle.
7 And thou shalt make curtains of goats' hair to be a covering upon the tabernacle: eleven curtains shalt thou make.
8 The length of one curtain shall be thirty cubits, and the breadth of one curtain four cubits: and the eleven curtains shall be all of one measure.
9 And thou shalt couple five curtains by themselves, and six curtains by themselves, and shalt double the sixth curtain in the forefront of the tabernacle.
10 And thou shalt make fifty loops on the edge of the one curtain that is outmost in the coupling, and fifty loops in the edge of the curtain which coupleth the second.
11 And thou shalt make fifty taches of brass, and put the taches into the loops, and couple the tent together, that it may be one.
12 And the remnant that remaineth of the curtains of the tent, the half curtain that remaineth, shall hang over the backside of the tabernacle.
13 And a cubit on the one side, and a cubit on the other side of that which remaineth in the length of the curtains of the tent, it shall hang over the sides of the tabernacle on this side and on that side, to cover it.
14 And thou shalt make a covering for the tent of rams' skins dyed red, and a covering above of badgers' skins.
15 And thou shalt make boards for the tabernacle of shittim wood standing up.
16 Ten cubits shall be the length of a board, and a cubit and a half shall be the breadth of one board.
17 Two tenons shall there be in one board, set in order one against another: thus shalt thou make for all the boards of the tabernacle.
18 And thou shalt make the boards for the tabernacle, twenty boards on the south side southward.
19 And thou shalt make forty sockets of silver under the twenty boards; two sockets under one board for his two tenons, and two sockets under another board for his two tenons.
20 And for the second side of the tabernacle on the north side there shall be twenty boards:
21 And their forty sockets of silver; two sockets under one board, and two sockets under another board.
22 And for the sides of the tabernacle westward thou shalt make six boards.
23 And two boards shalt thou make for the corners of the tabernacle in the two sides.
24 And they shall be coupled together beneath, and they shall be coupled together above the head of it unto one ring: thus shall it be for them both; they shall be for the two corners.
25 And they shall be eight boards, and their sockets of silver, sixteen sockets; two sockets under one board, and two sockets under another board.
26 And thou shalt make bars of shittim wood; five for the boards of the one side of the tabernacle,
27 And five bars for the boards of the other side of the tabernacle, and five bars for the boards of the side of the tabernacle, for the two sides westward.
28 And the middle bar in the midst of the boards shall reach from end to end.
29 And thou shalt overlay the boards with gold, and make their rings of gold for places for the bars: and thou shalt overlay the bars with gold.
30 And thou shalt rear up the tabernacle according to the fashion thereof which was shewed thee in the mount.
31 And thou shalt make a vail of blue, and purple, and scarlet, and fine twined linen of cunning work: with cherubims shall it be made:
32 And thou shalt hang it upon four pillars of shittim wood overlaid with gold: their hooks shall be of gold, upon the four sockets of silver.
33 And thou shalt hang up the vail under the taches, that thou mayest bring in thither within the vail the ark of the testimony: and the vail shall divide unto you between the holy place and the most holy.
34 And thou shalt put the mercy seat upon the ark of the testimony in the most holy place.
35 And thou shalt set the table without the vail, and the candlestick over against the table on the side of the tabernacle toward the south: and thou shalt put the table on the north side.
36 And thou shalt make an hanging for the door of the tent, of blue, and purple, and scarlet, and fine twined linen, wrought with needlework.
37 And thou shalt make for the hanging five pillars of shittim wood, and overlay them with gold, and their hooks shall be of gold: and thou shalt cast five sockets of brass for them.
Eksodo 26
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Chihema cha Mapemphero
26 “Panga chihema pogwiritsa ntchito nsalu khumi zofewa, zosalala ndi zolukidwa bwino, zobiriwira, zapepo ndi zofiira. Ndipo anthu aluso apete pa nsaluzo Akerubi. 2 Nsalu zonse zikhale zofanana. Mulitali mwake zikhale mamita khumi ndi atatu, mulifupi mamita awiri. 3 Ulumikize nsalu zisanu kuti ikhale nsalu imodzi. Uchite chimodzimodzi ndi nsalu zisanu zinazo. 4 Panga zokolowekamo za nsalu yobiriwira mʼmphepete mwa nsalu imodzi yotsiriza ya mbali ina. Uchitenso chimodzimodzi ndi nsalu yotsiriza ya mbali inayo. 5 Upange zokolowekamo 50 pa nsalu yoyamba ndi zokolowekamo makumi asanu zinanso pa nsalu inayo. Upange motero kuti zokolowekamozo ziziyangʼanana. 6 Kenaka upange ngowe zagolide makumi asanu zolumikizira nsalu ziwirizo kuti zipange chihema chimodzi.
7 “Upange nsalu za ubweya wambuzi zophimba pamwamba pa chihemacho. Nsalu zonse pamodzi zikhale khumi ndi imodzi. 8 Nsalu zonse khumi ndi imodzi zikhale zofanana. Mulitali mwake mukhale mamita khumi ndi anayi ndipo mulifupi mwake mukhale mamita awiri. 9 Ulumikize nsalu zisanu kuti ikhale nsalu imodzi ndipo zina zisanu ndi imodzi uzilumikizenso kuti ikhale nsalu imodzinso. Nsalu yachisanu ndi chimodzi imene ili kutsogolo kwa tenti uyipinde pawiri. 10 Upange zokolowekamo 50 mʼmphepete mwa nsalu imodzi yotsirizira ya nsalu yoyamba yolumikiza ija. Upangenso zokolowekamo zina 50 mʼmphepete mwa nsalu yotsirizira ya nsalu inanso yolumikiza ija. 11 Kenaka upange ngowe 50 zamkuwa ndipo uzilowetse mu zokolowekazo. Ndiye uphatikize nsalu ziwirizo kuti tentiyo ikhale imodzi. 12 Theka lotsalira la nsaluyo lidzalendewera kumbuyo kwa chihemacho. 13 Nsalu yotsalira ya masentimita 46 mulitali mwake mʼmbali zonse ziwiri idzalendewere kuphimba mbali ziwirizo. 14 Upange chikopa cha nkhosa zazimuna cha utoto wofiira chophimbira tentiyo ndipo pamwamba pake upangireponso chophimbira china cha zikopa za akatumbu.
15 “Upange maferemu amatabwa amtengo wa mkesha oyimikira chihemacho. 16 Feremu iliyonse ikhale yotalika mamita anayi ndipo mulifupi mwake mukhale masentimita 69. 17 Thabwa lililonse likhale ndi zolumikizira ziwiri. Upange maferemu onse a chihemacho ndi matabwa otere. 18 Upange maferemu makumi awiri a mbali yakummwera kwa chihemacho. 19 Ndipo upange matsinde 40 asiliva ndipo uwayike pansi pa maferemuwo. Pansi pa feremu iliyonse pakhale matsinde awiri ogwiriziza zolumikizira ziwiri zija. 20 Ndipo mbali yakumpoto ya chihemacho upangenso maferemu makumi awiri. 21 Upangenso matsinde 40 asiliva, awiri pansi pa feremu iliyonse. 22 Upange maferemu asanu ndi imodzi a kumbuyo kwa tenti, kumbali yakumadzulo. 23 Ndipo upangenso maferemu awiri a pa ngodya yakumbuyo kwenikweni kwa tenti. 24 Pa ngodya ziwirizi pakhale maferemu awiri, kuyambira pansi mpaka pamwamba ndipo alumikizidwe pa ngowe imodzi. Maferemu onse akhale ofanana. 25 Choncho pakhale maferemu asanu ndi atatu ndiponso matsinde 16 asiliva, awiri akhale pansi pa feremu iliyonse.
26 “Upange mitanda ya matabwa amtengo wa mkesha: mitanda isanu ikhale ya maferemu a mbali imodzi ya chihema, 27 mitanda isanu inanso ikhale ya maferemu a mbali inayo. Pakhalenso mitanda ina isanu ya mbali yakumadzulo, kumapeto kwenikweni kwa chihema. 28 Mtanda wapakati pa maferemuwo uchokere pa maferemu a mbali ina mpaka mbali inanso. 29 Maferemuwo uwakute ndi golide ndiponso upange mphete zagolide zogwiriziza mitandayo. Ndipo mitandayonso uyikute ndi golide.
30 “Upange chihema mofanana ndi momwe ndinakuonetsera pa phiri paja.
31 “Upange nsalu yokhala ndi mtundu wamtambo, wapepo ndi ofiira ndipo nsaluyo ikhale yolukidwa bwino, yofewa ndi yosalala. Ndipo anthu aluso apetepo zithunzi za Akerubi. 32 Nsaluyo uyikoloweke pa nsanamira zinayi zamtengo wa mkesha zokutidwa ndi golide zomwe zili ndi ngowe zagolide, zomwe zayima pa matsinde asiliva anayi. 33 Ukoloweke kataniyo ku ngowe ndipo uyike Bokosi la Chipangano mʼkatimo. Kataniyo idzalekanitse malo wopatulika ndi malo wopatulika kwambiri. 34 Uyike chivundikiro pa bokosi laumboni ku malo wopatulika kwambiri. 35 Uyike tebulo kunja kwa katani yotchinga cha kumpoto kwa chihema ndipo uyike choyikapo nyale chija kummwera moyangʼanana ndi tebulolo.
36 “Pa chipata cholowera mu chihema, uyikepo nsalu yamtundu wamtambo, wapepo ndi ofiira, yomwe ndi yofewa ndi yosalala, yopetedwa bwino ndi amisiri aluso. 37 Upange ngowe zagolide za nsaluyo ndi nsanamira zisanu zamtengo wa mkesha ndipo uzikute ndi golide. Upangenso matsinde asanu amkuwa a nsanamirazo.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.