Miyambo 24:23
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Malangizo Enanso a Anthu Anzeru
23 Malangizo enanso a anthu anzeru ndi awa:
Kukondera poweruza mlandu si chinthu chabwino:
Miyambo 28:21
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
21 Kukondera si kwabwino,
ena amachita zolakwazo chifukwa cha kachidutswa ka buledi.
Yakobo 2:1-9
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Kuchita Tsankho Nʼkosaloledwa
2 Abale anga, okhulupirira Yesu Khristu waulemerero, musaonetse tsankho. 2 Tangoganizirani, pakati panu patabwera munthu atavala mphete yagolide ndi zovala zapamwamba, ndipo winanso wosauka nʼkulowa atavala sanza. 3 Ngati musamala kwambiri munthu wovala bwinoyu uja, nʼkumuwuza kuti, “Khalani pa mpando wabwinowu,” koma wosauka uja nʼkumuwuza kuti, “Ima apo,” kapena “Khala pansi pafupi ndi chopondapo mapazi angawa,” 4 kodi simunachite tsankho pakati panu ndi kukhala oweruza a maganizo oyipa?
5 Tamverani abale anga okondedwa, kodi Mulungu sanasankhe amene dziko lapansi limawaona ngati amphawi kuti akhale olemera mʼchikhulupiriro ndi kulowa ufumu umene Iye analonjeza kwa amene amamukonda? 6 Koma mwakhala mukunyoza amphawi. Kodi si anthu olemerawa amene akukudyerani masuku pamutu? Si anthu amenewa amene amakukokerani ku bwalo la milandu? 7 Kodi si omwewa amene amachita chipongwe dzina la wolemekezeka, limene inu mumatchulidwa?
8 Ngati musungadi lamulo laufumu lija lopezeka mʼMalemba lakuti, “Konda mnansi wako monga iwe mwini,” ndiye kuti mukuchita bwino. 9 Koma mukamaonetsa tsankho mukuchimwa, ndipo ndinu wochimwa monga wophwanya lamulo.
Read full chapterThe Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.