Numeri 1:51
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
51 Pamene akusamutsa tentiyo, Alevi ndiwo aziyitsitsa, akafuna kuyimanganso, Alevi ndiwo aziyimiritsa. Wina aliyense amene adzayandikire tentiyo adzaphedwa.
Read full chapter
Numbers 1:51
New International Version
51 Whenever the tabernacle(A) is to move,(B) the Levites are to take it down, and whenever the tabernacle is to be set up, the Levites shall do it.(C) Anyone else who approaches it is to be put to death.(D)
Numeri 4:5-15
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
5 Pamene anthu akusamuka pa msasa, Aaroni ndi ana ake aamuna azilowa mu tenti ndi kuchotsa chinsalu chotchingira ndi kuphimba nacho bokosi la umboni. 6 Ndipo azikuta bokosilo ndi zikopa za akatumbu ndi kuyala pamwamba pake nsalu ya mtundu wa thambo ndi kuyika mitengo yonyamulira mʼmalo mwake.
7 “Pa tebulo pamene pamakhala buledi wa ansembe aziyalapo nsalu ya mtundu wa thambo, ndipo aziyikapo mbale, mabeseni, zipande ndi mitsuko yoperekera nsembe yachakumwa. Aziyikaponso buledi wokhala pamenepo nthawi zonse. 8 Tsono pamwamba pa izi aziyalapo nsalu yofiira, ndi kuzikuta mʼzikopa za akatumbu ndi kuyika mitengo yonyamulira mʼmalo mwake.
9 “Azitenga nsalu ya mtundu wa thambo ndi kukutira choyikapo nyale, pamodzi ndi nyale zake, zopanira zake, zotengera zake ndi mitsuko yonse yosungiramo mafuta. 10 Kenaka achikulunge pamodzi ndi zipangizo zake zonse mʼzikopa za akatumbu ndi kuchiyika pa chonyamulira chake.
11 “Pamwamba pa guwa la golide aziyalapo nsalu ya mtundu wa thambo ndi kukutira ndi zikopa za akatumbu ndi kuyika mʼmalo mwake mitengo yonyamulira.
12 “Azitenga zipangizo zonse zogwiritsira ntchito ku malo wopatulika, azizikulunga mʼnsalu ya mtundu wa thambo, azizikuta ndi zikopa za akatumbu ndi kuziyika pa zonyamulira zake.
13 “Azichotsa phulusa la pa guwa lansembe lamkuwa ndi kuyalapo nsalu yapepo pamwamba pake. 14 Kenaka aziyikapo zipangizo zonse zogwiritsira ntchito potumikira pa guwa, kuphatikizapo miphika yowotchera nyama, mafoloko otengera nyama, zowolera phulusa ndi mbale zowazira magazi pa guwa lansembe ndipo pamwamba pake aziyalapo zikopa za akatumbu ndi kuziyika mʼzonyamulira zake.
15 “Aaroni ndi ana ake aamuna akamaliza kukutira ziwiya za ku malo wopatulika ndi zipangizo zopatulika zonse, ndipo akakonzeka kusamuka pamalopo, Akohati abwere kudzazinyamula koma asagwire zinthu zopatulikazo. Akatero adzafa. Izi ndizo zinthu zimene Akohati ayenera kunyamula mu tenti ya msonkhano.
Read full chapter
Numbers 4:5-15
New International Version
5 When the camp is to move,(A) Aaron and his sons are to go in and take down the shielding curtain(B) and put it over the ark of the covenant law.(C) 6 Then they are to cover the curtain with a durable leather,[a](D) spread a cloth of solid blue over that and put the poles(E) in place.
7 “Over the table of the Presence(F) they are to spread a blue cloth and put on it the plates, dishes and bowls, and the jars for drink offerings;(G) the bread that is continually there(H) is to remain on it. 8 They are to spread a scarlet cloth over them, cover that with the durable leather and put the poles(I) in place.
9 “They are to take a blue cloth and cover the lampstand that is for light, together with its lamps, its wick trimmers and trays,(J) and all its jars for the olive oil used to supply it. 10 Then they are to wrap it and all its accessories in a covering of the durable leather and put it on a carrying frame.(K)
11 “Over the gold altar(L) they are to spread a blue cloth and cover that with the durable leather and put the poles(M) in place.
12 “They are to take all the articles(N) used for ministering in the sanctuary, wrap them in a blue cloth, cover that with the durable leather and put them on a carrying frame.(O)
13 “They are to remove the ashes(P) from the bronze altar(Q) and spread a purple cloth over it. 14 Then they are to place on it all the utensils(R) used for ministering at the altar, including the firepans,(S) meat forks,(T) shovels(U) and sprinkling bowls.(V) Over it they are to spread a covering of the durable leather and put the poles(W) in place.
15 “After Aaron and his sons have finished covering the holy furnishings and all the holy articles, and when the camp is ready to move,(X) only then are the Kohathites(Y) to come and do the carrying.(Z) But they must not touch the holy things(AA) or they will die.(AB) The Kohathites are to carry those things that are in the tent of meeting.
Footnotes
- Numbers 4:6 Possibly the hides of large aquatic mammals; also in verses 8, 10, 11, 12, 14 and 25
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.
Holy Bible, New International Version®, NIV® Copyright ©1973, 1978, 1984, 2011 by Biblica, Inc.® Used by permission. All rights reserved worldwide.
NIV Reverse Interlinear Bible: English to Hebrew and English to Greek. Copyright © 2019 by Zondervan.