Yohane 18:1-13
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Amugwira Yesu
18 Yesu atamaliza kupemphera, Iye anachoka ndi ophunzira ake ndi kuwoloka chigwa cha Kidroni. Kumbali inayo kunali munda wa Olivi, ndipo Iye ndi ophunzira ake analowamo.
2 Tsopano Yudasi, amene anamupereka amadziwa malowo chifukwa Yesu ankakumana ndi ophunzira ake kumeneko. 3 Choncho Yudasi anabwera ku munda, akutsogolera gulu la asilikali ndi akuluakulu ena ochokera kwa akulu a ansembe ndi Afarisi. Iwo anali atanyamula miyuni, nyale ndi zida.
4 Yesu, podziwa zonse zimene zimati zichitike kwa Iye, anatuluka ndi kuwafunsa kuti, “Kodi mukufuna ndani?”
5 Iwo anayankha kuti, “Yesu wa ku Nazareti.”
Yesu anati, “Ndine.” (Ndipo Yudasi womuperekayo anali atayima nawo pamenepo). 6 Pamene Yesu anati, “Ndine,” iwo anabwerera mʼmbuyo ndi kugwa pansi.
7 Iye anawafunsanso kuti, “Kodi mukumufuna ndani?”
Ndipo iwo anati, “Yesu wa ku Nazareti.”
8 Yesu anayankha kuti, “Ine ndakuwuzani kuti Ndine. Ngati inu mukufuna Ine, asiyeni anthu awa apite.” 9 Izi zinachitika kuti mawu amene Iye anayankhula akwaniritsidwe: “Ine sindinataye ndi mmodzi yemwe mwa iwo amene mwandipatsa.”
10 Kenaka Simoni amene anali ndi lupanga analitulutsa ndi kutema nalo wantchito wa wamkulu wa ansembe, nadula khutu lake la kudzanja lamanja. (Dzina la wantchitoyo ndi Makusi).
11 Yesu analamula Petro kuti, “Bwezera lupanga mʼchimake! Kodi Ine ndisamwere chikho chimene Atate andipatsa?”
Amutengera Yesu kwa Anasi
12 Kenaka gulu la asilikali ndi olamulira wawo ndi akuluakulu a Ayuda anamugwira Yesu. Iwo anamumanga. 13 Poyamba anapita naye kwa Anasi amene anali mkamwini wa Kayafa, mkulu wa ansembe chaka chimenecho.
Read full chapterThe Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.