Eksodo 25:31-39
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Choyikapo Nyale
31 “Upange choyikapo nyale chagolide wabwino kwambiri. Tsinde lake ndi mphanda zake zikhale zosulidwa ndi nyundo. Zikho zake zokhala ndi mphukira ndi maluwa ake zipangidwire kumodzi. 32 Mʼmbali mwake mukhale mphanda zisanu ndi imodzi, zitatu mbali iliyonse. 33 Zikho zitatu zokhala ngati za maluwa amtowo, mphukira ndi duwa zikhale pa mphanda yoyamba. Pa mphanda yachiwiri pakhalenso zikho zitatu zokhala ngati za maluwa amtowo, mphukira ndi duwa. Ndipo mphanda zonse zisanu ndi imodzi zikhale chimodzimodzi ndipo zituluke mʼchoyikapo nyalecho. 34 Pa choyikapo nyalecho pakhale zikho zinayi zopangidwa ngati maluwa amtowo ali ndi mphukira ndi maluwa. 35 Mphukira yoyamba ikhale mʼmunsi mwa nthambi ziwiri zoyamba za pa choyikapo nyale. Mphukira yachiwiri ikhale mʼmunsi mwa nthambi ziwiri zinazo. Ndipo mphukira yachitatu ikhale mʼmunsi mwa nthambi zina ziwirinso. Zonse pamodzi zikhale nthambi zisanu ndi imodzi 36 Mphukira ndi nthambi zonse zisulidwe kumodzi ndi choyikapo nyalecho ndi golide wabwino kwambiri.
37 “Ndipo upange nyale zisanu ndi ziwiri ndi kuziyika pa choyikapo nyalecho kuti ziwunikire kutsogolo. 38 Mbaniro ndi zowolera phulusa zikhale zagolide wabwino kwambiri. 39 Choyikapo nyale ndi zipangizo zonse zipangidwe ndi golide wabwino kwambiri wolemera makilogalamu 34.
Read full chapterThe Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.