Aroma 10
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
10 Abale, chokhumba cha mtima wanga ndi pemphero langa kwa Mulungu ndi chakuti Aisraeli apulumutsidwe. 2 Popeza ndiwachitira umboni kuti ndi achangu pa zinthu za Mulungu koma osati mwachidziwitso. 3 Pakuti sanadziwe chilungamo chochokera kwa Mulungu ndipo anafuna kukhazikitsa chawochawo. Iwo sanagonjere chilungamo cha Mulungu. 4 Khristu ndiye mathero amalamulo kuti aliyense amene akhulupirira akhale olungama pamaso pa Mulungu.
5 Mose akulemba motere zachilungamo cha malamulo, “Munthu amene achita zinthu izi adzakhala ndi moyo pozichita.” 6 Koma chilungamo cha chikhulupiriro chikuti, “Usanene mu mtima mwako kuti, ‘Kodi ndani amene akwere kumwamba?’ ” (ndiko, kukatsitsa Khristu) 7 “kapena ‘Ndani adzatsikira ku dziko la anthu akufa?’ ” (ndiko, kukamutenga Khristu kwa akufa). 8 Nanga akuti chiyani? “Mawu ali pafupi ndi inu. Ali mʼkamwa mwanu ndi mu mtima mwanu.” Ndiwo mawu achikhulupiriro amene ife tikuwalalikira, 9 kuti ngati udzavomereza ndi pakamwa pako kuti, “Yesu ndiye Ambuye,” ndi kukhulupirira mu mtima mwako kuti Mulungu anamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka. 10 Pakuti ndi mtima wanu mukhulupirira ndi kulungamitsidwa, ndipo ndi pakamwa panu muvomereza ndi kupulumutsidwa. 11 Pakuti Malemba akuti, “Aliyense amene akhulupirira Iye, sadzachititsidwa manyazi.” 12 Pakuti palibe kusiyana pakati pa Myuda ndi a mitundu ina, pakuti Ambuye mmodzi yemweyo ndi Ambuye wa onse ndipo amadalitsa mochuluka onse amene ayitana pa Iye 13 pakuti, “Aliyense amene adzayitana pa dzina la Ambuye adzapulumuka.”
14 Kodi adzayitana bwanji amene sanamukhulupirire? Ndipo adzakhulupirira bwanji asanamve za Iye? Ndipo adzamva bwanji popanda wina kulalikira kwa iwo? 15 Ndipo iwo adzalalikira bwanji osatumidwa? Kwalembedwa kuti, “Akongoladi mapazi a iwo amene amabweretsa Uthenga Wabwino!”
16 Koma si onse amene anavomereza Uthenga Wabwino. Pakuti Yesaya akuti, “Ambuye, ndani amene wakhulupirira uthenga wathu?” 17 Motero, chikhulupiriro chimabwera pamene timva uthenga ndipo uthenga umamveka kuchokera ku mawu a Khristu. 18 Koma ndikufunsa kuti kodi iwo anamva? Inde, iwo anamva kuti,
“Liwu lawo linamveka ponseponse pa dziko lapansi.
Mawu awo anafika ku malekezero a dziko lonse.”
19 Ine ndifunsanso kuti, kodi Israeli sanazindikire? Poyamba Mose akuti,
“Ine ndidzawachititsa kuti achite nsanje ndi mtundu wina wopandapake.
Ine ndidzawakwiyitsa ndi mtundu wina wachabechabe.”
20 Ndipo Yesaya molimba mtima akuti,
“Anandipeza anthu amene sanali kundifunafuna.
Ndinadzionetsera kwa amene sanafunse za Ine.”
21 Koma zokhudzana ndi Aisraeli akuti,
“Tsiku lonse ndinatambasulira manja anga
kwa anthu osandimvera ndi okanika.”
Romans 10
King James Version
10 Brethren, my heart's desire and prayer to God for Israel is, that they might be saved.
2 For I bear them record that they have a zeal of God, but not according to knowledge.
3 For they being ignorant of God's righteousness, and going about to establish their own righteousness, have not submitted themselves unto the righteousness of God.
4 For Christ is the end of the law for righteousness to every one that believeth.
5 For Moses describeth the righteousness which is of the law, That the man which doeth those things shall live by them.
6 But the righteousness which is of faith speaketh on this wise, Say not in thine heart, Who shall ascend into heaven? (that is, to bring Christ down from above:)
7 Or, Who shall descend into the deep? (that is, to bring up Christ again from the dead.)
8 But what saith it? The word is nigh thee, even in thy mouth, and in thy heart: that is, the word of faith, which we preach;
9 That if thou shalt confess with thy mouth the Lord Jesus, and shalt believe in thine heart that God hath raised him from the dead, thou shalt be saved.
10 For with the heart man believeth unto righteousness; and with the mouth confession is made unto salvation.
11 For the scripture saith, Whosoever believeth on him shall not be ashamed.
12 For there is no difference between the Jew and the Greek: for the same Lord over all is rich unto all that call upon him.
13 For whosoever shall call upon the name of the Lord shall be saved.
14 How then shall they call on him in whom they have not believed? and how shall they believe in him of whom they have not heard? and how shall they hear without a preacher?
15 And how shall they preach, except they be sent? as it is written, How beautiful are the feet of them that preach the gospel of peace, and bring glad tidings of good things!
16 But they have not all obeyed the gospel. For Esaias saith, Lord, who hath believed our report?
17 So then faith cometh by hearing, and hearing by the word of God.
18 But I say, Have they not heard? Yes verily, their sound went into all the earth, and their words unto the ends of the world.
19 But I say, Did not Israel know? First Moses saith, I will provoke you to jealousy by them that are no people, and by a foolish nation I will anger you.
20 But Esaias is very bold, and saith, I was found of them that sought me not; I was made manifest unto them that asked not after me.
21 But to Israel he saith, All day long I have stretched forth my hands unto a disobedient and gainsaying people.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.