1 Samueli 11:9-15
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
9 Tsono Sauli anawuza amithenga ochokera ku Yabesi aja kuti, “Mukawawuze anthu a ku Yabesi Giliyadi kuti mawa nthawi ya masana adzapulumutsidwa.” Pamene amithengawo anapita ndi kukafotokoza nkhani imeneyi kwa anthu a ku Yabesi, iwo anasangalala kwambiri. 10 Choncho anthu a ku Yabesi anawuza Nahasi kuti, “Mawa tidzadzipereka kwa inu ndipo inu mudzachite nafe chilichonse chokukomerani.”
11 Tsono mmawa mwake Sauli anagawa anthuwo mʼmagulu atatu. Mmamawa kusanache iwo analowa mʼmisasa ya Aamoni ndi kuwapha mpaka masana. Amene anapulumuka anabalalika, aliyense kwakekwake.
Sauli Avomerezedwa kukhala mfumu
12 Kenaka anthu anafunsa Samueli kuti, “Kodi ndani aja ankanena kuti, ‘Kodi Sauli nʼkutilamulira ife?’ Bwera nawoni kuno kuti tidzawaphe.”
13 Koma Sauli anati, “Palibe amene ati aphedwe lero, pakuti lero lino Yehova wagwira ntchito yopulumutsa Israeli.”
14 Ndipo Samueli anati kwa anthuwo, “Tiyeni tipite ku Giligala kuti tikatsimikizenso kuti Sauli ndi mfumu yathu.” 15 Choncho anthu onse anapita ku Giligala ndipo kumeneko Samueli anakalonga Sauli ufumu pamaso pa Yehova. Pambuyo pake anthu anapereka nsembe zachiyanjano pamaso pa Yehova, ndipo Sauli ndi Aisraeli onse anachita chikondwerero chachikulu.
Read full chapterThe Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.