Add parallel Print Page Options

“Iye anayankha kuti, ‘Migolo yamafuta a olivi 800.’

“Kapitawo uja anamuwuza iye, ‘Tenga pamene unalemba ngongole yakoyo, khala pansi msanga ndipo lemba kuti ndi migolo 400.’

“Kenaka iye anafunsa wachiwiri kuti, ‘Nanga iwe uli ndi ngongole yotani?’

“Iye ayankha kuti madengu a tirigu 1,000.

“Iye anati, ‘Tenga pamene unalemba ngongole yakoyo ndipo ulembepo 800.’

“Bwana anayamikira kapitawo wosakhulupirikayo popeza anachita mochenjera. Pakuti anthu a dziko lino lapansi ndi ochenjera kwambiri akamachita zinthu ndi anthu ofanana nawo kuposa anthu a kuwunika.

Read full chapter