但以理書 2
Chinese Contemporary Bible (Traditional)
尼布甲尼撒的夢
2 尼布甲尼撒在執政第二年做了夢,心裡煩亂,無法入睡, 2 便派人召來術士、巫師、行法術的和占星家[a],為他解夢。他們都來到王面前。 3 王對他們說:「我做了一個夢,心裡煩亂,想知道夢的意思。」 4 占星家用亞蘭話對王說:「願王萬歲!請將夢告訴僕人,僕人好解釋夢的意思。」 5 王對占星家說:「我的旨意已定,你們若不能將夢和夢的意思告訴我,必被碎屍萬段,你們的家必淪為廢墟。 6 你們若能將夢和夢的意思告訴我,我必給你們禮物、賞賜和極大的尊榮。所以你們要將夢和夢的意思告訴我。」 7 他們再次對王說:「請王將夢告訴僕人,僕人好解釋夢的意思。」 8 王說:「我敢肯定,你們是在拖延時間,因為你們知道我的旨意已定, 9 你們若不將夢告訴我,我必懲治你們。你們串通起來在我面前胡言亂語,期待情況會改變。現在將夢告訴我,我就相信你們能解夢。」 10 占星家說:「王所要求的,世上無人能做到,因為再偉大、再有權勢的君王也沒問過術士、巫師或占星家這樣的事。 11 王問的事太難,除了不在人間居住的神明外,無人能為王解答。」 12 王大怒,下令處死巴比倫所有的智者。 13 於是,處死智者的諭旨發出,但以理和他的同伴都在被殺之列。
14 王的護衛長亞略奉命要處死巴比倫的智者,但以理機智、謹慎地應對。 15 他問王的護衛長亞略:「王的命令為何這樣緊急?」亞略就把情況告訴他。 16 但以理便進宮求王寬限,以便為王解夢。 17 然後,他回到居所將這事告訴同伴哈拿尼雅、米沙利和亞撒利雅, 18 要同伴祈求天上的上帝施憐憫,顯明這奧秘,以免他們和其他巴比倫的智者一起被殺。 19 這奧秘在夜間的異象中向但以理顯明,他便頌讚天上的上帝, 20 說:
「上帝的名永永遠遠當受稱頌,
因為智慧和能力都屬於祂。
21 祂改變時令和季節,廢王立王,
賜智慧給智者,賜知識給哲士。
22 祂顯明深奧隱秘之事,
洞悉暗中的隱情,
有光與祂同住。
23 我祖先的上帝啊,我感謝你,讚美你,
因你賜我智慧和能力,
應允我們的祈求,
使我們明白王的夢。」
但以理解夢
24 於是,但以理去見王指派處死巴比倫智者的亞略,對他說:「不要處死巴比倫的智者,請帶我去見王,我要為王解夢。」 25 亞略急忙帶但以理去見王,對王說:「我在被擄的猶大人中找到一個能為王解夢的。」 26 王就問又名伯提沙撒的但以理:「你能將我做的夢和夢的意思告訴我嗎?」 27 但以理回答說:「沒有智者、術士、巫師或占星家可以解答王所問的奧秘, 28-30 但天上的上帝能揭開奧秘,祂已把將來要發生的事告訴了王。王啊,你在床上夢見了將來的事,揭開奧秘的上帝已把將來的事指示給你。上帝將王做的夢啟示給我,並非因為我的智慧勝過其他人,而是要讓王知道夢的意思和王的心事。以下是王在床上做的夢和腦中出現的異象。
31 「王啊,你夢見一個高大宏偉、極其明亮的塑像站在你面前,相貌可怕, 32 有純金的頭、銀的胸和臂、銅的肚腹和大腿、 33 鐵的小腿和半鐵半泥的腳。 34 在你觀看的時候,有一塊非人手鑿出的石頭打在塑像半鐵半泥的腳上,砸碎了腳。 35 鐵、泥、銅、銀、金隨即粉碎,猶如夏天麥場上的糠秕,被風吹得無影無蹤。但打碎這像的石頭變成一座大山,充滿整個大地。
36 「這就是夢的內容。現在我們要為王解夢。 37 王啊,你是萬王之王,天上的上帝已將國度、權柄、能力和尊榮賜給你, 38 也將居住在各地的世人、走獸和飛禽都交在你手中,讓你管理。你就是那金頭。 39 在你之後,必有另一國興起,不及你的國強大。之後是將要統治天下的第三個國,是銅的。 40 接著是堅如鐵的第四國,能擊垮、打碎列國,正如鐵能擊垮、打碎一切。 41 你看見半鐵半陶泥的腳和腳趾,表示那將是一個分裂的國。正如你看見鐵和泥混雜在一起,它必有鐵一般的力量。 42 半鐵半泥的腳趾表示那國必半強半弱。 43 你看見鐵和泥混雜在一起,這表示那國的民族彼此混雜通婚,卻不能團結,正如鐵和泥無法混合。 44 在以上列王統治的時候,天上的上帝必設立一國——永不滅亡、外族無法奪其政權。這國將擊垮、消滅列國,並且永遠長存。 45 你看見那塊非人手從山中鑿出的石頭打碎鐵、銅、泥、銀和金。偉大的上帝已把將來的事告訴了王。這夢是真實的,解釋是可靠的。」
46 尼布甲尼撒王俯伏在地,向但以理下拜,並下令給他獻供物和香。 47 王對但以理說:「你們的上帝真是萬神之神、萬王之主、奧秘的啟示者,因為你能揭開這個奧秘。」 48 王賜但以理高官及許多貴重的禮物,派他治理巴比倫全省,管理巴比倫所有的智者。 49 王又應允但以理的請求,派沙得拉、米煞和亞伯尼歌負責巴比倫省的事務。但以理仍在朝中供職。
Danieli 2
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Maloto a Nebukadinezara
2 Chaka chachiwiri cha ulamuliro wake, Nebukadinezara analota maloto; anavutika mu mtima mwake ndipo analephera kugona. 2 Tsono mfumu inayitana amatsenga, owombeza, amawula ndi oyangʼana nyenyezi kuti amufotokozere zomwe analota. Pamene iwo analowa ndi kuyima pamaso pa mfumu, 3 mfumuyo inawawuza kuti, “Ndalota loto lomwe likundisautsa ndipo ndikufuna kudziwa tanthauzo lake.”
4 Pamenepa alawuli anati kwa mfumu mʼChiaramu, “Mukhale ndi moyo wautali mfumu! Tiwuzeni ife atumiki anu zimene mwalota, ndipo tidzakuwuzani tanthauzo lake.”
5 Mfumu inayankha alawuliwo kuti, “Zimene ndatsimikiza kuchita ndi izi: Ngati inu simundifotokozera zimene ndalota ndi tanthauzo lake, mudzadulidwa nthulinthuli ndipo nyumba zanu ndidzazisandutsa bwinja. 6 Koma ngati mundiwuza zimene ndalota ndi tanthauzo lake, ndidzakupatsani mphatso ndi mphotho ndi ulemu waukulu. Choncho mundiwuze zimene ndalota ndi tanthauzo lake.”
7 Iwo anayankhanso kachiwiri kuti, “Mfumu iwuze atumiki ake chimene yalota, ndipo ife tidzatanthauzira.”
8 Ndipo mfumu inayankha kuti, “Ine ndikudziwa kuti mukungozengereza kufuna kutaya nthawi chabe chifukwa mukuzindikira kuti izi ndi zimene ndatsimikiza kuchita. 9 Ngati simundiwuza zimene ndalota, chilango chake ndi chimodzi. Inu mwagwirizana kuti mundiwuze ine bodza ndi chinyengo ndi kuyembekeza kuti ine ndisintha. Tsono mundiwuze zimene ndalota, ndipo ine ndidzadziwa kuti mukhoza kunditanthauzira.”
10 Alawuli anayankha mfumu kuti, “Palibe munthu pa dziko lapansi amene akhoza kuchita chimene mfumu ikufunsa! Palibe mfumu, kaya yayikulu kapena yamphamvu bwanji imene inafunsapo amatsenga, owombeza kapena alawuli aliwonse zimenezi. 11 Zimene mfumu yafunsa ndi zapatali. Palibe wina amene angathe kuwulula izi kwa mfumu kupatula milungu, ndipo sikhala pakati pa anthu.”
12 Zimenezi zinapsetsa mtima mfumu ndipo inakwiya kwambiri kotero inalamula kuti anzeru onse a ku Babuloni aphedwe. 13 Choncho lamulo linaperekedwa kuti anthu anzeru aphedwe, ndipo anatuma anthu kukafunafuna Danieli ndi anzake kuti iwonso aphedwe.
14 Danieli anayankhula mwanzeru ndi mwaulemu kwa Ariyoki, mkulu wa asilikali olondera mfumu amene anatumidwa kukapha anthu anzeru a ku Babuloni. 15 Danieli anafunsa Ariyoki kapitawo wa mfumu kuti, “Chifukwa chiyani mfumu yapereka lamulo lankhanza lotere?” Kenaka Ariyoki anafotokoza nkhaniyi kwa Danieli. 16 Danieli anapita mofulumira kwa mfumu ndipo anamupempha kuti amupatse nthawi kuti amuwuze zimene walota ndi tanthauzo lake.
17 Kenaka Danieli anabwerera ku nyumba kwake ndi kukafotokozera anzake aja zimenezi: Hananiya, Misaeli ndi Azariya. 18 Danieli anadandaulira anzake kuti apemphe kwa Mulungu wakumwamba kuti awachitire chifundo ndi kumuwululira chinsinsi, kuti iye ndi anzakewo asanyongedwe pamodzi ndi anzeru ena onse a ku Babuloni. 19 Usiku Yehova anamuwululira Danieli chinsinsi chija mʼmasomphenya. Pamenepo Danieli anatamanda Mulungu wakumwamba, 20 ndipo anati:
“Litamandike dzina la Mulungu ku nthawi za nthawi;
nzeru ndi mphamvu zonse ndi zake.
21 Amasintha nthawi ndi nyengo;
amakweza mafumu ndipo amawatsitsanso.
Amapatsa nzeru kwa anzeru
ndi chidziwitso kwa ozindikira zinthu.
22 Amavumbulutsa zinthu zozama ndi zobisika;
amadziwa zimene zili mu mdima,
ndipo kuwunika kumakhala ndi Iye.
23 Ndikuyamika ndi kutamanda Inu Mulungu wa makolo anga:
mwandipatsa nzeru ndi mphamvu,
mwandiwululira zomwe tinakupemphani,
mwatiwululira maloto a mfumu.”
Danieli Atanthauzira Maloto
24 Motero Danieli anapita kwa Ariyoki, amene mfumu inamusankha kuti akaphe anthu anzeru a ku Babuloni, ndipo anati kwa iye, “Musaphe anthu anzeru a ku Babuloni. Ndiperekezeni kwa mfumu, ndipo ndidzayimasulira maloto ake.”
25 Ariyoki anapita naye Danieli kwa mfumu nthawi yomweyo ndipo anati, “Ndapeza munthu pakati pa akapolo ochokera ku Yuda amene akhoza kuwuza mfumu zimene maloto ake akutanthauza.”
26 Mfumu inafunsa Danieli (wotchedwanso Belitesezara) kuti, “Kodi ukhoza kundiwuza zomwe ine ndinaona mʼmaloto anga ndi tanthauzo lake?”
27 Danieli anayankha kuti, “Palibe munthu wanzeru, wowombeza, wamatsenga kapena wamawula amene akhoza kufotokozera mfumu chinsinsi chimene mwafuna kudziwa, 28 koma kuli Mulungu kumwamba amene amawulula zinsinsi. Iye waonetsera mfumu Nebukadinezara zimene zidzachitika mʼmasiku akutsogolo. Maloto ndi masomphenya anu amene munawaona mukugona pa bedi lanu ndi awa:
29 “Mukugona pa bedi, inu Mfumu, maganizo anakufikirani a zinthu zakutsogolo, ndipo Yehova wowulula zinsinsi anakuonetserani zimene zidzachitika. 30 Koma chinsinsi ichi chavumbulutsidwa kwa ine, si chifukwa chakuti ndili ndi nzeru zochuluka kuposa anthu ena onse, koma kuti mfumu mudziwe tanthauzo la maloto anu ndi kuti muzindikire maganizo amene anali mu mtima mwanu.
31 “Inu mfumu, munaona chinthu chowumba chachikulu chimene chinayima pamaso panu. Chowumbachi chinali chonyezimira mʼmaonekedwe. 32 Mutu wa chowumbacho unali wagolide wabwino kwambiri. Chifuwa ndi manja ake zinali zasiliva. Mimba ndi ntchafu zake zinali zamkuwa. 33 Miyendo yake inali yachitsulo, mapazi ake anali achitsulo chosakaniza ndi dongo. 34 Inu mukuona, mwala unagamuka, koma osati ndi manja a munthu. Unagwera fanolo pa mapazi ake achitsulo chosakaniza ndi dongo aja ndi kuwaphwanya. 35 Tsono chitsulo, dongo, mkuwa, siliva ndi golide zonse zinaphwanyika pamodzi ndikukhala tizidutswa towuluka ndi mphepo ngati mungu wa mowombera tirigu nthawi ya chilimwe. Zonse zinawuluka ndi mphepo osasiyako chilichonse. Koma mwala umene unagwera pa chowumba chija unasanduka phiri lalikulu ndi kudzaza dziko lonse lapansi.
36 “Maloto aja ndi amenewa; tidzafotokoza tanthauzo lake kwa mfumu. 37 Inu mfumu, ndinu mfumu ya mafumu. Mulungu wakumwamba wakupatsani ufumu, ulamuliro ndi mphamvu ndi ulemerero; 38 Iye anayika mʼmanja mwanu anthu ndi nyama zakuthengo ndi mbalame zamlengalenga. Kulikonse kumene zikhala, iye anakuyikani wolamulira wa zonse. Inu ndinu mutu wagolidewo.
39 “Pambuyo pa inu, ufumu wina udzadzuka, wochepa mphamvu poyerekeza ndi wanuwu. Padzabweranso ufumu wachitatu, wamkuwa, udzalamulira dziko lonse lapansi. 40 Pomaliza, padzakhala ufumu wachinayi, wolimba ngati chitsulo popeza chitsulo chimaphwanya ndi kutikita chilichonse. Ndipo monga chitsulo chimaphwanya zinthu ndikuteketeratu, choncho udzawononga ndi kuphwanya maufumu ena onse. 41 Ndipo monga munaonera kuti mapazi ndi zala zake zinali za chitsulo chosakaniza ndi dongo, choncho uwu udzakhala ufumu wogawikana; komabe udzakhala ndi mphamvu zina zachitsulo zotikita. 42 Monga zala zinali za chitsulo chosakaniza ndi dongo, choncho ufumu uwu udzakhala pangʼono wolimba ndi pangʼono wofowoka. 43 Ndipo monga munaona chitsulo chosakanizidwa ndi dongo, choncho anthu adzakhala wosakanizana ndipo sadzagwirizana, monga muja chitsulo sichingasakanizike ndi dongo.
44 “Pa nthawi ya mafumu amenewo, Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu umene sudzawonongedwa, kapenanso kuperekedwa kwa anthu ena. Udzawononga maufumu onse aja ndi kuwatheratu, koma iwo wokha udzakhalapobe mpaka muyaya. 45 Limeneli ndilo tanthauzo la masomphenya a mwala umene unagamuka pa phiri, koma osati ndi manja a anthu; mwala umene unaphwanya chitsulo, mkuwa, dongo, siliva ndi golide mʼtizidutswa.
“Mulungu wamkulu wakuonetsani mfumu chimene chidzachitika kutsogolo. Malotowo ndi woona ndipo tanthauzo lake ndi lodalirika.”
46 Pamenepo mfumu Nebukadinezara inadzigwetsa chafufumimba pamaso pa Danieli ndi kumupatsa ulemu. Ndipo inalamula kuti anthu onse amuthirire Danieli nsembe ndi kumufukizira lubani. 47 Mfumu inati kwa Danieli, “Zoonadi, Mulungu wako ndi Mulungu wa milungu ndi Ambuye wa mafumu ndi wowulula zinsinsi, pakuti iwe wathadi kuwulula chinsinsi ichi.”
48 Ndipo mfumu inamukweza Danieli ndi kumupatsa mphatso zambiri. Anamuyika kuti akhale wolamulira chigawo chonse cha Babuloni ndi kutinso akhale woyangʼanira anthu ake onse anzeru. 49 Komanso, monga mwa pempho la Danieli, mfumu inayika Sadirake, Mesaki ndi Abedenego, kuti akhale oyangʼanira chigawo cha Babuloni, pamene Danieliyo ankakhazikika mʼbwalo la mfumu.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.