Genesis 23
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Kumwalira kwa Sara
23 Sara anakhala ndi moyo zaka 127. 2 Anamwalirira ku Kiriyati-Araba, kumeneku ndi ku Hebroni, mʼdziko la Kanaani, ndipo Abrahamu anapita kukakhuza maliro a Sara, namulirira.
3 Kenaka Abrahamu ananyamuka pamene panali mtembo wa mkazi wakepo kupita kukayankhula ndi anthu a ku Hiti. Ndipo anati, 4 “Ine ndine mlendo wongoyendayenda kwanu kuno. Bwanji mundigulitse malo woti akhale manda kuti ndiyikepo thupi la mkazi wanga.”
5 Anthu a ku Hiti aja anamuyankha Abrahamu kuti, 6 “Tatimverani mbuye wathu, inu ndinu mwana wa mfumu wamkulu pakati pathu. Chonde ikani thupi la mkazi wanu mʼmanda aliwonse amene mungafune. Palibe mmodzi wa ife amene adzakukanizani manda ake kuti musayike mkazi wanu.”
7 Tsono Abrahamu anayimirira naweramira anthu a dziko la Hiti aja 8 nati, “Ngati mwaloladi kuti ndiyike mkazi wanga kuno, ndiye ndimvereni. Mundipemphere kwa Efroni mwana wa Zohari 9 kuti andigulitse phanga la Makipela, limene lili kumapeto kwa munda wake. Mumupemphe kuti andigulitse pamtengo wake ndithu inu mukuona kuti akhale manda.”
10 Pamenepo nʼkuti Efroni Mhiti ali pomwepo pakati pa anthuwo amene anabwera ku chipata cha mzindawo. Ndipo onse akumva anamuyankha Abrahamu 11 nati, “Ayi mbuye wanga tandimverani, ine ndikukupatsani mundawo ndiponso phanga limene lili mʼmenemo. Ndikukupatsani malowa pamaso pa anthu a mtundu wanga. Chonde ikani mtembo wamkazi wanu.”
12 Apo Abrahamu anaweramanso mwaulemu pamaso pa anthu a mʼdzikolo 13 ndipo anthu onse akumva Abrahamu anati kwa Efroni, “Ngati kungatheke, chonde ndimvereni. Ine ndichita kugula mundawu. Landirani ndalama za mundawu kuti ine ndiyike mkazi wanga mʼmenemo.”
14 Koma Efroni anamuyankha Abrahamu nati, 15 “Mundimvere mbuye wanga; mundawo mtengo wake ndi masekeli asiliva okwana 400. Koma zimenezo nʼchiyani pakati pa ine ndi inu? Ikani mtembo wa mkazi wanu.”
16 Abrahamu anavomera mtengo umene ananena Efroni Ahiti onse akumva ndipo anamuwerengera masekeli asiliva okwana 400 monga mwa mtengo wa ndalama umene amalonda a nthawi imeneyo ankagwiritsa ntchito.
17 Choncho munda wa Efroni wa ku Makipela umene unali kufupi ndi Mamre, kuphatikiza munda, phanga linali mʼmenemo pamodzi ndi mitengo yonse ya mʼmundamo, zinaperekedwa 18 kwa Abrahamu ngati chuma chake pamaso pa anthu onse a ku Hiti amene anabwera ku chipata cha mzindawo. 19 Zitatha izi, Abrahamu anayika mkazi wake Sara mʼphanga la mʼmunda wa ku Makipela, kufupi ndi ku Mamre (kumene ndi ku Hebroni) mʼdziko la Kanaani. 20 Choncho Ahiti anapereka munda pamodzi ndi phanga la mʼmenemo kwa Abrahamu kuti akhale manda.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.